Pitani ku nkhani yake

Pitani ku mitu ya nkhani

Anali Kukondwera ndi Chilamulo cha Yehova

Anali Kukondwera ndi Chilamulo cha Yehova

Anali Kukondwera ndi Chilamulo cha Yehova

ALBERT D. SCHROEDER, wa m’Bungwe Lolamulira la Mboni za Yehova, anamaliza moyo wake wapadziko lapansi Lachitatu, pa March 8, 2006. Anali ndi zaka 94 ndipo anathera zaka zoposa 73 mu utumiki wa nthawi zonse.

Mbale Schroeder anabadwira ku Saginaw, ku Michigan, m’dziko la Unites States, m’chaka cha 1911. * Ali mwana, anaphunzira zambiri za Baibulo kuchokera kwa agogo ake aakazi akuchikazi, amenenso anamuphunzitsa kukonda kuwerenga Mawu a Yehova. Anaphunzira Chilatini, Chijeremani, ndi ntchito zamagetsi pa yunivesite ya Michigan. Komabe, atayamba kukonda kwambiri Malemba, anasiya maphunziro akewo kuti ayambe kulalikira za Ufumu nthawi zonse. M’chaka cha 1932 anayamba kutumikira pa Beteli ku Brooklyn, New York.

Mu 1937, ali ndi zaka 26, Mbale Schroeder anasankhidwa kuti azikayang’anira ntchito ya Mboni za Yehova ku Britain. Chifukwa cha khama lake, anthu ambiri kumeneko analimbikitsidwa kuyamba utumiki wa nthawi zonse. Mnyamata wina amene anakhalapo naye ku Beteli ya ku London anali John E. Barr. Kenako anakatumikira limodzi kwa zaka zambiri m’Bungwe Lolamulira.

Ntchito imene Mbale Schroeder ankagwira m’malo mwa Mboni za Yehova, inali kuoneka m’zaka zimene kunali nkhondo. Mu August 1942 anapitikitsidwa kuchoka ku Britain. Pambuyo pa ulendo wotopetsa wodutsa panyanja ya Atlantic m’nthawi ya nkhondo yachiwiri ya padziko lonse, anafikanso ku Brooklyn mu September.

Panthawi imeneyo, atumiki a Yehova anali akuyembekezera kuti pambuyo pa nkhondo yachiwiri ya padziko lonse padzakhala ntchito yaikulu yofunika kuigwira. Mbale Schroeder anadabwa komanso anali wachimwemwe kulandira utumiki wina, woti athandize kukonza maphunziro a Sukulu ya Gileadi Yophunzitsa Baibulo. Kwa zaka zingapo, anatumikira kumeneko monga mlangizi, ndipo anali kuthandiza nawo kuphunzitsa amishonale. Ophunzira amene anawaphunzitsa ku Gileadi ndipo kenako pa Sukulu ya Utumiki wa Ufumu, amakumbukirabe mmene iye ankaphunzitsira. Ankakonda kuphunzitsa ophunzira ake kukonda malamulo a Mulungu ndi kutsindika kufunika kodziwa Yehova.

M’chaka cha 1956, Mbale Schroeder anakwatira Charlotte Bowin, ndipo mwana wawo, Judah Ben, anabadwa mu 1958. Mbale Schroeder anali mwamuna ndiponso bambo wachikristu wabwino. M’chaka cha 1974, anayamba kutumikira m’Bungwe Lolamulira, ndipo anthu omwe ankagwira naye ntchito anali kuyamikira kwambiri luntha lake. Anali munthu wokoma mtima ndiponso wodzichepetsa, amene koposa zonse, ankafuna kukweza dzina la Mulungu. Tili ndi chikhulupiriro kuti Mbale Schroeder analandira mphoto yake monga Mkristu wodzozedwa, amene moonadi, ‘anali kukondwera ndi chilamulo cha Yehova.’​—Salmo 1:2.

[Mawu a M’munsi]

^ ndime 3 Nkhani ya moyo wa Mbale Schroeder inasindikizidwa mu Nsanja ya Olonda ya March 1, 1988.