Pitani ku nkhani yake

Pitani ku mitu ya nkhani

Khalidwe Labwino Limabala Zipatso Zabwino

Khalidwe Labwino Limabala Zipatso Zabwino

 Khalidwe Labwino Limabala Zipatso Zabwino

PA CHILUMBA china chaching’ono cha kufupi ndi gombe la kum’mwera kwa dziko la Japan, mayi wina ndi ana ake ang’onoang’ono atatu anayamba kuphunzira Baibulo ndi Mboni za Yehova. Poona zimenezi, anansi a mayiyu m’dera la kutali ndi tawuni limeneli, lomwe anthu ake n’ngokonda kwambiri chikhalidwe chawo, anasiya kumulankhula akamuona. Mayiyu anati: “Chomwe chinkandiwawa kwambiri kuposa kusandilankhulako chinali chakuti anthu sankamasuka kucheza ndi mwamuna wanga ndiponso ana anga.” Komabe iye anauza ana ake kuti: “Tipitirize kupatsa moni anansi athu n’cholinga choti tikondweretse Yehova.”​—Mateyu 5:47, 48.

Kunyumba, mayiyu anaphunzitsa anawo kukhala aulemu ngakhale anthu atapanda kusangalala nawo. Paulendo wawo wanthawi zonse wopita ku malo a akasupe a madzi otentha, anawo ankayesezera moni wawo ali m’galimoto. Akafika kumalowo, nthawi zonse anawo ankalankhula mokweza ndi mwansangala kuti, “Konnichiwa!,” kutanthauza kuti “Moni!” Banjali linapitiriza kupatsa moni aliyense amene lakumana naye, ngakhale kuti anansi awowo sankawayankha mwansangala. Komabe, anthu anaona khalidwe labwino la anawo.

Kenako, anansi awo aja mmodzi ndi mmodzi anayamba kumayankha moni, amvekere, “Konnichiwa.” Pamene zaka ziwiri zimatha, pafupifupi munthu aliyense mumzinda wawowo anali kuyankha moni wa banjalo. Komanso anthuwo anali atayamba kupatsana moni okhaokha ndiponso kumasukirana kwambiri. Wachiwiri kwa meya wa mumzindawo anafuna kuyamikira anawo chifukwa cha mbali yomwe anachita yothandiza kuti zinthu zisinthe n’kufika pamenepo. Koma mayi wa anawo anam’tsimikizira kuti anawo ankangochita zomwe Akristu amayenera kuchita. Kenako, pa mpikisano wina wa kulankhula wa pachilumba chonsecho, mwana mmodzi wa mayiyu anafotokoza mmene mayi awo anaphunzitsira banjalo kupatsa anthu moni mwaulemu kaya ayankhe zotani. Mwanayo analandira mphoto yoyamba chifukwa cha zimene anafotokozazi, zomwenso zinasindikizidwa m’nyuzipepala ya mumzinda wawo. Masiku ano banjali likusangalala kwambiri poona kuti kutsatira mfundo zachikristu kunabala zipatso zabwino chonchi. Kulalikira uthenga wabwino sikuvuta m’pang’ono pomwe ngati anthu ali omasukirana.