Pitani ku nkhani yake

Pitani ku mitu ya nkhani

Kodi Kukhumudwa Koyenera N’kotani?

Kodi Kukhumudwa Koyenera N’kotani?

 Kodi Kukhumudwa Koyenera N’kotani?

PA MLALIKI 7:9, Baibulo limati: “Mkwiyo ugona m’chifuwa cha zitsiru.” Vesi limeneli limasonyeza kuti tisamangokhumudwa ndi zilizonse zimene winawake watichitira; m’malo mwake tizikhululuka.

Komabe, kodi lemba la Mlaliki 7:9 limatanthauza kuti tisamakhumudwe n’china chilichonse kapena wina aliyense, ndiponso kuti tizingokhululuka basi ngakhale munthu atatilakwira motani ndiponso nthawi zambiri bwanji? Kodi pa zolankhula ndiponso zochita zathu tisamadere nkhawa n’kuyesetsa kusakhumudwitsa munthu popeza tikudziwa kuti iyeyo ayenera kutikhululukira basi? Ayi sichoncho.

Yehova Mulungu ndiye chimake cha chikondi, chifundo, kukhululukira, ndiponso kuleza mtima. Komabe, Baibulo limatchula nthawi zambiri kuti iye anakhumudwitsidwapo. Mlandu ukakhala waukulu, iye ankalanga anthu opalamulawo. Tiyeni tionepo zitsanzo zina.

Kulakwira Yehova

Nkhani ya pa 1 Mafumu 15:30 imanena za machimo a Yerobiamu amene ‘anachimwitsa nawo Aisrayeli, ndi kuutsa kwake kumene anaputa nako mkwiyo wa Yehova.’ Pa 2 Mbiri 28:25, Baibulo limanena za Mfumu Ahazi ya Yuda kuti: “Anamanga misanje ya kufukizira milungu ina, nautsa mkwiyo wa Yehova Mulungu wa makolo ake.” Chitsanzo china timachipeza pa lemba la Oweruza 2:11-14 lomwe limati: “Israyeli anachita choipa pamaso pa Yehova, natumikira Abaala. . . , nautsa mkwiyo wa Yehova. . . . Pamenepo mkwiyo wa Yehova unayakira Israyeli, ndipo anawapereka m’manja a ofunkha.”

Palinso zinthu zina zimene zinkakhumudwitsa Yehova ndipo zimenezo sankazilekelera ngakhale pang’ono. Mwachitsanzo, pa Eksodo 22:18-20, timawerenga kuti: “Wanyanga usam’lola akhale ndi moyo. Aliyense agona ndi choweta aphedwe ndithu. Wakuphera nsembe mulungu wina, wosati Yehova yekha, awonongeke konse.”

Yehova sanapitirize kukhululukira machimo akuluakulu a Aisrayeli akale iwowo akamapitiriza kumukhumudwitsa popanda kusonyeza kuti akulapadi zenizeni. Pamene anali kusonyeza kuti sanalape zenizeni komanso pamene zochita zawo sizinali kusonyeza kuti asiyadi zoipazo n’kuyamba kumvera Yehova, Mulungu ankawalanga polola kuti awonongedwe. Zimenezi zinachitikirapo mtundu wonsewo m’chaka cha 607 B.C.E., pamene unawongedwa ndi Ababulo, ndiponso mu 70 C.E., pamene unawonongedwa ndi Aroma.

Inde, Yehova amakhumudwa ndi zinthu zoipa zimene anthu amanena ndiponso kuchita. Iye amathanso kulanga anthu om’chimwira mosalapa amene achita machimo aakulu kwambiri. Koma kodi pamenepa ndiye kuti Yehova ali m’gulu la anthu otchulidwa pa Mlaliki 7:9? Ayi ndithu. Iye amakhumudwa pa zifukwa zabwino ngati munthu wachita tchimo lalikulu, ndipotu nthawi zonse Yehova amaona zinthu mwachilungamo. Baibulo limanena kuti Yehova “ntchito yake ndi yangwiro; pakuti njira zake zonse ndi chiweruzo; Mulungu wokhulupirika ndi wopanda chisalungamo; Iye ndiye wolungama ndi wolunjika.”​—Deuteronomo 32:4.

Kulakwira Anthu Anzathu pa Zinthu Zazikulu

M’Chilamulo chimene Mulungu anapatsa Aisrayeli akale, anthu ankalangidwa kwambiri akalakwira anzawo pa zinthu zazikulu.  Mwachitsanzo, mbava ikabwera m’nyumba usiku ndipo mwininyumbayo akaipha, iyeyo sankaimbidwa mlandu. Ankatengedwa kuti wavutitsidwa ndi mbavayo popanda kuilakwira chilichonse. N’chifukwa chake timawerenga m’Baibulo mawu akuti: “Akam’peza wakuba alim’kuboola, nakam’kantha kotero kuti wafa, palibe chamwazi [kwa mwininyumbayo].”​—Eksodo 22:2.

Mkazi amene wagwiriridwa ayenera kukhumudwa nazo kwambiri, chifukwa kwa Mulungu, umenewu ndi mlandu waukulu. M’Chilamulo cha Mose, mwamuna amene wagwirira mkazi anayenera kufa “pakuti mlandu uwu ukunga munthu waukira mnzake namupha.” (Deuteronomo 22:25, 26) Ngakhale kuti panopo sitiyendera Chilamulo, Chilamulochi chimatithandiza kuona mmene Yehova amaonera uchinyama wosaneneka wogwirira munthu.

M’nthawi yathu ino, mlandu wogwirira umatengedwa kuti ndi mlandu waukulu wokhala ndi chilango chachikulunso. Ndithu, munthu wogwiriridwayo ayenera kukanena nkhaniyi ku polisi. Potero, aboma angathe kupereka chilango kwa munthu wogwirira mnzakeyo. Ndipo ngati wogwiriridwayo ali mwana, makolo ake ayenera kuchita zimenezi.

Zolakwa Zing’onozing’ono

Komano, si zolakwa zonse zimene zimafunika kuti akulukulu achitepo kanthu. Motero, sitiyenera kukhumudwa kwambiri ndi zinthu zing’onozing’ono zimene ena amatilakwira, koma tizikhululuka. Kodi tiyenera kukhululuka kwa nthawi yochuluka motani? Mtumwi  Petro anafunsa Yesu kuti: “Ambuye, mbale wanga adzandilakwira kangati, ndipo ine ndidzam’khululukira iye? Kufikira kasanu ndi kawiri kodi?” Yesu anam’yankha kuti: “Sindinena kwa iwe kufikira kasanu ndi kawiri, koma kufikira makumi asanu ndi awiri kubwerezedwa kasanu ndi kawiri.”​—Mateyu 18:21, 22.

Ngakhale zili choncho, tonsefe timafunika kuyesetsa kukhala ndi umunthu wachikristu kuti tichepetse kukhumudwitsa ena. Mwachitsanzo, kodi nthawi zina mukamachita zinthu ndi ena simusamalako za mmene zingawakhudzire mumtima? Kodi mumachita zinthu mosaganizira, mwinanso mowapweteketsa mtima? Mukamachita zinthu m’njira yotere m’posavuta kukhumudwitsa ena. Wokhumudwitsa mnzakeyo ayenera kuzindikira kuti iyeyo ndiye wakhumudwitsa mnzake, ndipo asamaganize kuti wokhumudwayo ndiye walakwa chifukwa chokhumudwa ndi nkhaniyo, ndiponso kuti ndiye kwenikweni ayenera kukhululuka. Wokhumudwitsa mnzakeyo ayenera kuyesetsa kuganizira bwino zochita zake ndi zolankhula zake kuti asamakhumudwitse anzake. Kuyesetsa kutero kungachititse kuti tisamakhumudwitse anzathu kawirikawiri. Baibulo limatikumbutsa kuti: “Alipo wonena mwansontho ngati kupyoza kwa lupanga; koma lilime la anzeru lilamitsa.” (Miyambo 12:18) Tikakhumudwitsa anzathu, ngakhale ngati sitinachitire dala, kupepesa kumathandiza kwambiri kuthetsa vutolo.

Mawu a Mulungu amasonyeza kuti tiyenera ‘kulondola zinthu za mtendere, ndi zinthu zakulimbikitsana wina ndi mnzake.’ (Aroma 14:19) Tikamachita zinthu moganizira mmene ena akumvera ndiponso mokoma mtima, timakwaniritsa mwambi wa m’Baibulo wakuti: “Mawu oyenera a pa nthawi yake akunga zipatso zagolidi m’nsengwa zasiliva.” (Miyambo 25:11) Kuchita zimenezi kumatsitsimula kwambiri mitima ya anzathuwo. Kulankhula modekha, ndiponso mosamala kungathenso kusintha anthu okanika, osamva za ena, monga Baibulo limanenera kuti: “Lilime lofatsa lithyola fupa.”​—Miyambo 25:15.

Ndiye chifukwa chake, Mawu a Mulungu amatilangiza kuti: “Mawu anu akhale m’chisomo, okoleretsa, kuti mukadziwe inu mayankhidwe anu a kwa yense akatani.” (Akolose 4:6) Mawu akuti ‘kukoleretsa’ amatanthauza kuti mawu athu azikhala osangalatsa kwa ena. Tikatero, zizikhala zovuta kuti tikhumudwitse ena. Pa zonena ndi zochita zawo, Akristu amayesetsa kutsatira malangizo a m’Baibulo akuti: “Afunefune mtendere ndi kuulondola.”​—1 Petro 3:11.

Choncho, n’zoonekeratu kuti lemba la Mlaliki 7:9 limatanthauza kuti tiyenera kupewa kukhumudwa ndi zinthu zing’onozing’ono zimene ena akutilakwira. Zinthu zake ndi monga zinthu zimene iwo angachite chifukwa cha kupanda ungwiro, kapenanso zimene angachitire mwadala, komano zili zazing’ono. Koma tchimo likakhala lalikulu, m’pomveka ngati wolakwiridwayo wakhumudwa ndipo wachitapo kanthu.​—Mateyu 18:15-17.

[Chithunzi patsamba 14]

Yehova anawononga Aisrayeli osalapa pogwiritsira ntchito Aroma mu 70 C.E.

[Chithunzi patsamba 15]

“Mawu oyenera a pa nthawi yake akunga zipatso zagolidi”