Pitani ku nkhani yake

Pitani ku mitu ya nkhani

Mfundo Zazikulu za M’buku la Yobu

Mfundo Zazikulu za M’buku la Yobu

 Mawu a Yehova Ndi Amoyo

Mfundo Zazikulu za M’buku la Yobu

YOBU ankakhala ku Uzi, dera lomwe panopo lili ku Arabia. Panthawiyi Aisrayeli ambiri ankakhala ku Igupto. Ngakhale kuti Yobu sanali Mwisrayeli, iye ankalambira Yehova Mulungu. Ponena za Yobu Baibulo limati: “Palibe wina wonga iye m’dzikomo, munthu wangwiro ndi woongoka, wakuopa Mulungu ndi kupewa zoipa.” (Yobu 1:8) Yobu ayenera kuti anakhala ndi moyo pakati pa nthawi ya atumiki a Yehova awiri okhulupirika, Yosefe, mwana wa Yakobo ndi mneneri Mose.

Zikuoneka kuti Mose ndiye analemba buku la Yobu, ndipo n’kutheka kuti anamva za Yobu pa zaka 40 zimene anakhala ku Midyani, komwe kunali kufupi ndi ku Uzi. Mose ayenera kuti anamva nkhani ya moyo wa Yobuyo atatsala pang’ono kufa panthawi imene Aisrayeli anali ku Uzi, cha kumapeto kwa ulendo wawo wa zaka 40 m’chipululu. * Nkhani ya Yobu anailemba mosangalatsa kwambiri moti imaikidwa m’gulu la nkhani zolembedwa mwaluso kwabasi. Koma chofunika kwambiri n’chakuti bukuli limayankha mafunso monga akuti: N’chifukwa chiyani anthu abwino amavutika? N’chifukwa chiyani Yehova amalola kuti pakhale zoipa? Kodi anthu opanda ungwiro angathe kukhala okhulupirika kwa Mulungu? Monga mbali ya Mawu a Mulungu ouziridwa, uthenga wa m’buku la Yobu ndi wamoyo ndipo uli ndi mphamvu ngakhale panopo.​—Ahebri 4:12.

“LITAYIKE TSIKU LOBADWA INE”

(Yobu 1:1–3:26)

Tsiku lina Satana anauza Mulungu kuti akukayikira zoti Yobu n’ngokhulupirikadi. Yehova anamulola Satana kum’bweretsera Yobu mavuto otsatizanatsatizana. Koma Yobu anakana ‘kuchitira Mulungu mwano.’​—Yobu 2:9.

Anzake atatu a Yobu anafika “kum’lirira” kapena kuti kudzam’limbikitsa. (Yobu 2:11) Iwo anangokhala duu osanena chilichonse moti Yobu ndiye anayambitsa kulankhula pamene ananena kuti: “Litayike tsiku lobadwa ine.” (Yobu 3:3) Iye analakalaka atakhala “ngati makanda osaona kuunika,” kapena kuti makanda amene anabadwa atafa kale.​—Yobu 3:11, 16.

Kuyankha Mafunso a M’Malemba:

1:4​—Kodi ana a Yobu ankachita chikondwerero cha tsiku lobadwa? Ayi, sankatero. Pa Chihebri liwu lakuti “tsiku” n’losiyana ndi liwu lakuti “tsiku lakubadwa,” ndipo liwu lililonse lili ndi tanthauzo lake. (Genesis 40:20) Mawu akuti “tsiku” amene ali pa Yobu 1:4 amatanthauza nthawi yoyambira pa kutuluka kwa dzuwa kufikira pa kulowa kwa dzuwa. Zikuoneka kuti ana asanu ndi awiri a Yobu chaka chilichonse ankachita phwando la masiku asanu ndi awiri limene onse pachibale pawo ankapezekapo. Chifukwa choti ankati chaka chino kupita kwa uyu chinacho kwa wina, zinali ngati kuti ankachita phwandolo panyumba pa mwana aliyense “pa tsiku lake.”

1:6; 2:1—Ndani ankaloledwa kuonekera kwa Yehova? Ena mwa amene ankaonekera pamaso pa Yehova anali Mwana wobadwa yekha wa Mulungu, amene amatchedwa kuti Mawu; angelo okhulupirika; ndiponso angelo ena omwe ali “ana a Mulungu” osamvera, pamodzinso ndi Satana Mdyerekezi. (Yohane 1:1, 18) Satana ndi ziwanda zake sanathamangitsidwe kumwamba mpaka patangotsala pang’ono kuti Ufumu wa Mulungu ukhazikitsidwe mu 1914. (Chivumbulutso 12:1-12) Polola kuti Satana ndi ziwanda azionekera pamaso  pake, Yehova anabweretsa pamaso pa angelo onse nkhani zimene Satana anayambitsa.

1:7; 2:2—Kodi Yehova ankalankhula ndi Satana maso ndi maso? Baibulo silinena zambiri za mmene Yehova amalankhulira ndi zolengedwa zauzimu. Komabe mneneri Mikaya anaona m’masophenya mngelo akulankhula mwachindunji ndi Yehova. (1 Mafumu 22:14, 19-23) Motero zikuoneka kuti Yehova ankalankhula ndi Satana mosagwiritsa ntchito m’khalapakati aliyense.

1:21—Kodi Yobu akanabwerera bwanji ‘m’mimba ya mayi ake’? Popeza kuti Yehova anapanga munthu “ndi dothi lapansi,” mawu akuti “mayi” palembali akuphiphiritsira nthaka.​—Genesis 2:7.

2:9—Kodi maganizo a mkazi wa Yobu ayenera kuti anali otani pamene anauza mwamuna wake kuti achitire mwano Mulungu kuti afe? Mkazi wa Yobu nayenso anali wokhudzidwa chimodzimodzi pa kuwonongedwa kwa zinthu zonse zimene iye ndi mwamuna wake anali nazo. Ziyenera kuti zinam’pweteka kwambiri kuona mwamuna wake amene poyamba anali wathanzi akupupulika ndi matenda ozunza. Ana ake onse anali atafa. Zinthu zonsezi ziyenera kuti zinamusokoneza kwambiri maganizo moti sankathanso kuona kuti chinthu chofunikira koposa zonse chinali ubwenzi wawo ndi Mulungu.

Zimene Tikuphunzirapo:

1:8-11; 2:3-5. Monga mmene nkhani ya Yobu ikusonyezera, kuti tikhale okhulupirika kwa Yehova timafunika kuchita ndiponso kulankhula zoyenerera komanso timafunika kutumikira Yehova ndi zolinga zoyenerera.

1:21, 22. Tikakhala okhulupirika kwa Yehova pa zabwino ndi pamavuto pomwe, tingathe kutsimikizira kuti Satana n’ngwabodza.​—Miyambo 27:11.

2:9, 10. Monga Yobu, tiyenera kukhalabe olimba m’chikhulupiriro ngakhale ngati achibale amaona kuti zochita zathu n’zopanda phindu kapena ngati akulimbikitsa kuti tisiye chikhulupiriro chathu.

2:13. Anzake a Yobu sananene chilichonse cholimbikitsa chokhudza Mulungu ndi malonjezo ake chifukwa choti sanali anthu auzimu.

“SINDITAYA UNGWIRO WANGA”

(Yobu 4:1–31:40)

Mfundo yaikulu imene anzake atatu a Yobu ananena inali yakuti chilipo chimene Yobu anachita kuti Mulungu amulange chonchi. Elifazi ndiye anayamba kunena zimenezi. Kenaka Bilidadi anatsatira ndipo iyeyu ndiye anachita kunyanya kumunyoza Yobu. Zofara naye anachita kuposa Bilidadi chipongwe chake.

Yobu sanavomereze mfundo zabodza za anthu odzamuzondawo. Posamvetsa chifukwa chimene Mulungu walolera kuti iyeyo avutike, Yobu ankangoganizira zodzilungamitsa basi. Komabe Yobu anali kukonda Mulungu moti anati: “Mpaka kufa ine sinditaya ungwiro wanga.”​—Yobu 27:5.

Kuyankha Mafunso a M’Malemba:

7:1; 14:14—Kodi mawu oti “nkhondo” kapena “ntchito” [ntchito yokakamiza, NW] akuimira chiyani? Yobu anali atavutika kwambiri moti moyo wake ankangouna ngati ntchito yokakamiza. (Yobu 10:17) Popeza kuti munthu sakhala mu Shelo mwa kufuna kwake, kuchokera panthawi imene wamwalira n’kufika panthawi imene adzaukitsidwe, Yobu anaiyerekezera ndi ntchito yochita kukakamizidwa.

7:9, 10; 10:21; 16:22—Kodi mawu a m’mavesi amenewa amasonyeza kuti Yobu sankakhulupirira za kuuka kwa akufa? Pamenepa Yobu anali kunena za panthawiyo osati za kutsogolo kwambiri ayi. Ndiyeno kodi ankatanthauza chiyani? N’kutheka kuti ankatanthuza kuti ngati atafa, anzakewo sakanathanso kumuona. Motero kwa iwowo, Yobuyo sakanabwereranso kunyumba kwake kapenanso kudziwidwanso, kufikira nthawi imene Mulungu anaika. N’zothekanso kuti Yobu ankatanthauza kuti palibe munthu amene angabwereko ku Shelo payekha. Mfundo yoti Yobu ankakhulupirira kuti m’tsogolo akufa adzauka imaonekera pa lemba la Yobu 14:13-15.

10:10—Kodi Yehova ‘anatsanula Yobu ngati mkaka, ndi kumulimbitsa ngati mase’ m’njira yotani? Awa ndi mawu a ndakatulo osonyeza mmene Yobu anapangidwira m’mimba mwa amake.

19:20—Kodi Yobu ankatanthauza chiyani ponena kuti “ndapulumuka ndili nazo nkhama za mano anga [khungu la mano  anga, NW]”? Mano alibe khungu, motero ponena kuti anapulumuka ndi khungu la mano ake, n’kutheka kuti Yobu ankatanthauza kuti anapulumuka popanda chilichonse.

Zimene Tikuphunzirapo:

4:7, 8; 8:5, 6; 11:13-15. Tisapupulume kuganiza kuti munthu akakhala pa mavuto ndiye kuti akututa zimene anafesa ndi kuti sakuyanjidwa ndi Mulungu.

4:18, 19; 22:2, 3Malangizo athu azizikidwa m’Mawu a Mulungu, osati zoganiza zathu ayi.​—2 Timoteo 3:16.

10:1. Yobu anaipidwa kwambiri ndi ululu wa mavuto ake moti sanaganizire kuti ndi zifukwa zina ziti zimene mwina zam’bweretsera mavuto akewo. Tikamavutika tisamaipidwe popeza tikudziwa bwinobwino zifukwa zimene timavutikira.

14:7, 13-15; 19:25; 33:24. Chiyembekezo cha kuuka kwa akufa chingatilimbikitse pa chiyeso chilichonse chimene Satana angatibweretsere.

16:5; 19:2. Mawu athu ayenera kulimbikitsa ena, osati kuwapweteka mtima.​—Miyambo 18:21.

22:5-7. Uphungu wom’patsa munthu popanda umboni weniweni woti munthuyo walakwa n’ngopanda ntchito ndiponso n’ngovulaza.

27:2; 30:20, 21. Sitifunikira kukhala angwiro kuti tikhale okhulupirika. Yobu analakwa podzudzula Mulungu.

27:5. Kupatulapo Yobu mwiniyo, palibe aliyense amene akanam’lepheretsa Yobu kukhulupirika chifukwa choti kukhulupirika kumadalira chikondi chimene munthuyo ali nacho pa Mulungu. Motero tiyenera kuyesetsa kuti tizim’konda kwambiri Mulungu.

28:1-28. Anthu amadziwa kumene kuli chuma padziko lapansi. Chifukwa cha nzeru zawo, pofunafuna chumacho amatha kufika pansi panthaka pomwe ngakhale mbalame yoona patali kwambiri ikamasaka singapaone. Koma nzeru za Mulungu timazipeza chifukwa choopa Yehova.

29:12-15. Tiyenera kukomera mtima anthu amene akufunikira thandizo.

31:1, 9-28. Yobu anatipatsa chitsanzo chifukwa anapewa kukopana, chigololo, kukondera, nkhanza, kukonda chuma, komanso kulambira mafano.

“KULAPA M’FUMBI NDI MAPULUSA”

(Yobu 32:1–42:17)

Elihu, yemwe anali wachinyamata, anangokhala duu n’kumamvetsera anzakewo akulankhula. Koma kenaka anayamba kulankhulapo. Anam’tsutsa Yobu ndiponso anzake atatu amene ankamunyozawo.

Elihu atangomaliza kulankhula, Yehova anayankha m’kavumvulu. Sanalongosolepo chifukwa chimene Yobu anali kuzunzikira. Koma pomufunsa mafunso osiyanasiyana, Mulungu Wamphamvuyonse anam’thandiza Yobu kuona mphamvu zosaneneka ndiponso nzeru zakuya zimene Iye ali nazo. Yobu anavomereza kuti analankhula mosaganiza ndipo anati: “Ndekha ndidzinyansa, ndi kulapa m’fumbi ndi mapulusa.” (Yobu 42:6) Chiyeso cha Yobu chitatha Mulungu anam’dalitsa chifukwa cha kukhulupirika kwake.

Kuyankha Mafunso a M’Malemba:

32:1-3—Kodi Elihu anafikapo nthawi yanji? Popeza kuti Elihu anamva mawu onse amene anzake onse aja ananena, ayenera kuti anakhala cha pafupi n’kumamvetsera kwa kanthawi ndithu Yobu asanayambe kulankhulitsana ndi anzake atatuwo, amene anangokhala duu kwa masiku seveni.​—Yobu 3:1, 2.

34:7—Kodi Yobu anali “wakumwa mwano ngati madzi” m’njira yotani? Pa mavuto akewo, Yobu ankangoona kuti zonena zonse za anzakewo zinali zomunyoza, ngakhale kuti potero anzakewo kwenikweni anali kunyoza Mulungu. (Yobu 42:7) Motero iye ankangomvetsera mwano wawowo ngati munthu amene akumwa madzi mosangalala.

 Zimene Tikuphunzirapo:

32:8, 9Nzeru sizibwera ndi ukalamba okha ayi. Kuti munthu akhale wanzeru amafunika kumvetsa Mawu a Mulungu ndi kutsogoleredwa ndi mzimu wake.

34:36. Timatsimikizira kuti ndife okhulupirika panthawi imene ‘tayesedwa mpaka mapeto’ m’njira inayake.

35:2. Elihu anamvetsera mwatcheru ndipo asanayambe kulankhula anatchula kaye pamene panagona nkhani. (Yobu 10:7; 16:7; 34:5) Asanayambe kupereka uphungu, akulu ayenera kumva kaye nkhaniyo mosamala, kutsimikizira zinthu zonse bwinobwino, ndi kumvetsa bwinobwino pamene pagona nkhani.​—Miyambo 18:13.

37:14; 38:1–39:30. Kusinkhasinkha za ntchito zamphamvu za Yehova, kapena kuti zochitika zosonyeza mphamvu ndi nzeru zake, kumatithandiza kukhala odzichepetsa n’kuona kuti chinthu chofunika koposa zofuna zathu ndicho kutsimikizira kuti Yehova ndiye woyenera kulamulira.​—Mateyu 6:9, 10.

40:1-4. Tikaona kuti tikufuna kuyamba kudandaula ndi zochita za Mulungu Wamphamvuyonse ‘tizigwira pakamwa pathu.’

40:15–41:34. Mvuu ndiponso ng’ona zili ndi mphamvu osati masewera! Kuti tipitirizebe kutumikira Mulungu, timafunikira kupatsidwa mphamvu ndi Mlengi wa zinyama zamphamvuzi, chifukwa Iye ndiye amatipatsa mphamvu.​—Afilipi 4:13.

42:1-6. Kumva mawu a Yehova ndiponso kukumbutsidwa mphamvu zimene Iye amasonyeza kunathandiza Yobu ‘kupenya Mulungu,’ kapena kuti kuzindikira zoona zake za Mulungu. (Yobu 19:26) Zimenezi zinam’thandiza kuti akonze maganizo ake. Tikapatsidwa malangizo ochokera m’Malemba, tizivomereza kulakwa kwathu mwamsanga n’kusintha.

Tsanzirani “Chipiriro cha Yobu”

Buku la Yobu limasonyeza momveka bwino kuti amene amachititsa kuti anthu azivutika si Mulungu ayi koma Satana. Polola kuti anthu azivutika padziko pano Mulungu watipatsa mwayi woti ifeyo patokha tisonyeze mbali imene tili pankhani ya ulamuliro wa Yehova ndiponso kukhulupirika kwathu.

Monga Yobu, anthu onse okonda Yehova amayesedwa. Nkhani ya Yobu imatilimbitsa mtima kuti n’zotheka kupirira. Imatithandiza kuona kuti mavuto athu sadzakhalapo mpaka kalekale. Lemba la Yakobo 5:11 limati: “Mudamva za chipiriro cha Yobu, ndipo mwaona chitsiriziro cha Ambuye.” Yehova anadalitsa Yobu chifukwa chokhala wokhulupirika. (Yobu 42:10-17) Tilitu ndi chiyembekezo chosangalatsa kwambiri chodzakhala ndi moyo wosatha m’Paradaiso padziko lapansi! Motero, tiyeni titsanzire Yobu poyesetsa kukhalabe okhulupirika.​—Ahebri 11:6.

[Mawu a M’munsi]

^ ndime 2 Buku la Yobu lili ndi nkhani zomwe zinachitika zaka zopitirira 140, pakati pa chaka cha 1657 ndi 1473 B.C.E.

[Zithunzi patsamba 16]

Kodi tingaphunzire chiyani pa “chipiriro cha Yobu”?