Pitani ku nkhani yake

Pitani ku mitu ya nkhani

Amakonda Kuchita Chifuniro cha Mulungu

Amakonda Kuchita Chifuniro cha Mulungu

 Amakonda Kuchita Chifuniro cha Mulungu

YESU anakhazikitsa chitsanzo kwa Akristu onse mwa kupemphera kwa Atate wake kuti: “Si kufuna kwanga ayi, komatu kwanu kuchitike.” (Luka 22:42) Mamiliyoni a atumiki a Mulungu masiku ano amachita mogwirizana ndi pemphero limeneli, losonyeza kugonjera kwa Yehova modzichepetsa. Ena mwa atumiki amenewo ndi ophunzira 52 a m’kalasi ya nambala 120 ya Sukulu ya Gileadi ya Watchtower Yophunzitsa Baibulo. Atamaliza maphunziro awo pa March 11, 2006, ophunzirawo anasangalala kwambiri chifukwa cha chiyembekezo chawo chokatumikira Mulungu m’mayiko osiyanasiyana, ngakhale kuti akakumana ndi mavuto.

Kodi chinawachititsa ophunzirawa kuti aziyendera chifuniro cha Yehova pa moyo wawo n’chiyani? Chris ndi mkazi wake Leslie, omwe anawatumiza kukachita umishonale ku Bolivia, anati: “Popeza ife tadzikana tokha, ndife okonzeka kuchita ntchito iliyonse ya m’gulu la Yehova.” (Marko 8:34) Jason ndi Chere, omwe anatumizidwa ku Albania anati: “Utumiki uliwonse womwe tachitapo m’gulu la Yehova wakhala ndi zovuta zake. Komabe, tikupitiriza kudalira Yehova kwambiri.”

Analimbikitsidwa Kugonjera Chifuniro cha Yehova

Yemwe anapereka pemphero loyamba pa pulogalamuyo ndi George Smith, wa m’banja la Beteli ndipo amatumikira m’Dipatimenti Yojambula Zithunzi. Tcheyamani wa pulogalamuyo, Stephen Lett, wa m’Bungwe Lolamulira la Mboni za Yehova, analandira ndi manja awiri anthu onse omwe anasonkhana. Alendo ochokera m’mayiko 23 anafika ku mwambo wosangalatsawu ku Likulu la Maphunziro la Watchtower ku Patterson, mu mzinda wa New York. Mbale Lett anauza anthu omaliza maphunzirowo kuti adzachita zinthu “zamphamvu.” Anawalimbikitsa ‘kukapasula malinga,’ monga ziphunzitso zonyenga, zomwe amishonale atsopanowo akazigonjetse mwamphamvu ya Malemba. (2 Akorinto 10:4, 5) Anamaliza ndi mawu oti: “Yehova akamakakugwiritsani ntchito yogwetsa malinga kwa anthu oona mtima mu utumiki wanu, mudzakhala ndi chimwemwe kwambiri!”

Harold Jackson, yemwe amatumikira kulikulu la Mboni za Yehova, anakamba nkhani ya mutu wakuti “Zinthu Zingapo Zoti Muzikumbukira.” Iye anati amishonalewo asakaiwale ‘kufuna ufumu choyamba ndi chilungamo cha Mulungu.’ (Mateyu 6:33) Azikumbukiranso kuti ‘chikondi chimamangirira’ ndipo n’chofunika kwambiri kuti apambane mu utumiki wawo. (1 Akorinto 8:1) Iye anati: “Chikondi chizikutsogolerani m’zochita zanu ndi anthu ena.”

Kenako, Geoffrey Jackson, wa m’Bungwe Lolamulira yemwenso anali m’mishonale kuyambira mu 1979 mpaka mu 2003, anafunsa ophunzirawo kuti, “Kodi ndi Udindo Wanu?” Iye anagogomezera kufunika koti azidziona moyenerera eni akewo ndi utumiki wawo. Akristu ali ndi udindo wogwira ntchito yodzala ndi kuthirira mbewu za choonadi mwakhama. Komabe, yemwe ali ndi udindo wokulitsa mwauzimu ndi Yehova, chifukwa ‘Mulungu ndiye  amakulitsa.’ (1 Akorinto 3:6-9) Mbale Jackson anawonjezera kuti: “Yehova amayembekezera kuti mukhalebe olimba mwauzimu. Koma kodi udindo wanu waukulu kwambiri ndi wotani? Kukonda Yehova ndi kukondanso anthu omwe mukawatumikire.”

Mlangizi wa Gileadi, Lawrence Bowen anakamba nkhani ya mutu wakuti “Dziwani Mmene Mukachitire Zinthu.” Anawakumbutsa ophunzirawo kuti Yehova anatsogolera ndi kuteteza Aisrayeli modabwitsa m’chipululu. (Eksodo 13:21, 22) Njira imodzi imene Yehova amatitsogolera ndi kutiteteza masiku ano ndi mwa kugwiritsa ntchito gulu la Akristu odzozedwa, omwe ndi “mzati ndi mchirikizo wa choonadi.” (1 Timoteo 3:14, 15) Amishonale atsopanowo ayenera kuchirikiza choonadi, chomwe chimatsogolera ndi kuteteza anthu odzichepetsa.

 Mlangizi wina wa Gileadi, Wallace Liverance, analimbikitsa ophunzirawo kuti asakaiwale mawu a Mulungu omwe ali “kumbuyo” kwawo. Mawu a Mulungu ali kumbuyo kwathu m’lingaliro lakuti Baibulo linamalizidwa kulembedwa zaka mazana ambiri m’mbuyomu. Monga mbusa amene potsogolera nkhosa amakhala kumbuyo kwa gulu la nkhosalo, Yehova ali kumbuyo kwa anthu ake, kuwapatsa malangizo kudzera mwa “kapolo wokhulupirika ndi wanzeru.” (Yesaya 30:21; Mateyu 24:45-47) Sukulu ya Gileadi yathandiza anthu omaliza maphunzirowo kuyamikira gulu la kapolo limeneli. Ndipotu “kapolo” waperekanso Baibulo la New World Translation of the Holy Scriptures. Wokamba nkhaniyi analimbikitsa amishonale atsopanowo kuti: “Tengani chuma chimenechi, ndipo mukachigwiritse ntchito pophunzitsa anthu ena.”​—Mateyu 13:52.

Kuchita Chifuniro cha Yehova mu Utumiki wa Kumunda

M’nkhani yakuti “Ofunitsitsa Kulalikira Uthenga Wabwino,” mlangizi wina wa Gileadi, Mark Noumair, analongosola zina mwa zinthu zosangalatsa zomwe ophunzirawo anakumana nazo mu ulaliki wawo panthawi yomwe anali pa Sukulu ya Gileadiyo. (Aroma 1:15) Anafunsa mafunso ophunzirawo, ndipo zimenezi zinaonetsa bwino kuti analidi ofunitsitsa kulalikira panthawi iliyonse yomwe anali ndi mpata.

Amishonale atsopanowo analimbikitsidwanso pamene Mbale Kenneth Flodin anafunsa mafunso oyang’anira oyendayenda atatu amene tsopano akutumikira ku United States. Richard Keller ndi Alejandro Lacayo, amene anatumikirapo ku South America ndiponso ku Central America, analongosola mmene anapiririra ziyeso zosiyanasiyana, ndiponso anatchula ena mwa madalitso amene anapeza m’nthawi imene anali amishonale. Moacir Felisbino, analongosola za mmene amishonale anam’thandizira pa nthawi imene iye ankagwira nawo ntchito limodzi ku Brazil, komwe anakulira.

David Schafer, anafunsa mafunso Robert Jones, Woodworth Mills, ndi Christopher Slay, omwe ndi amishonale aluso. Abale atatuwa analongosola mmene anaphunzirira kuchita zinthu modalira Yehova pamene akumana ndi mavuto. Iwo anatsimikizira amishonale atsopanowo kuti maphunziro omwe alandira m’gulu la Yehova, ndi othandiza kwambiri mu utumiki wawo wa umishonale. Mbale Mills anamaliza motere: “Chomwe chinandithandiza kwambiri si mfundo zakuya ndi zochititsa chidwi za ku Gileadi ayi, koma kudzichepetsa ndi chikondi zomwe ndinaphunzira kusukuluyi.”

Guy Pierce yemwe ndi wa m’Bungwe Lolamulira, anakamba nkhani yaikulu ya mutu wakuti “Yehova Salephera.” Adamu analephera, koma kodi zimenezi zikutanthauza kuti Mulungu analephera? Kodi Mulungu analephera kulenga Adamu wangwiro, monga mmene anthu ena amanenera? Ayi, chifukwa “Mulungu analenga anthu owongoka mtima.” (Mlaliki 7:29) Mmene Yesu anakhalira wokhulupirika kwambiri panthawi ya ziyeso zikuluzikulu, zimasonyeza kuti “Adamu analibe zifukwa zodzikhululukira, analibe chifukwa cholepherera,” anatero wokamba nkhaniyo. Chiyeso chomwe Adamu anakumana nacho m’munda wa Edeni chinali chosavuta poyerekezera ndi ziyeso zomwe Yesu anazigonjetsa. Ngakhale zinatero, Adamu analephera. Koma Yehova salephera. Cholinga chake chidzakwaniritsidwa. (Yesaya 55:11) Mbale Pierce anauza amishonale atsopanowo kuti: “Muli ndi mwayi wolemekeza Yehova ndi mzimu wodzimana. Yehova akhale ndi wina aliyense wa inu kulikonse komwe mukatumikire monga amishonale.”

Atamaliza kupereka moni wochokera ku maofesi a nthambi a Mboni za Yehova a m’mayiko osiyanasiyana, Mbale  Lett, tcheyamani wa pulogalamuyo, anapereka madipoloma kwa ophunzirawo ndipo aliyense anauzidwa komwe akatumikire. Vernon Wisegarver, yemwe watumikira kwa nthawi yaitali pa Beteli, anapereka pemphero lomaliza.

Anthu onse 6,872 omwe anasonkhana pamwambowo anati pulogalamuyo inawonjezera changu chawo pochita chifuniro cha Mulungu. (Salmo 40:8) Ena mwa omaliza maphunzirowo, Andrew ndi Anna anati: “Tinapereka miyoyo yathu kwa Yehova. Tinalonjeza Yehova kuti tidzachita chilichonse chomwe angatiuze. Ndipo Yehova watiuza kuti tipite ku Cameroon, ku Africa.” Iwo pamodzi ndi anzawo amene amaliza maphunzirowo, ndi ofunitsitsa kuchita ntchito yomwe idzawakhutiritsa ndi kuwasangalatsa. Inde, iwo amakonda kuchita chifuniro cha Mulungu.

[Bokosi patsamba 17]

ZA OPHUNZIRAWO

Chiwerengero cha mayiko kumene ophunzira anachokera: 6

Chiwerengero cha mayiko kumene anawatumiza: 20

Chiwerengero cha ophunzira: 52

Avereji ya zaka zakubadwa: 35.7

Avereji ya zaka zimene akhala m’choonadi: 18.3

Avereji ya zaka zimene akhala mu utumiki wa nthawi zonse: 14.5

[Chithunzi patsamba 18]

Kalasi la Nambala 120 la Omaliza Maphunziro a Sukulu ya Gileadi ya Watchtower Yophunzitsa Baibulo

Pa m’ndandanda umene uli pansipa, mizera yayambira kutsogolo kupita kumbuyo, ndipo mayina tawandandalika kuyambira kumanzere kupita kumanja mumzera uliyonse.

(1) Wright, S.; Suárez, B.;Croisant, B.Davenport, L. (2) Johnson, A.; Ali, C.; Cady, K.; Guerrero, P.; Ases, A. (3) Ortiz, L.; Lyall, K.; Uzeta, M.; Perez, R.; Backus, K.; Caterina, C. (4) Palmer, B.; Loving, D.; Macdonough, J.; Bostock, D.; Benetatos, L. (5) Jasicki, M.; Sarafianos, E.; Stelter, C.; Vaira, R.; Woon, J.; Prentice,  K. (6) Davenport, H.; Croisant, H.; Perez, M.; Vaira, E.; Suárez, A.; Caterina, I.; Wright, C. (7) Cady, K.; Macdonough, J.; Ortiz, M.; Woon, J.; Ali, J.’ Ases, M. (8) Sarafianos, G.; Lyall, D.; Uzeta, C.; Stelter, P.; Prentice, G.; Johnson, A.; Benetatos, C. (9) Palmer, J.; Jasicki, W.; Backus, J.; Bostock, S.; Guerrero, J.M.; Loving, S.