Pitani ku nkhani yake

Pitani ku mitu ya nkhani

Njira Yokhayo Yothetsera Imfa

Njira Yokhayo Yothetsera Imfa

 Njira Yokhayo Yothetsera Imfa

MUNTHU wina wotchedwa Lazaro pamodzi ndi alongo ake, Marita ndi Mariya, ankakhala m’tawuni ya Betaniya, yomwe inali pa mtunda wa makilomita atatu kunja kwa Yerusalemu. Yesu anali mnzawo wa anthuwa ndipo tsiku lina Yesuyo atatalikira, Lazaro anadwala mwakayakaya. Alongo ake aja anada nkhawa kwambiri, motero anatumiza uthenga kwa Yesu. Patatha nthawi ndithu atamva uthengawo, Yesu ananyamuka kukamuona Lazaro. M’njira, Yesu anauza ophunzira ake kuti akupita kukadzutsa Lazaro kutulo. Ophunzirawo sanamvetse, motero Yesu anawauza mosapita m’mbali kuti: “Lazaro wamwalira.”​—Yohane 11:1-14.

Yesu atafika pa manda a Lazaro, analangiza anthu kuti achotse mwala wa pakhomo pa mandawo. Kenako anapemphera mokweza, n’kunena kuti: “Lazaro, tuluka.” Ndipo Lazaro anatulukadi. Munthu woti anali atafa kwa masiku anayi anaukitsidwa.​—Yohane 11:38-44.

Nkhani ya Lazaroyi imasonyeza kuti njira yeniyeni yothetsera imfa ndiyo kuuka kwa akufa. Koma kodi chozizwitsa chimenechi chinachitikadi? Baibulo limalongosola kuti nkhaniyi inachitikadi. Iwerengeni pa Yohane 11:1-44, ndipo muona kuti inalongosoledwa motsatirika bwino zedi. Ndiye kodi mungatsutse kuti inachitikadi? Ngati mutatero ndiye kuti mungatsutsenso zozizwitsa zonse zolembedwa m’Baibulo. Mungatsutse ngakhale za kuuka kwa Yesu Kristu amene. Ndipo Baibulo limati “ngati Kristu sanaukitsidwa, chikhulupiriro chanu chili chopanda pake.” (1 Akorinto 15:17) Chiphunzitso cha kuuka kwa akufa n’chiphunzitso cha m’Malemba chofunika kwambiri. (Ahebri 6:1, 2) Koma kodi mawu akuti “kuuka kwa akufa” amatanthauza chiyani?

Kodi Tanthauzo la “Kuuka kwa Akufa” N’chiyani?

M’Malemba Achigiriki Achikristu oyambirira, mawu akuti “kuuka kwa akufa” amapezeka nthawi zoposa 40. Liwu la Chigirikilo kwenikweni limatanthauza “kuimiriranso.” Pamene la Chihebri limatanthauza “kukhalanso ndi moyo.” Kodi n’chiyani chimaukitsidwa munthu akafa? Silingakhale thupi ayi, chifukwa thupi limawola n’kusanduka fumbi la m’nthaka. Motero si thupilo limaukitsidwa koma ndi munthu yemwe anafayo. Kutanthauza kuti kuuka kwa akufa n’kubwezeretsa moyo wonse wa munthuyo, kapena kuti zochita zake zonse, mbiri yake yonse, ndi zinthu zonse zokhudza umunthu wake.

Yehova Mulungu saiwala chilichonse, motero sangavutike kukumbukira moyo wonse wa anthu amene anafa. (Yesaya 40:26) Popeza kuti Yehova ndiye Woyambitsa moyo, iye angathe kuukitsa munthu mosavuta n’kumupatsa thupi latsopano. (Salmo 36:9) Komanso Baibulo limanena kuti Yehova Mulungu ‘amakhumba,’ kapena kuti amafunitsitsa, kuukitsa anthu akufa. (Yobu 14:14, 15) N’zosangalatsa kudziwa kuti Yehova angathe kuukitsa munthu wakufa komanso ndi wofunitsitsa kutero.

Pankhani ya kuukitsa akufa, Yesu Kristu naye ali ndi mbali yaikulu. Patangotha chaka chimodzi atayamba utumiki wake, Yesu anati: “Monga Atate aukitsa akufa, nawapatsa moyo, momwemonso Mwana apatsa moyo iwo amene Iye afuna.” (Yohane 5:21) Nkhani ya Lazaro imasonyezeratu kuti Yesu Kristu ali ndi mphamvu komanso n’ngofunitsitsa kuukitsa akufa.

Komano ena amati pali chinachake mwa ife chimene chimakhalabe ndi moyo tikafa. Kuuka kwa akufa sikugwirizana ndi chiphunzitso chimenechi. Ngati chinachake mwa ife sichifa, kuukitsa akufa kungakhale ndi ntchito yanji?  Marita, mlongo wake wa Lazaro, sankakhulupirira kuti mchimwene wake atamwalira, anakakhala mzimu kwinakwake. Iye ankakhulupirira kuuka kwa akufa. Yesu atamulimbikitsa ndi mawu akuti “mlongo wako adzauka,” Marita anati: “Ndidziwa kuti adzauka m’kuuka tsiku lomaliza.” (Yohane 11:23, 24) Ndipo Lazaro ataukitsidwa, sanafotokozepo chilichonse chosonyeza kuti anali kudziko linalake lauzimu. Iye anafa basi. Baibulo limati: “Akufa sadziwa kanthu bi. . . . Mulibe ntchito ngakhale kulingirira ngakhale kudziwa, ngakhale nzeru, kumanda ulikupitako.”​—Mlaliki 9:5, 10.

Motero, Baibulo limasonyeza kuti njira yokhayo yothetsera imfa ndiyo kuuka kwa akufa. Koma kodi ndani adzaukitsidwe pa anthu ambirimbiri amene anafa, ndipo adzaukitsidwira kuti?

Ndani Adzaukitsidwe?

Yesu anati: “Ikudza nthawi, imene onse ali m’manda adzamva mawu [a Yesu], nadzatulukira.” (Yohane 5:28, 29) Mogwirizana ndi lonjezo limeneli, anthu amene ali m’manda a chikumbutso, kapena kuti anthu amene Yehova akuwakumbukira, adzaukitsidwa. Ndiyeno funso n’lakuti, kodi pa anthu onse amene anafa, ndi ati amene Mulungu akuwakumbukira omwe akudikira kuti adzawaukitse?

Buku la Ahebri chaputala 11 limatchula maina a amuna ndi akazi amene anatumikira Mulungu mokhulupirika. Iwowa, ndiponso atumiki ena a Mulungu amene amwalira m’zaka zaposachedwapa adzaukitsidwa. Nanga bwanji anthu amene sanatsatire miyezo yolungama ya Mulungu, mwina chifukwa chosadziwa? Kodi amenewanso Mulungu akuwakumbukira? Inde, ambiri mwa amenewa Mulungu akuwakumbukira, chifukwatu Baibulo limalonjeza kuti: “Kudzakhala kuuka kwa olungama ndi osalungama.”​—Machitidwe 24:15.

Komabe, sikuti aliyense amene anakhalako padziko pano adzaukitsidwa. Baibulo limati: “Pakuti tikachimwa ife eni ake, titatha kulandira chidziwitso cha choonadi, siitsalanso nsembe ya kwa machimo, koma kulindira kwina koopsa kwa chiweruziro.” (Ahebri 10:26, 27) Pali anthu ena amene anachita machimo oti  sangakhululukidwe. Iwowa sali mu Hade (manda a anthu onse akufa) koma ali ku Gehena, malo ongophiphiritsira osonyeza chiwonongeko chotheratu. (Mateyu 23:33) Komabe tisamale kuti tisamaweruze kuti wakutiwakuti adzaukitsidwa, pamene wakutiwakuti ayi. Woweruza ndi Mulungu. Iye akudziwa anthu amene ali ku Hade ndi amene ali ku Gehena. Ifeyo tizingoyesetsa kuchita chifuniro cha Mulungu m’moyo wathu.

Ndani Adzaukitsidwire Kumwamba?

Kuuka kodabwitsa kwambiri kuposa kuuka konse kunali kuuka kwa Yesu Kristu. Iye ‘anaphedwa m’thupi, koma anapatsidwa moyo mumzimu.’ (1 Petro 3:18) Palibe munthu amene anali ataukitsidwapo m’njira imeneyi. Yesu mwiniwakeyo anati: “Kulibe munthu anakwera Kumwamba, koma Iye wotsikayo kuchokera Kumwamba, ndiye Mwana wa munthu.” (Yohane 3:13) Inde, Mwana wa munthu anali woyamba kuukitsidwa kukhala munthu wauzimu. (Machitidwe 26:23) Komabe pali ena amene anateronso pambuyo pake. Malemba amati: “Yense m’dongosolo lake la iye yekha, chipatso choundukula Kristu; pomwepo iwo a Kristu, pa kubwera kwake.”​—1 Akorinto 15:23.

Kagulu kakang’ono ka anthu, kamene akatchula kuti “iwo a Kristu,” kadzaukitsidwa kukakhala ndi moyo kumwamba kukachita ntchito yapadera. (Aroma 6:5) Iwowa pamodzi ndi Kristu ‘adzachita ufumu padziko.’ (Chivumbulutso 5:9, 10) Komanso adzakhala ansembe m’njira yakuti adzathandiza nawo pochotsa mavuto obwera chifukwa cha uchimo umene anthu anatengera kwa munthu woyamba, Adamu. (Aroma 5:12) Anthu amene adzalamulire ndi Kristu monga mafumu alipo 144,000. (Chivumbulutso 14:1, 3) Kodi amaukitsidwa ndi matupi otani? Baibulo limati amaukitsidwa ndi “thupi lauzimu.” N’chifukwa chake anthuwa amatha kukakhala kumwamba.​—1 Akorinto 15:35, 38, 42-45.

Kodi kuukitsidwira kumwamba kudzachitika liti? Lemba la 1 Akorinto 15:23 limanena kuti kudzachitika “pa kubwera kwake, [kwa Kristu]” kapena kuti kukhalapo kwake. Zochitika za padziko lonse kuyambira m’chaka cha 1914 zimasonyeza kuti kukhalapo kwa Kristu ndiponso “mathedwe a nthawi ya pansi pano” zinayamba m’chaka chimenecho. (Mateyu 24:3-7) Motero m’pomveka kunena kuti kuukitsidwa kwa Akristu okhulupirika okakhala kumwamba kunayamba kale, ngakhale kuti anthufe sitiwaona akuuka. Zimenezi zikutanthauza kuti atumwi ndiponso Akristu oyambirira anaukitsidwa kale kukakhala kumwamba. Nanga bwanji Akristu amasiku ano amene ali ndi chiyembekezo chopatsidwa ndi Mulungu chokalamulira ndi Kristu kumwamba? Iwowa amaukitsidwa “m’kutwanima kwa diso,” kapena kuti nthawi yomweyo imene afayo. (1 Akorinto 15:52) Popeza kuti amene akuyamba kuukitsidwa ndiwo anthu a m’kagulu ka anthu 144,000, kuukitsidwa kumeneku kumatchedwa “kuuka koyamba” ndiponso “kuuka koyambirira.” Kenaka padzakhala kuuka kwa chikhamu cha anthu amene adzakhale padziko lapansi.​—Afilipi 3:11, NW; Chivumbulutso 20:6.

Ndani Adzaukitsidwire Padziko Lapansi?

Malemba amati anthu ambiri akufa adzaukitsidwira padziko lapansi. (Salmo 37:29; Mateyu 6:10) Pofotokoza masomphenya omwe anaona, mtumwi Yohane anati: “Nyanja inapereka akufawo anali momwemo, ndipo imfa ndi Hade zinapereka akufawo anali mmenemo; ndipo anaweruzidwa yense monga mwa ntchito zake. Ndipo imfa ndi Hade zinaponyedwa m’nyanja yamoto. Iyo ndiyo imfa yachiwiri, ndiyo nyanja yamoto.” (Chivumbulutso 20:11-14) Anthu amene ali m’Hade, kapena kuti manda a anthu onse akufa, akukumbukiridwa ndi Mulungu. Aliyense wa anthuwa adzaukitsidwa. (Salmo 16:10; Machitidwe 2:31) Akadzaukitsidwa, adzaweruzidwa mogwirizana ndi zimene adzachite panthawiyo. Nangano n’chiyani chimene chidzachitikire imfa ndi Hade? Zidzaponyedwa “m’nyanja ya moto.” Kutanthauza  kuti anthuwa sadzakhudzidwanso ndi imfa imene anthufe tinatengera kwa Adamu.

Tangoganizirani mmene lonjezo la kuuka kwa akufali limatsitsimulira aliyense amene mnzake kapena mbale wake anafa! Yesu ataukitsa mwana yekhayo wa mayi wamasiye wa ku Naini, mayiyo ayenera kuti anasangalala kwambiri! (Luka 7:11-17) Ndipo Baibulo limati Yesu ataukitsa mtsikana wina wa zaka 12, makolo ake “anadabwa pomwepo ndi kudabwa kwakukulu.” (Marko 5:21-24, 35-42; Luka 8:40-42, 49-56) M’dziko latsopano limene Mulungu analonjeza, tidzasangalala kulandira anzathu ndi abale athu.

Kodi kudziwa choonadi chokhudza kuuka kwa akufa kungatikhudze motani? Buku lotchedwa The World Book Encyclopedia limati: “Anthu ambiri amaopa imfa ndipo safuna n’komwe kuiganizira.” Chifukwa chiyani? Chifukwa chakuti anthu ambiri amaona kuti imfa ndi chinthu choopsa, chosamvetsetseka. Kudziwa zoona zake za anthu akufa ndiponso kukhala ndi chiyembekezo cha kuuka kwa akufa kungatilimbikitse panthawi imene takumanizana ndi “mdani wotsiriza” ameneyu, yemwe ndi “imfa.” (1 Akorinto 15:26) Kudziwa zimenezi kumachepetsanso chisoni chathu mnzathu kapena mbale wathu akamwalira.

Kodi kuukitsa anthu okhala padziko lapansi kudzayamba liti? Panopo dziko ladzaza ndi chiwawa, mavuto, kuphana, ndiponso likuwonongedwa. Motero, chisangalalo chimene chingakhalepo akufa ataukitsidwa m’dziko lotereli, sichingakhalitse. Komano Mlengi analonjeza kuti posachedwapa awononga dziko lilipoli, lomwe likulamulidwa ndi Satana. (Miyambo 2:21, 22; Danieli 2:44; 1 Yohane 5:19) Motero cholinga cha Mulungu polenga dziko lapansi chatsala pang’ono kukwaniritsidwa. Zimenezi zikadzachitika, anthu mabiliyoni ambiri amene ali mtulo ta imfa adzatsegula maso awo m’dziko la Mulungu lamtendere.

[Chithunzi patsamba 7]

Akufa ambiri adzaukitsidwira padziko lapansi