Pitani ku nkhani yake

Pitani ku mitu ya nkhani

Kodi Ndi Bwino Kuganizira Mmene Ena Amationera?

Kodi Ndi Bwino Kuganizira Mmene Ena Amationera?

 Kodi Ndi Bwino Kuganizira Mmene Ena Amationera?

PAFUPIFUPI aliyense amasangalala akamayamikiridwa. Ena akamatiyamikira timamva bwino ndipo timaona kuti tikuchita bwino. Kuyamikiridwa kumathanso kutilimbikitsa kuchita zinthu zoposa zimene tikuchita panopo. Koma maganizo onsewa sakhalapo tikaona kuti anthu ena sakuyamikira zochita zathu. Ena akapanda kuonetsa chidwi ndi zimene tachita kapenanso akamazinyoza tingathe kufooka. Zimene ena amatiganizira zingatichititse kuti nafenso tizidziona m’njira yomweyo.

N’kulakwa kunyalanyaza zimene ena amatiganizira. Kwenikweni tingapindule polola kuti ena aziona bwinobwino khalidwe lathu. Maganizo a anzathu amakhalidwe abwino angatipindulitse kwambiri, n’kutilimbikitsa kukhala anthu owongoka mtima. (1 Akorinto 10:31-33) Komabe, kawirikawiri maganizo a anthu ambiri sakhala achilungamo. Taganizirani maganizo olakwika okhudza Yesu Kristu amene akulu ansembe ndiponso anthu ena anali nawo pamene “anafuula, nanena, m’pachikeni, m’pachikeni.” (Luka 23:13, 21-25) M’pofunika kuti tisamavutike ndi maganizo aliwonse amene anthu ena amakhala nawo chifukwa cha nsanje kapena tsankho. Motero, tiyenera kuona maganizo a ena mwanzeru ndiponso mosamala.

Kodi Ndi Maganizo a Ndani Amene Ali Ofunika?

Timafuna kuti anthu amene timagwirizana nawo pa kulambira koona azitiganizira zabwino. Amenewa ndi anthu monga achibale athu a chikhulupiriro chofanana ndi chathu ndiponso abale ndi alongo athu achikristu. (Aroma 15:2; Akolose 3:18-21) Chikondi ndiponso ulemu umene okhulupirira anzathu amatipatsa komanso ‘kutonthozedwa pamodzi ndi iwo’ kungatilimbikitse kwambiri. (Aroma 1:11, 12) Pokhala ‘odzichepetsa mtima, timaona kuti anthu ena n’ngotiposa ifeyo.’ (Afilipi 2:2-4) Kuphatikizanso apo, timachita zotheka kuti ‘amene akutsogolera pakati pathu,’ omwe ndi akulu mumpingo mwathu, azitiganizira zabwino.​—Ahebri 13:17.

Komanso china chofunika n’chakuti ‘ngakhale akunja azitiikira umboni wabwino.’ (1 Timoteo 3:7) Zimakhalatu bwino achibale athu amene ali osakhulupirira, anthu a kuntchito kwathu, ndiponso anthu okhala moyandikana nafe akamatilemekeza. Ndiponsotu timayesetsa kukhala ndi mbiri yabwino kwa anthu amene timawalalikira chifukwa izi zimawathandiza kumvetsera uthenga waufumu mosavuta. Anthu a kumene tikukhala akamadziwa kuti ndife amakhalidwe abwino, owongoka mtima, ndiponso oona mtima, Mulungu amalemekezedwa. (1 Petro 2:12) Komabe, sitiyenera kuswa mfundo za m’Baibulo kuti ena atikonde; ndiponso sitiyenera kuchita zinthu zachiphamaso kuti atigomere. Tiyenera kuzindikira kuti n’zosatheka kusangalatsa aliyense. Yesu anati: “Mukadakhala a dziko lapansi, dziko lapansi likadakonda zake za lokha; koma popeza simuli a dziko lapansi, koma ine ndakusankhani inu mwa dziko lapansi, chifukwa cha ichi likudani inu.” (Yohane 15:19) Kodi pali chilichonse chimene tingachite kuti olimbana nafe azitilemekeza?

Kuti Olimbana Nafe Azitilemekeza

Yesu anachenjeza kuti: “Adzada inu anthu onse chifukwa cha dzina langa; koma iye wakupirira  kufikira chimaliziro, iyeyu adzapulumutsidwa.” (Mateyu 10:22) Chidani chimenechi nthawi zina chimachititsa kuti anthu azitiimba milandu yoopsa. Akuluakulu aboma odana nafe angauze anthu kuti ndife “oukira boma” kapena “osokoneza.” Anthu odana nafe kwambiri anganene kuti ndife gulu lampatuko lovutitsa anthu ndipo tiyenera kuletsedwa. (Machitidwe 28:22) Nthawi zina mabodza ngati amenewa tingathe kuwathetsa. Tingatero motani? Tingatero potsatira malangizo a Petro akuti: “[Khalani] okonzeka nthawi zonse kuchita chodzikanira pa yense wakukufunsani chifukwa cha chiyembekezo chili mwa inu, komatu ndi chifatso ndi mantha.” (1 Petro 3:15) Komanso, tiyenera kunena “mawu olama osatsutsika; kuti iye wakutsutsana achite manyazi, posakhala nako kanthu koipa kakutinenera ife.”​—Tito 2:8.

Inde, ndibwino kuonetsetsa kuti dzina lathu silikuipitsidwa, komabe tisamalefuke kwambiri anthu akamatinenera zoipa. Yesu, yemwe anali mwana wangwiro wa Mulungu, ananenedwa kuti anali munthu wochitira Mulungu mwano, woukira boma, ndiponso wokhulupirira mizimu. (Mateyu 9:3; Marko 3:22; Yohane 19:12) Mtumwi Paulo nayenso ananyozedwapo. (1 Akorinto 4:13) Yesu ndiponso Paulo sanalimbane nazo zimenezi koma anangopitiriza kuchita ntchito yawo. (Mateyu 15:14) Iwowa ankadziwa kuti adani awo sangawakonde popeza kuti “dziko lonse lapansi ligona mwa woipayo.” (1 Yohane 5:19) Masiku ano timapezana ndi mavuto ngati omwewa. Tisamachite mantha anthu odana nafe akamatinamizira.​—Mateyu 5:11.

Maganizo Ofunikadi Kuwaganizira

Anthu amatiganizira zinthu zosiyanasiyana, malingana ndi zolinga zawo ndiponso zimene amva zokhudza ifeyo. Ena amatiyamikira ndi kutilemekeza, pamene ena amatinyoza ndi kutida. Komabe, tikamachita zinthu motsatira mfundo za m’Baibulo, palibe chifukwa choti tizikhalira osasangalala ndiponso osowa mtendere.

Mtumwi Paulo analemba kuti: “Lemba lililonse adaliuzira Mulungu, ndipo lipindulitsa pa chiphunzitso, chitsutsano, chikonzero, chilangizo cha m’chilungamo: kuti munthu wa Mulungu akhale woyenera, wokonzeka kuchita ntchito iliyonse yabwino.” (2 Timoteo 3:16, 17) Yehova Mulungu ndiponso Mwana wake Yesu Kristu amayamba kuyanjana nafe tikavomereza ndi mtima wonse kutsatira Mawu a Mulungu pa zochita zathu zonse. Ndipotu maganizo amene ali ofunika kwambiri ndi maganizo a Yehova ndi Mwana wake. Iwowa ndiwo amadziwadi kufunika kwathu. Ndipotu kuti tidzakhale ndi moyo wosatha, timafunika kusangalatsa iwowa.​—Yohane 5:27; Yakobo 1:12.

[Mawu Otsindika patsamba 30]

“Kutamandidwa kumandichititsa manyazi. Mumtimamu ndimakufuna, koma pamaso pa ena ndimakukana.” ANATERO RABINDRANATH TAGORE, WOLEMBA NDAKATULO WA KU INDIA

[Zithunzi patsamba 31]

Ndi bwino kuganizira mmene Akristu anzathu amationera

[Mawu a Chithunzi patsamba 30]

Culver Pictures