Pitani ku nkhani yake

Pitani ku mitu ya nkhani

Kuthandiza Anthu A ku China Omwe Akukhala ku Mexico

Kuthandiza Anthu A ku China Omwe Akukhala ku Mexico

 Kuthandiza Anthu A ku China Omwe Akukhala ku Mexico

“AMUNA khumi adzagwira, ndiwo a manenedwe onse a amitundu, inde adzagwira mkawo wa munthu ali Myuda, ndi kuti, Tidzamuka nanu, pakuti tamva kuti Mulungu ali ndi inu.” (Zekariya 8:23) Masiku ano, ulosi wosangalatsawu ukukwaniritsidwa padziko lonse. Anthu “a manenedwe onse a amitundu” akugwira mkawo wa Israyeli wauzimu n’cholinga cholambira Yehova Mulungu. Mboni za Yehova zili ndi chidwi kwambiri ndi kukwaniritsidwa kwa ulosi umenewu. Mboni zambiri zikuphunzira chinenero china kuti zithe kuchita nawo ntchito yolalikira padziko lonse.

Mboni za Yehova ku Mexico nazonso zikuchita chimodzimodzi. Anthu pafupifupi 30,000 olankhula Chitchaina akukhala ku Mexico. Mu 2003, anthu 15 olankhula Chitchaina anapezeka pa Chikumbutso cha imfa ya Kristu ku Mexico City. Chotero, Mboni ku Mexico zinazindikira kuti gawo la anthu olankhula Chitchaina lingakule mwauzimu. Kuti akhale ndi anthu ambiri oti azilalikira anthu olankhula Chitchaina, anayamba maphunziro a miyezi itatu ophunzitsa Mboni za ku Mexico ulaliki wosavuta m’Chimandarini. Mboni zonse zokwana 25 zinayamba maphunzirowo. Atamaliza maphunzirowa, mkulu wina wochokera ku dera la anthu olankhula Chimandarini ku Mexico City anapezekapo pa mwambowo. Zimenezi zinasonyeza mmene anthu olankhula Chitchaina anakhudzidwira. Bungwe la Chitchaina la kumeneko linalipirira ophunzira atatu sukulu kuti apite kunja kukawonjezera maphunziro awo a Chitchaina.

Maphunziro achinenero anaphatikizapo kuyeserera kulankhula chinenerochi. Ataphunzira mawu osavuta kwambiri, nthawi yomweyo ophunzirawo anayamba kulalikira m’Chitchaina m’chigawo cha malonda ku Mexico City. Ophunzira achanguwo anayambitsa maphunziro a Baibulo 21. Bulosha lakuti Kodi Mulungu Amafunanji kwa Ife? la m’Chitchaina lolembedwa m’zilembo zodziwika, zotchedwa Pinyin, linathandiza kwmbiri.

Kodi Mboni zimene zinali zitayamba kumene kuphunzira Chitchaina zinachititsa bwanji maphunziro a Baibulo? Poyamba, ankatha kungonena chabe kuti, “Qing Du [Tawerengani]” ndi kuloza ndime ndiyeno n’kuloza funso. Munthuyo akawerenga ndi kuyankha m’Chitchaina, ankanena kuti,“Shei shei [Zikomo]” ndiponso kuti, “Hen Hao [Mwachita bwino kwambiri].”

Mboni ina inayamba kuphunzira Baibulo mwa njira imeneyi ndi mkazi wina amene ankadzitcha Mkristu. Itaphunzira katatu ndi mkaziyo, inayamba kukayikira ngati anali kumva zimene anali kuphunzira. Chotero  Mboniyo inapita ndi mbale amene chinenero chake chinali Chitchaina. Atafunsa mkaziyo ngati anali ndi mafunso alionse, mkaziyo anati: “Kodi ndifunikira kudziwa kusambira kuti ndibatizidwe?”

Sipanapite nthawi yaitali, Phunziro la Buku la Mpingo linakhazikitsidwa ndipo pamapezeka anthu 9 olankhula Chitchaina ndiponso Mboni 23 zachimekisiko. Pa anthu opezekapo panali dokotala wa Chitchaina, amene analandira magazini a Nsanja ya Olonda ndi Galamukani! a m’Chisipanya kuchokera kwa wodwala wake wina. Popeza sankatha kuwerenga Chisipanya, munthu wina anamumasulira mizera yochepa. Poona kuti magazini akukamba za Baibulo, anapempha wodwalayo ngati angapeze magaziniwo m’Chitchaina. Wodwalayo anapeza magazini a Chitchaina, ndipo kudzera mu ofesi ya nthambi ya Mboni za Yehova ku Mexico, anakonza zoti Mboni yolankhula Chitchaina imufikire. Amayi a dokotalayu omwe ali ku China anali ndi Baibulo, ndipo dokotalayu ankasangalala kuliwerenga. Pamene anafuna kupita ku Mexico, amayi ake anamuuza kuti asakasiye kuwerenga Baibulo. Chotero anali kupemphera kuti papezeke wina amene angam’thandize kuphunzira zambiri zonena za Mulungu wa m’Baibulo. Iye anafuula kuti: “Mulungu wayankha pemphero langa!”

Enanso omwe ankapezeka pa phunziro la buku linali banja la Chitchaina limene linkachita lendi m’nyumba ya mayi wina Mmekisiko yemwe ankaphunzira Baibulo ndi Mboni za Yehova. Ngakhale kuti banja la Chitchaina linkamva pang’ono Chisipaniya, ankapezekapo pamakambirano a Baibulo. M’kupita kwa nthawi, banjalo linafunsa Mboni yomwe inali kuchititsa phunziro ngati inali ndi buku lililonse la Chitchaina. Sipanapite nthawi, banjalo linayamba kuphunzira Baibulo m’Chitchaina ndipo linafuna kuyamba kulalikira kwa anthu akwawo ndiponso kudzipereka kwa Yehova.

N’zoona kuti Chitchaina n’chovuta kuphunzira. Koma monga momwe taonera, anthu a zinenero zambiri, kuphatikizapo Chitchaina, akuphunzira chifuniro cha Mulungu ku Mexico, ndiponso kumayiko ena padziko lapansi. Akuchita zimenezi mothandizidwa ndi Yehova.

[Chithunzi patsamba 17]

Kalasi yophunzira Chitchaina ku Mexico City

[Chithunzi patsamba 18]

Mboni ya ku Mexico ikuchititsa phunziro la Baibulo m’Chitchaina

[Chithunzi patsamba 18]

Kulalikira khomo ndi khomo m’Chitchaina ku Mexico City