Pitani ku nkhani yake

Pitani ku mitu ya nkhani

Anthu Nthawi Zambiri Amachotserana Ulemu

Anthu Nthawi Zambiri Amachotserana Ulemu

 Anthu Nthawi Zambiri Amachotserana Ulemu

“Chilichonse chokhudza moyo wa kundende yozunzira anthu chinali chom’chotsera munthu ulemu wake.”​—ANATERO MAGDALENA KUSSEROW REUTER, YEMWE ANAPULUMUKA KU NDENDE YOZUNZIRAKO ANTHU YA ANAZI.

NGAKHALE kuti nkhanza zimene zinkachitika m’ndende zozunzirako anthu za chipani cha Nazi pa nkhondo yachiwiri ya padziko lonse zinali zosaneneka, imeneyi siinali nthawi yoyamba kapenanso yotsiriza kuti anthu awachotsere ulemu wawo. Kaya tiganizire za kale kapena za masiku ano, mfundo yoonekeratu n’njakuti: Anthu anayamba ‘kuwachotsera ulemu wawo’ kuyambira kale kwambiri.

Komatu si nkhanza za kale zokha zimene zakhala zikuchotsera anthu ulemu wawo. Nthawi zambiri anthu amawachotsera ulemu wawo m’njira zosaonekera kwambiri. Mwachitsanzo, mwana angathe kumanyozedwa ndi anzake chifukwa cha maonekedwe enaake a thupi lake. Kapenanso munthu wochokera kunja angathe kumasekedwa chifukwa cha zochita zinazake “zakunja.” Komanso munthu angathe kumasalidwa chifukwa cha mtundu wa khungu lake kapena chifukwa cha fuko lake. Anthu ochita zimenezi angamaone ngati ndi nkhani yoseketsa, koma kuwawidwa mtima kwa anthu amene akunyozedwa m’njira imeneyi si nkhani yoseketsa ayi.​—Miyambo 26:18, 19.

Kodi Ulemu N’chiyani?

Buku lina lotanthauzira mawu limati, ulemu ndi “khalidwe labwino lodzilemekeza ndi kulemekezanso anthu ena.” Motero ulemu umakhudza  mmene timadzionera patokha ndiponso mmene anthu ena amachitira nafe zinthu. N’zoona kuti pali zinthu zosiyanasiyana zimene zimakhudza mmene timadzionera, koma chinthu china chimene chimakhudza kwambiri ulemu umene timadzipatsa tsiku ndi tsiku ndicho mmene anthu ena amationera ndi mmene amachitira nafe zinthu.

Kulikonseko kuli anthu osauka, osatha kudziteteza, ndiponso osavuta kudyeredwa masuku pamutu. Mavuto amenewa paokha sachititsa munthu kusiya kudziona kuti n’ngoyenera kupatsidwa ulemu. Koma zochita za anthu ena ndi zimene zingachititse munthu kudziona kuti n’ngosayenera kupatsidwa ulemu. N’zomvetsa chisoni kuti anthu ovutika ndi amene amachotseredwa ulemu wawo. Nthawi zambiri tikamva kuti anthu okalamba, osauka, kapenanso amisala ndi opunduka amazunzidwa, timauzidwa kuti ankawatchula kuti “opanda ntchito,” “achabechabe,” ndiponso “zitsiru.”

N’chifukwa chiyani anthu amachotserana ulemu choncho? Kodi zidzatheka kuti anthu adzakhale ndi ufulu wawo wopatsidwa ulemu, womwe uli ufulu wofunikira kwambiri? Nkhani yotsatirayi ipereka yankho logwira mtima lochokera m’Mawu a Mulungu, Baibulo.