Pitani ku nkhani yake

Pitani ku mitu ya nkhani

Ofatsa Adzalandira Dziko Lapansi

Ofatsa Adzalandira Dziko Lapansi

 Ofatsa Adzalandira Dziko Lapansi

“Ndikuganiza kuti chilengedwe chidzakonzedwa ndi kubwezeretsedwanso. . . . Osati posachedwapa ayi, koma m’tsogolo kwambiri, pamene kudzakhale kumwamba kwatsopano ndi dziko lapansi latsopano.”​—Anatero katswiri wina wa zachilengedwe wa ku France, Jean-Marie Pelt.

POMVA chisoni ndi mmene chilengedwe komanso anthu akukhalira padziko lapansi pano, ambiri angasangalale kuona dziko lathuli litasanduka paradaiso. Komabe, chiyembekezo chimenechi sichinayambe lero ayi. Kalekale, Baibulo linalonjeza za kubwezeretsedwa kwa Paradaiso padziko lapansi. Mawu a Yesu akuti, “ofatsa . . . adzalandira dziko lapansi” ndiponso akuti “monga kumwamba chomwecho pansi pano,” ndi ena mwa mawu odziwika bwino kwambiri a m’Malemba. (Mateyu 5:5; 6:10) Komabe, masiku ano, si anthu ambiri amene amakhulupirira kuti anthu ofatsa adzakhala m’paradaiso padziko lapansi. Chifukwa chakuti anthu ambiri amene amadzitcha Akristu, sakhulupiriranso kuti kudzakhala Paradaiso.

Magazini ina ya ku France yotuluka mlungu uliwonse, ya La Vie, inafotokoza chifukwa chimene makamaka Tchalitchi cha Katolika chinasiyira kukhulupirira za paradaiso, kaya wa padziko lapansi pano kapena kumwamba. Inati: “Pambuyo pokhala mbali yaikulu ya ziphunzitso za Chikatolika kwa zaka zosachepera 1,900, [chiphunzitso cha] paradaiso sichikuphunzitsidwanso ku mibindikiro yauzimu, pa mapemphero a Lamlungu, m’maphunziro a ubusa, ndi m’makalasi a katekisima.” Anthu amati mawu oti paradaiso “n’ngovuta kuwamvetsa ndiponso ndi osokoneza.” Alaliki ena amapewa mwadala kugwiritsa ntchito mawuwa chifukwa “amabweretsa zithunzithunzi zambiri m’maganizo a anthu, za chimwemwe m’paradaiso padziko lapansi.”

Kwa Frédéric Lenoir, katswiri woona zamakhalidwe a anthu yemwe anaphunzira makamaka za chipembedzo, ziphunzitso za paradaiso zangosanduka “zikhulupiriro zopanda maziko.” N’chimodzimodzinso ndi Jean Delumeau, wolemba mbiri ndiponso amene analemba mabuku angapo pankhani imeneyi. Iye amaganiza kuti malonjezo a m’Baibulo makamaka adzakwaniritsidwa mophiphiritsa. Analemba kuti: “Pafunso lakuti, ‘Kodi chiphunzitso cha Paradaiso chidakalipobe?’ chikhulupiriro cha Akristu chimapereka yankho lakuti: Tiziyamikira chifukwa cha kuuka kwa Mpulumutsi, tsiku lina tidzagwirana manja ndipo tidzaona chimwemwe.”

Kodi uthenga wa dziko lapansi la paradaiso n’ngofunikabe? Kodi tingayembekezere zotani m’tsogolomu makamaka ponena za dziko lapansi? Kodi chithunzi cha tsogolo lathu n’chosaoneka bwino kapena n’zotheka kuti chikhale chooneka bwino? Nkhani yotsatirayi iyankha mafunso amenewa.

 [Mawu a Chithunzi patsamba 2]

COVER: Emma Lee/​Life File/​Getty Images