Pitani ku nkhani yake

Pitani ku mitu ya nkhani

Mafunso Ochokera kwa Owerenga

Mafunso Ochokera kwa Owerenga

 Mafunso Ochokera kwa Owerenga

Kodi pali zifukwa zotani zonenera kuti mawu akuti “amene Iye yekha ali nawo moyo wosatha,” ndiponso akuti “amene munthu sanamuona, kapena sakhoza kumuona” akunena za Yesu osati za Yehova Mulungu?

Mtumwi Paulo analemba kuti: “Limene adzalionetsa m’nyengo za Iye yekha, amene ali Mwini Mphamvu wodala ndi wayekha, ndiye Mfumu ya mafumu ndi Mbuye wa ambuye; amene Iye yekha ali nawo moyo wosatha wakukhala m’kuunika kosakhozeka kufikako; amene munthu sanamuona, kapena sakhoza kumuona.”​—1 Timoteo 6:15, 16.

Othirira ndemanga pa Baibulo nthawi zambiri amati: ‘Kodi mawu akuti “amene Iye yekha ali nawo moyo wosatha,” “Mwini Mphamvu . . . wayekha,” ndi “amene munthu sanamuona, kapena sakhoza kumuona,” anganenenso za ndani kuposa Wamphamvuyonse?’ Zoonadi, tingatchule mawu amenewa kunena Yehova. Komabe, nkhani imene Paulo anali kufotokoza ikusonyeza kuti pa 1 Timoteo 6:15, 16 iye kwenikweni anali kunena za Yesu.

Kumapeto kwa vesi 14, Paulo anatchula za “maonekedwe a Ambuye wathu Yesu Kristu.” (1 Timoteo 6:14) Motero pamene Paulo ananena mu vesi 15 kuti “[“maonekedwe amenewa adzawaonetsa,” NW] m’nyengo za Iye yekha, amene ali Mwini Mphamvu wodala ndi wayekha, “ anali kunena za kuonekera kwa Yesu, osati kwa Yehova Mulungu. Ndiye, kodi “Mwini Mphamvu . . . wayekha,” kapena kuti Wamphamvu yekhayu, ndi ndani? N’zomveka kunena kuti Yesu ndiye Wamphamvu amene Paulo anali kunena. N’chifukwa chiyani tikutero? Nkhani imene anali kufotokozayi ikusonyeza kuti Paulo anali kuyerekeza Yesu ndi anthu olamulira. Monga mmene Paulo analembera, ndithudi Yesu ndi “Mfumu ya [anthu amene ali] mafumu ndi Mbuye wa [anthu amene ali] ambuye.” * Inde, poyerekeza ndi anthu amenewo, Yesu ndi ‘Wamphamvu yekhayo.’ Yesu wapatsidwa “ulamuliro, ndi ulemerero, ndi ufumu, kuti anthu onse, ndi mitundu yonse ya anthu, ndi a manenedwe onse, amutumikire.” (Danieli 7:14) Palibe munthu aliyense wamphamvu amene anganene kuti ali ndi mphamvu zoterozo.

Nanga bwanji za mawu akuti “amene Iye yekha ali nawo moyo wosatha [“wosakhoza kufa,” NW]”? Apanso akuyerekeza Yesu ndi anthu omwe ndi mafumu. Palibe wolamulira aliyense pa dziko lapansi amene anganene kuti anapatsidwa moyo wosakhoza kufa, komatu Yesu anapatsidwa moyo woterowo. Paulo analemba kuti: “Podziwa kuti Kristu anaukitsidwa kwa akufa, sadzafanso; imfa siichitanso ufumu pa Iye.” (Aroma 6:9) Motero Yesu ndiye woyamba kutchulidwa m’Baibulo kuti analandira mphatso ya moyo wosakhoza kufa. Ndithudi, panthawi imene Paulo analemba mawu amenewa, Yesu yekha ndi amene anali atapatsidwa moyo umene sungafe.

Tiyeneranso kukumbukira kuti sizikanakhala zoona kuti Paulo anene kuti Yehova Mulungu yekha ndiye anali ndi moyo wosakhoza kufa, chifukwa nayenso Yesu anali ndi moyo wosakhoza kufa panthawi imene Paulo analemba mawu amenewa. Koma Paulo anatha kunena kuti Yesu yekha ndiye anali ndi moyo wosakhoza kufa pomuyerekezera ndi olamulira a pa dziko lapansi.

Ndiponso, n’zoona kuti Yesu atauka kwa akufa n’kukwera kumwamba, tinganene kuti “munthu sanamuona, kapena sakhoza kumuona.” Inde, ophunzira ake odzozedwa adzamuona Yesu iwo akamwalira n’kuukitsidwa kukakhala kumwamba monga zolengedwa zauzimu. (Yohane 17:24) Koma palibe munthu pa dziko lapansi amene angaone Yesu ali mu ulemerero umene anapatsidwa. Motero, n’zoona kunena kuti palibe “munthu” amene anaonapo Yesu kuchokera pamene iye anauka kwa akufa n’kukwera kumwamba.

Inde, munthu akawerenga koyamba lemba la 1 Timoteo 6:15, 16 angaone ngati kuti zimene zikunenedwa m’mavesiwa, zikunena za Mulungu. Koma nkhani imene anali kufotokoza Paulo pamenepa, limodzinso ndi malemba ena ogwirizana ndi nkhaniyi, zikusonyeza kuti Paulo anali kunena za Yesu.

[Mawu a M’munsi]

^ ndime 5 Mawu ofanana ndi amenewa anagwiritsidwa ntchito ponena za Yesu pa 1 Akorinto 8:5, 6; Chivumbulutso 17:12, 14; 19:16.