Pitani ku nkhani yake

Pitani ku mitu ya nkhani

Kodi Alipo Amene Angasinthedi Dzikoli?

Kodi Alipo Amene Angasinthedi Dzikoli?

Kodi Alipo Amene Angasinthedi Dzikoli?

“Anthu osauka amatiuza kuti chinthu choyamba chimene iwo amafuna ndi kukhala mwamtendere ndi motetezeka, ndipo kenako apeze mwayi wotukula miyoyo yawo. Amafuna mfundo zachilungamo m’mayiko mwawo ndiponso padziko lonse kuti zomwe iwo amachita zisamasokonezedwe ndi mphamvu zochuluka zimene mayiko ndi makampani olemera ali nazo.”

UMU ndi mmene mkulu wa bungwe lina la padziko lonse lothandiza anthu pakagwa mavuto adzidzidzi anafotokozera zimene anthu osauka amafuna. Ndipotu, mawu akewa akufotokoza bwino zimene anthu onse okhudzidwa ndi masoka ndiponso kusoweka chilungamo padzikoli amafuna. Onse amafunitsitsa kukhala m’dziko la mtendere weniweni ndiponso la chitetezo chokwanira. Koma kodi n’zothekadi kukhala ndi dziko loterolo? Kodi pali aliyense amene ali ndi mphamvu ndiponso nzeru zosintha dziko limene lilibiretu chilungamoli?

Kuyesetsa Kusintha Zinthu

Anthu ambiri ayesapo kusintha zinthu. Mwachitsanzo, mngelezi wina wa m’zaka za m’ma 1800, dzina lake Florence Nightingale, anadzipereka moyo wake wonse kusamalira bwino odwala. Masiku amenewo, n’kuti kusanabwere mankhwala opha tizilombo toyambitsa matenda m’thupi la munthu, ndipo odwala sankathandizidwa ngati mmene amathandizidwira masiku ano. Buku lina limati: “Manesi [anali] osaphunzira, auve, otchuka ndi uchidakwa ndiponso chiwerewere.” Kodi zimene Florence Nightingale ankafuna kuchita, zoyesa kusintha mmene odwala anali kuthandizidwira, zinathekadi? Inde. Mofanana ndi zimenezi, nazonso ntchito za anthu ambirimbiri oganizira anzawo ndiponso amtima wofuna kuthandizadi zakhala zikuthandiza kwambiri. Iwo ayesetsa kuthandiza anthu m’njira zosiyanasiyana, monga pankhani za maphunziro, mankhwala, nyumba, ndiponso za chakudya. Izi zachititsa kuti miyoyo ya anthu ambiri ovutika itukuke kwambiri.

Komabe, sitinganyalanyaze mfundo yokhumudwitsa iyi yakuti: Anthu ankhaninkhani akuvutikabe ndi nkhondo, umbanda, matenda, njala, ndiponso mavuto ena. Bungwe lina lothandiza anthu ovutika la ku Ireland, lotchedwa Concern linati: “Anthu 30,000 amafa tsiku ndi tsiku chifukwa cha umphawi.” Ngakhalenso ukapolo, vuto limene anthu ambiri ofuna kusintha zinthu m’mbuyomu analimbana nalo kwambiri, udakalipobe. “Panopo kuli akapolo ambiri kusiyana ndi anthu onse amene anabedwa ku Africa panthawi ya malonda a ukapolo owoloka nawo nyanja yamchere ya Atlantic,” linatero buku lakuti Disposable People​—New Slavery in the Global Economy.

Kodi n’chiyani chasokoneza ntchito za anthu ofuna kusintha zinthu kwamuyaya? Kodi ndi mphamvu zochuluka zimene anthu olemera ndi amphamvu ali nazo basi, kapena pali zinthu zinanso?

Zolepheretsa Kusintha

Malinga ndi Mawu a Mulungu, Satana Mdyerekezi ndiye wolepheretsa wamkulu wa zimene anthu akuchita zofuna kuti padzikoli pakhale chilungamo chenicheni. Mtumwi Yohane akutiuza kuti “dziko lonse lapansi ligona mwa woipayo.” (1 Yohane 5:19) Ndipo tikunena pano, Satana akusokeretsa dziko lonse lapansi. (Chivumbulutso 12:9) Anthu adzapitirizabe kukumana ndi mavuto ndiponso kusoweka kwa chilungamo, pokhapokha ngati maganizo oipa amene iye amalimbikitsa atachotsedwa. Kodi n’chiyani chinachititsa kuti zinthu zifike pomvetsa chisonipa?

Makolo athu oyambirira, Adamu ndi Hava, anapatsidwa paradaiso amene cholinga chake chinali choti anthu onse azikhalamo. Dziko limenelo linali ‘labwino ndithu.’ (Genesis 1:31) Kodi ndani anachititsa kuti zinthu zisinthe? Anali Satana. Iye anatsutsana ndi zoti Mulungu ndi woyenerera kuika malamulo oti anthu azitsatira. Iye ananena kuti Mulungu salamulira mwachilungamo. Iye anachititsa kuti Adamu ndi Hava asankhe kukhala moyo wodziimira paokha, n’cholinga choti azidzisankhira okha chabwino ndi choipa. (Genesis 3:1-6) Izi zinabweretsa uchimo ndi kupanda ungwiro, zomwe ndi chinthu chachiwiri chomwe chikuchititsa kuti zoyesayesa za anthu pofuna kuti dziko likhale lachilungamo zisamayende bwino.​—Aroma 5:12.

Kodi Analoleranji Zimenezi?

Ena angafunse kuti, ‘Komano Mulungu analoleranji kuti pakhale uchimo ndi kupanda ungwiro? Bwanji sanangogwiritsa ntchito mphamvu zake zopanda malire kuwononga ogalukirawo ndi kungoyambiranso?’ Izi zikuoneka ngati njira yachidule. Komatu pamakhala mafunso akuluakulu pankhani yogwiritsa ntchito mphamvu. Kodi simukuvomereza kuti limodzi mwa madandaulo akuluakulu a anthu osauka ndi oponderezedwa padzikoli n’lakuti anthu akugwiritsa ntchito mphamvu zawo molakwika? Kodi anthu amaganizo olongosoka sakayikira mtsogoleri wina wankhanza akamagwiritsa ntchito mphamvu zake kupha aliyense amene sakugwirizana ndi mfundo zake?

Pofuna kutsimikizira anthu amaganizo olongosoka kuti Iye sagwiritsa ntchito mphamvu zake molakwika ndiponso mwankhanza, Mulungu anasankha kuti, kwa nthawi yochepa chabe, alole Satana pamodzi ndi anthu omugalukira aja kukhala modziimira, mosatsatira malamulo ndiponso mfundo zake. Mulungu ankadziwa kuti m’kupita kwa nthawi zidzaoneka zokha kuti ulamuliro Wake ndi ulamuliro wokhawo wabwino. Zidzasonyeza kuti zilizonse zimene Iye amatiletsa kuti tisachite amatero chifukwa chotifunira zabwino. Ndipotu, zinthu zomvetsa chisoni zomwe zachitika chifukwa cha kugalukira ulamuliro wa Mulungu zasonyeza kale kuti zimenezi ndi zoona. Ndipo zatsimikizira kuti Mulungu ali ndi zifukwa zomveka zogwiritsira ntchito mphamvu zake zazikulu kuthetsa kuipa konse panthawi yomwe adzafune kutero, ndipotu adzachita zimenezi posachedwapa.​—Genesis 18:23-32; Deuteronomo 32:4; Salmo 37:9, 10, 38.

Kufikira panthawi imene Mulungu adzachitepo kanthuyo, panopa sitingachitire mwina, tizikhalabe m’dziko lopanda chilungamoli, momwe tonse ‘tikubuula, ndi kugwidwa m’zowawa.’ (Aroma 8:22) Tikhoza kuchita zambiri pofuna kuti tisinthe zinthu, koma sitingachotse Satana, kapenanso kuthetseratu kupanda ungwiro, komwe ndi gwero la mavuto onse omwe tikukumana nawo. Ifeyo sitingathe kuthetsa mavuto obwera chifukwa cha uchimo womwe tinatengera kwa kholo lathu Adamu.​—Salmo 49:7-9.

Yesu Kristu Adzasintha Zinthu Kwamuyaya

Kodi zimenezi zikutanthauza kuti palibe chiyembekezo chilichonse? Ayi, sichoncho. Wina wamphamvu zochuluka kuposa za anthu wapatsidwa udindo wosintha zinthu. Kodi ameneyu ndani? Ndi Yesu Kristu. Baibulo limati iye ndi “Mtsogoleri” kapena kuti Woimira Wamkulu wa Mulungu wopulumutsa anthu.​—Machitidwe 5:31.

Panopo akudikirira “nthawi” ya Mulungu kuti agwire ntchito yake. (Chivumbulutso 11:18) Koma kodi adzachitanji makamaka? Iye ‘adzakonzanso zinthu zonse, zimene Mulungu analankhula za izo m’kamwa mwa aneneri ake oyera chiyambire.’ (Machitidwe 3:21) Mwachitsanzo, Yesu “adzapulumutsa waumphawi wofuulayo; ndi wozunzika amene alibe mthandizi. . . . Adzawombola moyo wawo ku chinyengo ndi chiwawa.” (Salmo 72:12-16) Kudzera mwa Yesu Kristu, Mulungu akulonjeza kudzathetsa “nkhondo ku malekezero adziko lapansi.” (Salmo 46:9) Akulonjeza kuti “wokhalamo [m’dziko lake loyeretsedwalo] sadzanena, Ine ndidwala.” Akhungu, ogontha, olumala, tingoti onse ovutika ndi matenda, adzakhala athanzi labwino kwambiri. (Yesaya 33:24; 35:5, 6; Chivumbulutso 21:3, 4) Ngakhale anthu amene anafa zaka zambiri zapitazo adzapindula ndi zimene iye adzachite. Yesu akulonjezanso kuti adzaukitsa anthu amene anafa chifukwa cha kusoweka kwa chilungamo ndiponso kuponderezedwa.​—Yohane 5:28, 29.

Kusintha kumene Yesu Kristu adzabweretse sikuti kudzangokhala kwa zinthu zina chabe, ndiponso kongoyembekezera chabe ayi. Adzathetseratu zinthu zonse zimene zikulepheretsa kuti padzikoli pakhale chilungamo chenicheni. Adzachotsa uchimo ndi kupanda ungwiro ndi kuwononga Satana Mdyerekezi ndiponso anthu onse amene amatsatira zochita zake zopanduka. (Chivumbulutso 19:19, 20; 20:1-3, 10) Mavuto amene Mulungu walola kuti akhalepo kwa nthawi yochepa ‘sadzauka kawiri.’ (Nahumu 1:9) Izi n’zimene Yesu anali kuganiza pamene anatiphunzitsa kupemphera kuti Ufumu wa Mulungu udze ndipo kufuna kwa Mulungu kuchitidwe ‘monga Kumwamba chomwecho pansi pano.’​Mateyu 6:10.

Mwina mungatsutse zimenezi n’kunena kuti, ‘Komano kodi si Yesu yemweyo amene anati “tidzakhala nawo aumphawi pamodzi nafe nthawi zonse”? Kodi izi sizikutanthauza kuti kupanda chilungamo ndiponso umphawi zipitirirabe?’ (Mateyu 26:11) Ndi zoona, Yesu ananenadi kuti padzakhala anthu aumphawi nthawi zonse. Komano, zimene zinachititsa kuti anene zimenezi komanso malonjezo a m’Mawu a Mulungu zimasonyeza kuti anali kutanthauza kuti malinga ngati dongosolo ili la zinthu lilipo pazikhala anthu aumphawi. Anali kudziwa kuti palibe munthu amene angathe kuthetsa umphawi ndiponso kusoweka kwa chilungamo padzikoli. Ankadziwanso kuti iye adzasintha zonsezo. Posachedwapa adzasinthiratu zinthu. Adzabweretsa “miyamba yatsopano, ndi dziko latsopano” mmene simudzakhalanso zopweteka, matenda, umphawi, ndi imfa.​—2 Petro 3:13; Chivumbulutso 21:1.

‘Musaiwale Kuchita Chokoma’

Kodi izi zikutanthauza kuti n’kungotaya nthawi pachabe kuchita zinthu zothandiza anthu ena? Ayi. Baibulo limatilimbikitsa kuthandiza ena akakumana ndi mayesero ndiponso mavuto. “Oyenera kulandira zabwino usawamane; pokhoza dzanja lako kuwachitira zabwino,” inalemba motero Mfumu Solomo yakale kwambiri. (Miyambo 3:27) Naye mtumwi Paulo anatilimbikitsa kuti: “Musaiwale kuchitira chokoma ndi kugawira ena.”​—Ahebri 13:16.

Yesu Kristu mwiniwakeyo anatilimbikitsa kuchita zomwe tingathe kuti tithandize ena. Anafotokoza fanizo la Msamariya wachifundo yemwe anapeza munthu amene anamenyedwa ndi kufwambidwa. Yesu anati Msamariyayo “anagwidwa chifundo” ndi kugwiritsa ntchito zinthu zake kumangira mabala a munthu womenyedwayo ndiponso kum’thandiza kuti achire. (Luka 10:29-37) Sikuti Msamariya wachifundoyu anasintha dziko ayi, koma anasintha kwambiri moyo wa munthu wina. Ifenso tingathe kuchita zimenezo.

Komatu, Yesu Kristu angachite zambiri kuwonjezera pa kuwathandiza anthu. Iye angasinthedi zinthu, ndipo adzachita zimenezo posachedwapa. Akadzatero, anthu ovutika chifukwa cha kusoweka chilungamo masiku ano adzatha kutukula miyoyo yawo ndi kukhala pamtendere weniweni ndiponso motetezekadi.​—Salmo 4:8; 37:10, 11.

Pamene tikudikirira kuti zimenezo zidzachitike, tiyeni tisakayike kuchita chilichonse chimene tingathe, mwauzimu ndiponso m’njira zina, ‘pochitira chokoma’ onse amene akuvutika ndi dziko lopanda chilungamoli.​—Agalatiya 6:10.

[Zithunzi patsamba 5]

Florence Nightingale anasintha kwambiri chithandizo cha odwala

[Mawu a Chithunzi]

Courtesy National Library of Medicine

[Zithunzi patsamba 7]

Otsatira Kristu amachitira ena zabwino

[Mawu a Chithunzi patsamba 4]

The Star, Johannesburg, S.A.