Pitani ku nkhani yake

Pitani ku mitu ya nkhani

Opani Yehova Kuti Mukhale Achimwemwe

Opani Yehova Kuti Mukhale Achimwemwe

 Opani Yehova Kuti Mukhale Achimwemwe

“Wodala munthu wakuopa Yehova.”​—SALMO 112:1.

1, 2. Kodi kuopa Yehova kungabweretse chiyani?

SIZOPHWEKA kukhala wachimwemwe. Kuti munthu apeze chimwemwe chenicheni amafunika kusankha ndi kuchita zinthu moyenera ndiponso kupewa zoipa. Mlengi wathu, Yehova, watipatsa Mawu ake, Baibulo, kuti atiphunzitse kukhala moyo wabwino kwambiri. Posonyeza kuopa Yehova mwa kufunafuna ndi kutsatira malangizo ake, tingathe kukhala osangalala ndiponso achimwemwe chenicheni.​—Salmo 23:1; Miyambo 14:26.

2 M’nkhani ino, tiona zitsanzo za m’Baibulo ndi za masiku ano zosonyeza kuti kuopa Mulungu zenizeni kumalimbikitsa munthu kuyesetsa kupewa zoipa n’kumachita zabwino. Tiona kuti kuopa Mulungu kungatithandize kukhala achimwemwe potilimbikitsa kuchoka m’njira yolakwika, monga momwe anachitira Mfumu Davide. Tionanso kuti kuopa Yehova ndi cholowa chamtengo wapatali kwambiri chimene makolo angathe kupereka kwa ana awo. Inde, Mawu a Mulungu amatitsimikizira kuti: “Wodala munthu wakuopa Yehova.”​—Salmo 112:1.

Kukhalanso Achimwemwe

3. Kodi n’chiyani chinam’thandiza Davide atachimwa?

3 Monga tinaonera m’nkhani yapita ija, katatu konse Davide sanasonyeze kuopa Mulungu ndipo anachimwa. Komabe, anaonetsa kuti anali munthu woopa Mulungu chifukwa cha mmene anachitira ndi chilango chimene analandira kwa Yehova. Chifukwa choopa ndi kulemekeza Mulungu, iye anavomereza kulakwa kwake, anakonza njira yake n’kukhalanso ndi ubwenzi wabwino ndi Yehova. Ngakhale kuti zolakwa zakezo zinabweretsa mavuto kwa iyeyo ndi anthu ena, Yehova anapitiriza kumuthandiza ndi kumudalitsa chifukwa cholapa mochoka pansi pa mtima. Ndithu, chitsanzo cha Davide chingalimbitse mtima Akristu masiku ano ngati atachita tchimo lalikulu.

4. Kodi kuopa Mulungu kungathandize bwanji munthu kukhalanso wachimwemwe?

 4 Taganizirani chitsanzo cha Sonja. * Sonja anali mlaliki wanthawi zonse, koma anapezeka kuti wayamba kugwirizana ndi anthu amakhalidwe oipa mpaka kuchita zinthu zosemphana ndi makhalidwe achikristu, moti anachotsedwa mumpingo. Sonja atazindikira kulakwa kwake, anayesetsa kukonza ubwenzi wake ndi Yehova. Patapita nthawi, iye anabwezeretsedwa mumpingo. Nthawi yonseyi, Sonja sanasiye mtima wake wofuna kutumikira Yehova. Patsogolo pake, anayambanso utumiki wanthawi zonse wa upainiya. Kenaka anakwatirana ndi mkulu wachitsanzo chabwino, ndipo tsopano akutumikira limodzi mumpingo wawo. Ngakhale kuti Sonja amachita chisoni akaganiza zoti kwakanthawi anachoka m’njira yachikristu, iye n’ngosangalala kuti kuopa Mulungu kunam’thandiza kubwerera kwa Yehova.

Ndi Bwino Kuvutika Kusiyana N’kuchimwa

5, 6. Longosolani mmene zinakhalira kuti Davide asaphe Sauli kawiri konse ndipo n’chifukwa chiyani sanatero?

5 Inde, ndi bwino kupeweratu kuchimwa chifukwa choopa Mulungu. Zimenezi zinam’chitikirapo Davide. Nthawi ina Sauli, ali ndi asilikali 3,000 ankasakasaka Davide ndipo analowa m’phanga lomwe Davideyo anabisalamo ndi asilikali ake. Asilikaliwo analimbikitsa Davide kuti aphe Sauli. Iwo ankaona kuti Yehova ndiye wapereka mdani woopsa wa Davideyu m’manja mwake. Davide anayenda monyang’ama n’kufika panali Sauli n’kudulako pang’ono chovala cha Sauliyo. Popeza Davide ankaopa Mulungu, ngakhale zinthu zazing’ono zimene anachitazi zinam’pweteka chikumbumtima. Asilikali a Davide mitima inali m’mwamba koma iye anawauza kuti azipita, ponena kuti: “Mulungu andiletse kuchitira ichi mbuye wanga, wodzozedwa wa Yehova.” *​—1 Samueli 24:1-7.

6 Panthawi ina kutawadera, Sauli anamanga mahema, ndipo iye ndi asilikali ake onse anagona “tulo tatikulu tochokera kwa Yehova.” Davide ndi msilikali wolimba mtima Abisai, amene anali mwana wa mlongo wake, analowerera mozemba n’kufika pakati pa malo amene anamanga mahemapo n’kuimirira pamene panagona Sauli. Abisai anafuna zoti angothana naye Sauliyo pomupha. Koma Davide anam’letsa Abisai pomufunsa kuti: “Ndani adzasamula dzanja lake pa wodzozedwa wa Mulungu, ndi kukhala wosachimwa?”​—1 Samueli 26:9, 12.

7. N’chiyani chinathandiza Davide kuti asachimwe?

7 N’chifukwa chiyani Davide sanaphe Sauli atapeza mwayi wotero kawiri konse? Chifukwa chakuti ankaopa Yehova koposa Sauli. Chifukwa choopa Mulungu m’njira yoyenera, Davide analolera kuti avutike ngati atafunika kutero, kusiyana n’kuti achimwe. (Ahebri 11:25) Iye sankakayikira ngakhale pang’ono kuti Yehova amasamalira anthu ake ngakhalenso iyeyo payekha. Davide ankadziwa kuti kumvera ndi kukhulupirira Mulungu kungam’patse chimwemwe ndi madalitso ambiri koma kunyalanyaza Mulungu kungachititse kuti Mulungu asiye kumuyanja. (Salmo 65:4) Iye ankadziwanso kuti panthawi yake ndi m’njira yake, Mulungu adzakwaniritsa lonjezo lake lomuika iyeyo pa ufumu n’kuchotsapo Sauli.​—1 Samueli 26:10.

Kuopa Mulungu Kumabweretsa Chimwemwe

8. Kodi zimene Davide anachita ali pamavuto zimatipatsa chitsanzo m’njira yotani?

8 Akristufe timakhala okonzeka kunyozedwa, kuzunzidwa, ndiponso kukumana ndi ziyeso zina. (Mateyu 24:9; 2 Petro 3:3) Nthawi zina mavuto athu amakhalapo chifukwa cha olambira anzathu. Komabe timadziwa kuti Yehova amaona zinthu zonse, amamva mapemphero athu, ndipo panthawi yoyenera, adzakonza zinthu mogwirizana ndi chifuniro chake. (Aroma 12:17-21; Ahebri 4:16) Motero, sitiopa otitsutsa koma timaopa Mulungu ndipo timadalira iyeyo kuti atipulumutse. Monga Davide, sitifuna kubwezera kapena kuphwanya mfundo za makhalidwe olungama n’cholinga choti tipewe mavuto enaake. Mapeto ake, timakhala achimwemwe. Koma kodi zimenezi zimatheka bwanji?

9. Perekani chitsanzo cha mmene kuopa Mulungu kungathandizire munthu kukhala wosangalala ngakhale akuzunzidwa.

9 Mbale wina amene kwa nthawi yaitali wakhala akuchita umishonale ku Africa anati:  “Ndimaganizira chitsanzo cha mayi wina ndi mwana wake wamkazi wa zaka zosakwana 20, omwe anakana kugula makadi a chipani chifukwa chosafuna kulowerera nawo m’zandale poti ndi Akristu. Gulu la abambo linawamenya kwadzaoneni kenaka n’kuwauza kuti azipita kwawo. Akuyenda, mayi uja ankatonthoza mwana wakeyo, chifukwa sankamvetsa kuti zoterezi zinali kuchitika chifukwa chiyani. N’zoona kuti panthawiyi iwo sanali osangalala komabe anali ndi chikumbumtima choyera. Pambuyo pake, iwo anali osangalala kuti anamvera Mulungu. Akanagula makadiwo gulu lija likanasangalala kwambiri. Abambowo akanawapatsa zakumwa zoziziritsa kukhosi ndipo akanavina njira yonse mpaka kukawafikitsa pakhomo pawo. Koma mtsikanayo ndi mayi ake, akanakhumudwa kwambiri podziwa kuti agonja.” Kuopa Mulungu kunawathandiza kupewa zimenezi.

10, 11. Kodi mayi wina anapindula bwanji chifukwa choopa Mulungu?

10 Kuopa Mulungu kumathandizanso munthu kukhala wosangalala akamakumana ndi ziyeso zokhudza kulemekeza moyo. Pamene Mary anali ndi pakati pa mwana wake wachitatu, dokotala anamulimbikitsa kuti achotse pakatipo. Dokotalayo anati: “Mayi simuli bwino ngakhale pang’ono. Nthawi iliyonse mungathe kudwala kwambiri n’kufa pasanathe maola 24. Zikatere mwanayonso afa. Ngakhale mwanayo atapanda kufa, n’zokayikitsa kuti adzakhala mwana wabwinobwino.” Mary anali akuphunzira Baibulo ndi Mboni za Yehova koma anali asanabatizidwe. Iye anati: “Komabe ndinali nditatsimikiza kale kutumikira Yehova, ndipo ndinkafunitsitsa kupitiriza kumumvera ngakhale zinthu zitavuta bwanji.”​—Eksodo 21:22, 23.

11 Ali ndi pakati choncho, Mary analimbikira kuphunzira Baibulo ndi kusamalira banja lake. Kenaka mwana uja anabadwa. Mary anati: “Pobereka mwana ameneyu ndinavutika kwambiri poyerekezera ndi mmene ndinavutikira pobereka mwana wanga woyamba ndi wachiwiri, koma zonse zinayenda bwino.” Kuopa Mulungu kunathandiza Mary kukhala ndi chikumbumtima chabwino, ndipo posakhalitsa anabatizidwa. Polera mwanayo anamuphunzitsanso kuopa Yehova, ndipo tsopano akutumikira pa ofesi ya nthambi ya Mboni za Yehova.

‘Dzilimbitseni mwa Yehova’

12. Kodi kuopa Mulungu kunamulimbitsa bwanji Davide?

12 Kuopa Yehova kunathandiza Davide kupewa kuchita zoipa ndipo kunam’thandiza m’njira zinanso. Kunam’limbikitsa kuchita zinthu motsimikiza ndiponso mwanzeru pamene anakumana ndi zovuta. Kwa chaka chimodzi ndi miyezi inayi, Davide ndi asilikali ake anathawa Sauli n’kukabisala ku Zikilaga m’dziko la Afilisti. (1 Samueli 27:5-7) Nthawi ina iwowa atachokapo, gulu la Aamaleki linalowerera mumzinda wawo, kuuyatsa moto n’kutenga akazi awo onse, ana awo onse, ndi nkhosa zawo zonse. Atabwerera n’kuona zimene zachitika, Davide ndi asilikali ake analira. Posakhalitsa chisoni chija chinasanduka ukali, ndipo asilikaliwo anayamba kunena zoti am’ponya miyala Davideyo kuti afe. Ngakhale kuti Davide anali atavutika maganizo, sanataye mtima. (Miyambo 24:10) Chifukwa choopa Mulungu, iye anadalira Yehova ndipo “anadzilimbikitsa mwa Yehova.” Mothandizidwa ndi Mulungu, Davide ndi asilikali ake anagonjetsa Aamaleki ndi kuwalandanso zinthu zawo zonse zija.​—1 Samueli 30:1-20.

13, 14. Kodi kuopa Mulungu kunathandiza bwanji Mkristu wina kusankha zinthu bwino?

13 Atumiki a Mulungu masiku ano amakumananso ndi mavuto ofunika kuti munthu akhulupirire Yehova ndi kulimba mtima kuti athe kuchita zinthu motsimikiza. Mwachitsanzo, taganizirani za Kristina. Ali mwana, Kristina ankaphunzira Baibulo ndi Mboni za Yehova. Koma ankafuna kuti akadzakula adzakhale katswiri woimba nyimbo pa piyano, ndipo anayesetsa kulimbikira kwambiri kuti atero. Komanso kulalikira ankachita nako manyazi motero ankaopa udindo umene adzakhale nawo akadzabatizidwa. Kristina atapitiriza kuphunzira Mawu a Mulungu anayamba kuona mphamvu yake. Anali kuphunzira kuopa Yehova, ndipo anazindikira kuti Yehova amafuna kuti atumiki ake azim’konda ndi mtima wawo wonse, nzeru zawo zonse, ndi mphamvu zawo zonse. (Marko 12:30) Zimenezi zinam’chititsa kuti adzipereke kwa Yehova ndi kubatizidwa.

14 Kristina anapempha Yehova kuti amuthandize kupita patsogolo mwauzimu. Iye anati: “Ndinkadziwa  kuti katswiri woimba nyimbo pa piyano amakhala moyo woyendayenda ndipo pachaka amatha kukaimba m’malo osiyanasiyana mwina ka 400. Motero ndinaganiza kuti ndingokhala mphunzitsi kuti ndizitha kudzisamalira ndi kuchita utumiki wa nthawi zonse.” Panthawiyi, Kristina anali kale pa ndandanda yoti akaimbe piyano m’holo kwa nthawi yoyamba ndipo malo ake anali holo yodziwika kwambiri ya m’dziko mwawo. Kristina anati: “Nthawi yanga yoyamba kuimba piyano pagulu inalinso nthawi yanga yotsiriza.” Tikunena pano, Kristina anakwatiwa ndi mkulu mumpingo. Iwo akutumikira limodzi pa ofesi ina ya nthambi ya Mboni za Yehova. Iye n’ngosangalala kuti Yehova anamulimbikitsa kusankha zinthu bwino ndi kuti tsopano akutha kugwiritsa ntchito nthawi ndi mphamvu zake pom’tumikira.

Cholowa Chamtengo Wapatali

15. Kodi Davide ankafuna kuwasiyira cholowa chotani ana ake, ndipo kodi anatero motani?

15 Davide analemba kuti: “Idzani ananu ndimvereni ine: ndidzakulangizani zakumuopa Yehova.” (Salmo 34:11) Monga tate, Davide ankafunitsitsa kusiyira ana ake cholowa chamtengo wapatali, chomwe chinali kuopa Yehova zenizeni komanso moyenera. Mwa mawu ndiponso zochita zake, Davide anasonyeza kuti Yehova si Mulungu woopsa, wovuta kumusangalatsa, yemwe amangodikira kuti atole munthu chifukwa akangophonyetsa malamulo ake pang’ono. Koma anasonyeza kuti Yehova ndi Mulungu wachikondi, wosamalira ndiponso Tate wokhululukira ana ake a padziko lapansi pano. Davide anafunsa kuti: “Kodi ndani angawerengetsere zolakwa?” Kenaka, posonyeza kusakayika kuti Yehova sakhalira kuona zolakwa zathu, Davide ananenanso kuti: “Musandiimbe mlandu pa zinthu zosaonedwa!” Davide ankakhulupirira kuti atayesetsa kwambiri, mawu ake ndi maganizo ake angakhale  ovomerezeka kwa Yehova.​—Salmo 19:12, 14, Baibulo la Byington.

16, 17. Kodi makolo angaphunzitse bwanji ana kuopa Yehova?

16 Davide ndi chitsanzo kwa makolo masiku ano. Ralph amene akutumikira pa ofesi ya nthambi ya Mboni za Yehova pamodzi ndi mng’ono wake anati: “Makolo athu anatilera mwakuti tizisangalala kuti tili m’choonadi. Tili ana, ankatifunsa maganizo athu akamakambirana za kumpingo, ndipo tinayamba kukonda kwambiri choonadi monga iwowo. Anatilera m’njira yakuti tizikhulupirira kuti tingathe kuchita zinthu zopindulitsa mu utumiki wa Yehova. Ndipotu, kwa zaka zingapo banja lathu linkakhala m’dziko limene mukufunika ofalitsa ambiri a Ufumu, moti linathandiza kuyambitsa mipingo yatsopano m’dzikomo.

17 “Chinatithandiza kusachoka m’njira yoyenera si malamulo okhwima ambirimbiri koma n’chifukwa choti makolo athu ankaona kuti Yehova ndi weniweni ndipo n’ngokoma mtima zedi ndiponso n’ngwabwino. Ankafunitsitsa kum’dziwa bwino Yehova ndi kumusangalatsa, ndipo ifeyo tinaphunzirapo kanthu pa chitsanzo chawo cha kuopa Mulungu zenizeni ndi kum’konda. Ngakhale tikalakwa m’njira inayake, makolo athu sankatipangitsa kuona kuti Yehova sakutikondanso; ndipo sankatiikira malamulo ambirimbiri okhwima chifukwa chotipsera mtima. Nthawi zambiri ankangotikhazika pansi n’kutilankhula, ndipo nthawi zina mayi ankachita kufika potulutsa misozi poyesa kutilangiza mwakuti tikhudzidwe mtima. Ndipotu zimenezi zinathandizadi. Mawu ndi zochita za makolo athu zinatiphunzitsa kuti kuopa Yehova n’chinthu chosangalatsa ndi kuti kukhala Mboni yake kumabweretsa chimwemwe ndipo sikolemetsa.”​—1 Yohane 5:3.

18. Kodi tidzapeza chiyani chifukwa choopa Mulungu woona?

18 Pa zina zimene zili mu “mawu otsiriza a Davide,” pali mawu akuti: “Kudzakhala woweruza anthu molungama; woweruza m’kuopa Mulungu. Iye adzakhala ngati kuunika kwa m’mawa, potuluka dzuwa.” (2 Samueli 23:1, 3, 4) Zikuoneka kuti Solomo, mwana wa Davide yemwe analowa ufumu m’malo mwake anamvetsa mfundoyi, chifukwa anapempha kuti Yehova amupatse “mtima womvera” ndiponso luso loti ‘azindikire pakati pa zabwino ndi zoipa.’ (1 Mafumu 3:9) Solomo anazindikira kuti kuopa Yehova kumapereka nzeru ndi chimwemwe. Patsogolo pake, ponena mwachidule za mfundo zonse za m’buku la Mlaliki, iye anati: “Mawu atha; zonse zamveka zatha; opa Mulungu, musunge malamulo ake; pakuti choyenera anthu onse ndi ichi. Pakuti Mulungu adzanena mlandu wa zochita zonse, ndi zobisika zonse, ngakhale zabwino ngakhale zoipa.” (Mlaliki 12:13, 14) Tikamvera malangizo amenewo, tidzapeza kuti “mphoto ya chifatso ndi kuopa Yehova” si nzeru ndi chimwemwe zokha ayi komanso “chuma, ndi ulemu, ndi moyo.”​—Miyambo 22:4.

19. N’chiyani chingatithandize kuzindikira “kuopa Yehova”?

19 Pa zitsanzo za m’Baibulo ndiponso zochitika za masiku ano, tikuona kuti kuopa Mulungu moyenerera kumathandiza pa moyo wa atumiki oona a Yehova. Mantha amenewa angatiletse kuchita zinthu zosasangalatsa Atate wathu wakumwamba komanso angatilimbitse mtima kulimbana ndi adani athu ndi kutipatsa mphamvu kuti tipirire ziyeso ndi zovuta zimene timakumana nazo. Motero, kaya ndife ana kaya ndife achikulire, tiyeni tiyesetse kuphunzira Mawu a Mulungu, kusinkhasinkha zimene taphunzira, ndi kuyandikira kwa Yehova mwa kupemphera nthawi zonse ndiponso mochoka pansi pa mtima. Potero, ‘tidzam’dziwadi Mulungu’ ndi kuzindikira “kuopa Yehova.”​—Miyambo 2:1-5.

[Mawu a M’munsi]

^ ndime 4 Mayina tawasintha.

^ ndime 5 N’kutheka kuti nkhani inachitikayi ndi imodzi mwa nkhani zimene zinachititsa Davide kulemba Salmo 57 ndi 142.

Kodi Mungafotokoze?

Kodi kuopa Mulungu

• kungathandize bwanji munthu akachita tchimo lalikulu?

• kungabweretse bwanji chimwemwe poyesedwa ndiponso pozunzidwa?

• kungatilimbikitse bwanji kuchita chifuniro cha Mulungu?

• kungakhale bwanji cholowa chamtengo wapatali kwa ana athu?

[Mafunso]

[Chithunzi patsamba 26]

Chifukwa choopa Yehova Davide sanaphe Mfumu Sauli

[Zithunzi patsamba 29]

Kuopa Mulungu ndi cholowa chamtengo wapatali chimene makolo angasiyire ana awo