Pitani ku nkhani yake

Pitani ku mitu ya nkhani

Mafunso Ochokera kwa Owerenga

Mafunso Ochokera kwa Owerenga

Mafunso Ochokera kwa Owerenga

Chiyeso chomaliza chikadzatha pamapeto pa Zaka 1,000, kodi zizidzatheka kuti anthu achimwe ndi kufa?

Malemba awiri opezeka m’buku la Baibulo la Chivumbulutso amatithandiza kupeza yankho la funso limeneli motere: “Imfa ndi Hade zinaponyedwa m’nyanja yamoto. Iyo ndiyo imfa yachiwiri, ndiyo nyanja yamoto.” (Chivumbulutso 20:14) “Adzawapukutira misozi yonse kuichotsa pamaso pawo; ndipo sipadzakhalanso imfa; ndipo sipadzakhalanso maliro, kapena kulira, kapena chowawitsa; zoyambazo zapita.”​—Chivumbulutso 21:4.

Taonani nthawi imene ikutchulidwa pano. Kuponyedwa m’nyanja ya moto kwa “imfa ndi Hade” kudzachitika anthu opulumuka pa Armagedo, anthu oukitsidwa, ndi anthu onse amene adzabadwe pambuyo pa Armagedo ataweruzidwa mogwirizana ndi “zolembedwa m’mabuku,” kapena kuti zinthu zonse zimene Yehova adzafune kuti anthu akwaniritse m’zaka 1,000. (Chivumbulutso 20:12, 13) Mtumwi Yohane analemba masomphenya enanso, amene amapezeka m’buku la Chivumbulutso chaputala 21, amene adzakwaniritsidwe mu Ulamuliro wa Zaka 1,000 wa Kristu Yesu. Komabe, kukwaniritsidwa kwa masomphenya amenewo, kudzachitika makamaka pamapeto pa zaka 1,000, pa Tsiku la Chiweruzo. Zikadzatero, Yehova adzakhaladi ndi anthu popanda amkhalapakati, chifukwa Yesu adzakhala atapereka Ufumu kwa Atate wake. Yehova adzakhala mophiphiritsira ndi “anthu ake” m’njira yokhalitsa ndi yachindunji. Lonjezo lakuti “sipadzakhalanso imfa” lidzakwaniritsidwa anthu akadzafika pa ungwiro chifukwa chakuti mtengo wa nsembe ya dipo ya Kristu udzakhala utagwiradi ntchito yake.​—Chivumbulutso 21:3, 4.

Choncho, imfa imene inatchulidwa m’malemba amene agwidwa mawu pamwambapa ndi imfa ya Adamu, imene idzachotsedwa ndi dipo la Kristu. (Aroma 5:12-21) Imfa imene anthu anabadwa nayo kuchokera kwa munthu woyambirira ikadzatha, anthu adzakhala ngati mmene Adamu analili atangolengedwa. Adamu anali wangwiro, koma zimenezo sizinatanthauze kuti sakanatha kufa ayi. Yehova anauza Adamu kuti asadye zipatso za “mtengo wakudziwitsa zabwino ndi zoipa” ndipo anati: “Tsiku lomwe udzadya umenewo udzafa ndithu.” (Genesis 2:17) Imeneyo inali imfa imene inabwera chifukwa cha kuchimwa mwadala. Pambuyo pa chiyeso chomaliza pamapeto pa Ulamuliro wa Zaka 1,000, anthu adzakhalabe ndi ufulu wosankha zochita. (Chivumbulutso 20:7-10) Azidzatha kusankha kaya kupitiriza kutumikira Yehova kapena ayi. Choncho, sitinganene kuti palibe munthu amene adzapandukire Mulungu monga mmene anachitira Adamu.

Kodi chidzachitike n’chiyani kwa munthu amene adzasankhe kupanduka pambuyo pa chiyeso chomaliza pomwe imfa ndi Hade kudzakhala kulibe? Panthawi imeneyo, kudzakhala kulibe imfa ya Adamu. Ndiponso kudzakhala kulibe Hade, kapena kuti manda a anthu onse okhala ndi chiyembekezo chachiukiriro. Komabe, Yehova angadzawononge munthu aliyense wopanduka mwa kum’ponya m’nyanja ya moto, osam’patsa chiyembekezo chilichonse cha kuuka. Imfa imeneyo idzakhala yofanana ndi imfa imene anafa Adamu ndi Hava, osati ngati imfa imene anthu amabadwa nayo kuchokera kwa Adamu.

Komabe, palibe chifukwa choyembekezera kuti zinthu zotere zidzachitika. Anthu amene adzapambane chiyeso chomaliza adzakhala osiyana ndi Adamu pa chinthu chimodzi chachikulu. Adzakhala atayesedwa mokwanira. Tingatsimikize kuti chiyeso chomaliza chidzakhala chokwanira chifukwa Yehova amadziwa kusanthula mitima ya anthu. Sitikukayikira kuti chiyeso chomaliza chidzachotseratu aliyense amene adzagwiritse ntchito molakwa ufulu wake wosankha. Choncho, ngakhale kuli kotheka kuti anthu amene adzapambane chiyeso chomaliza angadzapandukire Mulungu, n’kuwonongedwa, n’zokayikitsa kwambiri kuti zimenezi zidzachitika.

[Chithunzi patsamba 31]

Kodi ndi motani mmene anthu adzakhalire ofanana ndi Adamu pambuyo pa chiyeso chomaliza?