Pitani ku nkhani yake

Pitani ku mitu ya nkhani

Armagedo Kodi ndi Tsoka Limene Lidzakhala Mapeto a Zonse?

Armagedo Kodi ndi Tsoka Limene Lidzakhala Mapeto a Zonse?

 Armagedo Kodi ndi Tsoka Limene Lidzakhala Mapeto a Zonse?

ARMAGEDO! Kodi mawuwa amakuchititsani kuganiza za chiwonongeko choopsa kapena kupsa ndi moto kwa zinthu zonse zakumwamba ndi za padziko lapansi? Pali mawu ochepa chabe a m’Baibulo omwe ndi odziwika kwambiri monga momwe alili mawu oti “Armagedo.” Anthu ambiri amagwiritsa ntchito mawu amenewa kufotokoza tsogolo losautsa limene anthu adzakumana nalo. Mafilimu, ma TV ndi mavidiyo achititsa anthu kuti aziganizira zinthu zoopsa kwambiri zokhudza “Armagedo” imene ikubwerayi. Tanthauzo la liwuli silidziwika bwinobwino ndipo ambiri amalimva molakwa. Ngakhale kuti pali malingaliro ambiri onena za tanthauzo lake, ambiri a matanthauzo amenewa sagwirizana ndi zimene Baibulo, gwero la mawuwa, limaphunzitsa ponena za Armagedo.

Popeza kuti Baibulo limagwirizanitsa Armagedo ndi “mathedwe” a dziko, kodi simukuvomereza kuti n’kofunika kudziwa bwinobwino zimene mawuwa amaimira kwenikweni? (Mateyu 24:3) Ndipo kodi sikungakhale kwanzeru kuyang’ana m’Mawu a Mulungu, gwero lenileni la choonadi, kuti tipeze mayankho ofotokoza zimene Armagedo ili ndi mmene idzakhudzira inuyo ndi banja lanu?

Kufufuza koteroko kudzasonyeza kuti m’malo mokhala tsoka la mapeto a zonse, Armagedo idzakhala chiyambi cha moyo wosangalatsa kwa anthu amene amafuna kukhala moyo wabwino m’dziko latsopano lolungama. Mudzamvetsa bwino kwambiri choonadi chofunika kwambiri cha m’Malemba chimenechi pamene muwerenga nkhani yofotokoza tanthauzo lenileni la Armagedo m’nkhani yotsatirayi.

[Bokosi/​Chithunzi patsamba 3]

KODI MUMAGANIZA KUTI ARMAGEDO N’CHIYANI?

• Kuwonongeka kwa dziko ndi mabomba a nyukiliya

• Kuwonongeka kwa zinthu zachilengedwe

• Kugundana kwa dziko lapansi ndi zinthu zakumwamba

• Nthawi imene Mulungu adzawononga oipa