Pitani ku nkhani yake

Pitani ku mitu ya nkhani

Musaleme Pakuchita Zabwino

Musaleme Pakuchita Zabwino

 Musaleme Pakuchita Zabwino

MTUMWI Petro anatilimbikitsa kuti: “Mayendedwe anu mwa amitundu akhale okoma.” (1 Petro 2:12) Mawu a Chigiriki amene anawamasulira kuti “okoma” amatanthauza chinthu “chokongola, chapamwamba, cholemekezeka, ndiponso chabwino koposa.” Masiku ano, zingaoneke kuti n’kungodzivuta kufuna kuona anthu ambiri ali ndi makhalidwe apamwamba kapena olemekezeka. Komano anthu a Yehova ambiri masiku ano ayesetsa kutsatira malangizo a Petro amenewa. Ndipotu padziko lonse amadziwika chifukwa cha khalidwe lawo lokoma.

Izitu n’zoyamikika kwambiri makamaka mukaganizira za zovuta ndiponso zosautsa zina zimene timakumana nazo mu “nthawi zowawitsa” zino. (2 Timoteo 3:1) Ziyeso ndi mbali ya moyo wathu wa tsiku ndi tsiku, ndipo kuvutitsidwa chifukwa chokhala moyo wachikristu n’kofala. Kuphatikizanso apo, ngakhale kuti ziyeso zina sizikhalitsa, zina sizitherapo ayi, ndipo zimangoipiraipira. Komabe, mtumwi Paulo anatilimbikitsa kuti: “Tisaleme pakuchita zabwino; pakuti pa nyengo yake tidzatuta tikapanda kufoka.” (Agalatiya 6:9) Koma kodi n’zotheka bwanji kupitirizabe kuchita zokoma tikamakumana ndi ziyeso zosaneneka ndiponso nsautso zochita kusowa popumira?

Zomwe Zingatithandize Kuchita Zokoma

N’zosachita kufunsa kuti makhalidwe ‘apamwamba, olemekezeka, komanso abwino koposa’ amachokera mumtima mwa munthu. Motero ngati munthu satsatira mfundo za m’Baibulo pa zochita zake zonse za tsiku ndi tsiku, n’zosatheka kuti asonyeze khalidwe lokoma panthawi imene wakumana ndi ziyeso ndiponso zovuta zina. Kodi ndi zinthu zina ziti zimene zingatithandize pa mbali imeneyi? Taonani zinthu zotsatirazi.

Yesetsani Kukhala ndi Maganizo a Kristu. Pamafunika kudzichepetsa kuti tithe kupirira tikamaona kuti ena akutilakwira. Munthu wodzikuza sangathe kupirira ena akam’lakwira. Koma Yesu “anadzichepetsa yekha, nakhala womvera kufikira imfa.” (Afilipi 2:5, 8) Potsatira chitsanzo chake, sitingafike ‘polema ndi kukomoka’ nawo utumiki wopatulika. (Ahebri 12:2, 3) Yesetsani kukhala wodzichepetsa potsatira mosanyinyirika malangizo a abale amene akutsogolera mpingo umene muli. (Ahebri 13:17) Phunzirani kuona kuti anthu ena ‘n’ngokuposani,’ ndipo mungatero potsogoza zofuna zawo osati zofuna zanu.​—Afilipi 2:3,4.

Musaiwale Kuti Yehova Amakukondani. Tiyenera kusakayika m’pang’ono pomwe kuti Yehova “alipo, ndi kuti ali wobwezera mphoto iwo akum’funa Iye.” (Ahebri 11:6) Iye amatiganiziradi ndipo amafuna kuti tidzapeze moyo wosatha. (1 Timoteo 2:4; 1 Petro 5:7) Kusaiwala kuti palibe chimene chingaletse Mulungu kutikonda kungatithandize kusabwerera m’mbuyo tikakumana ndi ziyeso.​—Aroma 8:38, 39.

Dalirani Yehova ndi Mtima Wonse. Kudalira Yehova n’kofunikira, makamaka ngati ziyeso zake zikuoneka kuti n’zosatherapo kapena n’zoika moyo wathu pachiswe. Tiyenera kudalira Yehova mosakayika ngakhale pang’ono kuti iye sangalole chiyeso chilichonse kukula ‘koposa chimene tingakhoze kupirira,’ ndiponso kuti nthawi zonse “adzaikanso populumukirapo.” (1 Akorinto 10:13) Tikamadalira Yehova,  ngakhale chiyeso chitaika moyo wathu pachiswe, tingalimbane nacho molimba mtima.​—2 Akorinto 1:8, 9.

Limbikirani Kupemphera. Kupemphera mochokera pansi pa mtima n’kofunika kwambiri. (Aroma 12:12) Kupemphera moona mtima ndi njira imodzi imene timayandikira kwa Yehova. (Yakobo 4:8) Malingana ndi zimene takumanapo nazo, timadziwa kuti “ngati tipempha kanthu . . . , [Iye] atimvera.” (1 Yohane 5:14) Ngati Yehova atalola kuti chiyeso chathu chipitirire pofuna kuyesa kukhulupirika kwathu, timapemphera kuti atithandize kupirira. (Luka 22:41-43) Pemphero limatiphunzitsa kuti Yehova satisiya tokha ayi, komanso kuti popeza Yehova ali nafe, palibe chilichonse chimene chingatibweze m’mbuyo.​—Aroma 8:31, 37.

Ntchito Zabwino ‘Zimabweretsa Chiyamiko ndi Ulemerero’

Nthawi ndi nthawi, Akristu onse amakumana ndi “chisoni ndi mayesero a mitundu mitundu.” Komatu “tisaleme pakuchita zabwino.” Mukakhala pa vuto, limbani mtima podziwa kuti mukakhulupirika, mapeto ake mudzalandira “chiyamiko ndi ulemerero ndi ulemu.” (1 Petro 1:6, 7) Gwiritsirani ntchito bwino zinthu zonse zauzimu zochokera kwa Yehova, polimbitsa chikhulupiriro chanu. Mukafuna thandizo pa vuto linalake, pitani kwa abale a mumpingo wachikristu amene amatumikira monga abusa, aphunzitsi ndiponso alangizi. (Machitidwe 20:28) Muzipita nthawi zonse ku misonkhano yonse ya mpingo, chifukwa ‘imatifulumiza ku chikondano ndi ntchito zabwino.’ (Ahebri 10:24) Kuwerenga Baibulo tsiku n’tsiku ndiponso kuphunzira Baibulo panokha kungakuthandizeni kukhala ogalamuka ndiponso amphamvu mwauzimu. Kulowa m’munda nthawi zonse, kungakuthandizeninso chimodzimodzi.​—Salmo 1:1-3; Mateyu 24:14.

Mukamaona chikondi ndiponso chisamaliro cha Yehova m’njira zosiyanasiyana, mudzayamba kufuna kwambiri kukhala “achangu pa ntchito zokoma.” (Tito 2:14) Musaiwale kuti, “iye wakulimbika chilimbikire kufikira kuchimaliziro, yemweyo adzapulumuka.” (Mateyu 24:13) Inde, yesetsani ‘kusalema pakuchita zabwino.’

[Mawu Otsindika patsamba 29]

Tiyenera kudalira Yehova mosakayika ngakhale pang’ono kuti iye sangalole kuti tikumane ndi chiyeso chilichonse ‘choposa chimene tingakhoze kupirira,’ komanso kuti nthawi zonse “adzaikanso populumukirapo”

[Zithunzi patsamba 30]

Kukhala otanganidwa ndi zinthu zauzimu kungatithandize kukonzekera ziyeso