Pitani ku nkhani yake

Pitani ku mitu ya nkhani

Mfundo Zazikulu za M’buku la Mafumu Woyamba

Mfundo Zazikulu za M’buku la Mafumu Woyamba

 Mawu a Yehova ndi Amoyo

Mfundo Zazikulu za M’buku la Mafumu Woyamba

“POCHULUKA olungama anthu akondwa; koma polamulira woipa anthu ausa moyo.” (Miyambo 29:2) Buku la m’Baibulo la Mafumu Woyamba likusonyeza bwino zedi kuti mwambi umenewu ndi woona. Likusimba mbiri ya moyo wa Solomo, amene mu ufumu wake mtundu wakale wa Israyeli unali wotetezeka ndiponso wolemera kwambiri. M’buku limeneli la Mafumu Woyamba mulinso nkhani ya kugawikana kwa mtunduwu pambuyo pa imfa ya Solomo, komanso nkhani ya mafumu 14 amene anabwera pambuyo pake, ena a iwo analamulira mu Israyeli ndipo ena mu Yuda. Awiri okha mwa mafumu amenewa ndi amene anakhulupirika kwa Yehova mpaka mapeto. Kuwonjezera pamenepo, bukuli likufotokozanso zochita za aneneri asanu ndi mmodzi kuphatikizapo Eliya.

Buku limeneli linalembedwa ndi mneneri Yeremiya ku Yerusalemu ndi ku Yuda, ndipo likufotokoza zochitika m’nyengo ya zaka 129, kuchokera mu 1040 B.C.E. kudzafika mu 911 B.C.E. Pamene anali kulemba buku limeneli, n’zachionekere kuti Yeremiya anagwiritsa ntchito mabuku ena akale monga ‘buku la machitidwe a Solomo.’ Mabuku amenewo osimba zochita za Solomo ndiponso mabuku ena akale sangapezekenso panopa.​—1 Mafumu 11:41; 14:19; 15:7.

MFUMU YA NZERU INALIMBIKITSA MTENDERE NDI CHITUKUKO

(1 Mafumu 1:1–11:43)

Buku la Mafumu Woyamba likuyamba ndi nkhani yochititsa chidwi ya Adoniya mwana mwa Mfumu Davide, pamene anayesa kulanda ufumu wa bambo ake. Mneneri Natani anachitapo kanthu mwamsanga ndi kulepheretsa chiwembucho, ndipo Solomo, mwana wa Davide analongedwa ufumu. Yehova anasangalala ndi pempho la mfumu yoikidwa kumeneyo ndipo anaipatsa “mtima wanzeru ndi wakuzindikira” komanso “chuma ndi ulemu.” (1 Mafumu 3:12, 13) Panalibe wina wa nzeru ngati mfumu imeneyi, ndipo chuma chake chinali chosayerekezeka. Imeneyi inali nthawi ya mtendere ndi chitukuko mu Israyeli.

Pa ntchito yake yomanga, mwa zina Solomo anamanga kachisi wa Yehova ndi nyumba zina za boma. Yehova anatsimikizira Solomo kuti: “Ine ndidzakhazikitsa chimpando cha ufumu wako pa Israyeli nthawi yosatha.” Izi zikanakhala choncho ngati mfumuyo ikanakhalabe yomvera. (1 Mafumu 9:4, 5) Mulungu woona anachenjezanso mfumuyo za zotsatirapo za kusamvera. Komabe, m’kupita kwa nthawi Solomo anakwatira akazi achilendo ambirimbiri. Mu ukalamba wake Solomo anakopedwa ndi akazi amenewa ndi kuyamba kulambira konyenga. Yehova ananeneratu kuti ufumu wa Solomo udzagawanika. Solomo anamwalira m’chaka cha 997 B.C.E, ndipo amenewo anali mapeto a ulamuliro wake wa zaka 40. Mwana wake Rehabiamu ndiye analowa ufumu wake.

Kuyankha Mafunso a M’Malemba:

1:5—N’chifukwa chiyani Adoniya anayesa kulanda ufumu Davide adakali moyo? Baibulo silinena chifukwa chake. Komabe, m’pomveka kunena kuti anachita zimenezi chifukwa chakuti Adoniya anaganiza kuti woyenera kulowa ufumuwo ndi iyeyo monga mwana wamkulu mwa ana onse a Davide omwe anali moyo. Panthawiyi n’kuti Amnoni ndi Abisalomu, omwe anali akulu ake a Adoniya atamwalira kale. N’kuthekanso kuti Kileabu, mwana wina wa Davide analinso atamwalira. (2 Samueli 3:2-4; 13:28, 29; 18:14-17) Mwinamwake, Adoniya anali wotsimikiza kuti chiwembu chakecho chiyenda bwino chifukwa anali kuthandizidwa ndi mkulu wa asilikali wamphamvu, Yoabu, komanso Abyatara, mkulu wa ansembe wotchuka. Baibulo silinena ngati anali kudziwa maganizo a Davide ofuna kupereka mpando wachifumuwo kwa Solomo. Komabe,  Adoniya sanaitane Solomo ndi ena amene anali okhulupirika kwa Davide kuti akakhale nawo pamene iye anali kupereka nsembe. (1 Mafumu 1:9, 10) Zimenezi zikusonyeza kuti iye anali kuona Solomo ngati mdani wake.

1:49-53; 2:13-25—N’chifukwa chiyani Solomo anapha Adoniya pambuyo pomukhululukira? Solomo anazindikira cholinga chenicheni cha pempho la Adoniya lakuti Batiseba akapemphe mfumu kuti ipereke Abisagi kwa Adoniya kuti akhale mkazi wake, ngakhale kuti Batiseba sanathe kuzindikira cholinga chimenecho. Ngakhale kuti Davide sanagone ndi Abisagi, mkazi wokongolayu, anali kuonedwabe monga mkazi wamng’ono wa Davide. Malinga ndi mwambo komanso malamulo a panthawiyo, munthu woyenera kulowa ufumu wa Davide yekha, ndi amene anali ndi ufulu wonse wotenga mkazi ameneyu. N’kutheka kuti Adoniya ankaganiza kuti akatenga Abisagi kukhala mkazi wake, zidzathekanso kulanda mpando wachifumuwo. Popeza kuti Solomo anazindikira kuti pempho la Adoniya linali chizindikiro chakuti akufuna ufumuwo, Solomo anasintha maganizo ndi kufafaniza kukhululuka kuja.

6:37–8:2—Kodi ndi liti pamene anatsegulira kachisi? Kachisi anamalizidwa m’mwezi wa chisanu ndi chitatu m’chaka cha 1027 B.C.E., chaka cha khumi ndi chimodzi cha ulamuliro wa Solomo. Zikuoneka kuti zinatenga miyezi khumi ndi umodzi kuti abweretse zipangizo zina ndi kukonzekera zina ndi zina. Kutsegulira kachisiyu kuyenera kuti kunachitika m’mwezi wa chisanu ndi chiwiri m’chaka cha 1026 B.C.E. Nkhaniyi ikufotokoza ntchito zina zomanga zimene zinachitika kachisi atamalizidwa, koma asanatchule za kutsegulira kwake. Mwachionekere, anatchula ntchito zimenezi pofuna kufotokoza mowonjezeka ntchito zina zomanga zimene zinali kuchitika panthawiyo.​—2 Mbiri 5:1-3.

9:10-13—Kodi zimene Solomo anachita popereka midzi 20 ya m’dziko la Galileya monga mphatso kwa mfumu Hiramu ya Turo zinali zogwirizana ndi Chilamulo cha Mose? Mwinamwake, ankaona kuti Chilamulo chopezeka pa lemba la Levitiko 25:23, 24 chinali kugwira ntchito pa madera okhawo amene Aisrayeli anali kukhalamo. N’kutheka kuti midzi imene Solomo anapereka kwa Hiramu munali kukhala anthu omwe sanali Aisrayeli, ngakhale kuti inali m’kati mwa Dziko Lolonjezedwa. (Eksodo 23:31) N’kuthekanso kuti zimene Solomo anachita unali umboni wa kulephera kwake kutsatira bwinobwino Chilamulo, monga momwe anachitira pamene ‘anadzichulukitsira akavalo’ ndi kutenga akazi ambiri. (Deuteronomo 17:16, 17) Mulimonse mmene zinalili, Hiramu sanakhutire ndi mphatsoyo. Mwinamwake midzi imeneyi sinali kusamalidwa bwino ndi anthu achikunja amene anali kukhalamo, kapena mwina sinali pa malo abwino.

11:4—Kodi Solomo anakhala wosakhulupirika chifukwa chokalamba kwambiri? Zikuoneka kuti chifukwa chake sichinali chimenechi. Solomo anayamba kulamulira ali wamng’ono ndithu, ndipo ngakhale kuti analamulira zaka 40, sikuti anali atakalamba modetsa nkhawa. Komanso, sikuti anasiyiratu kulambira Yehova. Zikuoneka kuti anali kuphatikiza zikhulupiriro zosiyana.

 Zimene Tikuphunzirapo:

2:26, 27, 35. Zimene Yehova wanena nthawi zonse zimachitika. Kuchotsedwa kwa Abyatara, mbadwa ya Eli, kunakwaniritsa “mawu a Yehova amene aja adalankhula . . . za mbumba ya Eli.” Kuchotsa Abyatara ndi kuika Zadoki wa mzera wa Pinehasi kunakwaniritsa lemba la Numeri 25:10-13.​—Eksodo 6:25; 1 Samueli 2:31; 3:12; 1 Mbiri 24:3.

2:37, 41-46. N’zoopsa kwabasi kuganiza kuti munthu angaswe malamulo a Mulungu koma osalandira chilango. Amene amapatuka mwadala pa njira ‘yochepetsa yakumuka nayo kumoyo’ adzakumana ndi zotsatira za chosankha chawo chopanda nzerucho.​—Mateyu 7:14.

3:9, 12-14. Yehova amayankha mapemphero ochokera pansi pa mtima a atumiki ake opempha nzeru, kuzindikira, ndi chitsogozo pamene akum’tumikira.​—Yakobo 1:5.

8:22-53. Apatu Solomo anayamikira Yehova kuchokera pansi pa mtima. Iye alidi Mulungu wokoma mtima mwachikondi, Wokwaniritsa malonjezo, ndiponso Wakumva mapemphero. Kusinkhasinkha mawu a m’pemphero la Solomo lotsegulira kachisi kudzatithandiza kuwonjezera kuyamikira kwathu mbali zimenezi ndi zinanso za umunthu wa Mulungu.

11:9-14, 23, 26. Solomo atakhala wosakhulupirika kumapeto kwa moyo wake, Yehova anautsa adani. Mtumwi Petro anati: “Mulungu akaniza odzikuza, koma apatsa chisomo kwa odzichepetsa.”​—1 Petro 5:5.

11:30-40. Mfumu Solomo anafuna kupha Yerobiamu chifukwa cha zimene Ahiya analosera zokhudza Yerobiamu. Pamenepatu Mfumuyi inachita zosiyana kwambiri ndi zimene inachita zaka 40 zapitazo, pamene inakana kubwezera Adoniya ndi ena omwe anam’konzera chiwembu. (1Mafumu 1:50-53) Mtima wake unasintha chomwechi chifukwa chakuti anam’siya Yehova.

UFUMU WOGWIRIZANA UNAGAWANIKA

(1 Mafumu 12:1–22:53)

Yerobiamu ndi anthu ena anabwera kwa mfumu Rehabiamu kudzapempha kuti apeputseko mtolo umene bambo wake Solomo anasenzetsa anthuwo. M’malo mochita zofuna za anthuwo, Rehabiamu anawopseza kuti awawonjezera mtolo winanso wolemera koposa. Zitatero, mafuko khumi anapanduka ndi kusankha Yerobiamu kukhala mfumu yawo. Pamenepo ufumu unagawanika. Rehabiamu anali kulamulira ufumu wa kummwera wa fuko la Yuda ndi Benjamini, ndipo Yerobiamu anayamba kulamulira kumpoto mu ufumu wa Israyeli wa mafuko khumi.

Pofuna kuletsa anthu kuti asamapite ku Yerusalemu kukapembedza, Yerobiamu anaika ana ang’ombe awiri agolide, mmodzi ku Dani ndipo wina ku Beteli. Ena mwa mafumu amene analamulira Israyeli Yerobiamu atamwalira anali Nadabu, Basa, Ela, Zimiri, Tibini, Omri, Ahabu ndi Ahaziya. Ndipo amene analamulira Yuda pambuyo pa Rehabiamu ndi Abiya, Asa, Yehosafati ndi Yehoramu. Aneneri omwe anali kunenera m’masiku a mafumu amenewa ndi Ahiya, Semaya, ndi munthu wa Mulungu amene sanatchulidwe dzina, komanso Yehu, Eliya, ndi Mikaya.

Kuyankha Mafunso a M’Malemba:

18:21—N’chifukwa chiyani anthu anangokhala chete Eliya atawapempha kuti asankhe kutsatira Yehova kapena Baala? Mwina anazindikira kulephera kwawo kulambira Yehova yekha monga mmene Mulunguyo amafunira, choncho anali kudziimba mlandu. Kapena chikumbumtima  chawo chinali chakufa mwakuti sanaone cholakwika chilichonse ndi kulambira Baala ndipo panthawi imodzimodziyo m’kumanena kuti amalambira Yehova. Koma Yehova atasonyeza mphamvu zake, m’pamene iwo ananena kuti: “Yehova ndiye Mulungu, Yehova ndiye Mulungu.”​—1 Mafumu 18:39.

20:34—Yehova atathandiza Ahabu kugonjetsa Aaramu, n’chifukwa chiyani Ahabu sanaphe Benihadadi mfumu yawo? M’malo mwa kupha Benihadadi, Ahabu anapangana naye pangano lakuti misewu ya ku Damasiko, mzinda waukulu wa Aramu, aipereke kwa Ahabu, mwachionekere kuti amangemo nyumba zikuluzikulu za malonda, kapena misika. Nthawi inayake mmbuyomo, bambo ake a Benihadadi anadzitengera okha misewu ku Samariya kuti azichitamo malonda. Chotero, Benihadadi anamasulidwa kuti Ahabu athe kumachita malonda ku Damasiko.

Zimene Tikuphunzirapo:

12:13, 14. Posankha zochita pankhani yaikulu m’moyo, tiyenera kufunsira malangizo kwa anthu anzeru ndi okhwima omwe amadziwa bwino Malemba ndipo amalemekeza kwambiri mfundo za Mulungu za makhalidwe abwino.

13:11-24. Malangizo kapena malingaliro omwe akuoneka kuti ndi okayikitsa, ngakhale ochokera kwa wokhulupirira mnzathu woona mtima, tiyenera kuwayerekezera ndi malangizo anzeru opezeka m’Mawu a Mulungu.​—1 Yohane 4:1.

14:13. Yehova amatifufuza kuti aone mbali zabwino mwa ife. Ngakhale mbali yabwinoyo itakhala yaing’ono chotani, amaikulitsa tikamayesetsa kumutumikira.

15:10-13. Tiyenera kukana mpatuko molimba mtima ndipo m’malo mwake tilimbikitse kupembedza koona.

17:10-16. Mkazi wamasiye wa ku Zarefati anazindikira kuti Eliya ndi mneneri ndipo anam’chereza monga mneneri, chotero Yehova anadalitsa ntchito zake za chikhulupiriro. Masiku anonso, Yehova amaona ntchito zathu za chikhulupiriro, ndipo amapereka mphoto kwa onse amene akuchirikiza ntchito ya Ufumu m’njira zosiyanasiyana.​—Mateyu 6:33; 10:41, 42; Ahebri 6:10.

19:1-8. Pamene tikutsutsidwa mwamphamvu, tiyenera kukhala ndi chidaliro kuti Yehova adzatithandiza.​—2 Akorinto 4:7-9.

19:10, 14, 18. Opembedza oona sali okha. Yehova ali nawo komanso ali mu ubale wa padziko lonse.

19:11-13. Yehova si Mulungu amene tingamuyerekezere ndi mphamvu iliyonse ya chilengedwe ayi.

20:11. Pamene Benihadadi anadzitukumula kuti adzawononga Samariya, mfumu ya Israyeli inayankha kuti: ‘Wakumanga zida [pokonzekera nkhondo] asadzikuze ngati wovula’ zida zake atapambana kunkhondo. Ngati tapatsidwa ntchito yatsopano, tiyenera kupewa kudzidalira mopambanitsa monga mmene amachitira munthu wodzitukumula.​—Miyambo 27:1; Yakobo 4:13-16.

Ndi Lopindulitsa Kwambiri kwa Ife

Atafotokoza za kuperekedwa kwa Chilamulo pa phiri la Sinai, Mose anauza ana a Israyeli kuti: “Taonani, ndili kuika pamaso panu lero dalitso ndi temberero; dalitso, ngati mudzamvera malamulo a Yehova Mulungu wanu amene ndikuuzani lerolino; koma temberero, ngati simudzamvera malamulo a Yehova Mulungu wanu, ndi kupatuka m’njira ndikuuzani lerolino.”​—Deuteronomo 11:26-28.

Mfundo yofunika imeneyi yaonekeradi bwino kwambiri m’buku la Mafumu Woyamba. Monga momwe taonera, buku limeneli likutiphunzitsanso mfundo zina zofunika kwambiri. Uthenga wake ulidi wamoyo ndi wamphamvu.​—Ahebri 4:12.

[Chithunzi patsamba 29]

Kachisi ndi nyumba zina zomwe Solomo anamanga

[Chithunzi pamasamba 30, 31]

Yehova atasonyeza mphamvu zake, anthu anafuula kuti: “Yehova ndiye Mulungu”