Pitani ku nkhani yake

Pitani ku mitu ya nkhani

Mfundo Zazikulu za M’buku la Estere

Mfundo Zazikulu za M’buku la Estere

 Mawu a Yehova Ndi Amoyo

Mfundo Zazikulu za M’buku la Estere

CHIWEMBU chakecho chikuoneka kuti sichilephera, chitheka basi. Si nanga akonza zothana ndi Ayuda onse, kuwapulula? Ndipo aika tsiku loti aphe Ayuda onse okhala mu ufumuwo, kuyambira ku Indiya kufikira Kusi. Akuganiza choncho munthu amene wakonza chiwembucho. Koma waiwala mfundo imodzi yofunika kwambiri yakuti, Mulungu wakumwamba angapulumutse anthu ake amene iye anawasankha, kaya akhale m’mavuto otani. Ndipo buku la m’Baibulo la Estere likusimba za chipulumutso chimenecho.

Amene analemba buku la Estere ndi Myuda winawake wachikulire, dzina lake Moredekai. Bukuli limasimba zimene zinachitika pa zaka pafupifupi 18 mu ulamuliro wa Mfumu Ahaswero, kapena kuti Sasta Woyamba wa Perisiya. Nkhani yochititsa nthumanzi imeneyi imasonyeza mmene Yehova amapulumutsira anthu ake ku ziwembu za adani awo, ngakhale pamene atumiki akewo ali omwazikana mu ufumu waukulu. Masiku ano, kudziwa zimenezi kumalimbitsadi chikhulupiriro cha anthu a Yehova, amene akuchita utumiki wake wopatulika m’mayiko 235. Ndiponso, anthu ofotokozedwa m’buku la Estere ndi zitsanzo kwa ife. Ena ndi zitsanzo zimene tiyenera kutsanzira. Ena sitiyenera kuwatsanzira. Indedi, “mawu a Mulungu ali amoyo, ndi ochitachita.”​—Ahebri 4:12.

MKAZI WA MFUMU AYENERA KULOWERERAPO

(Estere 1:1–5:14)

Chaka chachitatu (493 B.C.E.) cha ulamuliro wake, Mfumu Ahaswero wakonza madyerero. Vasiti, mkazi wa mfumu wokongola kwambiri, akukwiyitsa mfumuyo ndipo am’landa udindo wake. Pa anamwali onse okongola m’dzikolo asankhapo Hadasa, Myuda, kuti atenge malo a Vasiti. Polangizidwa ndi Moredekai mlongo wake, mayiyu akubisa kuti ndi Myuda ndipo akugwiritsa ntchito dzina lake lachiperisiya lakuti Estere.

Patapita nthawi, mwamuna winawake wodzikuza, dzina lake Hamani, akukwezedwa udindo kukhala nduna yaikulu. Chifukwa chakuti Moredekai wakana ‘kuweramira kapena kugwadira Hamani,’ Hamaniyo akukwiya kwambiri ndipo akukonza chiwembu chopha Ayuda onse mu ufumu wa Perisiya. (Estere 3:2) Kenako, Hamani akunyengerera Ahaswero kuti agwirizane naye ndipo mfumu ikulola n’kupereka lamulo lakuti achite mbanda imeneyo. Moredekai atadziwa zimenezi, ‘akuvala chiguduli ndi mapulusa.’ (Estere 4:1) Apa tsopano Estere ayenera kulowererapo. Iye akupempha mfumu ndi nduna yake yaikulu kuti abwere kumadyerero apadera. Iwo atafika kumeneko mosangalala, Estere akuwapemphanso kuti mawa lake afike kumadyerero ena. Ndiye Hamani akuchoka pamenepo akukondwera kwabasi. Koma akukwiya kwambiri ataona kuti Moredekai sakufuna kum’lemekeza,  ndipo akukonza chiwembu choti aphe Moredekai asanapite kumadyerero aja mawa lake.

Kuyankha Mafunso a M’Malemba:

1:3-5—Kodi madyererowo anachitika masiku 180? Lembali silinena kuti madyererowo anachitika masiku ambiri choncho koma kuti mfumu inaonetsa akalonga chuma ndi ulemerero wa ufumu wake waukuluwo masiku 180. Mwina mfumu inagwiritsa ntchito nthawi yaitali imeneyo kuonetsa ulemerero wa ufumu wake pofuna kudabwitsa akalonga kuti iwo akhulupirire kuti iye anali ndi mphamvu yochita zimene akufuna. Ngati zinatero, ndiye kuti mavesi 3 ndi 5 ayenera kuti akunena za madyerero a masiku 7 amene anachitika atatha masiku 180 a madyerero.

1:8—Kodi zinatheka bwanji kuti ‘panalibe kukakamiza pa kamwedwe monga mwa lamulo’? Zikuoneka kuti Aperisi anali ndi mwambo wolimbikitsana kumwa vinyo wochuluka mwakuti, pamadyerero ngati amenewa. Koma apa Mfumu Ahaswero analamula kuti zimenezo zisachitike. Buku lina limanena kuti: “Zinali kwa iwo kumwa vinyo mmene anali kufunira, kaya wochuluka kapena wochepa.”

1:10-12—N’chifukwa chiyani Vasiti, mkazi wa mfumu, anakana kupita kwa mfumu? Akatswiri ena anena zoti mkazi wa mfumuyu anakana chifukwa sanafune kuti akadzichotsere ulemu pamaso pa alendo a mfumu amene anali ataledzera. N’kuthekanso kuti mkazi wa mfumu wamaonekedwe okongola ameneyu anali ndi mtima wosagonjera. Ngakhale kuti Baibulo silinena chifukwa chake anachita zimenezo, amuna anzeru masiku amenewo anaona kuti kukana kwake kumvera mwamuna wake inali nkhani yaikulu ndipo chitsanzo choipa chimene Vasiti anaonetsa chikanasokoneza akazi onse m’zigawo za Perisiya.

2:14-17—Kodi Estere anachita chiwerewere ndi mfumu? Yankho lake ndi lakuti ayi. Nkhaniyo imanena kuti m’mawa mwake, akazi enawo amene anawabweretsa kwa mfumu anawabweza ku nyumba yachiwiri imene mdindo wa mfumu, “wosunga akazi aang’ono,” anali kuyang’anira. Choncho akazi amene anakagona ndi mfumu usiku anakhala akazi ake aang’ono. Koma Estere ataonana ndi mfumu, sanam’tengere ku nyumba ya akazi aang’ono. Pamene Estere anam’bweretsa kwa Ahaswero, “mfumu inakonda Estere koposa akazi onse, nalandira iye kuyanja ndi chifundo pamaso pake, koposa anamwali onse.” (Estere 2:17) Kodi Estere ‘analandira bwanji kuyanja ndi chifundo pamaso’ pa Ahaswero? Zimenezi zinachitika mofanana ndi mmene anapezera chiyanjo pamaso pa ena. “Namwaliyo anam’komera [Hege], nam’chitira chifundo.” (Estere 2:8, 9) Hege anayanja Estere chifukwa cha zimene anaona. Zimene anaonazo ndi maonekedwe ake ndi makhalidwe ake abwino basi. Ndipotu ‘Estere anayamikiridwa pamaso pa onse om’penya.’ (Estere 2:15) Momwemonso, mfumu inachita chidwi ndi zimene inaona mwa Estere ndipo inam’konda kwambiri.

3:2; 5:9—N’chifukwa chiyani Moredekai anakana kugwadira Hamani? Kwa Aisrayeli, sikunali kulakwa ngati wina agwadira munthu waudindo polemekeza udindo wakewo. Koma pa Hamani panali zambiri. Hamani anali wa ku Agagi. Mwina anali Mwamaleki, ndipo Yehova anali atanena kuti mtundu wa Amaleki unayenera kuthedwa wonse. (Deuteronomo 25:19) Moredekai anaona kuti akanagwadira Hamani, akanakhala wosakhulupirika kwa Yehova. N’chifukwa chake anakana kwamtuwagalu, n’kunena kuti anali Myuda.​—Estere 3:3, 4.

Zimene Tikuphunzirapo:

2:10, 20; 4:12-16. Estere analandira malangizo ndi uphungu kwa munthu wachikulire wopembedza Yehova. Choncho, ndi nzeru ‘kumvera atsogoleri [athu], ndi kuwagonjera.’​—Ahebri 13:17.

2:11; 4:5. ‘Tisapenyerere zathu za ife tokha, koma tizipenyereranso za anzathu.’​—Afilipi 2:4.

2:15. Mwa kusafuna zokongoletsa ndi zovala zinanso kuwonjezera pa zimene Hege anam’patsa, Estere anaonetsa kuti anali  wodzichepetsa ndi wodziletsa. Mfumu inam’yanja Estere chifukwa cha “munthu wobisika wamtima, m’chovala chosaola cha mzimu wofatsa ndi wachete.”​—1 Petro 3:4.

2:21-23. Estere ndi Moredekai ndi zitsanzo zabwino pa ‘kumvera maulamuliro aakulu.’​—Aroma 13:1.

3:4. Nthawi zina, chingakhale chanzeru kusawauza ena kuti ndife ndani, ngati mmene Estere anadzibisira. Koma ikakhala nkhani yaikulu yakuti tiima mbali iti, monga pa nkhani yokhudza ulamuliro wa Yehova ndi kukhulupirika kwathu, tisachite mantha kuwauza ena kuti ndife Mboni za Yehova.

4:3. Tikakumana ndi mayesero, tizipemphera kwa Yehova kuti atipatse mphamvu ndi nzeru.

4:6-8. Moredekai anatsatira njira yogwirizana ndi malamulo pothetsa chiwembu chimene Hamani anakonza.​—Afilipi 1:7.

4:14. Mwa kudalira Yehova kotheratu, Moredekai anatisiyira chitsanzo.

4:16. Podalira Yehova ndi mtima wonse, Estere mokhulupirika ndi molimba mtima analimbana ndi nkhani yovuta imene ikanam’phetsa. Ndi bwino titaphunzira kudalira Yehova m’malo modzidalira ife eni.

5:6-8. Kuti apeze chiyanjo pamaso pa Ahaswero, Estere anamuitana ku madyerero achiwiri. Anachita mwanzeru, ngati mmene ife tiyenera kuchitira.​—Miyambo 14:15.

ZINTHU ZIKUTEMBENUKA MOTSATIZANA

(Estere 6:1–10:3)

Kenako zinthu zikutembenuka. Hamani anyongedwa pamtengo umene anati anyongerepo Moredekai, ndipo Moredekaiyo amene anati aphedwe akukhala nduna yaikulu. Nanga chikuchitika n’chiyani ndi chiwembu chija anakonza chopulula Ayuda? Apanso zinthu zikutembenuka modabwitsa.

Estere wokhulupirikayo akulankhulanso molimba mtima. Akuika moyo wake pachiswe mwa kukaonekera pamaso pa mfumu ndi pempho poyesa kupeza njira yolepheretsera chiwembu cha Hamani. Ahaswero akudziwa chochita.  Ndiye tsiku litafika limene anakonza kuti aphe Ayuda, amene akuphedwa si Ayudawo koma adani awo amene anali kufuna kuwapweteka. Kenako, Moredekai akulamula kuti chaka chilichonse azichita Phwando la Purimu pokumbukira chipulumutso chachikulu chimenechi. Pokhala wachiwiri kwa Mfumu Ahaswero, Moredekai ‘akufunira mtundu wake zokoma, ndi kunena za mtendere kwa mbewu yawo yonse.’​—Estere 10:3.

Kuyankha Mafunso a M’Malemba:

7:4—Kodi kuwonongedwa kwa Ayuda kukanabweretsa bwanji “kusowa kwa mfumu”? Mwa kufotokoza mwanzeru kuti iye sakanavutika Ayuda akanagulitsidwa kukhala akapolo, Estere anatsindika mmene kuwonongedwa kwawo kukanapwetekera mfumu. Ndalama za siliva 10,000 zimene Hamani anali atalonjeza sizinali zaphindu pa chuma cha mfumu kuyerekeza ndi chuma chimene chikanapezeka Hamani akanakhala kuti anakonza chiwembu chogulitsa Ayuda kukhala akapolo. Chiwembu cha Hamani chikanatheka, mfumu ikanataya mkazi wake.

7:8—N’chifukwa chiyani nduna za m’nyumba ya mfumu zinaphimba nkhope ya Hamani? Ayenera anachita zimenezi pofuna kuonetsa kuti iye anachita zamanyazi kapena kuonetsa tsoka limene linali kum’dikirira. Malinga ndi buku lina, “anthu akale nthawi zina anali kuphimba mutu wa munthu woti akupita kokanyongedwa.”

8:17—Kodi ndi m’njira yotani imene ‘ambiri a mitundu ya anthu a m’dziko anasandukira Ayuda’? Mwachionekere, Aperisi ambiri analowa Chiyuda, poganiza kuti kutembenuka kwa zinthu unali umboni wakuti Mulungu anali ndi Ayudawo. N’zimenenso zikuchitika pokwaniritsa ulosi umene uli m’buku la Zekariya. Ulosiwo umati: “Amuna khumi adzagwira, ndiwo a manenedwe onse a amitundu, inde adzagwira mkawo wa munthu ali Myuda, ndi kuti, Tidzamuka nanu, pakuti tamva kuti Mulungu ali ndi inu.”​—Zekariya 8:23.

9:10, 15, 16—Ngakhale kuti lamulo linalola kulanda zofunkha, n’chifukwa chiyani Ayuda sanachite zimenezo? Kusachita kwawo zimenezo unali umboni wakuti cholinga chawo chinali kuteteza mtundu wawo osati kudzilemeretsa ayi.

Zimene Tikuphunzirapo:

6:6-10. “Kunyada kutsogolera kuwonongeka; mtima wodzikuza ndi kutsogolera kupunthwa.”​—Miyambo 16:18.

7:3, 4Kodi timalimba mtima n’kudzidziwitsa kwa ena kuti ndife Mboni za Yehova, ngakhale ngati tingazunzidwe chifukwa cha zimenezo?

8:3-6. Tingachite apilo ndipo tiyenera kuchita apilo kuboma ndi kumakhoti kuti atiteteze kwa adani athu.

8:5. Estere mwanzeru sanatchule mlandu umene mfumu inali nawo pa lamulo limene analikonza la kupha Ayuda. Ifenso tizichita mwanzeru polalikira akuluakulu a boma.

9:22. Tisaiwale aumphawi amene ali pakati pathu.​—Agalatiya 2:10.

Yehova Adzapereka “Chithandizo ndi Chipulumutso”

Moredekai ananena kuti chinali cholinga cha Mulungu kuti Estere akhale mkazi wa mfumu. Ayuda atawopsezedwa, anasala kudya ndipo anapemphera kuti athandizidwe. Mkazi wa mfumu anaonekera kangapo pamaso pa mfumu popanda kuitanidwa koma anamulandira bwino maulendo onsewo. Mfumu sinathe kugona tulo usiku wofunika kwambiri. Inde, buku la Estere likusonyeza mmene Yehova amayendetsera zinthu kuti athandize anthu ake.

Nkhani yochititsa chidwi ya Estere imatilimbikitsa kwambiri ife amene tikukhala mu “nthawi ya chimaliziro.” (Danieli 12:4) “Masiku otsiriza,” kapena mbali yomaliza ya nthawi ya mapeto, Gogi wa Magogi​—Satana Mdyerekezi​—adzaukira anthu a Yehova ndi ukali waukulu. Cholinga chake sichidzakhala china ayi koma kupulula opembedza oona basi. Monga masiku a Estere, Yehova adzapereka “chithandizo ndi chipulumutso” kwa omupembedza.​—Ezekieli 38:16-23; Estere 4:14.

[Chithunzi patsamba 10]

Estere ndi Moredekai ali pamaso pa Ahaswero