Pitani ku nkhani yake

Pitani ku mitu ya nkhani

“Achimwemwe Ali Awo Ozindikira Kusowa Kwawo Kwauzimu”

“Achimwemwe Ali Awo Ozindikira Kusowa Kwawo Kwauzimu”

 “Achimwemwe Ali Awo Ozindikira Kusowa Kwawo Kwauzimu”

MBALAME zikadzuka m’mawa, kawirikawiri zimalira kwa kanthawi ndipo kenako zimauluka kupita kukafunafuna chakudya. Madzulo zimabwerera kuzisa zawo, ndipo zikafika zimaliranso, kenako zimagona. Panyengo zina zimaikira mazira ndi kuswa ana. Mofanana ndi mbalame zimenezi, nyama zinanso zimachita zinthu zina zodziwikiratu.

Koma sizili choncho kwa anthufe. N’zoona kuti timadya, kugona, ndi kubereka ana, koma ambiri a ife sitikhutira ndi zinthu zokhazi basi. Timafuna kudziwa chifukwa chake tili ndi moyo. Timafufuza cholinga cha moyo wathu. Timafunanso kukhala ndi chiyembekezo cha m’tsogolo. Zofunika zazikulu zimenezi zikusonyeza kuti pali khalidwe lapadera lopezeka mwa anthu okha. Khalidwe limeneli ndilo kukonda zinthu zauzimu, kapena kuti timafunikira zinthu zauzimu ndipo tingathe kuziphunzira.

Tinapangidwa M’chifanizo cha Mulungu

Baibulo limafotokoza chifukwa chake anthu mwachibadwa amafunika zinthu zauzimu, limati: “Mulungu ndipo adalenga munthu m’chifanizo chake, m’chifanizo cha Mulungu adam’lenga iye; adalenga iwo mwamuna ndi mkazi.” (Genesis 1:27) Popeza tinapangidwa “m’chifanizo cha Mulungu,” zikutanthauza kuti tingathe kuonetsa makhalidwe ena a Mulungu, ngakhale kuti ndife ochimwa komanso opanda ungwiro. (Aroma 5:12) Mwachitsanzo, tili ndi luso lopanga zinthu. Tilinso ndi nzeru, timafuna chilungamo, ndipo timatha kusonyezana chikondi chodzimana. Kuwonjezera pamenepo, timatha kukumbukira zomwe zinachitika m’mbuyo ndi kukonza tsogolo.​—Miyambo 4:7; Mlaliki 3:1, 11; Mika 6:8; Yohane 13:34; 1 Yohane 4:8.

Chilakolako chathu chachibadwa chofuna kupembedza Mulungu, ndi umboni woonekeratu wakuti timafunikira kukhutiritsa uzimu wathu. Sitingapeze chimwemwe chenicheni ndiponso chosatha pokhapokha ngati tili pa ubwenzi wolimba ndi Mlengi wathu. Yesu anati: “Achimwemwe ali awo  ozindikira kusowa kwawo kwauzimu.” (Mateyu 5:3, NW) Komano, tifunika kusamala kuti tikwaniritse kusowa kwa uzimu kumeneku mwa kuphunzira choonadi, kapena kuti zoona zenizeni ponena za Mulungu, miyezo yake, ndi chifuno chake kwa anthu. Kodi choonadi chimenechi tingachipeze kuti? Tingachipeze m’Baibulo.

“Mawu Anu Ndi Choonadi”

Mtumwi Paulo analemba kuti: “Lemba lililonse adaliuzira Mulungu, ndipo lipindulitsa pa chiphunzitso, chitsutsano, chikonzero.” (2 Timoteo 3:16) Mawu a Paulo amenewa akugwirizana ndi zimene Yesu ananena popemphera kwa Mulungu kuti: “Mawu anu ndi choonadi.” Masiku ano, tikudziwa kuti Mawu amenewo ndi Baibulo Lopatulika, ndipo n’chinthu chanzeru kupenda ngati zikhulupiriro ndi miyezo yathu ya makhalidwe ikugwirizana ndi miyezo ya m’Baibulo.​—Yohane 17:17.

Tikamayerekezera zikhulupiriro zathu ndi Mawu a Mulungu, ndiye kuti tikutsanzira anthu a ku Bereya wakale, omwe anafuna kutsimikizira ngati ziphunzitso za Paulo zinali kugwirizanadi ndi Malemba. M’malo modzudzula Abereyawo, Luka anawayamikira chifukwa cha maganizo awowo. Iye analemba kuti, iwo “analandira mawu ndi kufunitsa kwa mtima wonse, nasanthula m’malembo masiku onse, ngati zinthu zinali zotero.” (Machitidwe 17:11) Poona kuchuluka kwa ziphunzitso zotsutsana za zipembedzo ndi za makhalidwe masiku ano, m’pofunika kutsanzira chitsanzo cha Abereya okonda kufufuza malembawo.

Njira ina yodziwira choonadi ndiyo kuona mmene choonadicho chikukhudzira miyoyo ya anthu. (Mateyu 7:17) Mwachitsanzo, kutsatira choonadi cha m’Baibulo m’banja kumachititsa munthu kukhala mwamuna wabwino, tate wabwino, mkazi wabwino, kapena mayi wabwino. Ndipo munthu wotere amalimbikitsa chimwemwe m’mbanjamo ndipo zimam’thandiza kukhala wokhutira. Yesu anati: “Odala [“achimwemwe,” NW] iwo akumva mawu a Mulungu, nawasunga.”​—Luka 11:28.

Mawu a Yesu amenewa akutikumbutsa mawu a Atate wake wakumwamba, omwe polankhula ndi Aisrayeli akale, anati: “Ine ndine Yehova, Mulungu wako, amene ndikuphunzitsa kupindula, amene ndikutsogolera m’njira yoyenera iwe kupitamo. Mwenzi utamvera malamulo anga mtendere wako ukanakhala ngati mtsinje, ndi chilungamo chako monga mafunde a nyanja.” (Yesaya 48:17, 18) Onse okonda zabwino ndiponso chilungamo mosakayikira adzachitapo kanthu pomvera pempho lachikondi limeneli.

Ena Amasankha ‘Kuyabwidwa M’khutu’

Mulungu anapereka pempho limeneli kwa Aisrayeli kuchokera pansi pa mtima chifukwa chakuti anali kusocheretsedwa ndi mabodza a zipembedzo. (Salmo 106:35-40) Nafenso tiyenera kusamala kuti wina asatinamize. Ponena za anthu odzitcha Akristu, Paulo analemba kuti: “Idzafika nthawi imene sadzalola chiphunzitso cholamitsa; komatu poyabwa m’khutu adzadziunjikitsa aphunzitsi monga mwa zilakolako za iwo okha: ndipo adzalubza dala pachoonadi.”​—2 Timoteo 4:3, 4.

Atsogoleri azipembedzo amayabwa anthu m’khutu mwa kulekerera makhalidwe okhutiritsa zilakolako zoipa, monga kugonana kwa anthu osakwatirana, kugonana kwa amuna kapena akazi okhaokha, ndi kuledzera. Baibulo limanena mosapita m’mbali kuti omwe amalekerera komanso omwe amachita makhalidwe amenewa “sadzalowa Ufumu wa Mulungu.”​—1 Akorinto 6:9, 10; Aroma 1:24-32.

 Kunena zoona, pamafunika kulimba mtima kuti munthu azichita zinthu mogwirizana ndi miyezo ya m’Baibulo, makamaka ngati akunyozedwa, komabe munthu angakwanitse ndithu. Pakati pa Mboni za Yehova pali anthu ambiri omwe kale anali okonda mankhwala osokoneza bongo, zidakwa, achiwerewere, zigandanga, mbava ndi onena mabodza. Komatu, analabadira Mawu a Mulungu ndipo ndi thandizo la mzimu woyera anasintha moyo wawo kuti athe ‘kuyenda moyenera Ambuye.’ (Akolose 1:9, 10; 1 Akorinto 6:11) Mwa kupanga mtendere ndi Mulungu, anapeza mtendere wa mumtima, ndipo monga momwe tionere, anapeza chiyembekezo chenicheni cha m’tsogolo.

Chiyembekezo cha Ufumu

Ufumu wa Mulungu udzakwaniritsa chiyembekezo cha m’Baibulo cha mtendere wosatha kwa anthu omvera. M’pemphero lake lachitsanzo, Yesu anati: “Ufumu wanu udze. Kufuna kwanu kuchitidwe, monga Kumwamba chomwecho pansi pano.” (Mateyu 6:10) Inde, ndi Ufumu wa Mulungu wokha umene udzatsimikizira kuti chifuniro cha Mulungu chachitikadi pa dziko lapansi. Chifukwa chiyani? Chifukwa chakuti Mulungu adzagwiritsa ntchito Ufumu wa kumwamba umenewo, womwe ndi boma limene wolamulira wake ndi Yesu Kristu, posonyeza kuti Mulungu ndiye woyeneradi kulamulira dziko lonse lapansi.​—Salmo 2:7-12; Danieli 7:13, 14.

Monga Mfumu ya Ufumu wa kumwamba, Yesu Kristu adzamasula anthu ku nsinga za mtundu uliwonse, kuphatikizapo uchimo wa Adamu womwe wagwira anthu mwamphamvu, komanso zotsatira zake monga matenda ndi imfa. Lemba la Chivumbulutso 21:3, 4 limati: “Taonani, chihema cha Mulungu chili mwa anthu . . . ndipo [Yehova Mulungu] adzawapukutira misozi yonse kuichotsa pamaso pawo; ndipo sipadzakhalanso imfa; ndipo sipadzakhalanso maliro, kapena kulira, kapena chowawitsa; zoyambazo zapita.”

Mtendere wosatha udzadzaza dziko lonse lapansi. N’chifukwa chiyani tingatsimikize zimenezo? Chifukwa chake chavumbulidwa pa lemba la Yesaya 11:9, limene limati: “[Nzika za Ufumuwo] sizidzaipitsa, sizidzasakaza m’phiri langa lonse loyera, chifukwa kuti dziko lapansi lidzadzala ndi odziwa Yehova, monga madzi adzaza nyanja.” Inde, munthu aliyense padziko lapansi adzam’dziwa bwino Mulungu ndi kumumvera. Kodi chiyembekezo chimenechi chakuchititsani chidwi? Ngati ndi  choncho, ndiyetu nthawi yabwino ndi yomwe ino yoyamba kuphunzira kuti ‘mum’dziwe Yehova,’ chifukwa kum’dziwa Yehova ndi chinthu cha mtengo wapatali.

Kodi Mungamvetsere Uthenga wa Ufumu?

Pogwiritsa ntchito Ufumu umenewu, Mulungu adzafafaniza ntchito zonse za Satana ndi kuphunzitsa anthu njira Zake zolungama. Chotero n’zosadabwitsa kuti Ufumu ndiwo unali nkhani yaikulu ya ziphunzitso za Yesu. Iye anati: “Kundiyenera Ine ndilalikire Uthenga Wabwino wa Ufumu wa Mulungu . . . chifukwa ndinatumidwa kudzatero.” (Luka 4:43) Kristu analamula ophunzira ake kuti aziuzako ena uthenga wabwinowo. (Mateyu 28:19, 20) Iye ananeneratu kuti: “Uthenga uwu wabwino wa Ufumu udzalalikidwa padziko lonse lapansi, ukhale mboni kwa anthu a mitundu yonse; ndipo pomwepo chidzafika chimaliziro.” (Mateyu 24:14) Chimaliziro chimenecho chikuyandikira mofulumira. Chotero m’pofunikatu kwambiri kuti anthu oona mtima amve uthenga wabwino wopulumutsa moyo.

Albert, amene tinam’tchula m’nkhani yoyamba ija, anamva uthenga wa Ufumu pamene mkazi wake ndi mwana wawo wamwamuna anayamba kuphunzira Baibulo ndi Mboni za Yehova. Poyamba, Albert ankakaikakaika. Mwakuti anapempha mtsogoleri wachipembedzo wa komweko kuti akacheze ndi mkazi ndi mwana wakeyo kuti akatsutse ziphunzitso za Mbonizo. Koma mtsogoleri wachipembedzoyo sanafune kulowerera nkhani imeneyo. Choncho Albert anangoganiza zomamvetsera nawo makambirano a m’Baibulowo kuti azitola zifukwa m’ziphunzitso za Mboni. Atangomvetsera nawo mutu umodzi wokha, nayenso anayamba kutenga nawo mbali, ndi mtima wofunitsitsa kuphunzira. Patapita nthawi anafotokoza chifukwa chake anasintha maganizo. Iye anati: “Ndinapeza chimene ndinali kufunafuna kwa nthawi yaitali.”

Apa m’pamene Albert anayambira kukhutiritsa kusowa kwake kwauzimu, ndipo sakunong’oneza bondo. Choonadi cha m’Baibulo chinam’patsa chimene wakhala akufufuza moyo wake wonse. Anadziwa njira yothetsera kupanda chilungamo ndi katangale zomwe zafala kwambiri pakati pa anthu, komanso anapeza chiyembekezo cha m’tsogolo. Choonadi cha m’Baibulo chinam’thandiza kukhala ndi mtendere mumtima. Kodi mukukhutiritsa kusowa kwanu kwauzimu? Werengani mofatsa mafunso omwe ali m’bokosi pa tsamba 6. Ngati mukufuna kumva zambiri, Mboni za Yehova n’zokonzeka kukuthandizani.

[Bokosi/​Zithunzi patsamba 6]

KODI MUKUKHUTIRITSA KUSOWA KWANU KWAUZIMU?

Kodi mukukhutira ndi chakudya chauzimu chimene mukulandira? Tikukupemphani kuwerenga mafunso otsatirawa ndi kuona kuti ndi angati omwe mungayankhe molondola.

□ Kodi Mulungu ndani, nanga dzina lake ndani?

□ Kodi Yesu Kristu ndani? N’chifukwa chiyani anayenera kufa? Kodi imfa yakeyo mungapindule nayo motani?

□ Kodi Mdyerekezi alipodi? Ngati alipo, kodi anachokera kuti?

□ Kodi chimachitika n’chiyani kwa munthu akamwalira?

□ Kodi Mulungu ali ndi cholinga chotani ndi dziko lapansi ndiponso anthu?

□ Kodi Ufumu wa Mulungu n’chiyani?

□ Kodi miyezo ya Mulungu ya makhalidwe abwino ndi iti?

□ Kodi Mulungu anapereka maudindo ati kwa mwamuna, ndiponso kwa mkazi m’banja? Kodi zina mwa mfundo za m’Baibulo zomwe zimawonjezera chimwemwe m’banja ndi ziti?

Ngati yankho la funso linalake mwa mafunso amenewa simukulidziwa kwenikweni, itanitsani kabuku kakuti Kodi Mulungu Amafunanji kwa Ife? Kabuku kameneka, komwe kakufalitsidwa ndi Mboni za Yehova m’zinenero pafupifupi 300, kali ndi mitu 16 ya nkhani zikuluzikulu za m’Baibulo, ndipo kali ndi mayankho a m’Malemba a mafunso onse amene ali pamwambawa.

[Zithunzi patsamba 4]

Mosiyana ndi nyama, anthu ali ndi kusowa kwauzimu

[Chithunzi patsamba 5]

“Poyabwa m’khutu adzadziunjikitsa aphunzitsi.”​—2 Timoteo 4:3

[Chithunzi patsamba 7]

Ufumu wa Mulungu wa Umesiya ndi umene udzadzetsa mtendere wosatha