Pitani ku nkhani yake

Pitani ku mitu ya nkhani

N’zotheka Aliyense Kumadzapatsidwa Ulemu

N’zotheka Aliyense Kumadzapatsidwa Ulemu

N’zotheka Aliyense Kumadzapatsidwa Ulemu

“Tiyenera kusintha dzikoli kuti likhale labwino kwambiri, loti anthu onse azipatsidwa ulemu wobadwa nawo.”​—ANATERO PULEZIDENTI WA DZIKO LA UNITED STATES, A HARRY TRUMAN, MUMZINDA WA SAN FRANCISCO, KU CALIFORNIA, KU UNITED STATES, PA APRIL 25, 1945.

PULEZIDENTI Truman ankakhulupirira zimene anthu ambiri ankakhulupirira panthawiyo. Apa n’kuti patapita zaka zingapo chichitikireni nkhondo yachiwiri ya padziko lonse ndipo ambiri ankakhulupirira kuti anthu angatengepo phunziro pa zochitika za m’mbuyomo ‘n’kusintha dziko’ kuti aliyense akhale ndi ulemu wake. N’zomvetsa chisoni kuti zochitika za masiku ano zikusonyeza kuti zinthu sizili choncho ayi. “Ulemu wobadwa nawo” ukuponderezedwa chifukwa choti vutoli anayambitsa si anthu, koma ndi mdani wamkulu wa anthu.

Amene Anayambitsa Vutoli

Baibulo limatiuza kuti mdani ameneyu ndi Satana Mdyerekezi, yemwe ndi cholengedwa choipa chauzimu, amene wakhala akutsutsa ufulu wa Mulungu wolamulira ndipo wakhala akutero kuchokera pachiyambi cha mbiri ya anthu. Kuyambira pamene Satana analankhula ndi Hava m’munda wa Edene, cholinga chake chakhala choti asiyitse anthu kutumikira Mlengi wawo. (Genesis 3:1-5) Taganizirani mavuto amene Adamu ndi Hava anakhala nawo chifukwa chomvera Mdyerekezi. Chinthu choyamba chimene chinawachitikira chifukwa chosamvera lamulo la Mulungu lokhudza chipatso choletsedwa chinali chakuti iwo ‘anabisala pamaso pa Yehova Mulungu.’ N’chifukwa chiyani anatero? Adamu ananena chifukwa chake motere: “Ndinaopa chifukwa ndinali wamaliseche ine; ndipo ndinabisala.” (Genesis 3:8-10) Ubwenzi wa Adamu ndi Atate wake wakumwamba unasintha ndipo anayamba kudziona mosiyana ndi mmene ankadzionera poyamba. Anali ndi manyazi ndipo sanalinso womasuka kuonekera pamaso pa Yehova.

N’chifukwa chiyani Mdyerekezi anafuna kuti Adamu adzichotsere ulemu? N’chifukwa choti munthu analengedwa m’chifanizo cha Mulungu, ndipo Satana amasangalala akaona munthu akuchita zinthu zodetsa chifanizo chake cha ulemerero wa Mulungu. (Genesis 1:27; Aroma 3:23) Zimenezi zikutithandiza kumvetsa chifukwa chimene nkhani ya kuchotsera anthu ulemu yakhalapo m’mbiri yonse ya anthu. Popeza kuti Satana ndiye “mulungu wa nthawi ino ya pansi pano,” walimbikitsa mzimu umenewu panopa, ‘panthawi yakuti wina apweteka mnzake pom’lamulira.’ (2 Akorinto 4:4; Mlaliki 8:9; 1 Yohane 5:19) Kodi zimenezi zikutanthauza kuti anthu sadzapatsidwanso ulemu wowayenerera?

Yehova Amalemekeza Anthu Ake

Taganiziraninso mmene zinthu zinalili m’munda wa Edene, Adamu ndi Hava asanachimwe. Anthu awiriwa anali ndi zakudya zambirimbiri, ntchito yosangalatsa, ndipo iwo komanso ana awo akanakhala ndi moyo wathanzi komanso wosatha. (Genesis 1:28) Mbali iliyonse ya moyo wawo inasonyeza cholinga cha Mulungu chachikondi ndiponso cholemekeza anthu.

Kodi Adamu ndi Hava atachimwa, maganizo a Yehova pankhani ya kupatsa anthu ulemu wawo anasintha? Ayi. Iye anawaganizira pa manyazi amene anali nawo atayamba kudzimva kuti ali maliseche. Mwachikondi, Mulungu anawapatsa “malaya azikopa” kuti avale m’malo mwa “masamba amkuyu” amene iwo anasokerera n’kuvala. (Genesis 3:7, 21) Mulungu sanawasiye kuti achite manyazi, koma anawachitira ulemu.

M’tsogolo mwake, pochita zinthu ndi mtundu wa Israyeli, Yehova anachitira chifundo ana ndi amayi amasiye ndiponso alendo. Onsewa ndi anthu amene nthawi zambiri amachitidwa nkhanza. (Salmo 72:13) Mwachitsanzo, pokolola mbewu monga tirigu, zipatso za azitona, ndiponso minda ya mphesa, Aisrayeli anauzidwa kuti asamabwerere kukatola khunkha. M’malo mwake, Mulungu anawalamula kuti zokunkha azisiye “zikhale za mlendo, za mwana wamasiye, ndi za mkazi wamasiye.” (Deuteronomo 24:19-21) Malamulo amenewa akawatsatira, ankathandiza kuti pasakhale anthu opemphapempha ndiponso kuti ngakhale anthu osauka kwambiri azigwira ntchito yolemekezeka.

Yesu Ankalemekeza Ena

Mwana wa Mulungu, Yesu Kristu, ali padziko lapansi pano ankaganizira zolemekeza ena. Mwachitsanzo, ali ku Galileya, munthu wa khate loti lafika poipa zedi anabwera kwa iye. Malingana ndi Chilamulo cha Mose, poopa kupatsira ena matendawo, munthu wakhate anayenera kumakuwa kuti: “Wodetsedwa, wodetsedwa!” (Levitiko 13:45) Koma akupita kwa Yesu, munthuyu ananyalanyaza kuchenjeza ena. M’malo mwake, anagwetsa nkhope yake pansi n’kum’chonderera Yesu mwa kunena kuti: “Ambuye, ngati mufuna mungathe kundikonza.” (Luka 5:12) Kodi Yesu anatani? Yesu sanadzudzule munthuyo kuti waphwanya Chilamulo, ndipo sanam’nyalanyaze kapena kumupewa. M’malo mwake, analemekeza wakhateyu pomugwira n’kumuuza kuti: “Ndifuna, takonzeka.”​—Luka 5:13.

Palinso nthawi zina pamene Yesu anachiza anthu popanda kuwakhudza, ndipo nthawi zina Yesuyo ankakhala ali kutali ndi anthuwo. Koma apa Yesu anaganiza zoti munthu wakhateyu achite kumukhudza. (Mateyu 15:21-28; Marko 10:51, 52; Luka 7:1-10) Chifukwa choti munthuyo anali “wodzala ndi khate,” n’zosakayikitsa kuti kwa zaka zambiri sanakhudzidwe ndi munthu aliyense. Ndiye tangoganizirani mmene analimbikitsidwira kumva munthu wina akumukhudza! Munthu ameneyutu ankangofuna kuchira khate lakelo basi. Koma n’zosakayikitsa kuti njira imene Yesu anachizira munthuyu inathandiza mbali inanso, kubwezeretsa ulemu wa munthuyu. Kodi n’chinthu chanzeru kuganiza kuti masiku ano anthu angaganizire anzawo powapatsa ulemu wotere? Ngati n’choncho, kodi angasonyeze bwanji ulemu wotere?

Mfundo Yothandiza Kulemekezana

Yesu ananena mawu amene anthu ambiri amawaona kuti ndi malangizo otchuka kwambiri okhudza kuchita zinthu ndi anthu anzathu. Mawu ake ndi akuti: “Chifukwa chake zinthu zilizonse mukafuna kuti anthu achitire inu, inunso muwachitire iwo zotero.” (Mateyu 7:12) Malangizo a khalidwe labwino amenewa amalimbikitsa munthu kulemekeza munthu mnzake chifukwa akatero, amadziwa kuti nayenso alemekezedwa.

Zochitika za m’mbiri ya anthu zimasonyeza kuti munthu sangatsatire lamulo limeneli mwachibadwa, ndipo nthawi zambiri zinthu zimene anthu amachita mwachibadwa zimasemphana ndi lamuloli. Munthu wina amene timutchule kuti Harold anati: “Ndinkasangalala pochititsa manyazi anthu ena. Ndinkatha kulankhula mawu ochepa chabe koma n’kum’nyowetseratu munthu ndi manyazi moti mpaka kufika polira.” Koma chinachake chinam’thandiza Harold kusintha. Iye anati: “Anthu angapo a Mboni za Yehova anayamba kundiyendera. Ndikaganiza za nthawi imeneyo, ndimachita manyazi ndi zina mwa zinthu zimene ndinkanena komanso ndi zinthu zimene ndinkawachitira nthawi zina. Koma iwo sanatope ayi, ndipo pang’onopang’ono, choonadi cha m’Baibulo chinandikhudza mtima n’kundithandiza kusintha.” Panopo Harold ndi mkulu mumpingo.

Nkhani ya Harold ikupereka umboni wakuti: “Mawu a Mulungu ali amoyo, ndi ochitachita, ndi akuthwa koposa lupanga lakuthwa konsekonse, napyoza kufikira kugawira moyo ndi mzimu, ndi zimfundo ndi mafuta a m’mafupa, nazindikiritsa zolingirira ndi zitsimikizo za mtima.” (Ahebri 4:12) Mawu a Mulungu ali ndi mphamvu zotha kukhudza mtima wa munthu ndi kusintha kaganizidwe ndiponso khalidwe lake. Chinthu choyamba chothandiza munthu kulemekeza ena ndicho kukhala ndi mtima wofunitsitsa kuthandiza osati kuvulaza ena, mtima wofunitsitsa kuwapatsa ulemu osati kuwachititsa manyazi.​—Machitidwe 20:35; Aroma 12:10.

Kuyambanso Kulandira Ulemu

Mtima umenewu ndi umene umachititsa kuti Mboni za Yehova zizidziwitsa anthu ena za chiyembekezo chosangalatsa chofotokozedwa m’Baibulo. (Machitidwe 5:42) Palibe njira ina yabwino yolemekezera anthu anzathu yoposa kuwadziwitsa za “uthenga wabwino wa zinthu zabwino.” (Yesaya 52:7) Zina mwa “zinthu zabwino” zimenezi ndizo kuvala ‘umunthu watsopano,’ umene umafetsa “chilakolako choipa” chofuna kuchititsa ena manyazi. (Akolose 3:5-10) Komanso china mwa “zinthu zabwino” zimenezi ndi cholinga cha Yehova choti posachedwapa achotse zinthu ndiponso maganizo amene amachotsera anthu ulemu wawo, pamodzinso ndi Satana Mdyerekezi, yemwe amalimbikitsa khalidwe limeneli. (Danieli 2:44; Mateyu 6:9, 10; Chivumbulutso 20:1, 2, 10) Panthawiyi dziko “lidzadzala ndi odziwa Yehova” ndipo m’pokhapa pamene zidzatheke kuti anthu onse adzalemekezedwe.​—Yesaya 11:9.

Tikukupemphani kuti muphunzire za chiyembekezo chosangalatsachi. Posonkhana ndi Mboni za Yehova mudzaona nokha kuti kutsatira mfundo za m’Baibulo kumapatsa ena ulemu wawo. Ndipo mudzadziwa mmene Ufumu wa Mulungu ‘udzasinthire dzikoli kuti likhale labwino kwambiri,’ ndipo panthawiyo “anthu onse adzapatsidwa ulemu wobadwa nawo,” mpaka kalekale.

[Bokosi/​Chithunzi patsamba 6]

Anadzisungira Ulemu Pokhalabe Okhulupirika

Chifukwa cha zikhulupiriro zawo, Mboni za Yehova zoposa 2,000 zinatsekeredwa m’ndende za Nazi zozunzirako anthu, pa nkhondo yachiwiri ya padziko lonse. Poona kukhulupirika kodabwitsa kwa Mbonizi, Gemma La Guardia Gluck, yemwe kale anali mkaidi m’ndende ya ku Ravensbrück, ananena izi m’buku lake lakuti My Story: “Panthawi ina a Gestapo analengeza kuti munthu aliyense wa m’gulu la Ophunzira Baibulo akavomereza kuti wasiya zikhulupiriro zake n’kusayina chikalata chofotokoza zimenezi, adzam’patsa ufulu wake n’kusiya kumuzunza.” Ponena za anthu amene anakana kusayina chikalatacho, iye analemba kuti: “Iwo analolera kupitirizabe kuvutika ndi kudikirira tsiku la chipulumutso moleza mtima.” N’chifukwa chiyani anatero? Magdalena, yemwe tam’tchula m’nkhani yoyamba ija, tsopano ali ndi zaka za m’ma 80 ndipo anafotokoza motere: “Kukhala okhulupirika kwa Yehova chinali chinthu chofunika kuposa kukhala ndi moyo. Kuti tikhalebe ndi ulemu wathu tinafunika kukhalabe okhulupirika. *

[Mawu a M’munsi]

^ ndime 23 Onani Nsanja ya Olonda ya February 15, 1986, masamba 10 mpaka 15 kuti mumve tsatanetsatane wa nkhani ya banja la a Kusserow.

[Chithunzi patsamba 5]

Yesu ankalemekeza anthu amene ankawachiritsa

[Chithunzi patsamba 7]

Mboni za Yehova zimalemekeza ena powauza “uthenga wabwino wa zinthu zabwino”