Pitani ku nkhani yake

Pitani ku mitu ya nkhani

Tsanzirani Kuleza Mtima kwa Yehova

Tsanzirani Kuleza Mtima kwa Yehova

 Tsanzirani Kuleza Mtima kwa Yehova

“Ambuye sazengereza nalo lonjezano, . . . komatu aleza mtima.”​—2 PETRO 3:9.

1. Kodi ndi mphatso iti yosayerekezeka imene Yehova wapatsa anthu?

YEHOVA watipatsa chinthu chimene munthu wina aliyense sangatipatse. Chinthucho n’chosangalatsa kwambiri ndiponso n’chamtengo wapatali, koma sitingathe kuchigula kapena kuchipeza chifukwa cha khama lathu. Inde, iye watipatsa mphatso ya moyo wosatha. Kwa ambirife, mphatso imeneyi idzakhala moyo wosatha m’paradaiso padziko lapansi pano. (Yohane 3:16) Komatu ndiye tidzasangalala! Nthawi imeneyo, sikudzakhalanso zinthu zobweretsa chisoni monga chidani, chiwawa, umphawi, umbanda, matenda, ngakhale imfa. Ufumu wa Mulungu ukadzayamba kulamulira mwachikondi, anthu adzakhala ndi mtendere weniweni ndi umodzi. Paradaiso ameneyu timam’lakalaka kwambiri!​—Yesaya 9:6, 7; Chivumbulutso 21:4, 5.

2. N’chifukwa chiyani mpaka pano Yehova sanachotse dongosolo ili la zinthu la Satana?

2 Nayenso Yehova amayembekezera ndi chidwi nthawi imene adzakhazikitse Paradaiso padziko lapansi. Pajatu iye amakonda chiweruzo ndi chilungamo. (Salmo 33:5) Sakondwa akamaona dzikoli, limene anthu ake alibe chidwi ndipo amadana ndi mfundo zake zolungama. Komanso amakana ulamuliro wake ndipo amazunza anthu ake. Koma pali zifukwa zabwino zimene mpaka pano sanachotsere dongosolo ili loipa la Satana. Zifukwazo zagona pa nkhani zokhudza ulamuliro wake ngati uli wabwino kapena woipa. Pothetsa nkhani zimenezi, Yehova akuonetsa khalidwe losangalatsa kwambiri limene anthu ambiri lero alibe. Khalidwe limenelo ndi kuleza mtima.

3. (a) Kodi mawu a Chigiriki ndi a Chihebri amene m’Baibulo anawamasulira kuti “kuleza mtima,” amatanthauza chiyani? (b) Ndiye tikambirana mafunso otani?

3 Mawu a Chigiriki amene anawamasulira kuti “kuleza mtima” kwenikweni amatanthauza “kukhala ndi mzimu wautali.” Mawu onse awiri, a Chigiriki ndi a Chihebri, omwe anawamasulira kuti “kuleza mtima” alinso ndi tanthauzo la kulolera ndi kusakwiya msanga. Kodi timapindula bwanji ndi kuleza mtima kwa Yehova? Kodi tingaphunzirepo chiyani pa kuleza mtima ndi kupirira kumene Yehova ndi atumiki ake okhulupirika aonetsa? Nanga tikudziwa bwanji kuti kuleza mtima kwa Yehova kuli ndi malire? Tiyeni tikambirane zimenezi.

Ganizirani za Kuleza Mtima kwa Yehova

4. Kodi mtumwi Petro analemba zotani pa kuleza mtima kwa Yehova?

4 Mtumwi Petro analemba za kuleza mtima kwa Yehova. Iye anati: “Ichi chimodzi musaiwale, okondedwa inu, kuti tsiku limodzi likhala kwa Ambuye ngati zaka chikwi, ndi zaka chikwi ngati tsiku limodzi. Ambuye sazengereza nalo lonjezano, monga ena achiyesa chizengerezo; komatu aleza mtima kwa inu, wosafuna kuti ena awonongeke, koma kuti onse afike kukulapa.” (2 Petro 3:8, 9) Taonani mfundo ziwiri zimene zatchulidwa palembali zimene zingatithandize kumvetsa kuleza mtima kwa Yehova.

5. Kodi zochita za Yehova zimakhala zotani chifukwa cha mmene amaonera nthawi?

5 Mfundo yoyamba n’njakuti, mmene Yehova amaonera nthawi si mmene ife timaonera. Pokhala wamuyaya, amaona zaka chikwi ngati tsiku limodzi. Sapanikizika ndi nthawi, komanso sachedwa kuchita zinthu. Popeza ali  ndi nzeru zopanda malire, Yehova amadziwa mosaphonyetsa nthawi yabwino yochitira zinthu zothandiza onse ofunikira thandizo, ndipo amadikirira nthawi imeneyo moleza mtima. Koma tisaganize kuti Yehova sizim’khudza atumiki ake akamakumana ndi mavuto panopo. Iye ndi Mulungu ‘wamtima wachifundo,’ ndipo ndiye chikondi. (Luka 1:78; 1 Yohane 4:8) Atha kuthetsa zopweteka zonse zimene zabwera chifukwa chakuti iye walola mavuto kwa nthawi yochepa, ndipo akazithetsa sizidzakhalakonso.​—Salmo 37:10.

6. Kodi sitiyenera kuganiza chiyani za Mulungu, ndipo n’chifukwa chiyani?

6 Kunena zoona, kudikirira chinthu chimene ukuchilakalaka n’kovuta. (Miyambo 13:12) N’chifukwa chake anthu akamazengereza kukwaniritsa malonjezo awo, ena amaganiza kuti anthuwo sakufuna kukwaniritsa zimene analonjezazo. Kungakhale kupanda nzeru kwambiri kuganiza kuti umu ndi mmene Mulungu alili. Tikamaona kuleza mtima kwa Mulungu ngati kuchedwa, tingayambe kukayikakayika ndiponso kutaya mtima, mwina mpaka kuwodzera kumene mwauzimu, imene ndi ngozi. Ndipo choopsa kwambiri n’chakuti anthu onyoza ndiponso opanda chikhulupiriro, amene Petro anati tichenjere nawo, angatisocheretse. Anthu amenewa amanena monyodola kuti: “Lili kuti lonjezano la kudza kwake? Pakuti kuyambira kuja makolo adamwalira zonse zikhala monga chiyambire chilengedwe.”​—2 Petro 3:4.

7. N’chifukwa chiyani tikunena kuti Yehova amaleza mtima pofuna kuti anthu alape?

7 Mfundo yachiwiri imene tikuipeza pa mawu a Petro n’njakuti Yehova amaleza mtima chifukwa chakuti akufuna kuti anthu onse alape. Anthu aliuma amene amakana kusiya njira zawo zoipa Yehova adzawapha. Ngakhale zili choncho, Mulungu sakondwera ndi imfa ya munthu woipa. Amasangalala kuona anthu akulapa, kusiya njira zawo zoipa, ndi kukhala ndi moyo. (Ezekieli 33:11) N’chifukwa chake akuleza mtima ndipo akuonetsetsa kuti uthenga wabwino ukulalikidwa padziko lonse lapansi kuti anthu akhale ndi mpata wokwanira wopezera moyo.

8. Kodi kuleza mtima kwa Mulungu kumaoneka bwanji ndi mmene anachitira zinthu ndi mtundu wa Israyeli?

8 Kuleza mtima kwa Mulungu kumaonekanso ndi mmene anachitira zinthu ndi mtundu wakale wa Israyeli. Kwa zaka zambiri, sanachitepo kanthu pa kusamvera kwawo. Kudzera mwa aneneri ake, anawalimbikitsa mobwerezabwereza  kuti: “Bwererani kuleka ntchito zanu zoipa, nimusunge malamulo anga ndi malemba anga, monga mwa chilamulo chonse ndinachilamulira makolo anu, ndi kuchitumizira inu mwa dzanja la atumiki anga aneneri.” Kodi iwo anatani? N’zachisoni kuti anthuwo “sanamvera.”​—2 Mafumu 17:13, 14.

9. Kodi kuleza mtima kwa Yesu kunafanana bwanji ndi kwa Atate wake?

9 Pomaliza, Yehova anatumiza Mwana wake, amene sanaleke kuchonderera Ayuda kuti ayanjanitsidwenso ndi Mulungu. Kuleza mtima kwa Yesu kunafanana ndendende ndi kuleza mtima kwa Atate wake. Podziwa kuti sipatenga nthawi kuti aphedwe, Yesu analira kuti: “Ha, Yerusalemu, Yerusalemu, amene umapha aneneri, ndi kuwaponya miyala iwo otumidwa kwa iwe! Ine ndinafuna kangati kusonkhanitsa pamodzi ana ako, inde monga thadzi lisonkhanitsa anapiye ake m’mapiko ake, koma inu simunafuna ayi!” (Mateyu 23:37) Woweruza wokakala mtima amene akulakalaka kulanga wina wake sangalankhule mawu odandaula ndi omvetsa chisoni ngati amenewa. Amene angalankhule mawu amenewa ndi bwenzi lachikondi loleza mtima. Yesu, monga Atate wake wakumwamba, anafuna kuti anthu alape ndi kupewa chilango choopsa. Ena anamvera machenjezo amene Yesu anapereka ndipo anapulumuka chilango choopsa chimene Yerusalemu analandira mu 70 C.E.​—Luka 21:20-22.

10. Kodi tapindula bwanji ndi kuleza mtima kwa Mulungu?

10 Kodi sitiyenera kugoma ndi kuleza mtima kwa Mulungu? Ngakhale kuti anthu akhala osamvera kwambiri, Yehova wapatsa aliyense wa ife, limodzinso ndi anthu ena ambiri, mpata woti timudziwe ndi kukhala ndi chiyembekezo chodzapulumuka. Polembera Akristu anzake, Petro anati: “Yesani kulekerera kwa Ambuye wathu chipulumutso.” (2 Petro 3:15) Kodi sitikuyamikira kuti tili ndi chiyembekezo chodzapulumuka chifukwa cha kuleza mtima kwa Yehova? Kodi timapemphera kuti Yehova apitirize kuleza mtima nafe pamene tikum’tumikira tsiku ndi tsiku?​—Mateyu 6:12.

11. Ngati tikumvetsa kuleza mtima kwa Yehova, tidzalimbikitsidwa kuchita chiyani?

11 Tikamvetsa chifukwa chake Yehova ali woleza mtima, zimatithandiza kudikirira moleza mtima chipulumutso chimene iye adzabweretse, ndipo sitiganiza m’pang’ono pomwe kuti akuchedwa kukwaniritsa malonjezo ake. (Maliro 3:26) Pamene tikupitiriza kupemphera kuti Ufumu wa Mulungu udze, tili ndi chikhulupiriro chakuti Mulungu akudziwa nthawi yabwino yoyankhira pemphero limenelo. Ndiponso, timalimbikitsidwa kutsanzira Yehova mwa kukhala oleza mtima ngati iyeyo pochita zinthu ndi abale athu ndi anthu amene timawalalikira. Ifenso sitikufuna kuti ena awonongeke koma kuti alape ndi kukhala ndi chiyembekezo cha moyo wosatha ngati ifeyo.​—1 Timoteo 2:3, 4.

Ganizirani za Kuleza Mtima kwa Aneneri

12, 13. Malinga ndi Yakobo 5:10, kodi mneneri Yesaya anatha bwanji kukhala woleza mtima?

12 Tikamaganizira za kuleza mtima kwa Yehova, zimatithandiza kuyamikira khalidwe limeneli ndi kuyesetsa kuti tikhale nalo. Inde n’zovuta anthu opanda ungwirofe kukhala oleza mtima, koma n’zotheka. Tikuphunzira zimenezi kwa atumiki akale a Mulungu. Wophunzira Yakobo analemba kuti: “Tengani, abale, chitsanzo cha kumva zowawa ndi kuleza mtima, aneneri amene analankhula m’dzina la Ambuye.” (Yakobo 5:10) Tikamadziwa kuti ena anapirira mavuto amene tikukumana nawo, zimatitonthoza mtima ndi kutilimbikitsa.

13 Mwachitsanzo, titenge mneneri Yesaya. Mneneri ameneyu anafunikiradi kuleza mtima pa ntchito yake. Yehova anasonyeza zimenezo mwa kumuuza kuti: “Kauze anthu awa, Imvani inu ndithu, koma osazindikira; yang’anani inu ndithu, koma osadziwitsa. Nenepetsa mtima wa anthu awa, lemeretsa makutu awo, nutseke maso awo; angaone ndi maso awo, angamve ndi makutu awo, angazindikire ndi mtima wawo, nakabwerenso, nachiritsidwe.” (Yesaya 6:9, 10) Ngakhale kuti anthu anali osamva, Yesaya analengeza moleza mtima uthenga wachenjezo wochokera kwa Yehova zaka zosachepera 46!  Ifenso kuleza mtima kudzatithandiza kupirira pa ntchito yathu yolalikira uthenga wabwino, ngakhale kuti ambiri samva.

14, 15. Kodi n’chiyani chimene chinathandiza Yeremiya kupirira mavuto ndi kusiya kutaya mtima?

14 Ndipotu pamene aneneri anali kuchita utumiki wawo, sikuti anali kungolimbana ndi kusamvera kwa anthu; koma anazunzikanso. Yeremiya anaikidwa m’matangadza, “m’nyumba yandende,” ndipo anaponyedwa m’chitsime. (Yeremiya 20:2; 37:15; 38:6) Amene anamuzunza ndi anthu omwewo amene iye anali kufuna kuwathandiza. Koma iye sanawawidwe mtima kapena kubwezera. Anapirira moleza mtima zaka zambiri.

15 Zinthu monga kuzunzika ndi kunyozedwa sizinam’tseke pakamwa Yeremiya, ndipo sizititseka pakamwa ifeyo masiku ano. Inde, tingataye mtima nthawi zina. Ngakhalenso Yeremiya anataya mtima. Analemba kuti: “Mawu a Mulungu ayesedwa kwa ine chitonzo, ndi choseketsa, dzuwa lonse. Ndipo ngati nditi, Sindidzam’tchula Iye, sindidzanenanso m’dzina lake.” Atatero, chinachitika n’chiyani? Kodi Yeremiya analeka kulalikira? Iye anapitiriza kunena kuti: “M’mtima mwanga [mawu a Mulungu anakhala] ngati moto wotentha wotsekedwa m’mafupa anga, ndipo ndalema ndi kupirira, sindingathe kupiriranso.” (Yeremiya 20:8, 9) Onani kuti pamene iye anali kuganizira kwambiri zakuti anthu akumunyoza, anasiya kusangalala. Koma pamene anaganiza kwambiri za ubwino ndi kufunika kwa uthenga wakewo, anayambiranso kusangalala. Ndiponso Yehova anali ndi Yeremiya “ngati wamphamvu ndi woopsa,” kum’limbikitsa kulengeza mawu a Mulungu mwachangu ndi molimba mtima.​—Yeremiya 20:11.

16. Kodi tingakhalebe bwanji osangalala pantchito yathu yolalikira uthenga wabwino?

16 Kodi mneneri Yeremiya anasangalala ndi ntchito yake? Inde! Iye anati kwa Yehova: “Mawu anu anapezeka, ndipo ndinawadya; mawu anu anakhala kwa ine chikondwerero ndi chisangalalo cha mtima wanga; pakuti ndatchedwa dzina lanu, Yehova.” (Yeremiya 15:16) Yeremiya anasangalala kukhala ndi mwayi woimira Mulungu woona ndi kulalikira mawu ake. Ifenso timasangalala. Ndiponso timasangalala, mofanana ndi angelo akumwamba, kuti padziko lonse lapansi anthu ambiri akulandira uthenga wa Ufumu, kulapa, ndi kulowa panjira ya kumoyo wosatha.​—Luka 15:10.

“Chipiriro cha Yobu”

17, 18. Kodi Yobu anapirira motani, ndipo zotsatira zake zinali zotani?

17 Atanena za aneneri akale, wophunzira Yakobo analemba kuti: “Mudamva za chipiriro cha Yobu, ndipo mwaona chitsiriziro cha Ambuye, kuti Ambuye ali wodzala chikondi, ndi wachifundo.” (Yakobo 5:11) Mawu a Chigiriki amene pano anawamasulira kuti “chipiriro” ali ndi tanthauzo lofanana ndi mawu a “kuleza mtima” amene Yakobo anagwiritsa ntchito m’vesi lapitalo. Pofotokoza kusiyana kwa mawu awiriwo, katswiri wina anati: “Mawu oyambawo amanena za kuleza mtima pamene anthu akutizunza, pamene achiwiriwo amanena za kupirira molimba mtima tikakumana ndi zovuta.”

18 Yobu anaona mavuto aakulu. Anataya chuma chake, ana ake, ndipo anadwala nthenda yowawa. Anavutikanso ndi mabodza oti Yehova  anali kum’langa. Yobu sanangokhala chete povutika; anadandaula za mavuto akewo ndipo mpaka anafika poonetsa ngati kuti iye anali wolungama kuposa Mulungu. (Yobu 35:2) Koma sanataye chikhulupiriro chake, ngakhalenso umphumphu wake. Sanatukwane Mulungu ngati mmene Satana ananenera. (Yobu 1:11, 21) Nanga zotsatira zake zinali zotani? Yehova “anadalitsa chitsiriziro cha Yobu koposa chiyambi chake.” (Yobu 42:12) Yehova anachiritsa Yobu, anam’bwezera chuma chake kuwirikiza, ndipo anam’dalitsa ndi moyo wabwino ndi banja lake. Ndiponso chifukwa cha kupirira kwake mokhulupirika, Yobu anam’dziwa bwino Yehova.

19. Kodi tikuphunzirapo chiyani pa kupirira kwa Yobu koleza mtima?

19 Kodi tikuphunzirapo chiyani pa kupirira kwa Yobu koleza mtima? Monga Yobu, tingadwale kapena kukumana ndi mavuto. Sitingamvetse chifukwa chake Yehova akutilola kuyesedwa mwanjira inayake. Koma tikudziwa chinthu chimodzi: Ngati tikhala okhulupirika, tidzadalitsidwa. Yehova salephera kudalitsa anthu amene akum’funafuna ndi mtima wonse. (Ahebri 11:6) Yesu anati: “Iye wakupirira kufikira chimaliziro, iyeyu adzapulumutsidwa.”​—Mateyu 10:22; 24:13.

“Tsiku la Ambuye Lidzadza”

20. N’chifukwa chiyani ife sitikukayika kuti tsiku la Ambuye lidzadza?

20 Ngakhale kuti Yehova ali woleza mtima, alinso wolungama ndipo sadzalekerera zoipa mpaka muyaya. Kuleza mtima kwake kuli ndi malire. Petro analemba kuti: “[Mulungu] sanalekerera dziko lapansi lakale.” Pamene Nowa ndi banja lake anapulumuka, dziko loipalo linamira ndi madzi. Yehova anawononganso Sodomu ndi Gomora, kukhala phulusa lokhalokha. Mwa kupereka zilango zimenezi, anaika ‘chitsanzo kwa iwo osapembedza.’ Ife sitikukayika kuti: ‘Tsiku la Ambuye lidzadza.’​2 Petro 2:5, 6; 3:10.

21. Kodi tingaonetse bwanji kuleza mtima ndi kupirira, ndipo tidzakambirana mfundo yanji m’nkhani yotsatira?

21 Ndiye, tiyeni titsanzire kuleza mtima kwa Yehova mwa kuthandiza ena kuti alape ndipo akapulumuke. Titsanzirenso aneneri mwa kulalikira uthenga wabwino moleza mtima ngakhale pamene anthu amene timawalalikira sakumva. Ndiponso tikudziwa kuti Yehova adzatidalitsa ngati tipirira ziyeso ndi kusunga umphumphu wathu mofanana ndi Yobu. Tili ndi zifukwa zabwino zokhalira osangalala ndi utumiki wathu tikaganiza za madalitso ochuluka amene Yehova waika pa anthu ake amene akuyesetsa kulalikira uthenga wabwino padziko lonse lapansi. Tidzaona zimenezi m’nkhani yotsatira.

Kodi Mukukumbukira?

• N’chifukwa chiyani Yehova amaleza mtima?

• Kodi tikuphunzirapo chiyani pa kuleza mtima kwa aneneri?

• Kodi Yobu anapirira bwanji, ndipo zotsatira zake zinali zotani?

• Tikudziwa bwanji kuti kuleza mtima kwa Yehova kuli ndi malire?

[Mafunso]

[Chithunzi patsamba 18]

Kuleza mtima kwa Yesu kunafanana ndendende ndi kwa Atate wake

[Zithunzi patsamba 20]

Kodi Yehova anafupa Yeremiya motani pa kuleza mtima kwake?

[Zithunzi patsamba 21]

Kodi Yehova anafupa Yobu motani pa kupirira kwake?