Pitani ku nkhani yake

Pitani ku mitu ya nkhani

Banja Lathu Linagwirizana Patatha Zaka Zambiri

Banja Lathu Linagwirizana Patatha Zaka Zambiri

 Mbiri ya Moyo Wanga

Banja Lathu Linagwirizana Patatha Zaka Zambiri

YOSIMBIDWA NDI SUMIKO HIRANO

Ndinapeza moyo wabwino kwambiri ndipo ndinkafuna kuti mwamuna wanga nayenso akhale ndi moyo womwewu. Panatha zaka 42 kuti zimenezi zitheke.

TINAKWATIRANA mu 1951, ine ndili ndi zaka 21. Potha zaka zinayi n’kuti tili ndi ana awiri aamuna, ndipo ndinkaona kuti moyo wanga uli bwino kwambiri.

Tsiku lina mu 1957, mkulu wanga anandiuza kuti mmishonale wa Mboni za Yehova wakhala akumuyendera. Ngakhale kuti mkulu wangayu anali Mbuda, anayamba kuphunzira Baibulo ndi mmishonaleyo ndipo atandilimbikitsa kuti nanenso ndiphunzire Baibulo ndinavomera. Apa n’kuti ndikupita ku tchalitchi cha Chipulotesitanti ndipo ndinaganiza kuti a Mboni za Yehovawo ndikatha kuwasonyeza zinthu zolakwika pa ziphunzitso zawo.

Posakhalitsa ndinazindikira kuti Baibulo sindinkalidziwa kwenikweni. Ndinachita kufunsa kwa mmishonaleyo kuti: “Kodi Yehova ndani?” Ndinali ndisanamvepo dzina limeneli kutchalitchi kwathu. Mmishonaleyo, yemwe dzina lake anali Daphne Cooke (kenaka anadzakhala Daphne Pettitt), anandisonyeza lemba la Yesaya 42:8, lomwe limanena momveka bwino kuti Yehova ndilo dzina la Mulungu Wamphamvuyonse. Daphne anayankha mafunso anga onse pogwiritsa ntchito Baibulo.

Nditafunsa abusa athu mafunso omwewo, anayankha kuti: “Kufunsa mafunso ndi tchimo. Uzingokhulupirira zimene wauzidwazo basi.” Ngakhale kuti sindinakhulupirire kuti kufunsa mafunso n’kulakwa, kwa miyezi sikisi ndinkapitabe kutchalitchi Lamlungu lililonse m’mawa ndipo madzulo ndinkapita ku misonkhano ya Mboni za Yehova.

 Mmene Zinakhudzira Banja Langa

Zimene ndinkaphunzira m’Baibulo zinandisangalatsa kwambiri, ndipo ndinayamba kumuuza mwamuna wanga, Kazuhiko. Pambuyo pa phunziro ndiponso msonkhano uliwonse, ndinkamuuza zimene ndaphunzira. Zimenezi zinayamba kusokoneza mgwirizano wathu. Iye sankafuna kuti ndikhale wa Mboni za Yehova. Koma kuphunzira Baibulo kunkandisangalatsa kwambiri moti ndinapitirizabe kuphunzira ndi kusonkhana ndi Mbonizo.

Madzulo aliwonse amene ndinkapita kumisonkhano, sindinkachoka ndisanamuphikire Kazuhiko zakudya zimene amakonda kwambiri, koma anayamba kudya ku lesitilanti. Ndikabwera kunyumba kuchoka kumisonkhano, ankakhala atalunda ndipo sankafuna kundilankhula. Pakatha masiku awiri kapena atatu, ankasintha, koma ndiye kuti tsiku la misonkhano inanso limakhala litafika.

Panthawi imeneyi, ndinadwala chifuwa chachikulu cha TB, ndipo apa n’kuti anthu angapo a m’banja la mwamuna wanga atafa ndi matenda amenewa. Mwamuna wanga Kazuhiko anada nkhawa kwambiri ndipo anandiuza kuti ndikadzachira azidzandilola kuchita chilichonse chimene ndikufuna. Koma ine ndinangomupemphapo kuti asamadzandiletse kupita kumisonkhano. Anavomera.

Ndinachira patatha miyezi sikisi, ndipo panthawi imene ndimadwalayo ndinkaphunzira Baibulo mwakhama zedi. Ndinkafufuza kuti ndipeze zinthu zotsutsana pa ziphunzitso za Mboni, poganiza kuti ndikangopeza chimodzi chotere basi ndisiya kuphunzira. Koma palibe chimene ndinapeza. M’malo mwake zolakwa za tchalitchi cha Chipulotesitanti n’zimene zinaonekera kwambiri. Ndinazindikira chikondi ndi chilungamo cha Yehova n’kuona ubwino wokhala moyo wogwirizana ndi malamulo ake.

Nditachira, mwamuna wanga anasunga lonjezo lake moti sankandiletsa kupita kumisonkhano. Ndinapitiriza kukula mwauzimu, ndipo mu May 1958, ndinabatizidwa monga wa Mboni za Yehova. Ndinkafunitsitsa banja langa litamalambira Mulungu woona limodzi ndi ine.

Kuthandiza Ana Anga Mwauzimu

Nthawi zonse ana anga ankakhala nane kumisonkhano ndi kuntchito yolalikira, ndipo zinthu zina zimene zinachitika zinandithandiza kuona kuti anali kukula pa nkhani ya kudziwa Baibulo. Tsiku lina mwana wanga Masahiko, yemwe anali ndi zaka sikisi, ankasewera panja pa nyumba yathu. Ndinamva chiphokoso ndiponso munthu akukuwa. Mayi wina wapafupi analowa m’nyumba mwanga mothamanga, akukuwa kuti mwana wanga wagundidwa ndi galimoto. Kodi anali atafa? Ndinatuluka panja kwinaku ndikuyesetsa kudzilimbitsa. Ndinanthunthumira kuona mmene njinga yake inathyokera, koma kenaka ndinamuona akubwera poteropo, atangovulala pang’ono chabe. Anandikumbatira n’kunena kuti, “Amayi, Yehova ananditeteza eti?” Ndinalira poona kuti ali moyo n’kumumva akunena mawu osangalatsawa.

Tsiku lina, tili muutumiki tinakumana ndi bambo wina wokalamba amene anandikalipira motere: “Iwe n’zoona kamwanaka ungamakayendetse mtunda wonsewu? N’zachisoni kwabasi.” Ine ndikuti ndiziyankha, Tomoyoshi, yemwe anali ndi zaka eyiti, anati: “Ayi agogo, mayitu sandikakamiza kulalikira. Ndimalalikira chifukwa choti ndikufuna  kutumikira Yehova.” Gogoyo anangoti maso dwii osanena kanthu.

Mwauzimu, ana anga anali opanda bambo. Ineyo ndi amene ndinali ndi udindo wowaphunzitsa choonadi cha m’Baibulo, ngakhale kuti nanenso ndinali ndisanadziwe zinthu zambiri. Ndinayesetsa kuti ineyo pandekha ndikhale munthu wachikondi, chikhulupiriro, ndi changu ndipo ndinayesetsa kupereka chitsanzo chabwino. Tsiku lililonse ndinkapemphera kwa Yehova pamaso pa anawo. Ndinkawauza zimene zandichitikira kuntchito yolalikira. Zimenezi zinkawalimbikitsa. Panthawi ina anawo atakula, anafunsidwa kuti n’chiyani chinawachititsa kukhala apainiya, kapena kuti atumiki a nthawi zonse a Mboni za Yehova, ndipo iwo anayankha kuti: “Tinaona kuti mayi anali wosangalala pochita upainiya, ndipo nafe tinkafuna kukhala osangalala.”

Ndinkayesetsa kusanena zoipa zilizonse zokhudza abambo awo kapena munthu wina aliyense mumpingo. Ndinkadziwa kuti mawu osalimbikitsa angathe kufoola ana anga. Akanawasiyitsa kulemekeza anthu onenedwawo komanso kulemekeza ineyo onena anzangane.

Kuthana ndi Mavuto Olepheretsa Kupita Patsogolo

Chifukwa cha ntchito ya mwamuna wanga, mu 1963 banja lathu linasamukira ku Taiwan. Iye anandiuza kuti ndisamakalalikire kwa anthu ochoka ku Japan chifukwa potero ndingakayambitse mavuto. Tingathe kukabwezedwa ku Japan n’kuchititsa kuti kampani yake igwe m’mavuto. Iye ankafuna kuti titalikirane ndi a Mboni.

Ku Taiwan, misonkhano yonse inali m’Chitchaina, ndipo Mboni kumeneko zinatilandira ndi manja awiri. Ndinaganiza zophunzira Chitchaina kuti ndizilalikira kwa anthu a kumeneko m’malo mwa anthu a ku Japan. Ndinatero kuti ndipewe mavuto amene anatchula mwamuna wanga aja.

Ubwenzi wathu ndi Mboni za ku Taiwan unatilimbikitsa. Harvey Logan ndi mkazi wake Kathy, omwe anali amishonale, anatithandiza kwambiri. Mbale Logan anakhala bambo wauzimu wa ana anga. Anawasonyeza kuti moyo wotumikira Yehova si moyo wosasangalatsa, umene umalanda munthu ufulu wake. Sindikukayika kuti nthawi imene tinali ku Taiwan ndi imene ana angawa anaganiza zotumikira Yehova.

Tomoyoshi ndi Masahiko anapita ku sukulu ya azungu a ku America, kumene anakaphunzira Chingelezi ndi Chitchaina. Maphunziro amenewa anawathandiza m’tsogolo pa utumiki wawo monga atumiki a Mulungu woona, Yehova. Ndimathokoza kwambiri Yehova pochititsa kuti nthawi imene ikanakhala yovuta kwambiri kwa ife isanduke nthawi yolandira madalitso okhalitsa. Banja lathu linabwerera ku Japan, litakhala ku Taiwan kwa zaka zitatu ndi theka, zomwe sindidzaziiwala.

Apa n’kuti anyamatawo akuyandikira zaka za m’ma 20 ndipo anayamba kufuna kuchita zinthu modziimira paokha. Ndinkakambirana nawo mfundo za m’Malemba kwa nthawi yaitali, ndipo Yehova anawathandiza pa nthawi yovuta imeneyi. Tomoyoshi atamaliza sukulu ya sekondale  anayamba upainiya. Patatha zaka zingapo chabe atayamba upainiya, iye anathandiza anthu anayi kufika podzipereka kwa Mulungu n’kubatizidwa. Masahiko anatsatira chitsanzo cha mchimwene wake ndipo anayamba upainiya atangomaliza sukulu ya sekondale. Potha zaka zinayi kuchokera pamene anayambira upainiya anali atathandiza achinyamata anayi kukhala Mboni.

Kenaka Yehova anawadalitsa kwambiri anawa. Tomoyoshi anaphunzitsa mwamuna wa mayi wina amene ineyo ndinam’thandiza kuphunzira choonadi cha m’Baibulo. Ana awo awiri aakazi anakhalanso Mboni. Patsogolo pake, Tomoyoshi anakwatira Nobuko, yemwe anali wamkulu pa ana aakazi awiriwo, ndipo Masahiko anakwatira Masako, wamng’onoyo. Tomoyoshi ndi Nobuko tsopano akutumikira pa likulu la padziko lonse la Mboni za Yehova mumzinda wa Brooklyn, ku New York. Ndipo Masahiko ndi Masako ndi amishonale ku Paraguay.

Mwamuna Wanga Anayamba Kusintha Pang’onopang’ono

Masiku amenewo, mwamuna wanga sankachita chidwi ndi chikhulupiriro chathu, koma tinaona kuti wayamba kusintha pa zinthu zina. Anthu ena akamanditsutsa, iye ankandiikira kumbuyo pa zikhulupiriro zanga ndipo mosazindikira, iye kwenikweni ankathandiza kulimbikitsa choonadi cha m’Baibulo. Ankathandiza Mboni m’njira zosiyanasiyana. Paukwati wa mmodzi wa ana athu aja, iye anati: “Kuphunzitsa anthu kukhala moyo wabwino ndiko ntchito yabwino kwambiri imene munthu angachite, koma imeneyi ndiyo ntchito yovutanso kwambiri. Ana anga ndi akazi awo asankha kuchita ntchito yovuta kwambiri imeneyi pa moyo wawo. Chonde athandizeni.” Zonsezi zinandichititsa kuganiza kuti ndithu mwamuna wangayu adzayamba kutumikira Yehova limodzi nafe.

Ndinkaitana Mboni zinzathu kuti zidzacheze kunyumba kwathu. Ndipo mwamuna wanga ndinkamuitanira ku misonkhano ya mpingo, yadera, ndi yachigawo komanso ku Chikumbutso cha imfa ya Kristu. Ngati ali ndi mpata kuntchito kwake ankapita kumisonkhanoyi, ngakhale kuti ankatero monyinyirika. Nthawi zambiri ndinkaona kuti angathe kuvomera kuphunzira Baibulo, motero ndinkaitana akulu a mumpingo kunyumba kwathu. Koma iye ankakana kuphunzira. Sindinkamvetsa kuti vuto linali chiyani makamaka.

Ndinakumbukira mawu a mtumwi Petro akuti: “Akazi inu, mverani amuna anu a inu nokha; kuti, ngatinso ena samvera mawu, akakodwe opanda mawu mwa mayendedwe a akazi; pakuona mayendedwe anu oyera ndi kuopa kwanu.” (1 Petro 3:1, 2) Ndinazindikira kuti malangizo amenewa sindinkawatsatira nthawi zonse. Kuti ndithe kutsatira bwinobwino malangizo amenewa, ndinayenera kuyesetsa kuti ndilimbe pa moyo wanga wauzimu.

Mu 1970, ndinayamba upainiya n’cholinga chofuna kukhala munthu wauzimu kwambiri. Panapita zaka 10, kenaka 20. Koma sindinaonebe kuti mwamuna wanga akusintha mwauzimu m’njira ina iliyonse. Nthawi ina, mkazi wina amene ndinkaphunzira naye Baibulo anati: “Ziyenera kukhala zovuta kuthandiza anthu ena pamene ukulephera kuthandiza mwamuna wako yemwe.” Zimenezi zinandifooketsa, koma sindinagonje ayi.

Cha kumapeto kwa m’ma 1980, makolo athu anali atatsala pang’ono kumwalira. Ntchito yowasamalira ndi kukwaniritsa maudindo anga ena inandikulira kwambiri. Kwa zaka zambiri, makolo onsewo ankatsutsa chikhulupiriro changa mwa Yehova, koma ndinayesa kuwasonyeza chikondi chonse chimene ndikanatha. Mayi anga atangotsala pang’ono kumwalira, ali ndi zaka 96, anandiuza kuti: “Sumiko, ngati nditadzaukitsidwa, ndidzalowa chipembedzo chako.” Pamenepa ndinazindikira kuti khama langa silinapite pachabe.

Mwamuna wanga ankaona zinthu zonse zimene ndinkachita posamalira makolo athuwa. Posonyeza kuyamikira, iye anayamba kufika kumisonkhano nthawi zonse. Anatero kwa zaka zambiri koma sanapite kwambiri patsogolo mwauzimu. Ndinapitiriza kuchita zinthu zom’sangalatsa. Ndinkaitana anzake ngakhalenso anthu ochokera kunja amene ankagwira nawo ntchito kuti adzadye chakudya kunyumba kwathu. Komanso ndinkachita naye limodzi zinthu zosiyanasiyana zosangalatsa. Atachepetsa maola a utumiki wa upainiya kuti akhale maola 70 pamwezi, ndinayamba kukhala naye kwa nthawi yaitali.

Zinthu Zinasintha Atapuma Pantchito

Mwamuna wanga anapuma pantchito mu 1993. Panthawiyi ndinaganiza kuti tsopano apeza mpata wophunzira Baibulo. Koma iye anandiuza kuti kuyamba  kupembedza Mulungu chifukwa choti wapeza mpata n’kupembedza kwachiphamaso. M’malo mwake iye anati adzayamba kupembedza Mulungu mtima wake ukadzafuna kutero ndipo anandiuza kuti ndisachite kumukakamiza.

Tsiku lina mwamuna wangayu anandifunsa ngati tsopano ndingagwiritse ntchito moyo wanga wonse m’njira yom’sangalatsa iyeyo. Zimenezi zinandiwawa, chifukwa choti chikwatiriraneni ndinkayesetsa kuchita chilichonse chimene ndikanatha kuti ndim’sangalatse. Ndinkayesetsa zedi kuti ndim’sangalatse, koma iye ankaona kuti ndinkachita zinthu zosangalatsa kwambiri Yehova kuposa iyeyo. Nditaganizira nkhaniyi kwakanthawi, ndinamuuza kuti sindingachite chilichonse chowonjezera pa zimene ndimam’chitira. Koma ndinati ngati anganditsate pa zimene ndinali kuchita, ndiye kuti iyeyo ndi ine tingathe kuyamba moyo wosangalatsa kwambiri umene tingakhale nawo osati kwa zaka zochepa chabe koma kosatha. Kwa masiku ambiri mwamuna wanga sananene maganizo ake pankhaniyi. Koma kenaka anandifunsa kuti: “Kodi ungathe kuphunzira nane Baibulo?” Tsiku lililonse ndikaganizira mawu amenewo, mtima wanga umagunda.

Poyamba ndinakonza zoti mkulu mumpingo aziphunzira naye, koma mwamuna wangayo anandiuza kuti: “Sindikufuna kuphunzitsidwa ndi munthu wina aliyense kupatulapo iweyo.” Motero tinayamba kuphunzira Baibulo tsiku lililonse. Poti ndili mumpingo wa Chitchaina tinkachita phunziroli mu Chitchaina chifukwa mwamuna wanga amachidziwanso bwino chinenerochi. Tinawerenganso limodzi Baibulo lonse chaka chisanathe.

Panthawi imeneyi, mbale wina yemwe ndi mkulu mumpingo wa Chitchaina anayamba kugwirizana nafe pamodzi ndi mkazi wake. Ngakhale kuti anali aang’ono poyerekezera ndi ana athu, iwo anakhala anzathu apamtima. A Mboni enanso ambiri anayamba kugwirizana ndi mwamuna wanga. Ankatichereza ndipo mwamuna wanga Kazuhiko ankacheza naye ngati bambo wawo. Zimenezi zinam’sangalatsa kwambiri.

Tsiku lina tinalandira kalata yotiitana ku ukwati wa anthu ena a mumpingo wathu ndipo kalatayo analembapo dzina la mwamuna wanga. Iye Anakhudzidwa mtima kwambiri kuti anam’sonyeza kuti ndi mutu wa banja, ndipo anaganiza zopita ku ukwatiwu. Posakhalitsa anayamba kuwamasukira a Mboniwo ndipo anayamba kuphunzira Baibulo ndi mkulu wina mumpingo. Anayamba kupita patsogolo mwauzimu chifukwa choti amachita phunziro la Baibulo, amapita kumisonkhano, ndiponso ankakondedwa kumpingo.

Banja Lathu Linagwirizana

M’mwezi wa December m’chaka cha 2000, mwamuna wanga anabatizidwa posonyeza kudzipereka kwake kwa Yehova. Ana athu ndi akazi awo anabwera kuchokera kutalikutali kuti adzaone “chozizwitsa” chimenechi. Inde, panatha zaka 42, komabe tsopano banja lathu lonse linagwirizana.

Tsopano m’mawa uliwonse, ine ndi mwamuna wanga timawerenga lemba la tsiku ndi kuwerenga Baibulo limodzi. Tsiku lililonse timacheza nkhani zauzimu ndipo timachitira limodzi zinthu zauzimu. Tsopano mwamuna wanga ndi mtumiki wothandiza mumpingo, ndipo posachedwapa anakamba nkhani ya onse ya m’Baibulo mu Chitchaina. Ndimathokoza Yehova chifukwa chotigwirizanitsa. Ndikufunitsitsa kuti kwa muyaya wonse, ineyo pamodzi ndi anthu onse apamtima panga tidzapititse patsogolo dzina lake ndi ufulu wake wolamulira.

[Mapu patsamba 13]

(Onani m’magazini yeniyeni kuti mumvetse izi)

CHINA

DEMOCRATIC PEOPLE’S REPUBLIC OF KOREA

REPUBLIC OF KOREA

Nyanja ya Japan

JAPAN

Tokyo

Nyanja ya Kummawa kwa China

TAIWAN

Taipei

[Chithunzi patsamba 12]

Ndili ndi banja langa, mu 1958, chaka chimene ndinabatizidwa

[Zithunzi patsamba 13]

Pamene tinasamuka ku Tokyo kupita ku Taipei tinalimbikitsidwa mwauzimu ndi anzathu monga Harvey ndi Kathy Logan

[Chithunzi patsamba 15]

Panopo banja langa n’logwirizana pa kulambira koona