Pitani ku nkhani yake

Pitani ku mitu ya nkhani

Kodi Kukhala Wokhulupirika Kuli ndi Phindu Lililonse?

Kodi Kukhala Wokhulupirika Kuli ndi Phindu Lililonse?

 Kodi Kukhala Wokhulupirika Kuli ndi Phindu Lililonse?

“UKULIPIRA ndalama zambiri zedi pa inshuwalansi ya zaumoyo,” anatero Karl, yemwe amagwira ntchito ku kampani ya mainshuwalansi. * “Utakhala ndi inshuwalansi imeneyi ku kampani yathu, ukhoza kumapulumutsa madola 20 mwezi uliwonse. Ndi ndalamatu zambiri zimenezi.”

“Zimenezo zikhoza kukhala zoona,” anatero Jens poyankha. “Koma inshuwalansi yangayi ndakhala nayo ku kampani imeneyi kwa zaka zambiri. M’mbuyomu anandithandiza kwambiri, ndipo ndikufuna kuti nawonso aone kukhulupirika kwanga.”

“Kukhulupirika ndi kwabwino, komatu ukuwononga nako ndalama zambiri,” anayankha choncho Karl.

Karl anali kunena zoona. Nthawi zambiri kukhala wokhulupirika kwa munthu wina kungalire ndalama zambiri. Kumafunanso kuti munthu atherepo nthawi yake, mphamvu zake, ndiponso kukhala ndi maganizo odzipereka. Kodi kukhala wokhulupirika kumayenereradi zonsezi?

Khalidwe Limene Ambiri Amati N’labwino Koma N’ngochepa Amene Ali Nalo

Pa kafukufuku amene anachitika ku Germany ndi bungwe lofufuza za maganizo a anthu la Allensbach Opinion Research Institute, anapeza kuti anthu 96 mwa anthu 100 alionse amene anafunsidwa, amaona kuti kukhulupirika ndi khalidwe labwino zedi. Kafukufuku wachiwiri amene bungweli linachita pakati pa achinyamata a zaka zoyambira pa 18 kufika pa 24, anasonyeza kuti achinyamata awiri mwa atatu alionse amene anafunsidwa amati kukhala wokhulupirika ndiko “kubwera bwino kumeneko,” kutanthauza kuti, amaliona kuti ndi khalidwe labwino.

Ngakhale kuti anthu ambiri amati kukhulupirika ndi khalidwe labwino, si ochuluka amene amakhaladi okhulupirika. Mwachitsanzo, m’mayiko ambiri a ku Ulaya, anthu okwatirana kapena anthu a m’banja limodzi nthawi zambiri sakhala okhulupirika kwenikweni kwa wina ndi mnzake. Nthawi zambiri mabwenzi amakhala osakhulupirika pa ubwenzi wawowo. Ndipo kukhulupirika kumene kalelo kunalipo pakati pa bwana ndi antchito ake kapena pakati pa amalonda ndi ogula malondawo sikukuonekanso tsopano. Kodi n’chifukwa chiyani?

Nthawi zina kutangwanidwa ndi zochitika pamoyo kumachititsa anthu kukhala ndi nthawi yochepa kapenanso kusakhala ndi mtima wofunitsitsa kupanga maubwenzi amene amafuna munthu kukhala wokhulupirika. Anthu amene anzawo anayamba awagwiritsapo fuwa la moto kapena kuwakhumudwitsa pa zochitika zinazake mwinamwake tsopano safuna kukhala okhulupirika kwa wina aliyense. Ena amakonda kukhala moyo woti izi achitako n’kusiya, kuyamba zina n’kuzisiyanso, moyo womwe sulira kuti munthu akhale wokhulupirika.

Kaya chifukwa chake n’chotani, mfundo ndi yakuti kukhulupirika ndi khalidwe limene anthu ambiri amati n’labwino koma n’ngochepa amene ali nalo. N’chifukwa chake pakubuka mafunso akuti: Kodi kukhala wokhulupirika kuli ndi phindu lililonse? Ngati n’kwaphindu, kodi tiyenera kukhala okhulupirika kwa ndani, nanga tingatero m’njira zotani? Kodi tingapindule chiyani pokhala okhulupirika?

[Mawu a M’munsi]

^ ndime 2 Mayina ena m’nkhani ino ndiponso yotsatira tawasintha.

[Mawu Otsindika patsamba 3]

Kukhulupirika ndi khalidwe limene anthu ambiri amati n’labwino koma n’ngochepa amene ali nalo