Pitani ku nkhani yake

Pitani ku mitu ya nkhani

Kodi Mukukumbukira?

Kodi Mukukumbukira?

 Kodi Mukukumbukira?

Kodi mwapindula powerenga magazini aposachedwapa a Nsanja ya Olonda? Tayesani kuyankha mafunso otsatirawa:

Kodi zina mwa zinthu zimene zachititsa kuti pakhale zinthu zoipa kwambiri masiku ano ndi ziti?

Chimodzi mwa zinthu zimene zimachititsa kuipa ndicho mtima wa anthu wofuna kuchita zoipa. (Genesis 8:21) China n’chakuti anthu ambiri sadziwa molondola chifuniro cha Mulungu. Komanso, Satana, amene anayambitsa kuipa, akupitiriza kulowerera mu zochita za anthu.​—1/1, masamba 4 mpaka 6.

Kodi ubwino wa mawu abwino a panthawi yake ndi wotani? (Miyambo 12:25)

Angapangitse munthu wouzidwa mawuwo kusiya kudzikayikira, angamulimbikitse, ndiponso angam’chititse kumva kuti sali yekha. Komanso, tikamayesetsa kuyamikira ena, zimatithandiza kuona zabwino mwa anthu ena.​—1/1, masamba 16 ndi 17

Kodi mu likasa la chipangano munkakhala chiyani?

Munkakhala magome awiri a Chilamulo ndi mana. Kora atagalukira, ndodo ya Aroni anaiika mu Likasa monga umboni ku mbadwo wa masiku amenewo. (Ahebri 9:4) N’kutheka kuti ndodo ndi manawo anadzazichotsa mu Likasalo, kachisi wa Solomo asanaperekedwe.​—1/15, tsamba 31.

N’chifukwa chiyani Ayuda a m’masiku a Nehemiya anafunika kubweretsa nkhuni ku kachisi?

Chilamulo cha Mose sichinafune kuti anthu azipereka nsembe za nkhuni. Koma m’masiku a Nehemiya pankafunika nkhuni nthawi zonse zowotchera nsembe pa guwa.​—2/1, tsamba 11.

Kodi mpukutu wa Muratori n’chiyani?

Mpukutuwu unachokera ku mpukutu wolemba pamanja wa Chilatini. Mpukutu woyambirirawo unalembedwa m’Chigiriki, chakumapeto kwa zaka za m’ma 100 C.E. Mpukutuwu uli ndi mndandanda wakale kwambiri wa mabuku a Malemba Achigiriki Achikristu omwe ankawaona kuti ndi ovomerezeka, komanso uli ndi ndemanga zonena za mabuku ndi anthu amene analemba mabukuwo.​—2/15, masamba 13 ndi 14.

Kodi n’chifukwa chiyani Vasiti, mkazi wa mfumu ya ku Perisiya, anakana kupita kwa mfumu? (Estere 1:10-12)

Baibulo silinena cholinga chake pochita zimenezo. Akatswiri ena anena zoti iye anakana chifukwa sanafune kuti akadzichotsere ulemu pamaso pa alendo a mfumu amene anali ataledzera. N’kuthekanso kuti mkazi wa mfumu wamaonekedwe okongola ameneyu anali ndi mtima wosagonjera, motero anaonetsa chitsanzo choipa kwa akazi ena mu ufumu wa Perisiya.​—3/1, tsamba 9.

Kodi dipo limawombola motani?

Nsembe ya Yesu ingathe kutiwombola ku uchimo womwe tinatengera kwa makolo athu ndiponso ingathe kutimasula ku imfa, yomwe inabwera chifukwa cha uchimo. (Aroma 6:23) Nsembeyi imathandiza Akristu oona kukhala ndi chikumbumtima chabwino. Ndipo tikakhulupirira dipo, tingathe kuwomboledwa ku mantha oopa kuti mbiri yathu kwa Mulungu n’njoipa. (1 Yohane 2:1)​—3/15, tsamba 8.

Kodi tingaphunzirepo chiyani pa lamulo lomwe linali m’Chilamulo loletsa kuphika mwana wa mbuzi mu mkaka wa make? (Eksodo 23:19)

N’kutheka kuti kaphikidwe kameneka kanali mwambo wachikunja woitanitsira mvula. (Levitiko 20:23) Mulungu anapereka mkaka n’cholinga choti mbuzi iziyamwitsa mwana wake kuti azikula. Kuphika mwanayo mu mkaka umenewu kukanatha kusonyeza kunyoza mgwirizano wa pakati pa kholo ndi mwana wake, umene Mulungu anakhazikitsa. Lamulo loletsa zimenezi likusonyeza chifundo cha Mulungu.​—4/1, tsamba 31.