Pitani ku nkhani yake

Pitani ku mitu ya nkhani

Mafunso Ochokera kwa Owerenga

Mafunso Ochokera kwa Owerenga

 Mafunso Ochokera kwa Owerenga

Ngati munthu akuvutitsidwa ndi ziwanda, kodi angatani kuti ziwandazo zisiye kum’vutitsa?

Mawu a Mulungu amasonyeza kuti n’zotheka kuti anthu amene akuvutitsidwa ndi ziwanda asiye kuvutitsidwako. Pemphero limathandiza kwambiri kuti zimenezi zitheke. (Marko 9:25-29) Komabe munthu amene akuvutitsidwa ndi ziwanda angafunike kuchita zinthu zinanso kuwonjezera pa pemphero. Zimene zinachitika pakati pa Akristu oyambirira zikusonyeza kuti n’zinthu zotani zimene munthuyo angafunike kuchita.

Asanayambe kutsatira Kristu, anthu ena ku Efeso wakale ankachita zamizimu. Koma atatsimikiza zoti ayambe kutumikira Mulungu, “iwo akuchita zamatsenga anasonkhanitsa mabuku awo, nawatentha pamaso pa onse.” (Machitidwe 19:19) Mwa kutentha mabuku awo okhudza kuombeza, okhulupirira atsopano a ku Efesowa anapereka chitsanzo kwa aliyense amene akufuna kuti asiye kuvutitsidwa ndi ziwanda masiku ano. Anthu amenewa akufunika kupewa chilichonse chokhudzana ndi zamizimu. Zinthu zimenezi ndi monga, mabuku, magazini, mafilimu, nkhani za pa Intaneti, nyimbo zokhudza zamizimu, komanso zithumwa kapena zinthu zina zomwe anthu amakhala nazo poganiza kuti ziziwateteza, kapena pazifukwa zokhudzana ndi zamizimu.​—Deuteronomo 7:25, 26; 1 Akorinto 10:21.

Patatha zaka zikangapo kuchokera pamene Akristu a ku Efeso aja anatentha mabuku awo a zamatsenga, mtumwi Paulo analemba kuti: “Kulimbana kwathu [tikulimba ndi] a uzimu a choipa m’zakumwamba.” (Aefeso 6:12) Paulo analimbikitsa Akristu kuti: “Tavalani zida zonse za Mulungu, kuti mudzakhoze kuchirimika pokana machenjerero a Mdyerekezi.” (Aefeso 6:11) Malangizo amenewa akugwirabe ntchito mpaka pano. Akristu akufunika kuchita khama kwambiri kuti akhale olimba mwauzimu pofuna kudziteteza kwa mizimu yoipa. Paulo anatsindika kuti: ‘Koposa zonse mudzitengerenso chikopa cha chikhulupiriro, chimene mudzakhoza kuzima nacho mivi yonse yoyaka moto ya woipayo.’ (Aefeso 6:16) Munthu amalimbitsa chikhulupiriro mwa kuphunzira Baibulo. (Aroma 10:17; Akolose 2:6, 7) Motero, kuphunzira Baibulo nthawi zonse kumatithandiza kukhala ndi chikhulupiriro chomwe chimatiteteza ku mizimu yoipa.​—Salmo 91:4; 1 Yohane 5:5.

Komatu sikuti ndi zokhazi zimene Akristu a ku Efesowa anafunika kuchita. Paulo anawauza kuti: “Mwa pemphero lonse ndi pembedzero mupemphere nthawi yonse mwa Mzimu.” (Aefeso 6:18) Inde, anthu amene akufuna kuti ziwanda zisiye kuwavutitsa masiku ano, akufunika kupemphera kwambiri kuti Yehova awateteze. (Miyambo 18:10; Mateyu 6:13; 1 Yohane 5:18, 19) M’pake kuti Baibulo limati: “Potero mverani Mulungu; koma kanizani Mdyerekezi, ndipo adzakuthawani inu.”​—Yakobo 4:7.

Ngakhale kuti munthu amene akufuna kuti ziwanda zisiye kum’vutsayo ayenera kupemphera kwambiri, Akristu oona angapemphererenso munthu amene akufunitsitsa kutumikira Yehova ndipo akuyesetsa kulimbana ndi mizimu yoipa. Iwo angapemphere kwa Mulungu kuti munthu amene akuvutitsidwa ndi ziwandayo apeze mphamvu zauzimu zolimbanirana ndi ziwanda. Popeza Mawu a Mulungu amati “pemphero la munthu wolungama likhoza kwakukulu m’machitidwe ake,” mosakayikira mapemphero a atumiki a Mulungu angathandize anthu ovutitsidwa ndi ziwanda amene akuyesetsa ‘kukaniza Mdyerekezi.’​—Yakobo 5:16.

[Chithunzi patsamba 31]

Okhulupirira a ku Efeso anatentha mabuku awo a zamatsenga