Pitani ku nkhani yake

Pitani ku mitu ya nkhani

Kudziwa ndi Kuchita Chabwino

Kudziwa ndi Kuchita Chabwino

 Mbiri ya Moyo Wanga

Kudziwa ndi Kuchita Chabwino

YOSIMBIDWA NDI HADYN SANDERSON

Yesu anauza atumwi ake kuti: “Ngati mudziwa izi, odala inu ngati muzichita.” (Yohane 13:17) N’zoona kuti tikhoza kudziwa chabwino koma nthawi zina, kumakhala kovuta kuchita. Komabe, pambuyo pa zaka zoposa 80 zimene ndakhala ndi moyo, ndi zaka 40 mwa zaka zimenezi ndakhala ndikuchita umishonale, ndakhulupirira kuti mawu a Yesu amenewa ndi oona. Kuchita zimene Mulungu amanena, zoonadi kumabweretsa chimwemwe. Ndiloleni ndifotokoze.

M’CHAKA cha 1925, pamene ndinali ndi zaka zitatu, makolo anga anamvetsera nkhani ya Baibulo kutawuni ya kwathu ya Newcastle, m’dziko la Australia. Amayi atamva nkhani yakuti, “Anthu Mamiliyoni Ambiri Amene Ali ndi Moyo Sadzafa,” anakhulupirira kuti apeza choonadi, ndipo anayamba kupita ku misonkhano yachikristu mokhazikika. Chidwi cha bambo anga chinazilala mwamsanga, ndipo anayamba kutsutsana ndi zimene amayi anayamba kukhulupirira. Iwo ankaopseza kuti achoka ngati mayiwo sasiya kukhulupirira zimenezo. Amayi anga ankawakonda kwambiri bambo ndipo ankafuna kuti banja lawo lisasokonezeke. Komabe, anadziwa kuti kumvera Mulungu n’kofunika kwambiri, ndipo anali ndi mtima wofunitsitsa kuchita chabwino pamaso pa Mulungu. (Mateyu 10:34-39) Bambo anga aja anachoka, ndipo ndinkaonana nawo mwa apa ndi apo.

Ndikaganiza zimene amayi anakumana nazo, ndimanyadira kwambiri kuti iwo anakhala okhulupirika kwa Mulungu. Chifukwa cha zimene iwo anasankha, ine ndi mchemwali wanga Beulah, tinapeza madalitso auzimu. Komanso tinaphunzira phunziro lofunika kwambiri lakuti, pamene tadziwa chabwino, tiyenera kulimbikira kuchichita.

Chikhulupiriro Changa Chiyesedwa

Ophunzira Baibulo, dzina lomwe Mboni za Yehova zinkadziwika nalo nthawi imeneyo, anathandiza kwambiri banja lathu. Agogo anga aakazi anabwera  kudzakhala nafe kunyumba kwathu ndipo anaphunzira choonadi cha m’Baibulo. Nthawi zonse agogowo ndi amayi ankachitira limodzi ntchito yolalikira, ndipo anthu ankawalemekeza kwambiri chifukwa cha mmene ankakhalira komanso mmene ankaonekera.

Panthawi imeneyi, abale achikristu achikulire anayamba kundithandiza ndipo anandiphunzitsa zambiri. Posachedwa ndinaphunzira kugwiritsa ntchito khadi lochitira umboni pochita ulaliki wosavuta kwa anthu m’nyumba zawo. Komanso tinkaika nkhani za Baibulo pa galamafoni ya m’manja ndipo tinkalalikira mu msewu waukulu m’tawuni titanyamula zikwangwani. Zimenezi zinali zovuta, popeza kuti ndinkaopa anthu. Komabe, ndinkadziwa chabwino ndipo ndinayesetsa kuchita chimenecho.

Nditamaliza sukulu, ndinayamba kugwira ntchito kubanki, ndipo ntchito yake inali yoyendera nthambi zosiyanasiyana za bankiyo m’chigawo chonse cha New South Wales. Ngakhale kuti mbali imeneyo kunali Mboni zowerengeka, zimene ndinaphunzira zinandithandiza kusungabe chikhulupiriro changa. Amayi anga ankandilembera makalata ondilimbikitsa amene anandithandiza kukhala ndi chikhulupiriro cholimba.

Makalata amenewo anandipatsa thandizo la panthawi yake. Nkhondo yachiwiri ya padziko lonse inayamba, ndipo anandiitana kuti ndikalowe usilikali. Woyang’anira banki imene ndinkagwirako ntchito, anali Mkristu wokhulupirika ndiponso anali mtsogoleri wa asilikali kuderalo. Nditafotokoza kuti ndine Mkristu ndipo sindilowa nawo m’nkhondo, anandiuza moopseza kuti ndisankhe chinthu chimodzi, kusiya chipembedzo changacho kapena kusiya ntchito. Zinthu zinafika pakaindeinde pamene ndinafika ku malo olembetserako usilikali m’deralo. Mkulu wa banki uja anali komweko ndipo ankayang’ana mwachidwi pamene ndinkayandikira ku thebulo limene ankalembetseralo. Nditakana kusaina mapepala olowera usilikali, akuluakuluwo anakwiya kwambiri. Zinthu zinathina, komabe sindinafune kusiya kuchita chabwino. Ndi thandizo la Yehova, sindinachite mantha. Nditamva kuti anthu akundifunafuna kuti andimenye, ndinalongedza katundu wanga mofulumira, n’kukakwera sitima kuchoka m’tawuni imeneyo.

Nditabwerera ku Newcastle, ananditengera ku khoti kuti akandifunse mafunso pamodzi ndi abale ena seveni amene anakananso usilikali. Woweruza anatipatsa chilango chokhala miyezi itatu kundende ndi kugwira ntchito ya kalavula gaga. Ngakhale kuti kupita kundende sichinali chinthu chosangalatsa, kuchita chabwino kunabweretsa madalitso. Titatuluka kundende, mmodzi wa amene ndinali naye kundendeko, amene analinso wa Mboni, dzina lake Hilton Wilknson, anandiitana kuti ndizikam’gwirira ntchito ku nyumba yake yojambulira zithunzi. Kumeneko ndinakumana ndi mtsikana amene anadzakhala mkazi wanga, dzina lake Melody, yemwe ankagwira ntchito monga wolandira alendo. Nditangotuluka kundende, ndinabatizidwa posonyeza kudzipereka kwanga kwa Yehova.

Tinakhala ndi Cholinga Chochita Utumiki wa Nthawi Zonse

Titakwatirana, ine ndi mkazi wanga Melody tinatsegula nyumba yathu yojambulira zithunzi ku Newcastle. Posapita nthawi tinakhala ndi ntchito yambiri imene inayamba kusokoneza thanzi lathu ndi moyo wathu wauzimu. Chapanthawi yomweyo, Ted Jaracz, amene ankatumikira pa ofesi ya nthambi ya Mboni za Yehova ku Australia ndipo panopa ali m’Bungwe Lolamulira, anatifunsa zolinga zathu zauzimu. Pambuyo pokambirana zimenezi, tinaganiza zogulitsa bizinesi yathu ndi kukhala moyo wosafuna zambiri. M’chaka cha 1954 tinagula nyumba ya ngolo yaing’ono, n’kusamukira mu mzinda wa Ballarat m’chigawo cha Victoria, ndipo tinayamba kutumikira monga apainiya, kapena kuti alaliki a nthawi zonse.

Yehova anadalitsa ntchito imene tinkagwira pamodzi ndi mpingo waung’ono ku Ballarat. M’miyezi 18 yokha, chiwerengero cha anthu amene ankafika pa misonkhano chinakwera kuchokera pa 17 kufika pa 70. Kenako tinayamba utumiki  woyendayenda, kapena kuti ntchito yadera, m’chigawo cha kum’mwera kwa Australia. Tinkasangalala kuyendera mipingo kwa zaka zitatu mu mzinda wa Adelaide ndi dera limene ankapanga vinyo ndiponso limene ankalima zipatso monga malalanje, m’mphepete mwa mtsinje wa Murray. Moyo wathu unasintha kwambiri. Tinali osangalala kwambiri kutumikira limodzi ndi abale ndi alongo achikondi. Inalidi mphotho yaikulu imene tinapeza chifukwa chochita chimene timadziwa kuti n’chabwino.

Ntchito ya Umishonale

M’chaka cha 1958 tinadziwitsa ofesi ya nthambi ku Australia za cholinga chathu chofuna kukachita nawo msonkhano wa mayiko, wa mutu wakuti “Chifuniro cha Mulungu” womwe unachitikira ku New York City, chakumapeto kwa chaka chimenecho. Anatiyankha potitumizira mafomu oti tisaine a sukulu ya Gileadi yophunzitsa umishonale ku United States. Popeza kuti tinali titadutsa kale zaka 30, tinaganiza kuti sitingapite ku Gileadi. Komabe, tinatumiza mafomu athuwo ndipo tinaitanidwa kuti tikalowe m’kalasi la nambala 32. Tili pakatikati pa maphunzirowo, anatiuza kuti tidzapita ku India kumene tikachite umishonale wathu. Ngakhale kuti tinali ndi nkhawa, tinkafuna kuchita chimene chinali chabwino ndipo tinavomereza utumiki wathu mosangalala.

Tsiku lina m’mawa, m’chaka cha 1959, tinafika ku Bombay (tsopano Mumbai) pasitima ya panyanja. Antchito ambirimbiri anali atagona padokopo, ndipo fungo linangoti guu! Dzuwa litatuluka, tinakhala ndi chithunzithunzi cha zimene tizikumana nazo. Chiyambire sitinamvepo kutentha ngati mmene tinamvera nthawi imeneyo. Banja la amishonale limene tinkachita nalo upainiya ku Ballarat, Lynton ndi Jenny Dower, linatilandira. Anatiperekeza ku ofesi ya nthambi ya ku India ndiponso ku Nyumba ya Beteli, imene inali nyumba yosanja pafupi ndi malo amalonda a mu mzindawo ndipo inali yaing’ono. M’nyumbamo munkakhala antchito odzipereka a pa Beteli okwanira sikisi. Mbale Edwin Skinner, amene anakhala akuchita umishonale ku India kuyambira 1926, anatiuza kuti tigule zikwama zazikulu ziwiri zansalu, tisanapite kukayamba utumiki wathu. Zikwama zimenezi zinali zofala m’sitima za pamtunda za ku India ndipo zinatithandiza kwambiri pa maulendo athu.

Titayenda ulendo wa masiku awiri pa sitima ya pamtunda, tinafika kumene tinali kupita ku Tiruchchirappalli, mzinda umene uli kum’mwera kwa chigawo cha Madras (chimene tsopano ndi Tamil Nadu). Kumeneko, tinagwira ntchito limodzi ndi apainiya apadera atatu Achimwenye amene anali kulalikira anthu okwana 250,000. Malowa anali osatukuka kwenikweni. Nthawi ina, tinatsala ndi ndalama zosakwana madola 4 (a ku United States). Koma ndalama imeneyo itatha, Yehova sanatisiye. Munthu wina amene ankaphunzira Baibulo anatibwereka ndalama kuti tilipire nyumba imene tingathe kuchitiramo misonkhano. Tsiku lina titasowa chakudya, munthu wachifundo woyandikana naye nyumba anatibweretsera chakudya chimene anaphika chothira tsabola ndi kale. Chakudya chimenechi ndinachikonda kwambiri, kungoti tsabola wake anali wambiri moti ndinachita ntchitikiro.

Kulowa M’munda

Ngakhale kuti anthu ena a ku Tiruchchirappalli ankalankhula Chingelezi, anthu ambiri ankalankhula Chitamilu. Choncho, tinkalimbikira kuphunzira ulaliki wosavuta muutumiki wa kumunda m’chinenero cha Chitamilu. Chifukwa chophunzira chinenero chawo, anthu ambiri akumeneko ankatilemekeza kwambiri.

Tinkasangalala kwambiri ndi utumiki wa kunyumba ndi nyumba. Mwachibadwa, Amwenye ndi anthu okonda kuchereza alendo, ndipo ambiri ankatipatsa zakumwa zoziziritsa kukhosi. Poti kumalo amenewa kunali kotentha kwambiri mpaka kufika madigiri seshasi okwana 40, tinkayamikira kwambiri mtima wawo wochereza alendowo. Anthu a kumeneko pachikhalidwe chawo ankayamba ndi kukambirana nafe zinthu zaumwini tisanayambe kukambirana za uthenga wathu. Choncho eninyumba kawirikawiri ankatifunsa ine ndi mkazi wanga kuti: “Kodi munachokera kuti? Kodi muli ndi ana? N’chifukwa chiyani mulibe ana?” Ndipo akamva zoti tilibe ana, nthawi zambiri ankatiuza kuti alipo munthu wina amene amadziwa mankhwala. Mulimonsemo, makambirano amenewo ankawathandiza kuti atidziwe bwino ndiponso kuti tithe kuwafotokozera kufunika kwa ntchito yathu yophunzitsa anthu Baibulo.

Anthu ambiri amene tinkawalalikira anali a chipembedzo cha Chihindu, chipembedzo chimene chimasiyana kwambiri ndi Chikristu. M’malo mokangana nawo pa zimene Ahinduwo amakhulupirira, zomwe ndi zovuta kumvetsa, tinkangolalikira uthenga wabwino wa Ufumu wa Mulungu, ndipo  zotsatira zake zinali zabwino. Pa miyezi sikisi yokha, anthu pafupifupi 20 anayamba kufika pa misonkhano yomwe inkachitikira ku nyumba yathu ya amishonale. Mmodzi mwa anthuwa anali katswiri wa zomangamanga yemwe dzina lake anali Nallathambi. Iye ndi mwana wake wamwamuna, Vijayalayan, anadzathandiza anthu pafupifupi 50 kukhala atumiki a Yehova. Vijayalayan anatumikiranso kwa kanthawi pa nthambi ya ku India.

Maulendo Osatha

Tinakhala ku India miyezi yosakwana sikisi pamene anandiitana kuti ndikatumikire monga woyang’anira chigawo woyamba wokhazikika wa m’dzikolo. Zimenezi zinaphatikizapo kuyendera dziko lonse la India, kukonza misonkhano ndiponso kugwira ntchito limodzi ndi magulu a zinenero zosiyanasiyana zisanu ndi zinayi. Inali ntchito yovuta. Tinkalongedza zovala ndi zinthu zina zofunika zokwanira miyezi sikisi m’masutukesi a chitsulo ndi m’zikwama zathu zodalirika zansalu zija ndi kunyamuka kuchoka mu mzinda wa Madras (womwe tsopano ndi Chennai) pa sitima ya pamtunda. Popeza kuti dera lake linali lalikulu kwambiri moti kulizungulira limatenga mtunda wa makilomita 6,500, ndiye tinkayenda ulendo wosatha. Panthawi ina, tinamaliza msonkhano wa kum’mwera kwa mzinda wa Bangalore Lamlungu. Kenako tinapita kumpoto ku Darjeeling m’tsinde mwa phiri la Himalaya kuti tikachititse msonkhano wina sabata yotsatirayo. Kuti tikafike ku Darjeeling tinayenda mtunda wa makilomita pafupifupi 2,700 ndipo tinakwera masitima a pamtunda asanu osiyanasiyana paulendowo.

Pa maulendo athu oyambirira, tinkasangalala kusonyeza filimu ya The New World Society in Action. Filimu imeneyi inadziwitsa anthu za kukula kwa gulu la Yehova ndi ntchito yake padziko lonse lapansi. Kawirikawiri anthu ambirimbiri ankaonera nawo filimu imeneyi. Panthawi ina, tinaonetsa filimuyi kwa gulu la anthu amene anasonkhana m’mphepete mwa msewu. Ndipo filimuyi ili m’kati, mitambo ya mvula inasonkhana ndipo mofulumira inkasendera kumene ife tinali. Popeza kuti gulu la anthulo linali litachitapo chiwawa nthawi ina pamene filimuyi inadodometsedwa, ndinaganiza zopitiriza kuonetsa filimuyo koma moithamangitsa. Mwamwayi, mmene mvula inkayamba filimuyi inali itatha popanda kudodometsedwa.

M’zaka zotsatira, ine ndi Melody tinayenda m’madera ambiri a ku India. Popeza kuti dera lililonse linali ndi zinthu zosiyana ndi za m’dera lina monga chakudya, zovala, zinenero ndiponso kukongola kwake, ndiye tinkakhala ngati kuti tikuyenda kuchoka dziko lina kupita dziko lina. Zoonadi, m’chilengedwe cha Yehova muli zinthu zosangalatsa zosiyanasiyana! N’chimodzimodzinso ndi zinyama za ku India. Tsiku lina, titapita ku nkhalango ya ku Nepal, tinaona nyama yaikulu yonga kambuku yotchedwa taiga. Inali nyama yokongola kwambiri. Kuona nyama imeneyi kunalimbitsa chifuno chathu chodzakhala m’Paradaiso, mmene mudzakhale mtendere pakati pa anthu ndi nyama.

Kutsata Dongosolo la Gulu

M’masiku oyambirira amenewo, abale a ku India ankafunika kutsatira bwino lomwe dongosolo la gulu la Yehova. M’mipingo ina, amuna ankakhala mbali ina ya chipinda chochitiramo misonkhano ndipo akazi ankakhala mbali inanso. Nthawi zambiri misonkhano sinkayamba m’nthawi yake. Kumalo  ena, ankaliza belu laphokoso kwambiri kuti liitanire ofalitsa Ufumu ku misonkhano. Pamene kumalo ena, ofalitsa ankaonera dzuwa osati wotchi pofuna kudziwa kuti nthawi imene amayambira misonkhano yakwana. Misonkhano ikuluikulu ndiponso maulendo a oyang’anira oyendayenda ochezera mipingo, zinali kuchitika mwa apa ndi apo. Abale ankafuna kuchita chabwino, koma ankafunikira kuphunzitsidwa.

M’chaka cha 1959, gulu la Yehova linakhazikitsa Sukulu ya Utumiki wa Ufumu. Pulogalamu yophunzitsa ya dziko lonse imeneyi inathandiza oyang’anira dera, apainiya apadera, amishonale, ndi akulu a mipingo kukwanitsa bwino lomwe maudindo awo a m’Malemba. Pamene sukulu inayamba ku India mu December 1961, ndinali mlangizi. Pang’onopang’ono, phindu lake linafika ku mipingo m’dziko lonselo, ndipo mipingoyo inapita patsogolo kwambiri. Abalewo atadziwa chabwino, mzimu wa Mulungu unawalimbikitsa kuchita.

Misonkhano yachigawo ikuluikulu inkalimbikitsanso ndi kugwirizanitsa abale. Chinthu chimene chinali chosangalatsa kwambiri pa misonkhano yachigawo imeneyi chinali msonkhano wa mayiko, wa mutu wakuti “Uthenga Wabwino Wosatha” umene unachitikira ku New Delhi m’chaka cha 1963. Mboni zochokera m’madera onse a India zinayenda ulendo wa makilomita ambirimbiri kuti zikapezeke nawo pamsonkhano umenewo, ndipo ambiri anawononga ndalama zawo zonse zomwe ankasunga. Popeza kuti nthumwi zokwana 583 zochokera m’mayiko ena 27 zinali nawo pamsonkhanowo, aka kanali koyamba kuti Mboni zimene zinkakhala ku India zikumane ndi kucheza ndi abale ambiri chotero amene anali alendo.

M’chaka cha 1961, ine ndi mkazi wanga Melody tinaitanidwa kuti tikatumikire pa Beteli ku Bombay, komwe kenako ndinatumikira m’Komiti ya Nthambi. Ndinapatsidwanso ntchito zina. Kwa zaka zambiri, ndinakhala woyang’anira woyendera nthambi m’madera ena a ku Asia ndi Middle East. Popeza kuti ntchito yolalikira inali yoletsedwa m’mayiko ambiri m’maderawa, ofalitsa anafunika kukhala “ochenjera monga njoka, ndi oona mtima monga nkhunda.”​—Mateyu 10:16.

Ntchito Ikula Ndipo Zinthu Zisintha

Mu 1959 titafika koyamba ku India, ofalitsa amene ankalalikira m’dzikomo anali okwanira 1,514. Lero, chiwerengerocho chinakwera kufika pa ofalitsa oposa 24,000. Choncho kuti tithe kusamalira chiwerengero chimenechi, tinasamuka kawiri kupita ku malo a Beteli atsopano kufupi ndi Bombay. Ndipo, mu March 2002, banja la Beteli linasamukanso, koma tsopano linasamukira ku malo awo atsopano amene anamanga pafupi ndi Bangalore, kum’mwera kwa India. Pa Beteli yamakono imeneyi pali anthu okwana 240, ndipo ena mwa anthuwa amamasulira mabuku ofotokoza za m’Baibulo m’zinenero zokwana 20.

Ngakhale kuti ine ndi mkazi wanga Melody tinkayembekeza mwachidwi kusamukira ku Bangalore, thanzi lathu limene silinali bwino linatikakamiza kubwerera ku Australia mu 1999. Tsopano tili pa Beteli ku Sydney. Komabe ngakhale kuti tinachoka ku India, chikondi chimene tili nacho kwa anzathu okondedwa ndi ana athu auzimu kumeneko chidakali cholimba. Timasangalala kwambiri tikalandira makalata ochokera kwa anthu amenewo.

Tikaganiza zaka zoposa 50 zimene takhala muutumiki wa nthawi zonse, ine ndi Melody timaona kuti Yehova watidalitsa kwambiri. Poyamba, tinkagwira ntchito yojambula ndi kusunga zithunzi za anthu, koma tinachita bwino kwambiri kusankha kugwira ntchito yothandiza anthu kuti Mulungu aziwakumbukira. Tili ndi zokumana nazo zosangalatsa kwambiri chifukwa chosankha kuika chifuniro cha Mulungu patsogolo m’moyo. Zoonadi, ngati munthu akuchita zimene Mulungu amati n’zabwino, amapezadi chimwemwe.

[Mapu patsamba 15]

(Onani m’magazini yeniyeni kuti mumvetse izi)

INDIA

New Delhi

Darjeeling

Bombay (Mumbai)

Bangalore

Madras (Chennai)

Tiruchchirappalli

[Zithunzi patsamba 13]

Hadyn ndi Melody mu 1942

[Chithunzi patsamba 16]

Banja la Beteli ku India mu 1975