Pitani ku nkhani yake

Pitani ku mitu ya nkhani

Kodi Anali Mulungu Kapena Munthu?

Kodi Anali Mulungu Kapena Munthu?

 Kodi Anali Mulungu Kapena Munthu?

“INE ndine kuunika kwa dziko lapansi; iye wonditsata Ine sadzayenda mumdima, koma adzakhala nako kuunika kwa moyo.” (Yohane 8:12) Yesu Kristu ndiye ananena mawu amenewa. Munthu wina wophunzira wa m’zaka 100 zoyambirira analemba za Yesu kuti: “Zolemera zonse za nzeru ndi chidziwitso zibisika mwa Iye.” (Akolose 2:3) Kuphatikizanso apo, Baibulo limati: “Moyo wosatha ndi uwu, kuti akadziwe Inu Mulungu woona yekha, ndi Yesu Kristu amene munam’tuma.” (Yohane 17:3) Kuti tikhale osangalala mwauzimu timafunikira kudziwa zenizeni zokhudza Yesu.

Padziko lonse anthu ambiri anamvapo ndithu za Yesu Kristu. N’zosachita kufunsa kuti iye anakhudza kwabasi mbiri ya anthu. Ngakhale kawerengedwe ka madeti pa kalendala imene madera ambiri a padziko lonse amagwiritsira ntchito kamayambira pa chaka chimene akuti Yesu anabadwa. Buku la The World Book Encyclopedia limati: “Madeti a zinthu zimene zinachitika chaka chimenechi chisanakwane, anthu ambiri amawatchula kuti B.C., kapena kuti Kristu asanabadwe. Ndipo madeti a zinthu zimene zinachitika chaka chimenechi chitakwana amawatchula kuti A.D. kapena kuti m’chaka cha Ambuye wathu.”

Komabe, anthu sagwirizana chimodzi pa nkhani yakuti Yesu anali ndani makamaka. Kwa ena, iye anali munthu wotchuka basi, amene ndi wodziwika m’mbiri ya anthu. Koma ena amamulambira ngati Mulungu Wamphamvuyonse. Ahindu ena amayerekezera Yesu Kristu ndi mulungu wa Chihindu wotchedwa Krishna, amene ambiri amati ndi mulungu wovala thupi la munthu. Kodi Yesu anali munthu ngati wina aliyense, kapena kodi anali woyenera kumulambira? Kodi anali ndani makamaka? Anachokera kuti? Kodi anali wotani? Nanga panopo ali kuti? Monga tionere m’nkhani yotsatirayi, buku limene limanena zinthu zambiri zokhudza Yesu, lili ndi mayankho oona a mafunso amenewa.