Pitani ku nkhani yake

Pitani ku mitu ya nkhani

Kuopa Mulungu “Ndiko Mwambo Wanzeru”

Kuopa Mulungu “Ndiko Mwambo Wanzeru”

 Kuopa Mulungu “Ndiko Mwambo Wanzeru”

NZERU yakonza phwando lalikulu. “Yatuma anamwali ake, iitana pa misanje ya m’mudzi. Wachibwana yense apambukire kuno; iti kwa yense wosowa nzeru, Tiyeni, idyani chakudya changa; nimumwe vinyo wanga ndam’sanganiza. Lekani, achibwana inu, nimukhale ndi moyo; nimuyende m’njira ya nzeru.”​—Miyambo 9:1-6.

Kudya pagome la nzeru sikubweretsa vuto kapena chovulaza chilichonse. Kumvetsera nzeru zochokera kwa Mulungu zomwe zili m’miyambi youziridwa ndi kutsatira malangizo ake kumabweretsa zabwino zokhazokha. Zili chimodzimodzinso ndi mawu anzeru opezeka pa Miyambo 15:16-33, omwe tiwalongosole. * Kumvera malangizo a miyambi yosapita m’mbali imeneyi kungatithandize kukhala okhutira ndi zinthu zochepa zimene tili nazo, kusakhala anthu obwerera m’mbuyo, ndi kukhala achimwemwe pa moyo wathu. Kuchita zimenezi kungatithandizenso kusankha zinthu bwino ndi kusapatuka m’njira yopita kumoyo.

Ndi Bwino Kukhala ndi Zinthu Zochepa

Mfumu Solomo ya Israyeli wakale inati: “Zapang’ono, ulikuopa Yehova, zipambana ndi katundu wambiri pokhala phokoso.” (Miyambo 15:16) N’kupusa kunyalanyaza Mlengi n’kumalimbana kwambiri ndi zofuna kupeza chuma. Moyo wotere umatangwanitsa munthu ndi zinthu zambirimbiri zotopetsa ndi zobweretsa nkhawa. N’zomvetsatu chisoni kwambiri kumazindikira utakalamba kuti moyo wako wonse wakhala wachabechabe ndiponso wopanda phindu. Ndithu, kukhala ndi zinthu zambirimbiri koma uli ndi “phokoso” si kwanzeru. Koma ndi bwino kwambiri kudziwa chinsinsi chokhala wokhutira n’kumachita zinthu mogwirizana ndi chinsinsi chimenechi. Timakhala wokhutira zenizeni poopa Yehova, pokhala ndi ubwenzi ndi iyeyo, osati pokhala ndi chuma.​—1 Timoteo 6:6-8.

Pogogomezera kuti ubwenzi wabwino ndi anthu ena n’ngofunika kwambiri kuposa kukhala ndi chuma chambiri, Solomo anati: “Kudya masamba, pali chikondano, kuposa ng’ombe yonenepa pali udani.” (Miyambo 15:17) Inde, ndi bwino kwambiri kuti anthu azikhala mwachikondi panyumba kusiyana ndi kuti azidya bwino. M’banja limene mayi kapena bambo akulera yekha ana, zinthu zimakhala zochepa. M’mayiko ena kholo lotere lingakwanitse kugula zakudya wamba basi. Komabe banjalo limakhala losangalala pakakhala chikondi.

Ngakhale m’mabanja amene nthawi zambiri anthu amakondana, nthawi zina mumatha kubuka mavuto. Munthu wina m’banjamo anganene kapena kuchita zinazake zimene zingapwete mtima mnzake. Kodi amene wapwetekedwa  mtimayo ayenera kutani? Lemba la Miyambo 15:18 limati: “Munthu wozaza aputa makani; koma wosakwiya msanga atonthoza makangano.” Kuyankha mofatsa, osati mokwiya, kumalimbikitsa bata ndi mtendere. Malangizo a m’mwambi umenewu amagwiranso ntchito m’zochitika zina pa moyo, kuphatikizapo za kumpingo ndi muutumiki.

‘Njira Ikaundidwa Ngati Msewu’

Mwambi wotsatira ukusonyeza kusiyana kwa munthu amene sanalabadire nzeru ndi anthu amene atero. “Mayendedwe a wolesi akunga linga laminga, koma njira ya oongoka mtima iundidwa ngati msewu.”​Miyambo 15:19.

Linga laminga limatchingira anthu chifukwa limakhala lobaya. Munthu waulesi amalephera kuyambapo ntchito inayake poganizira zifukwa zambirimbiri zomwe zingamulepheretse kuchita ntchitoyo ndipo amanamizira kuti zikumulepheretsa ndi zimenezo. Koma anthu oongoka mtima salephera kuchita zinthu poopa kuti pali zinazake zimene zingawalepheretse. Amalimbikira ntchito ndi kuganizira kwambiri ntchito imene akuchita. Amapewa mavuto ambiri onga minga amene akanakumana nawo akanati achite zinthu motayirira. Njira yawo imakhala ‘younda,’ kutanthauza kuti imakhala yopita patsogolo. Amayamba ntchito yawo ndipo amasangalala ikamapita patsogolo.

Mwachitsanzo, taganizirani nkhani ya kudziwa molondola Mawu a Mulungu ndi kukula msinkhu mwauzimu. Nkhani imeneyi imafunika khama. Munthu angamalephere kuchita khama kuphunzira Baibulo payekha ponamizira kuti sukulu sanapite nayo patali, satha kuwerenga bwinobwino, kapena kuti sachedwa kuiwala zinthu. Komatu ndi bwino kwambiri kusaona zinthu zimenezi ngati zinthu zotilepheretsa kudziwa zinthu. Ngakhale titamavutika kuphunzira zinthu, tingachite khama kuti tizitha kuwerenga bwino ndi kumvetsa zimene tikuwerenga, ndipo mwina tingatero pogwiritsa ntchito dikishonale. Khama limatithandiza kudziwa zinthu ndi kupita patsogolo mwauzimu.

‘Kukondweretsa Tate’

Mfumu ya Israyeli inati: “Mwana wanzeru akondweretsa atate wake; koma munthu wopusa apeputsa amake.” (Miyambo 15:20) Kodi  makolo sasangalala ana awo akamachita zinthu mwanzeru? Inde, makolo amayenera kuphunzitsa ndi kulangiza ana awo bwino kuti akhale anzeru chonchi. (Miyambo 22:6) Ndipotu mwana wanzeru amasangalatsa kwambiri makolo ake. Koma mwana wopusa amawamvetsa chisoni nthawi zonse.

Mfumu ya nzeruyi ikutchulanso mawu akuti ‘kukondwera’ m’lingaliro lina. Iyo ikuti: “Wosowa nzeru akondwera ndi utsiru; koma munthu wozindikira awongola mayendedwe ake.” (Miyambo 15:21) Zitsiru zimakondwera ndi zinthu zopusa zoseketsa zomwe sizibweretsa chimwemwe chenicheni pamoyo. Koma munthu wozindikira amadziwa kuti n’kupusa kukhala ‘wokonda zokondweretsa munthu, osati wokonda Mulungu.’ (2 Timoteo 3:1, 4) Kutsatira mfundo zimene Mulungu amaphunzitsa kumam’thandiza kukhalabe woongoka mtima ndi kuyendabe m’njira yoongoka.

Pakakhala “Upo”

Kukhala mogwirizana ndi mfundo za Mulungu kumatipindulitsanso m’mbali zina za moyo wathu. Miyambo 15:22 amati: “Zolingalira zizimidwa popanda upo; koma pochuluka aphungu zikhazikika.”

Mawu akuti upo m’lembali akutanthauza kulankhulana pambali koma moona mtima. Mawu a m’Chihebri a palembali amenenso anawamasulira kuti “upo” pa Salmo 89:7 amatanthauza “gulu la anthu okondana.” Zimenezi zimasonyeza kugwirizana pamene mukulankhulana. Motero upo si kucheza chabe ayi koma n’kuuzana maganizo anu enieni ndiponso mmenedi mukumvera. Amuna ndi akazi awo komanso makolo ndi ana akamakambirana momasuka m’njira imeneyi, amakhala mwamtendere ndipo amagwirizana. Koma ngati pabanja anthu sakhala ndi upo woterewu, samvetsetsana ndipo pamabuka zovuta zosiyanasiyana.

Tikamaganizira nkhani zikuluzikulu, n’chanzeru kutsatira malangizo akuti: “Pochuluka aphungu zikhazikika.” Mwachitsanzo, tikamasankha chithandizo cha mankhwala, kodi si chinthu chanzeru kufunsa kwa madokotala angapo, makamaka ngati chithandizocho chikukhudza nkhani zikuluzikulu?

Kukhala ndi aphungu ambiri n’kofunika zedi posamalira nkhani zauzimu. Akulu akamakambirana n’kugwiritsa ntchito nzeru za akulu osiyanasiyana pa gulu lawolo, zokambirana zawozo ‘zimakhazikika’ kapena kuti zimakhala zothandiza. Komanso oyang’anira amene asankhidwa chakumene asamanyalanyaze kupempha nzeru kwa akulu achikulire ndiponso odziwa bwino zinthu, makamaka pa nkhani zovuta.

Kukondwera ndi “Mayankhidwe”

Kodi kulankhula moganizira bwino kungapindulitse bwanji munthu? Mfumu ya Israyeli inati: “Munthu akondwera ndi mayankhidwe a m’kamwa mwake; ndi mawu a pa nthawi yake kodi sali abwino?” (Miyambo 15:23) Kodi ifeyo sitisangalala anthu akatsatira yankho kapena  malangizo athu n’kupindula nawo? Komabe kuti malangizo athu akhale othandiza, ayenera kukhala ndi mbali ziwiri zofunika.

Choyamba, malangizowo ayenera kukhala ozikidwa m’Mawu a Mulungu, Baibulo. (Salmo 119:105; 2 Timoteo 3:16, 17) Chachiwiri, ayenera kunenedwa panthawi yoyenera. Ngakhale mawu oona angaononge zinthu ngati atanenedwa panthawi yolakwika. Mwachitsanzo, kupereka malangizo kwa munthu musanamve bwinobwino vuto lake sikwanzeru ndipo sikothandiza. Motero n’chinthu chofunika kwambiri kukhala “wotchera khutu, wodekha polankhula.”​—Yakobo 1:19.

‘Njira Yamoyo N’njokwerakwera’

Lemba la Miyambo 15:24 limati: “Anzeru ayesa njira yamoyo yokwerakwera, kuti apambuke kusiya kunsi kwa manda.” Munthu amene amachita zinthu mwanzeru ali panjira yotalikirana ndi kumanda. Iye amapewa makhalidwe oipa monga chiwerewere, kugwiritsa ntchito mankhwala osokoneza bongo, ndi uchidakwa, motero amapewa kufa msanga. Njira imene amatenga imapita kumoyo.

Koma taonani njira ya anthu opanda nzeru: “Yehova adzapasula nyumba ya wonyada; koma adzalembera mkazi wamasiye malire ake. Ziwembu zoipa zinyansa Yehova; koma oyera mtima alankhula mawu okondweretsa. Wopindula monyenga avuta nyumba yake; koma wakuda mitulo [ziphuphu] adzakhala ndi moyo.”​Miyambo 15:25-27.

Potisonyeza mmene tingapewere msampha wofala kwambiri, mfumu ya Israyeli inati: “Mtima wa wolungama uganizira za mayankhidwe; koma m’kamwa mwa ochimwa mutsanulira zoipa.” (Miyambo 15:28) Malangizo a mwambi umenewu n’ngofunika zedi. Mayankho opanda nzeru ndiponso opusa omwe amangotuluka m’kamwa nthawi zambiri sathandiza m’njira iliyonse. Tingapewe kunena zinthu zosayenera pa nkhani inayake zoti n’kudzavutika nazo, mwa kuyamba taganizira zinthu zosiyanasiyana zokhudza nkhaniyo, kuphatikizapo mmene zinthu zikuyendera m’moyo wa anthu amene angakhudzidwe ndi nkhaniyo ndiponso mmene iwowo angamvere.

Komano kodi phindu la kuopa Mulungu ndi kumvera malangizo ake n’chiyani? Munthu wanzeru akuyankha kuti: “Yehova atalikira oipa; koma pemphero la olungama alimvera.” (Miyambo 15:29) Mulungu woona sayandikira anthu oipa. Baibulo limati: “Wopewetsa khutu lake kuti asamve chilamulo, ngakhale pemphero lake linyansa.” (Miyambo 28:9) Anthu amene  amaopa Mulungu ndi kuyesetsa kuchita zoyenera kwa iye angathe kulankhula naye mwaufulu, osakayika n’komwe kuti amva pemphero lawo.

Chomwe ‘Chimakondweretsa Mtima’

Solomo akufanizira zinthu ziwiri m’njira yochititsa chidwi kwambiri ponena kuti: “Kuunika kwa maso kukondweretsa mtima; ndipo pomveka zabwino mafupa amatenga uwisi.” (Miyambo 15:30) Mafupa “amatenga uwisi” akakhala ndi mafuta m’kati mwake. Zimenezi zimapatsa mphamvu thupi lonse ndipo zimakondweretsa mtima. Kukondwera kwa mtimako kumaonekera m’kunyezimira kwa maso. Umu ndi mmene anthu amakhudzidwira akamva zabwino.

Kodi nkhani zabwino zimene timamva za kuwonjezeka kwa zinthu zosiyanasiyana zokhudza kupembedza Yehova sizitilimbikitsa kwambiri? Inde, kudziwa za zinthu zosiyanasiyana zimene zikukwaniritsidwa pa ntchito yolalikira za Ufumu ndi kupanga ophunzira kumatilimbikitsadi kuti tiwonjezere utumiki wathu. (Mateyu 24:14; 28:19, 20) Mitima yathu imadzadza n’chimwemwe tikamamva nkhani za anthu amene asankha kuti Yehova akhale Mulungu wawo n’kuyamba kulambira moona. Popeza kuti “mawu abwino akuchokera ku dziko lakutali” amabweretsa chimwemwe chotere, n’chinthu chofunika kwambiri kuti malipoti athu a ntchito imene tachita muutumiki azikhala olondola.​—Miyambo 25:25.

“Chifatso Chitsogolera Ulemu”

Pogogomezera kufunika komvera mwambo wosiyanasiyana, mfumu yanzeruyi inati: “Khutu lomvera chidzudzulo cha moyo lidzakhalabe mwa anzeru. Wokana mwambo apeputsa moyo wake; koma wosamalira chidzudzulo amatenga nzeru.” (Miyambo 15:31, 32) Chidzudzulo, kapena kuti mwambo umakhudza mtima wa munthu ndi kuuwongola, n’kumupatsa nzeru munthuyo. N’chifukwa chaketu ‘utsiru womangidwa mumtima mwa mwana’ umachotsedwa ndi ‘ntyole yom’langira.’ (Miyambo 22:15) Munthu womvera mwambo amatenga nzeru, kapena kuti amakhala ndi maganizo abwino. Komano kusamvera mwambo n’kukana moyo.

Inde, kukhala wokonzeka kulandira mwambo ndi kuuvomereza modzichepetsa n’kopindulitsa. Kuchita zimenezi kumathandiza kuti munthu akhale wosangalala, apite patsogolo, achite zinthu zambiri, komanso kuti adzalandire ulemerero ndi moyo. Lemba la Miyambo 15:33 limamaliza ndi mawu akuti: “Kuopa Yehova ndiko mwambo wanzeru; ndipo chifatso chitsogolera ulemu.”

[Mawu a M’munsi]

[Chithunzi patsamba 17]

Ndi bwino kuti anthu azikhala mwachikondi panyumba kusiyana ndi kuti azidya bwino koma palibe chikondi

[Chithunzi patsamba 18]

Khama lingatithandize kudziwa zinthu ngakhale ngati tili ndi vuto linalake lokhudza kuphunzira zinthu

[Chithunzi patsamba 19]

Kuchita upo kumatanthauza kuuzana maganizo anu enieni ndiponso zakukhosi kwanu

[Chithunzi patsamba 20]

Kodi mukudziwa kuti “pomveka zabwino mafupa amatenga uwisi” m’njira yotani?