Pitani ku nkhani yake

Pitani ku mitu ya nkhani

Anthu Oona Mtima Amatamanditsa Yehova

Anthu Oona Mtima Amatamanditsa Yehova

 Olengeza Ufumu Akusimba

Anthu Oona Mtima Amatamanditsa Yehova

PADZIKO lonse, a Mboni za Yehova, ana ndi akulu omwe, amadziwika kuti n’ngoona mtima. Taonani zitsanzo zitatu izi zomwe zachokera ku Africa kuno, ku South America ndi ku Asia.

Tsiku lina mtsikana wina wa zaka 17 wa ku Nigeria, dzina lake Olusola ankabwerera kunyumba kuchokera kusukulu ndipo panjira anatola kachikwama kandalama. Iye anakapereka kachikwamako kwa mphunzitsi wamkulu pasukulupo, yemwe anawerengera ndalamazo, n’kupeza kuti zinali zokwana pafupifupi madola 45. Iwo anabweza chikwamacho kwa mphunzitsi amene chinam’tayika. Pothokoza, mphunzitsiyo anam’patsa Olusola ndalama zokwana pafupifupi madola 7 n’kumuuza kuti alipirire fizi. Ana asukulu ena atamva zimenezi anam’seka Olusola. Patatha milungu ingapo, mwana wa sukulu wina ananena kuti am’bera ndalama, motero aziphunzitsi anauzidwa kuti aseche ana onsewo kuti apeze amene waba ndalamazo. Mphunzitsi wina anauza Olusola kuti: “Iweyo ima pambalipa. Ndikudziwa kuti iweyo sungabe poti ndiwe wa Mboni za Yehova.” Ndalamazo anazipeza ndi anyamata awiri amene ankam’seka Olusola aja, ndipo anawalanga kwadzaoneni. Olusola analemba kalata yonena kuti: “Ndine wosangalala kwambiri kudziwika kuti ndine wa Mboni za Yehova, amene saba, motero ndikutamanditsa Yehova.”

Marcelo, wa ku Argentina, tsiku lina akuchoka kunyumba, anapeza chikwama cham’manja chili pansi pafupi ndi khomo la kuseli kwa nyumba yake. Iyeyo ndi mkazi wake analowa nacho m’nyumba chikwamacho, n’kuchitsegula mosamala. Atatero anadabwa kwambiri kuona kuti m’chikwamamo munali ndalama zambirimbiri, makadi otengera zinthu pangongole, ndiponso macheke angapo osainidwa kale, ndipo chimodzi mwa machekewa chinali cha ndalama zokwana madola 335,000. M’chikwamacho anapezamo chiphaso chokhala ndi nambala ya telefoni. Motero anaimbira telefoni mwini chikwamayo n’kugwirizana zoti akakumane ku ntchito kwa Marcelo kuti akam’bwezere chikwamacho pamodzi ndi zonse zinali mmenemo. Mwini chikwamayo atafika kuntchitoko, ankaoneka kuti mtima suli m’malo ayi. Koma bwana wa Marcelo anauza munthuyo kuti akhazike mtima pansi chifukwa Marcelo ndi wa Mboni za Yehova. Chifukwa chopeza chikwamacho, mwini chikwamayo anam’patsa Marcelo chionamaso cha ndalama zongokwana madola 6 okha basi. Zimenezi zinakwiyitsa kwambiri bwana wa Marcelo chifukwa iyeyo anakhudzidwa kwambiri ndi kuona mtima kwa Marcelo. Pamenepa Marcelo anatengerapo mwayi wolongosola kuti poti iyeyo ndi wa Mboni za Yehova, amafuna kuchita zinthu moona mtima nthawi zonse.

Ku Kyrgyzstan kunachokera nkhani yotsatirayi. Kamnyamata kena ka zaka 6, dzina lake Rinat, kanapeza kachikwama kandalama ka mayi wina amene ankakhala kufupi ndi kwawo. M’kachikwamamo munali ndalama pafupifupi madola 25. Rinat anabweza kachikwamako kwa mayiyo, koma mayiyo atawerengera ndalamazo anauza mayi ake a Rinat kuti ndalama zokwana pafupifupi madola 5 zikusowa. Rinat analandula kuti sanatenge ndalama zosowazo. Kenaka onse ananyamuka kukafufuza ndalamazo ndipo anazipeza kufupi ndi kumene Rinat anatola kachikwama kaja. Mayiyo anasowa chonena. Anam’thokoza kwambiri Rinat chifukwa chobweza ndalamazo komanso mayi ake, chifukwa chom’lera m’njira yachikristu.