Pitani ku nkhani yake

Pitani ku mitu ya nkhani

Phunziro Lonena za Kunyada ndi Kudzichepetsa

Phunziro Lonena za Kunyada ndi Kudzichepetsa

 Phunziro Lonena za Kunyada ndi Kudzichepetsa

ZOMWE zinachitikira Mfumu Davide nthawi ina zikusonyeza kusiyana kwa kudzichepetsa kwenikweni ndi kunyada. Zinachitika Davide atagonjetsa mzinda wa Yerusalemu n’kuusandutsa likulu lake. Davide ankaona kuti Yehova ndiye Mfumu yeniyeni ya Israyeli, ndipo anakonza zoti Likasa, lomwe linkaimira kukhalapo kwa Mulungu, lipititsidwe mu mzindawo. Zimenezi zinali zofunika kwambiri kwa Davide moti anasonyeza chimwemwe chake kwa onse pamene ankatsatira ansembe amene ananyamula Likasalo. Anthu a ku Yerusalemu anaona Davide mfumu yawo “ali kutumphatumpha” ndi ‘kuvina ndi mphamvu yake yonse.’​—1 Mbiri 15:15, 16, 29; 2 Samueli 6:11-16.

Koma mkazi wa Davide, Mikala, sanakhale nawo pa gulu la anthu osangalalawo. Ankaonerera zochitikazo pawindo m’nyumba mwake, ndipo m’malo mokondwera ndi mmene Davide anali kutamandira Yehova, iye ‘anam’peputsa mumtima mwake.’ (2 Samueli 6:16) N’chifukwa chiyani Mikala anamva choncho? Zikuoneka kuti iye ankadzimva kwambiri chifukwa choona kuti anali mwana wa mfumu yoyamba ya Israyeli, Sauli, ndipo tsopano anali mkazi wa mfumu yachiwiri ya Israyeli. Iye mwina ankaona kuti mwamuna wake, yemwe anali mfumu, sanayenera kudzitsitsa mpaka kufika posangalalira limodzi ndi anthu wamba. Maganizo odzikuza amenewo anaonekera m’njira imene analonjerera Davide atafika kunyumba. Monyoza, iye anati: “Ha! Lero mfumu ya Israyeli inalemekezeka ndithu, amene anavula lero pamaso pa adzakazi a anyamata ake, monga munthu woluluka avula wopanda manyazi!”​—2 Samueli 6:20.

Kodi Davide anatani atanyozedwa chonchi? Anadzudzula Mikala pomuuza kuti Yehova anakana bambo ake, Sauli, chifukwa chokonda Davideyo. Davide anawonjezera kuti: “Ndidzawonjezanso kukhala ngati munthu woluluka, ndidzakhala wodzichepetsa m’maso a ine mwini; ndipo adzakazi udanenawo, ndi amenewo ndidzalemekezedwa.”​—2 Samueli 6:21, 22.

Inde, Davide anafunitsitsa kupitiriza kutumikira Yehova modzichepetsa. Mtima umenewu ukutithandiza kumvetsa chifukwa chimene Yehova ananenera kuti Davide anali ‘munthu wa pamtima pake.’ (Machitidwe 13:22; 1 Samueli 13:14) Ndipotu, Davide anali kutsatira chitsanzo chabwino kwambiri cha kudzichepetsa, cha Yehova Mulungu mwiniyo. N’zochititsa chidwi kuti mawu amene Davide anagwiritsa ntchito pamene ananena kwa Mikala kuti “ndidzakhala wodzichepetsa” ndi ochokera ku mawu a Chihebri amene amafotokozanso momwe Mulungu amaonera anthu. Ngakhale kuti Yehova ndiye wamkulu kwambiri m’chilengedwe chonse, lemba la Salmo 113:6, 7 limati iye ‘amadzichepetsa [kutanthauza kudzitsitsa pa udindo wako kapena pa ulemerero wako pofuna kuchita zinthu ndi wina wotsika] apenye zam’mwamba ndi za pa dziko lapansi. Amene autsa wosauka kum’chotsa kufumbi, nakweza waumphawi kum’chotsa kudzala.’

Popeza Yehova ndi wodzichepetsa, n’zosadabwitsa kuti amadana ndi anthu a ‘maso onyada.’ (Miyambo 6:16, 17) Chifukwa chosonyeza mtima woipawu ndi kunyoza munthu amene Mulungu anasankha kuti akhale mfumu, Mikala anamanidwa mwayi woberekera Davide mwana. Mpaka anamwalira alibe mwana. Limeneli ndi phunziro lofunika kwambiri kwa ife. Onse amene akufuna kusangalatsa Mulungu ayenera kumvera mawu awa: “Muvale kudzichepetsa kuti mutumikirane; pakuti Mulungu akaniza odzikuza, koma apatsa chisomo kwa odzichepetsa.”​—1 Petro 5:5.