Pitani ku nkhani yake

Pitani ku mitu ya nkhani

Yehova Amalanditsa Wovutika

Yehova Amalanditsa Wovutika

 Yehova Amalanditsa Wovutika

“Masautso a wolungama mtima achuluka: Koma Yehova am’landitsa mwa onsewa.”​—SALMO 34:19.

1, 2. Kodi Mkristu wina wokhulupirika anakumana ndi vuto lotani, ndipo n’chifukwa chiyani nafenso tingakumane ndi mavuto ofanana ndi limeneli?

MTSIKANA wina, dzina lake Keiko * wakhala mmodzi wa Mboni za Yehova kwa zaka zoposa 20. Panthawi ina ankatumikira monga mpainiya wokhazikika, kapena kuti wolengeza Ufumu wa nthawi zonse. Iye ankakonda kwambiri utumiki wapadera umenewu. Koma chaposachedwapa, Keiko anayamba kuvutika chifukwa chothedwa nzeru ndiponso kudzimva kuti anali yekhayekha. Iye anati: “Ndinkangokhalira kulira.” Pofuna kuthetsa kuvutika maganizo kumeneku, Keiko ankathera nthawi yochuluka kuchita phunziro laumwini. Iye anati: “Koma sindinathe kuthetsa maganizo amenewa. Zinthu zinafika poipa kwambiri moti ndinkangofuna kumwalira.”

2 Kodi inunso mwavutikapo chifukwa chothedwa nzeru? Popeza ndinu wa Mboni za Yehova, muli ndi zifukwa zambiri zokhalira wosangalala chifukwa chipembedzo “chikhala nalo lonjezano la ku moyo uno, ndi la moyo ulinkudza.” (1 Timoteo 4:8) Panopo muli m’paradaiso wauzimu. Koma kodi zimenezi zikutanthauza kuti timatetezedwa ku mavuto onse? Ayi. Baibulo limati: “Masautso a wolungama mtima achuluka.” (Salmo 34:19) Zimenezi sizodabwitsa chifukwa “dziko lonse lapansi ligona mwa woipayo,” Satana Mdyerekezi. (1 Yohane 5:19) Mwa njira zina, ife tonse timakhudzidwa ndi ulamuliro womwe Mdyerekezi ali nawo padziko lapansi.​—Aefeso 6:12.

Zotsatirapo za Kuvutika

3. Tchulani zitsanzo za m’Baibulo za atumiki a Mulungu omwe anavutikapo kwambiri.

3 Kuvutika nthawi yaitali kungasokoneze kaonedwe kathu ka zinthu zonse. (Miyambo 15:15) Taganizirani za munthu wolungama Yobu. Nthawi imene ankavutika kwambiri, anati: “Munthu wobadwa ndi mkazi n’ngwa masiku owerengeka, nakhuta mavuto.” (Yobu 14:1) Chimwemwe chonse cha Yobu chinali chitatheratu. Moti panthawi ina anafika poganiza kuti Yehova anali atam’taya. (Yobu 29:1-5) Yobu sanali mtumiki wa Mulungu yekhayo yemwe anavutika kwambiri. Baibulo limatiuza kuti Hana anali ndi “mtima wowawa” chifukwa chosakhala ndi mwana. (1 Samueli 1:9-11) Atavutika chifukwa cha mmene zinthu zinalili m’banja mwake, Rebeka anati: “Ndalema moyo wanga.” (Genesis 27:46) Poganizira zolakwa zake, Davide  anati: “Ndimayenda woliralira tsiku lonse.” (Salmo 38:6) Zitsanzo zochepazi zikusonyeza bwino kuti amuna ndi akazi oopa Mulungu omwe anakhalako Chikristu chisanayambe, nthawi zina ankavutika kwambiri.

4. N’chifukwa chiyani n’zosadabwitsa kuti masiku ano pali Akristu ovutika maganizo?

4 Nanga bwanji za Akristu? Mtumwi Paulo anaona kuti kunali koyenera kuuza Atesalonika kuti “limbikitsani amantha mtima” kapena kuti ovutika maganizo. (1 Atesalonika 5:14) Buku lina linati liwu la Chigiriki lomasuliridwa kuti “amantha mtima” lingatanthauze anthu omwe “akhala akuvutika maganizo kwa kanthawi kochepa chifukwa cha zinthu zina pa moyo wawo.” Mawu a Paulo akusonyeza kuti Akristu ena odzozedwa ndi mzimu mumpingo wa ku Tesalonika ankavutika maganizo. Masiku ano palinso Akristu omwe akuvutika maganizo. Koma n’chifukwa chiyani akuvutika maganizo? Tiyeni tikambirane zinthu zitatu zomwe nthawi zambiri zimachititsa Akristu ena kuvutika maganizo.

Tingavutike Maganizo Chifukwa cha Kupanda Ungwiro

5, 6. Kodi n’chitonthozo chotani chomwe timapeza pa Aroma 7:22-25?

5 Mosiyana ndi anthu oipa omwe ndi opandiratu khalidwe, Akristu oona amamva chisoni chifukwa cha kupanda ungwiro kwawo. (Aefeso 4:19) Iwo angamve mofanana ndi Paulo yemwe analemba kuti: “Pakuti monga mwa munthu wa m’kati mwanga, ine ndikondwera ndi chilamulo cha Mulungu: koma ndiona lamulo lina m’ziwalo zanga, lilikulimbana ndi lamulo la mtima wanga, ndi kundigonjetsa kapolo wa lamulo la m’ziwalo zanga.” Ndiyeno Paulo anati: “Munthu wosauka ine.”​—Aroma 7:22-24.

6 Kodi munayamba mwamvapo mofanana ndi Paulo? Sikuti n’kulakwa kudziwa bwino zofooka zanu, chifukwa zimenezi zingakuthandizeni kuona kuipa kwa tchimo ndipo zingakulimbikitseni kukhala wotsimikiza kupewa zoipa. Koma simufunikira kukhala wovutika maganizo nthawi zonse chifukwa cha zofooka zanu. Pa mawu ake osonyeza kuvutika maganizo omwe angotchulidwa kumenewa, Paulo anawonjezera kuti: “Ndiyamika Mulungu, mwa Yesu Kristu Ambuye wathu.” (Aroma 7:25) Ndithudi, Paulo anali ndi chikhulupiriro choti mwazi wokhetsedwa wa Yesu udzamuwombola ku uchimo wobadwa nawo.​—Aroma 5:18.

7. Kodi n’chiyani chingathandize munthu kuti asamavutike maganizo chifukwa cha zizolowezi zake zoipa?

7 Ngati mumavutika maganizo chifukwa cha kupanda ungwiro, mawu a mtumwi Yohane angakulimbikitseni. Iye analemba kuti: “Akachimwa wina, Nkhoswe tili naye kwa Atate, ndiye Yesu Kristu wolungama; ndipo Iye ndiye chiombolo cha machimo athu; koma wosati athu okha, komanso a dziko lonse lapansi.” (1 Yohane 2:1, 2) Mukamavutika maganizo chifukwa cha zizolowezi zanu zoipa, kumbukirani nthawi zonse kuti Yesu anafera anthu ochimwa osati angwiro. Ndipotu, ‘onse anachimwa, naperewera pa ulemerero wa Mulungu.’​—Aroma 3:23.

8, 9. N’chifukwa chiyani tiyenera kupewa maganizo odziimba mlandu?

8 Koma bwanji ngati kale munachita tchimo lalikulu? Mosakayikira, munam’fotokozera Yehova nkhaniyo m’pemphero, ndipo mwina munachita zimenezi nthawi zambiri. Munalandira thandizo lauzimu kuchokera kwa akulu achikristu. (Yakobo 5:14, 15) Munali wolapadi ndipo n’chifukwa chake mudakali mumpingo. Kapena mwina kwa kanthawi kochepa munasiya gulu la Mulungu, koma m’kupita kwa nthawi munalapa ndipo munakhala ndi makhalidwe abwino. Mulimonse mmene zinthu zinakhalira, mungakumbukire tchimo lanu lakale ndipo lingakuvutitseni maganizo. Zikakhala choncho, kumbukirani kuti Yehova amakhululukira “koposa” anthu olapadi. (Yesaya 55:7) Ndiponso iye safuna kuti inuyo muzimva kuti machimo anu sangakhululukidwe. Satana ndi yemwe amafuna kuti tizimva choncho. (2 Akorinto 2:7, 10, 11) Mdyerekezi adzawonongedwa ndipo n’zomwe zili zomuyenerera, koma iye amafuna kuti inunso muzimva kuti ndinu woyenera kuwonongedwa. (Chivumbulutso 20:10) Musalole Satana kuti awononge chikhulupiriro chanu mochenjera chonchi. (Aefeso 6:11) M’malo mwake, “mum’kanize” iye ndi machenjera akewa monga momwe mumachitira pa zinthu zina.​—1 Petro 5:9.

 9 Pa Chivumbulutso 12:10, Satana amatchedwa “wonenera wa abale athu,” Akristu odzozedwa. Iye ‘amawanenera usana ndi usiku’ pamaso pa Mulungu. Kuganizira lembali kungakuthandizeni kuona kuti Satana, wonenera wabodza, amasangalala tikamadziimba mlandu ndi kudziona wosafunikira, ngakhale kuti Yehova satiimba mlandu. (1 Yohane 3:19-22) Motero, n’kumavutikiranji maganizo chifukwa cha zofooka zanu, mpaka n’kumaona kuti ndi bwino kusiya kutumikira Mulungu? Musalole Satana kuwononga ubwenzi wanu ndi Mulungu. Musalekerere Mdyerekezi kuti akuchititseni kunyalanyaza mfundo yoti Yehova ndi “wachifundo ndi wachisomo, wolekereza, ndi wa ukoma mtima wochuluka.”​—Eksodo 34:6.

Zomwe Timalephera Kuchita Zingatifooketse

10. Kodi zolephera zathu zingatifooketse motani?

10 Akristu ena amafooledwa chifukwa cha mmene zolephera zawo zimakhudzira kutumikira kwawo Mulungu. Kodi ndi mmene zilili kwa inuyo? Mwinamwake, matenda, ukalamba kapena zinthu zina pa moyo wanu zikukulepheretsani kuthera nthawi yochuluka muutumiki monga momwe munkachitira kale. N’zoona kuti Akristu amalimbikitsidwa kuwombola nthawi yotumikira Mulungu. (Aefeso 5:15, 16) Koma bwanji ngati zinthu zina zokulepheretsani kuchita zambiri muutumiki zilipodi ndipo zimenezi zikukulefulani?

11. Kodi uphungu wa Paulo wolembedwa pa Agalatiya 6:4 ungatithandize motani?

11 Baibulo limatilangiza kuti tisakhale aulesi koma “akuwatsanza iwo amene alikulowa malonjezano.” (Ahebri 6:12) Tingachite zimenezi kokha ngati tiona zitsanzo zawo ndi kuyesetsa kutsanzira chikhulupiriro chawo. Koma sizingatithandize ngati tikudziyerekezera ndi ena mosayenera ndipo n’kumanena kuti palibe chabwino chomwe tingachite. Motero, zingakhale bwino kugwiritsa ntchito uphungu wa Paulo wakuti: “Yense ayesere ntchito yake ya iye yekha, ndipo pamenepo adzakhala nako kudzitamandira chifukwa cha iye yekha, si chifukwa cha wina.”​—Agalatiya 6:4.

12. N’chifukwa chiyani tingakhale osangalala potumikira Yehova?

12 Akristu ali ndi zifukwa zabwino zokhalira osangalala, ngakhale panthawi yomwe akulephera kuchita zinthu zina chifukwa cha matenda aakulu. Baibulo limatitsimikizira kuti: “Mulungu sali wosalungama kuti adzaiwala ntchito yanu, ndi chikondicho mudachionetsera ku dzina lake.” (Ahebri 6:10) Mwinamwake, zinthu zina zomwe simungathe kusintha zikukulepheretsani kutumikira Yehova monga momwe munkachitira kale. Koma mothandizidwa ndi Yehova, mwina mungathe kuchita nawo mokwanira mbali zina za utumiki wachikristu, monga ulaliki wa patelefoni ndi kulemba makalata. Khalani wotsimikiza kuti Yehova Mulungu adzakudalitsani chifukwa cha kum’tumikira ndi mtima wonse ndiponso chifukwa cha chikondi chimene muli nacho pa Iye komanso anthu ena.​—Mateyu 22:36-40.

Tingavutike Maganizo Chifukwa cha “Nthawi Zowawitsa”

13, 14. (a) Kodi “nthawi zowawitsa” zingativutitse maganizo m’njira zotani? (b) Kodi kupanda chikondi chachibadwidwe kukuonekera motani masiku ano?

13 Ngakhale kuti tikuyembekezera kudzakhala m’dziko lapansi latsopano ndi lolungama la Mulungu, panopo tikukhala mu “nthawi zowawitsa.” (2 Timoteo 3:1) N’zolimbikitsa kudziwa kuti zinthu zovutitsa maganizo zomwe zikuchitikazi zikusonyeza kuyandikira kwa chipulumutso chathu. Koma timakhudzidwa ndi mmene zinthu zilili panopo. Mwachitsanzo, kodi kukhala paulova kumakukhudzani motani? Ntchito zingakhale zovuta kupeza, ndipo m’kupita kwa nthawi, mungayambe kudzifunsa ngati Yehova akuona vuto lanulo kapena ngati amamva mapemphero anu. Kapena anthu ena mwina amakusankhani kapena kukuchitirani zinthu zina mopanda chilungamo. Ngakhale kuwerenga mitu ya nkhani za m’nyuzipepala kungakupangitseni kumva monga momwe mwamuna wolungama Loti anachitira. Iye anali “wolema mtima” (“ankavutika,” Chipangano Chatsopano mu Chichewa cha Lero) ndi mayendedwe onyansa a anthu omwe anayandikana nawo.​—2 Petro 2:7.

14 Pali mbali ina ya masiku otsiriza yomwe  sitifunikira kuinyalanyaza. Baibulo linalosera kuti anthu ambiri adzakhala “opanda chikondi chachibadwidwe.” (2 Timoteo 3:3) Kukondana kwa pachibale kukusowa kwambiri m’mabanja ambiri. Ndithudi, “umboni ukusonyeza kuti anthu akuphedwa, kumenyedwa, kuvutitsidwa kapena kugwiriridwa ndi anthu a m’banja mwawo kuposa anthu ena. Malo amene anthu ayenera kuona kuti akukondedwa ndipo ali otetezeka ndi amene akhala oopsa kwambiri kwa ena mwa achikulire ndi ana omwe,” linatero buku lakuti Family Violence. Anthu omwe analeredwa mwankhanza m’kupita kwa nthawi angakhale ndi nkhawa ndiponso angathedwe nzeru. Bwanji ngati zoterozi zakuchitikirani?

15. Kodi chikondi cha Yehova chimaposa motani cha munthu wina aliyense?

15 Wamasalmo Davide anaimba kuti: “Pakuti wandisiya atate wanga ndi amayi wanga, koma Yehova anditola.” (Salmo 27:10) N’zolimbikitsa kudziwa kuti chikondi cha Yehova chimaposa cha kholo lina lililonse. Ngakhale kuti kukanidwa ndiponso kuzunzidwa ndi makolo kungakhale kowawa kwambiri, sikungasinthe mmene Yehova amatisamalirira. (Aroma 8:38, 39) Kumbukirani kuti Yehova amakoka munthu yemwe wakonda. (Yohane 3:16; 6:44) Zilibe kanthu kuti anthu akhala akukuchitirani zotani, Atate wanu wakumwamba amakukondani.

Zomwe Zingatithandize Kuchepetsa Kuvutika Maganizo

16, 17. Kuti munthu akhalebe ndi nyonga zauzimu, kodi ayenera kuchita chiyani akathedwa nzeru?

16 Mungathe kuchita zinthu zokuthandizani kuti mupirire kuvutika maganizo. Mwachitsanzo, chitani nawo mokwanira utumiki wachikristu. Sinkhasinkhani Mawu a Mulungu, makamaka pamene mukuona kuti mulefulidwa kwambiri. Wamasalmo anaimba kuti: “Pamene ndinati, Literereka phazi langa, chifundo chanu, Mulungu, chinandichirikiza. Pondichulukira zolingalira zanga m’kati mwanga, zotonthoza zanu zikondweretsa moyo wanga.” (Salmo 94:18, 19) Kuwerenga Baibulo nthawi zonse kudzakuthandizani kuti mukhale ndi mawu otonthoza m’maganizo mwanu ndiponso mfundo zolimbikitsa.

17 Pemphero nalonso n’lofunika. Ngakhale kuti simungathe kufotokoza bwinobwino mmene mukumvera, Yehova amadziwa zimene mukufuna kunena. (Aroma 8:26, 27) Wamasalmo ananena mawu olimbikitsa awa: “Um’senze Yehova nkhawa zako, ndipo Iye adzakugwiriziza: Nthawi zonse sadzalola wolungama agwedezeke.”​—Salmo 55:22.

18. Kodi n’zinthu zothandiza zotani zimene munthu wovutika maganizo angachite?

18 Anthu ena amathedwa nzeru chifukwa cha matenda a maganizo. * Ngati mukuvutika ndi  matenda a maganizo, yesani kuganizirako za dziko latsopano la Mulungu ndiponso nthawi imene “wokhalamo sadzanena, Ine ndidwala.” (Yesaya 33:24) Ngati mukuona kuti mwavutika maganizo kwa nthawi yaitali, zingakhale bwino kupeza dokotala woti akuthandizeni. (Mateyu 9:12) Mufunikiranso kusamalira thupi lanu. Kudya chakudya cha magulu ndi kuchita zinthu zolimbitsa thupi kungakuthandizeni. Onetsetsani kuti mukukhala ndi nthawi yopumula. Musamagone mochedwa n’kumangoonerera TV ndipo pewani zosangalatsa zomwe zingatopetse thupi ndi maganizo anu. Koposa zonse, pitirizani kuchita ntchito zosangalatsa Mulungu. Ngakhale kuti ino si nthawi yoti Yehova ‘apukute misozi yonse,’ adzatithandiza kupirira.​—Chivumbulutso 21:4; 1 Akorinto 10:13.

Kukhala “Pansi pa Dzanja la Mphamvu la Mulungu”

19. Kodi n’chiyani chimene Yehova walonjeza anthu ovutika?

19 Baibulo limatitsimikizira kuti ngakhale kuti masautso a wolungama mtima ndi ambiri, “Yehova am’landitsa mwa onsewa.” (Salmo 34:19) Kodi Mulungu amachita bwanji zimenezi? Pamene mtumwi Paulo anapemphera mobwerezabwereza kuti “munga m’thupi” umuchoke, Yehova anamuuza kuti: “Mphamvu yanga ithedwa m’ufooko.” (2 Akorinto 12:7-9) Kodi Yehova analonjeza Paulo chiyani, ndipo akutilonjeza chiyani? Yehova salonjeza kuthetsa masautso panopo, koma watilonjeza mphamvu zoti tipirire.

20. Ngakhale kuti tikukumana ndi mayesero, kodi lemba la 1 Petro 5:6, 7, limatitsimikizira chiyani?

20 Mtumwi Petro analemba kuti: “Dzichepetseni pansi pa dzanja la mphamvu la Mulungu, kuti panthawi yake akakukwezeni; ndi kutaya pa Iye nkhawa yanu yonse pakuti Iye asamalira inu.” (1 Petro 5:6, 7) Yehova sadzakutayani chifukwa amakuganizirani. Iye adzakuthandizani ngakhale pamene mukukumana ndi mayesero. Kumbukirani kuti Akristu okhulupirika ali “pansi pa dzanja la mphamvu la Mulungu.” Pamene tikutumikira Yehova, amatipatsa nyonga zoti tipirire. Tikakhala okhulupirika kwa iye, palibe chimene chingatiwononge mwauzimu mpaka muyaya. Motero, tiyeni tikhale okhulupirika kwa Yehova kotero kuti tidzakhale ndi moyo wosatha m’dziko lapansi latsopano limene walonjeza, ndipo tidzaone tsiku limene Yehova adzapulumutsedi kotheratu wovutika.

[Mawu a M’munsi]

^ ndime 1 Dzina lasinthidwa.

^ ndime 18 Matenda a maganizo sikuvutika maganizo wamba koma ndi matenda omwe amapangitsa munthu kuvutika maganizo kwambiri komanso nthawi yaitali. Kuti mumve zambiri, onani magazini a Nsanja ya Olonda a October 15, 1988, masamba 25 mpaka 29; November 15, 1988, masamba 21 mpaka 24; ndi September 1, 1996, masamba 30 mpaka 31.

Kodi Mukukumbukira?

• N’chifukwa chiyani ngakhale atumiki a Yehova amavutika?

• Kodi n’zinthu zotani zimene zingachititse anthu a Mulungu ena kuvutika?

• Kodi Yehova amatithandiza motani kupirira nkhawa zathu?

• Kodi tili “pansi pa dzanja la Mulungu” m’njira yotani?

[Mafunso]

[Zithunzi patsamba 25]

Ngakhale kuti anthu a Yehova akukumana ndi mayesero, ali ndi chifukwa chabwino chokhalira osangalala

[Chithunzi patsamba 28]

Ulaliki wa patelefoni ndi njira imodzi imene mungatumikirire Yehova ndi mtima wonse