Pitani ku nkhani yake

Pitani ku mitu ya nkhani

Tidzapulumuka mwa Chisomo Osati mwa Ntchito Zokha

Tidzapulumuka mwa Chisomo Osati mwa Ntchito Zokha

 Tidzapulumuka mwa Chisomo Osati mwa Ntchito Zokha

“Muli opulumutsidwa . . . mwa chikhulupiriro, . . . chosachokera kuntchito, kuti asadzitamandire munthu aliyense.”​—AEFESO 2:8, 9.

1. Kodi Akristu amasiyana bwanji ndi anthu ena onse pankhani ya zochita zawo zoyamikika, ndipo n’chifukwa chiyani?

ANTHU masiku ano amanyada nazo kwambiri zinthu zoyamikika zimene achita, ndipo amakonda kudzichemerera nazo. Akristu satero ayi. Amapewa kudzichemerera pa zochita zawo zoyamikika, ngakhale zitakhala zokhudza kupembedza koona. Ngakhale kuti amasangalala ndi zinthu zimene gulu lonse la anthu a Yehova likuchita, Mkristu sadzichemerera pa zochita zake. Amadziwa kuti potumikira Yehova, kukhala n’zolinga zabwino n’kofunika koposa zochita zake. Aliyense amene adzapatsidwe mphatso ya moyo wosatha sadzapatsidwa mphatsoyi, chifukwa cha zinthu zoyamikika zimene iyeyo wachita, koma chifukwa cha chikhulupiriro chake ndiponso chisomo cha Mulungu.​—Luka 17:10; Yohane 3:16.

2, 3. Kodi Paulo anadzitamandira n’chiyani, ndipo n’chifukwa chiyani anatero?

2 Mtumwi Paulo ankadziwa bwino mfundo imeneyi. Atapemphera katatu kuti am’chotsere “munga m’thupi,” Yehova anamuyankha kuti: “Chisomo changa chikukwanira; pakuti mphamvu yanga ithedwa m’ufoko.” Pomvera yankho  la Yehovali modzichepetsa, Paulo anati: “Ndidzadzitamandira mokondweratu m’maufoko anga, kuti mphamvu ya Kristu ikhale pa ine.” Mtima wa Paulo wodzichepetsawu ndi umene tiyenera kuutsanzira.​—2 Akorinto 12:7-9.

3 Ngakhale kuti Paulo anachita ntchito zachikristu zoyamikika zedi, iye ankadziwa kuti sanakwanitse kuchita zonsezi chifukwa cha luso lake. Modzichepetsa iye anati: “Kwa ine wochepa ndi wochepetsa wa onse oyera mtima anandipatsa chisomo ichi ndilalikire kwa amitundu chuma chosalondoleka cha Kristu.” (Aefeso 3:8) Mawu a Paulowa si odzitamandira ayi komanso sakusonyeza mtima wodziona ngati wolungama kuposa ena. “Mulungu akaniza odzikuza, koma apatsa chisomo odzichepetsa.” (Yakobo 4:6; 1 Petro 5:5) Kodi timatsatira chitsanzo cha Paulo, pokhala odzichepetsa n’kumadziona kuti ndife otsika kuposa mbale kapena mlongo wapansi kwambiri?

“Yense Ayese Anzake Om’posa Iye Mwini”

4. Kodi n’chifukwa chiyani nthawi zina zingativute kuona kuti anzathu n’ngotiposa?

4 Mtumwi Paulo analangiza Akristu kuti: “Musachite kanthu monga mwa chotetana, kapena monga mwa ulemerero wopanda pake, komatu ndi kudzichepetsa mtima, yense ayese anzake om’posa iye mwini.” (Afilipi 2:3) Kuchita zimenezi kungativute, makamaka ngati tili ndi udindo. Mwina chinanso chimene chingabweretse vutoli n’chakuti maganizo athu anasokonezeka ndi mzimu wampikisano umene wafala kwambiri masiku anowu. N’kutheka kuti tili ana, tinaphunzitsidwa kupikisana ndi azing’ono athu kapena azikulu athu kunyumba kapenanso anthu a m’kalasi mwathu kusukulu. Mwina nthawi zonse tinkalimbikitsidwa kuti tiziyesetsa kukhala mwana woposa ana ena onse pa zamasewera kapena mwana wanzeru kwambiri pasukulupo. Inde, kuyesetsa kuchita khama pa zinthu zilizonse zoyenera, n’chinthu chabwino. Komabe, Akristu amatero, osati chifukwa chofuna kuti anthu awatame, koma kuti apindule kwambiri ndi zimene akuchitazo kapenanso kuti athandize anthu ena. Komano mtima womafuna kuti nthawi zonse muzitamidwa kuti ndinu woposa aliyense n’ngoopsa. Kodi n’ngoopsa m’njira yotani?

5. Kodi munthu atapanda kusamala, mzimu wokonda mpikisano ungam’fikitse potani?

5 Munthu atapanda kusamala, mzimu wampikisano kapena wodzikuza ungam’chititse kukhala wopanda ulemu ndiponso wosamva za ena. Munthuyo angathe kumachita nsanje akaona ena ali ndi luso linalake kapenanso mwayi winawake. Lemba la Miyambo 28:22 limati: “Mwini diso lankhwenzule akangaza kulemera, osadziwa kuti umphawi udzam’fikira.” Munthuyo angafike pomafuna maudindo amene iyeyo sanapatsidwe. Pofuna kuti zochita zakezo zioneke ngati zabwino, iye angayambe makhalidwe amene Akristu ayenera kupewa, monga kung’ung’udza ndi kunena anzathu. (Yakobo 3:14-16) Mulimonsemo munthuyu atapanda kusamala angathe kukhala ndi mtima wodzikonda.

6. Kodi Baibulo limatichenjeza motani kuti tisakhale ndi mzimu wopikisana?

6 Motero, Baibulo limalimbikitsa Akristu kuti: “Tisakhale odzikuza, outsana, akuchitirana njiru.” (Agalatiya 5:26) Mtumwi Yohane  ananenapo za Mkristu mnzake amene zikuoneka kuti anali ndi mzimu woterewu. Yohane anati: “Ndalemba kanthu kwa Mpingo; komatu Diotrefe uja, wofuna kukhala wamkulu wa iwo, satilandira ife. Momwemo, ndikadza ine, ndidzakumbutsa ntchito zake zimene achitazi, zakunena zopanda pake pa ife ndi mawu oipa.” N’zomvetsa chisoni kwambiri kuti khalidwe la Mkristu lichite kufika poterepa.​—3 Yohane 9, 10.

7. Kodi Mkristu ayenera kupewa zinthu zotani m’ntchito zopikisana za masiku anozi?

7 Inde, Mkristu sangathe kupeweratu zinthu zonse zokhudza mpikisano. Mwachitsanzo, angakhale pantchito yofunika kupikisana pa zamalonda ndi a malonda anzake. Komabe, ngakhale pa zinthu ngati zimenezi, Mkristu ayenera kuchita malonda akewo mwaulemu, mwachikondi, ndiponso moganizira ena. Azikana njira zophwanya malamulo aboma kapena achikristu ndiponso azipewa kukhala ndi mbiri yoti ndi munthu wongofuna kuti zinthu zizimuyendera iyeyo basi. Sayenera kuganiza kuti kukhala woposa aliyense pa zinthu zosiyanasiyana, ndiko kuli kofunika kwambiri m’moyo. Ngati zili choncho pa zinthu wamba, kuli bwanji pa zinthu zokhudza kupembedza?

‘Osadzifanizira ndi Wina Wake’

8, 9. (a) N’chifukwa chiyani akulu mumpingo sayenera kupikisana? (b) N’chifukwa chiyani lemba la 1 Petro 4:10 limakhudza atumiki onse a Mulungu?

8 Mzimu umene Akristu ayenera kukhala nawo pa kupembedza kwawo unatchulidwa m’mawu ouziridwa awa: “Munthu adziyese yekha ntchito zake. Kenaka iye anyadire mwa iye yekha, osadzifanizira iyeyo ndi wina wake.” (Agalatiya 6:4, Chipangano Chatsopano mu Chichewa cha Lero) Akulu mumpingo, amadziwa kuti sali pampikisano, motero amagwirizana ndi kuchitira ntchito pamodzi monga bungwe la akulu. Amasangalala ndi mmene aliyense wa iwo amathandizira kuti mpingo wonse uziyenda bwino. Motero amapewa kupikisana kogawanitsa anthu ndipo mpingo wonse umaphunzirapo kanthu pa chitsanzo chabwinochi cha mgwirizano.

9 Chifukwa cha msinkhu wawo, kapena luso lawo lachibadwa, akulu ena amadziwa kuyendetsa zinthu bwino kuposa ena, kapena mwina amakhala ndi nzeru zozindikira zinthu zambiri kuposa ena. Motero, akulu amakhala ndi maudindo osiyanasiyana m’gulu la Yehova. M’malo momadziyerekezera ndi anzawo, iwowa amakumbukira malangizo akuti: “Monga yense walandira mphatso, mutumikirane nayo, ngati adindo okoma a chisomo cha mitundu mitundu cha Mulungu.” (1 Petro 4:10) Kwenikweni, lemba limeneli limanena za atumiki onse a Yehova, chifukwatu tonsefe tinalandira mphatso yodziwa choonadi molondola ndipo tonsefe tili ndi mwayi wochita nawo ntchito yolalikira.

10. Kodi utumiki wathu wopatulika umakhala wovomerezeka kwa Yehova ngati tikuuchita motani?

10 Utumiki wathu wopatulika umasangalatsa Yehova ngati tikuuchita mwa chikondi ndiponso modzipereka, osati chifukwa chodzikweza kuti tipose ena. Motero n’kofunika kwambiri kuona bwino ntchito yathu yothandiza pa kupembedza koona. Inde, palibe aliyense wa ife  amene angadziwe zolinga zenizeni zimene wina akuchitira zinazake, koma Yehova ndiye “woyesa mitima.” (Miyambo 24:12; 1 Samueli 16:7) Motero, ndibwino kumadzifunsa nthawi ndi nthawi kuti: ‘Kodi cholinga changa pochita utumiki wa Yehova n’chiyani makamaka?’​—Salmo 24:3, 4; Mateyu 5:8.

Kuona Ntchito Zathu Moyenera

11. Kodi ndi mafunso otani okhudza utumiki wathu amene alidi mafunso ofunika kuwaganizira?

11 Ngati cholinga chochitira ntchito zathu ndicho chili chofunika koposa kuti Yehova atiyanje, kodi tiyenera kuvutika n’kuganizira kwambiri ntchito zathuzo? Ngati tikuchita utumiki wathu n’cholinga choyenera, kodi n’kofunikiradi kuchita kulemba malipoti a zimene timachita? Amenewa ndi mafunso omveka ndithu, chifukwa sibwino kuti tiziganizira kwambiri za manambala a pa lipoti lathu kuposa utumiki wathu wachikristu weniweniwo kapena kuganizira kwambiri zokhala ndi lipoti labwino.

12, 13. (a) Kodi ndi zifukwa zina zotani zimene timasungira malipoti a utumiki wathu wakumunda? (b) Kodi n’chifukwa chiyani tiyenera kusangalala tikamaona lipoti la padziko lonse la ntchito yolalikira?

12 Onani zimene buku la Gulu Lochita Chifuniro cha Yehova limanena. Bukuli limati: “Otsatira oyambirira a Yesu Kristu anaona malipoti onena za mmene ntchito yolalikira ikuyendera kukhala ofunikira. (Marko 6:30) Buku la m’Baibulo la Machitidwe limatiuza kuti panali anthu pafupifupi 120 amene anasonkhana pamene mzimu woyera unatsanuliridwa pa ophunzira pa Pentekoste. Posakhalitsa chiwerengero cha ophunzira chinakwera kufika pa 3,000, ndipo kenako pa 5,000. . . . (Mac. 1:15; 2:5-11, 41, 47; 4:4; 6:7) Nkhani zimenezi zonena za kupita patsogolo kwa ntchitoyo zinali kulimbikitsa kwambiri ophunzirawo.” Pachifukwa chomwechi, Mboni za Yehova masiku ano zimayesetsa kusunga malipoti olondola a ntchito imene ikuchitidwa padziko lonse pokwaniritsa mawu a Yesu akuti: “Uthenga uwu wabwino wa Ufumu udzalalikidwa padziko lonse lapansi, ukhale mboni kwa anthu a mitundu yonse; ndipo pomwepo chidzafika chimaliziro.” (Mateyu 24:14) Malipoti oterewa amasonyeza ntchito imene ikuchitikadi padziko lonse. Amasonyeza mbali imene ikufunika chithandizo ndiponso kuti pakufunika mabuku ati komanso ochuluka motani kuti ntchito yolalikira ipite patsogolo.

13 Motero, kupereka malipoti a ntchito yathu yolalikira uthenga wabwino wa Ufumu kumatithandiza kuchita bwino ntchitoyi. Kuwonjezera apo, kodi sitilimbikitsidwa tikamva za ntchito imene abale athu akuchita m’madera ena a  padziko lapansi? Nkhani za kuwonjezeka kwa zinthu zosiyanasiyana zokhudza ntchitoyi timasangalala nazo kwambiri, zimatipatsa mphamvu zotithandiza kulimbikira utumiki wathu, ndiponso zimatitsimikizira kuti Yehova akutidalitsa. Ndipotu n’zosangalatsa kwambiri kudziwa kuti lipoti lathu patokha limaiikidwa nawo m’lipoti la padziko lonse lija. Inde, lipoti lathuli silonunkha kanthu poliyerekezera ndi malipoti onsewo akawaphatikiza pamodzi, komatu Yehova amaliona. (Marko 12:42, 43) Musaiwale kuti patapanda lipoti lanulo, lipoti la padziko lonse lingakhale losamaliza.

14. Kodi kuphatikiza pa kulalikira ndi kuphunzitsa, n’zinthu zinanso ziti zimene tiyenera kuchita popembedza Yehova?

14 Inde n’zoona kuti zinthu zambiri zimene Mboni iliyonse imachita pokwaniritsa udindo wake monga mtumiki wodzipereka wa Yehova sizimalembedwa pa lipoti lake. Mwachitsanzo, pa lipoti sipakhala malo olembapo mmene mtumikiyo wakhala akuchitira zinthu monga kuphunzira Baibulo payekha, kupita ndiponso kutengapo mbali pa misonkhano yachikristu, kugwira ntchito za pampingo, kuthandiza Akristu anzake pakafunika thandizo, kupereka ndalama zothandizira ntchito ya padziko lonse ya Ufumu, ndi zinthu zina zotere. Motero, ngakhale kuti lipoti lathu la utumiki wa kumunda limatithandiza kukhala akhama polalikira ndiponso popewa kubwerera m’mbuyo, tiyenera kuliona m’njira yoyenerera. Sitiyenera kuliona ngati chiphaso kapena pasipoti, yolowera moyo wosatha.

“Achangu pa Ntchito Zokoma”

15. Ngakhale kuti ntchito pazokha sizingatipulumutse, n’chifukwa chiyani zili zofunikirabe?

15 N’zoonekeratu kuti ngakhale kuti ntchito pazokha sizingatipulumutse, ntchitozo n’zofunika ndithu. N’chifukwa chake Akristu amatchedwa ‘anthu ake enieni, achangu pa ntchito zokoma’ ndiponso n’chifukwa chake amalimbikitsidwa ‘kuganizirana wina ndi mnzake kuti afulumizane ku chikondano ndi ntchito zabwino.’ (Tito 2:14; Ahebri 10:24) Yakobo anafotokoza mfundo yomweyi mosapita m’mbali ponena kuti: “Monga thupi lopanda mzimu lili lakufa, koteronso chikhulupiriro chopanda ntchito chili chakufa.”​—Yakobo 2:26.

16. Kodi n’chiyani chili chofunika kuposa ntchito, koma kodi tiyenera kusamala kusachita chiyani?

16 Chinthu chofunika koposa ntchito zabwino ndicho kukhala ndi zolinga zabwino zochitira ntchitozo. Motero n’chinthu chanzeru kumadzifunsa nthawi ndi nthawi kuti kodi cholinga changa n’chiyani makamaka? Komabe, popeza kuti palibe munthu amene angathe kudziwadi bwinobwino zolinga za anzake, tiyenera kusamala kuti tisamakayikire zolinga za anzathu. Baibulo limatifunsa kuti: “Kodi ndiwe ndani uweruza wantchito wa mwini?” Ndipo limatipatsa yankho lachidziwikire, lakuti: “Mbuye wake yekha ndiye aweruze ngati iye wakhoza kapena walephera pa ntchito yake.” (Aroma 14:4, Chipangano Chatsopano mu Chichewa cha Lero) Yehova, Mbuye wa onse, ndiponso Woweruza wake Kristu Yesu, ndi amene adzatiweruze, ndipo sadzatiweruza mogwirizana ndi ntchito zathu zokha koma adzatiweruza mogwirizana ndi zolinga zathu, mipata imene tinali nayo,  chikondi chathu, ndiponso kudzipereka kwathu. Yehova ndi Kristu Yesu okha ndiwo amene angathe kudziwadi bwinobwino ngati takwanitsa kutsatira zinthu zonse zimene Akristu amalimbikitsidwa kuchita. Zinthu zimenezi Paulo anazifotokoza motere: ‘Uchite changu kudzionetsera kwa Mulungu wovomerezeka, wantchito wopanda chifukwa cha kuchita manyazi, wolunjika nawo bwino mawu a choonadi.’​—2 Timoteo 2:15; 2 Petro 1:10; 3:14.

17. Pamene tikuyesetsa kuchita zinthu mwamphamvu zonse, n’chifukwa chiyani tiyenera kukumbukira lemba la Yakobo 3:17?

17 Yehova safuna kuti tizichita zinthu zimene sitingathe. Malingana ndi Yakobo 3:17, “nzeru yochokera kumwamba,” mwa zina ndi ‘yamtendere,’ kapena kuti yololera. Kodi si chinthu chanzeru, ndiponso choyamikika, kutsanzira Yehova pa mfundo imeneyi? Motero, tisalimbane n’zomafuna kuti ifeyo patokha kapenanso abale athu achite zinthu zimene kwenikweni zili zosatheka.

18. Kodi ndi madalitso otani amene tingayembekezere chifukwa choona moyenera ntchito zathu ndiponso chisomo cha Yehova?

18 Tikamaona moyenerera ntchito zathu za chikhulupiriro ndiponso chisomo cha Yehova, tingakhale ndi chimwemwe chapadera chimene anthu a Yehova okha ndiwo amakhala nacho. (Yesaya 65:13, 14) Tizisangalala kuti Yehova akudalitsa anthu ake tonsefe, ngakhale kuti patokhapatokha ntchito zathu n’zochuluka mosiyanasiyana. Tisaleke “pemphero, ndi pembedzero, pamodzi ndi chiyamiko,” popempha Mulungu kuti atithandize kuchita zinthu mwakhama zedi. Tikatero, mosakayika n’komwe, ‘mtendere wa Mulungu wakupambana chidziwitso chonse, udzasunga mitima yathu ndi maganizo athu mwa Kristu Yesu.’ (Afilipi 4:4-7) Inde, tilimbe mtima ndiponso tilimbikitsidwe podziwa kuti tingathe kupulumutsidwa, osati mwa ntchito zokha, komanso mwa chisomo cha Yehova.

Kodi Mungafotokoze Chifukwa Chimene Akristu

• amapewera kudzitamandira pa zimene iwowo achita paokha?

• amapewera mzimu wopikisana?

• amaperekera malipoti a utumiki wawo wa m’munda?

• amapewera kuweruza Akristu anzawo?

[Mafunso]

[Chithunzi patsamba 15]

“Chisomo changa chikukwanira”

[Zithunzi pamasamba 16, 17]

Akulu amasangalala ndi zimene aliyense angachite pothandiza mpingo kuyenda bwino

[Zithunzi pamasamba 18, 19]

Patapanda lipoti lanu, lipoti la padziko lonse lingakhale losamaliza