Pitani ku nkhani yake

Pitani ku mitu ya nkhani

Zopereka Zimene Zimakondweretsa Mulungu

Zopereka Zimene Zimakondweretsa Mulungu

 Zopereka Zimene Zimakondweretsa Mulungu

ZIMENE Mfumukazi Ataliya inachita zinali zosasangalatsa. Mfumukaziyi inali italanda ufumu wa Yuda. Inachita izi mwachinyengo ndiponso mochita kupha anthu. Poganiza kuti onse oyenerera kulowa ufumuwo aphedwa, Ataliya anadzilonga kukhala mfumukazi. Mayi wina wochokera kubanja lachifumu, dzina lake Yoseba, yemwe ankakonda kwambiri Yehova ndi Chilamulo Chake, analimba mtima n’kubisa mwana wina wamng’ono wa kubanja lachifumu. Dzina la mwanayu linali Yoasi. Yoseba pamodzi ndi mwamuna wake Yehoyada, yemwe anali Mkulu wa Ansembe, anabisa mwana wodzalowa ufumuyu kwa zaka zisanu ndi chimodzi m’nyumba yomwe iwo ankakhala pakachisi.​—2 Mafumu 11:1-3.

Yoasi atakwanitsa zaka zisanu ndi ziwiri, Mkulu wa Ansembe Yehoyada anali wokonzeka kukwaniritsa cholinga chake, chochotsa pampando mfumukazi Ataliya yomwe inachita kulanda ufumu mwachinyengo. Anabweretsa poyera mwana ankabisa uja n’kumulonga kukhala mfumu yoyenerera. Kenako, alonda a kunyumba ya mfumu anakokera Mfumukazi yoipa ija, Ataliya, kunja kubwalo la kachisi n’kuipha. Anthu anapeza mpumulo chifukwa cha zimenezi komanso anali achimwemwe. Malinga ndi zochita zawo, Yehoyada ndi Yoseba anathandiza kwambiri pobwezeretsa kulambira koona m’dziko la Yuda. Koma chachikulu kuposa zimenezi chinali chakuti awiriwa anathandiza kuti mzera wachifumu wa Davide upitirire, womwe unadzafika mpaka pa Mesiya.​—2 Mafumu 11:4-21.

Nayonso mfumu yomwe anali atangoilonga kumeneyo inadzachita zinthu zofunika kwambiri zomwe zinakondweretsa Mulungu. Nyumba ya Yehova inkafunika kukonzedwa mwamsangamsanga. Chifukwa cha mtima wake wosakhutitsidwa wofuna kulamulira yekha dziko la Yuda, Ataliya anachititsa kuti anthu anyalanyaze kachisi komanso kuti afunkhemo zinthu. Motero, Yoasi ankafunitsitsa kubwezeretsa kachisiyo mwakale. Mosakhalitsa, analamula kuti pasonkhedwe ndalama zokonzetsera nyumba ya Yehova. Anati: “Landirani ndalama zonse za zinthu zopatulika azibwera nazo ku nyumba ya Yehova, ndizo ndalama za otha msinkhu, ndalama za munthu aliyense monga adamuyesa, ndi ndalama zimene yense azikumbuka m’mtima mwake kuti abwere nazo ku nyumba ya Yehova. Ansembe azilandire yense kwa iye amene adziwana naye, akonze nazo mogamuka nyumba, paliponse akapeza pogamuka.”​—2 Mafumu 12:4, 5.

Anthu analidi ndi mtima wofuna kuthandizapo. Komano, ansembe sanafune kugwira ndi mtima wonse ntchito yawo yokonzanso kachisi. Motero, mfumu inakonza zoti ndiyo iziyang’anira ntchitoyi ndi kulamula kuti ndalama zonse ziziikidwa m’bokosi lapadera. Mfumu inaika Yehoyada kukhala woyang’anira zimenezi, ndipo timawerenga kuti: “Yehoyada wansembe anatenga bokosi, naboola chiboo pa chivundikiro chake, naliika pafupi pa guwa la nsembe, ku dzanja lamanja polowera nyumba ya Yehova; ndipo ansembe akusunga pakhomo anaikamo ndalama zonse anabwera nazo anthu ku nyumba ya Yehova. Ndipo pakuona kuti ndalama zidachuluka m’bokosimo, anakwerako mlembi wa mfumu, ndi mkulu wansembe, nazimanga m’matumba,  naziyesa ndalama zopereka m’nyumba ya Yehova. Napereka ndalama zoyesedwa m’manja mwa iwo akuchita ntchitoyi, akuyang’anira nyumba ya Yehova; ndipo iwo analipira nazo amisiri a mitengo ndi omanga, akugwira ntchito ya pa nyumba ya Yehova, ndi omanga miyala ndi osema miyala, ndi kugula mitengo ndi miyala yosema kukakonza mogamuka nyumba ya Yehova, ndi zonse zoigulira nyumba zoikonzera.”​—2 Mafumu 12:9-12.

Anthu anadzipereka ndi mtima wonse pantchitoyi. Nyumba yolambiriramo ya Yehova inabwerera mwakale kuti anthu ayambirenso kum’pembedza m’njira yolemekezeka. Motero, ndalama zonse zomwe zinaperekedwa zinagwiritsidwa ntchito moyenerera. Mfumu Yoasi inaonetsetsa kuti zaterodi.

Masiku ano, gulu looneka la Yehova limaonetsetsa kuti ndalama zonse zimene anthu apereka zikugwiritsidwa ntchito moyenerera. Limaonetsetsa kuti zikugwira ntchito yopititsa patsogolo kulambira Yehova, ndipo mmene Akristu oona akuchitira zinthu zikufanana ndi mmene anachitira Aisrayeli kalekalelo. Akuthandiza ndi mtima wonse. N’kutheka kuti inu ndi mmodzi mwa anthu amene anathandiza nawo n’cholinga chopititsa patsogolo ntchito za Ufumu m’chaka chautumiki chapitachi. Tiyeni tione zina mwa ntchito zimene chithandizo chanucho chinagwira.

KUSINDIKIZA MABUKU

Padziko lonse, panasindikizidwa mabuku, magazini, mathirakiti ndiponso panakonzedwa mavidiyo otsatirawa oti aphunziridwe ndi kufalitsidwa:

• Mabuku: 47,490,247

• Timabuku: 6,834,740

• Mabulosha: 167,854,462

• Makalendala: 5,405,955

• Magazini: 1,179,266,348

• Mathirakiti: 440,995,740

• Mavidiyo: 3,168,611

Ntchito yosindikiza ikuchitikira ku Africa, North, Central, ndi South America, Asia, m’mayiko a m’zilumba za panyanja ya Pacific, ndi ku Ulaya. Mayiko onse amene amasindikizirako mabuku alipo 19.

“Dzina langa ndi Katelyn May. Ndine wazaka eyiti. Ndili ndi madola 28 awa ndipo ndikufuna kuti mutenge ndi kuwonjezera pa ndalama zolipirira makina osindikizira mabuku. Ndine mlongo wanu wachichepere, Katelyn.”

“Banja lathu linakhala pansi ndi kukambirana za makina atsopano osindikizira mabuku. Ana athu, wazaka 11 ndi wina wazaka 9, anaganiza zotapako ndalama zawo ku banki n’kuthandizapo. Ndife okondwa kukutumizirani thandizo lawolo pamodzi ndi lathu.”

 NTCHITO YOMANGA

Nazi zina mwa ntchito zomanga zimene zachitika kuti zipititse patsogolo ntchito za Mboni za Yehova:

• Nyumba za Ufumu m’mayiko osauka: 2,180

• Nyumba za Misonkhano: 15

• Nthambi: 10

• Atumiki odzifunira a nthawi zonse a padziko lonse: 2,342

“Mlungu uno tachita msonkhano woyamba m’Nyumba ya Ufumu yathu yatsopano. Tili ndi chimwemwe chodzadza tsaya kukhala ndi malo abwino otamandira Atate wathu, Yehova Mulungu. Tikuthokoza Yehova ndiponso inuyo potithandiza pa mavuto athu mwa kumanga Nyumba za Ufumu zambiri. Kunena zoona, Nyumba ya Ufumu yathu ndi yaphindu kwambiri m’dera lathu.”​—Chile.

“Abale ndi alongo amayamikira kwambiri thandizo limene gulu la Yehova limapereka. Mpaka pano, timafotokozabe za momwe tinasangalalira kukhala limodzi ndi gulu la omanga.”​—Moldova.

“Posachedwapa, ine ndi mkazi wanga tinali kukondwerera kuti takwanitsa zaka 35 tili m’banja. Timaganizaganiza kuti tigulirane chiyani pa chikondwererochi, ndipo tinaganiza zoti tim’bwezere kenakake Yehova ndiponso gulu lake, chifukwa padakapanda thandizo la Yehovayo ndi gulu lakelo, sibwenzi ukwati wathu ukuyenda bwino. Tikufuna kuti ndalama tatumizazi zigwire ntchito yothandizira kumanga Nyumba ya Ufumu m’dziko linalake losauka.”

“Posachedwapa ndinalandira cholowa changa, ndiye poti ‘zolakalaka’ pamoyo wanga ndi zochepa ndipo nazo ‘zofunika’ pamoyo wanga ndi zochepa kwambiri, ndikufuna kuti mutenge ndalama ndatumizazi kuti zithandize kumangitsira Nyumba za Ufumu, zimene zikufunika kwambiri m’mayiko ambiri.”

 THANDIZO PAKAGWA MASOKA

M’masiku omaliza ano, nthawi zambiri masoka amangotigwera mwadzidzidzi. Mboni za Yehova zambiri zimapereka thandizo lina lowonjezera pofuna kuthandiza abale awo omwe ali m’madera omwe mwagwa tsoka. Tikukumbutseni kuti zopereka zoti zithandize pakagwa masoka zimakalowa ku thumba la zopereka za ntchito yapadziko lonse. Nawa ena mwa madera amene anthu ovutika anathandizidwa ndi Mboni za Yehova kutagwa tsoka:

• Africa

• Asia

• Chigawo cha Caribbean

• Zilumba za panyanja ya Pacific

“Ine ndi mwamuna wanga tikufuna kukuyamikirani kwambiri chifukwa chotumiza katundu wachithandizo, mphepo za mkuntho zitawononga katundu. Tinatha kukhoma denga latsopano pa nyumba yathu. Tikuyamikira mochoka pansi pamtima chifukwa choti munachitapo kanthu mwamsanga.”

“Dzina langa ndine Connor, ndipo ndili ndi zaka 11. Nditaona zomwe zinachitika chifukwa cha tsunami, ndinafuna kuthandiza nawo. Ndikuganiza kuti izi zithandiza abale ndi alongo anga.”

 ATUMIKI A NTHAWI ZONSE APADERA

Akristu ambiri ndithu amagwira ntchito yolalikira nthawi zonse kapena amatumikira nthawi zonse panyumba za Beteli. Ena mwa antchito odzipereka a nthawi zonse amasamalidwa ndi chithandizo chomwe anthu amapereka modzifunira. Ena mwa anthu amenewa ndi:

• Amishonale: 2,635

• Oyang’anira oyendayenda: 5,325

• Atumiki a pa Beteli: 20,092

“Poti sindingatumikire pa Beteli panopo [mnyamata wazaka zisanu], ndikufuna kutumiza thandizo langali ndipo ndine wosangalala kwambiri. Ndikadzakula, ndidzapita ku Beteli kukagwira ntchito molimbika.”

Kupititsa Patsogolo Ntchito Yophunzitsa Baibulo

Yesu Kristu analamula anthu omutsatira ‘kuphunzitsa anthu a mitundu yonse.’ (Mateyu 28:19) Potsatira mawu akewa, Mboni za Yehova zikugwira ntchito mwakhama m’mayiko 235, kulalikira ndi kuphunzitsa anthu uthenga wa m’Baibulo. Mboni zimasindikiza ndi kufalitsa mabuku ofotokoza za m’Baibulo m’zinenero 413.

Kunena zoona, thandizo lamtengo wapatali limene Mkristu angapereke pothandiza anthu ambiri kuphunzira za Mulungu ndiponso zolinga zake, ndilo nthawi. Mboni za Yehova zathera nthawi yochuluka ndiponso nyonga zawo pothandiza anzawo. Komanso zathandiza ndi ndalama mowolowa manja, ndipo thandizo lawo lonse limene laperekedwa m’njira zosiyanasiyana, lachititsa kuti dzina la Yehova pamodzi ndi zolinga zake zidziwike padziko lonse. Yehova apitirize kudalitsa ntchito imeneyi, yofuna kuthandiza ena kudziwa zambiri zokhudza iyeyo. (Miyambo 19:17) Yehova amakondwera ndi mtima woterewu.​—Ahebri 13:15, 16.

[Bokosi pamasamba 28-30]

Njira Zimene Ena Amaperekera

ZOPEREKA ZA NTCHITO YA PADZIKO LONSE

Ambiri amaika padera ndalama zimene amaponya m’mabokosi a zopereka olembedwa kuti: “Zopereka za Ntchito ya Padziko Lonse​—Mateyu 24:14.”

Mwezi uliwonse mipingo imatumiza ndalama zimenezi ku ofesi ya Mboni za Yehova imene imayang’anira ntchito ya m’dziko lawo. Mungatumizenso nokha ndalama zimene mukufuna kupereka ku Accounting Office, Watch Tower Bible and Tract Society of Pennsylvania, P. O. Box 30749, Lilongwe 3, Malawi, kapena ku ofesi ya nthambi ya Mboni za Yehova ya m’dziko lanu. Mukamatumiza macheke ku adiresi yomwe ili pamwambayi, musonyeze kuti ndalamazo zipite kwa “Watch Tower.” Mungathenso kupereka zinthu ngati ndolo, mphete, zibangili, kapena zinthu zina zamtengo wapatali. Potumiza zinthu zimenezi, mulembe kalata yachidule yofotokoza kuti zimene mukutumizazo ndi mphatso.

MPHATSO ZINA

Kuwonjezera pa kupereka mphatso za ndalama, palinso njira zina zoperekera zinthu zopititsira patsogolo utumiki wa Ufumu padziko lonse. Zina mwa njirazi ndi izi:

Inshuwalansi: Mungalembetse kuti Watch Tower Society ndiyo idzapatsidwe phindu la inshuwalansi kapena ndalama za penshoni.

Maakaunti a ku Banki: Mukhoza kuikiza m’manja mwa Watch Tower Society maakaunti anu a ku banki, zikalata zosungitsira ndalama, kapena maakaunti a ndalama zimene mukusunga kuti mudzagwiritse ntchito mukadzapuma pantchito. Mukhozanso kukonza zoti mukadzamwalira a Watch Tower Society adzatenge zinthu zimenezi. Pochita zimenezi, mutsatire malamulo amene mabanki a m’dziko lanu amayendera.

Masheya: Mungapereke masheya amene muli nawo mu kampani ku Watch Tower Society monga mphatso.

Malo ndi Nyumba: Mungapereke monga mphatso malo ndi nyumba zoti zingagulitsidwe, kapena ngati ili nyumba yoti mukukhalamo mukhoza kupitiriza kukhalamo pamene muli ndi moyo. Musanakonze zopereka malo kapena nyumba iliyonse, lankhulani kaye ndi ofesi ya nthambi ya m’dziko lanu.

Chuma Chamasiye: Mukhoza kulemba mu wilo yovomerezeka ku boma kuti Watch Tower Society idzapatsidwe katundu wanu kapena ndalama zanu inuyo mukadzamwalira.

Ngati mukufuna kudziwa zambiri za mmene mungaperekere mphatso zimenezi, lankhulani ndi a ku Accounting Office pa telefoni kapena alembereni kalata pa adiresi imene ili pansipa kapena mungalembe kalata ku ofesi ya nthambi ya Mboni za Yehova ya m’dziko lanu.

Accounting Office

Watch Tower Bible and Tract Society of Pennsylvania

P. O. Box 30749

Lilongwe 3

Malawi

Telefoni: 01 762 111

[Mawu a Chithunzi patsamba 27]

Faithful video: Stalin: U.S. Army photo