Pitani ku nkhani yake

Pitani ku mitu ya nkhani

N’chifukwa Chiyani Ambiri Amalephera Kulingalira Bwino?

N’chifukwa Chiyani Ambiri Amalephera Kulingalira Bwino?

 N’chifukwa Chiyani Ambiri Amalephera Kulingalira Bwino?

“KODI vuto lake n’chiyani? Anayenera kudziwa kuti sayenera kutero,” wina akulankhula zimenezi ponena za mnzake amene wachita zinazake. Polephera kumvetsa, winanso akupukusa mutu ndipo akuchoka akulankhula motsitsa mawu kuti, “Akanangolingalira bwino pang’ono pokha, sakanachita zimenezi.” Kodi munamvapo wina akunena mawu ngati amenewa? Koma, kodi tikati “kulingalira bwino” timatanthauza chiyani?

Kulingalira bwino ndiko kuganiza mwaluso. Anthu ambiri amalola anthu ena kuwaganizira m’malo moti aganize okha. Amalola olemba ndi oulutsa nkhani komanso anzawo kuwasankhira zochita. Nthawi zina amangoyendera za m’chigulugulu.

Anthu ambiri masiku ano akuoneka kuti amalephera kulingalira bwino. Kodi tingatani kuti tizitha kulingalira bwino? Kodi kulingalira bwino kuli ndi phindu lanji?

Kodi Tingachite Bwanji Kuti Tizitha Kulingalira Bwino?

N’zotheka kukhala munthu wolingalira bwino, ngakhale kuti zimafuna nthawi, kuganiza mozama, ndi kuyesetsa nthawi zonse kuti mukulitse luso la kuzindikira ndi kusankha bwino zochita. Nazi zinthu zitatu zimene zingatithandize kukhala olingalira bwino.

Phunzirani Baibulo, ndi kutsatira uphungu wake. Baibulo, limene ndi buku lolembedwa mwaluso kwambiri ndiponso lotsatirika, ndi lothandiza kwambiri munthu akafuna kukhala wanzeru ndi wozindikira. (Aefeso 1:8) Mwachitsanzo, mtumwi Paulo analangiza Akristu anzake kuti: “Zinthu zilizonse zoona, zilizonse zolemekezeka, zilizonse zolungama, zilizonse zoyera, zilizonse zokongola, zilizonse zimveka zokoma; ngati kuli chokoma mtima china, kapena chitamando china, zilingirireni izi.” (Afilipi 4:8) Ngati nthawi zonse titsatira malangizo amenewa, tikhoza kumalingalira bwino ndi kuchita zinthu mwanzeru.

Phunzirani pa zimene zinakuchitikiranipo. Poonetsa kugwirizana kwa zokumana nazo m’moyo ndi kulingalira bwino, wolemba ndakatulo wina wa ku Switzerland anati: “Kulingalira bwino . . . ndiko kukumbukira zimene zinakuchitikirapo ndi kuona patali.” N’zoonadi kuti “wachibwana akhulupirira mawu onse; koma wochenjera asamalira mayendedwe ake.” (Miyambo 14:15) Munthu angaphunzire kulingalira bwino mwa kuonetsetsa zochitika zosiyanasiyana, kuphunzitsidwa ndiponso mwa zimene zam’chitikirapo m’moyo. M’kupita kwa nthawi  tingaphunzire kuchita bwino zinthu. Komano kuti tiphunzire pa zolakwa zathu, tifunika kukhala wodzichepetsa ndi wofatsa. Mzimu wodzitama, wodzikuza ndi waliuma umene anthu ali nawo masiku otsiriza ano n’chizindikiro chakuti kulingalira bwino n’kosowa.​—2 Timoteo 3:1-5.

Sankhani mwanzeru anzanu ocheza nawo. Anzathu amene timacheza nawo angatithandize kapena kutilepheretsa kugwiritsa ntchito nzeru ndi kulingalira bwino. Lemba la Miyambo 13:20 limati: “Ukayenda ndi anzeru udzakhala wanzeru: koma mnzawo wa opusa adzaphwetekedwa.” Sitiyenera kutengera malingaliro kapena nzeru za anthu amene samvera Mulungu ndipo amanyalanyaza Mawu ake. Lemba la Miyambo 17:12 limati: “Kukomana ndi chitsiru m’kupusa kwake kuopsa koposa chirombo chochichotsera ana ake.”

Kodi Kuli ndi Phindu Lanji?

Kukhala ndi luso lolingalira bwino n’kopindulitsa. Kumachititsa moyo kukhala wosangalatsa ndipo kungatithandize kusawononga nthawi. Kulingalira bwino kungatithandizenso kuchepetsa zokhumudwitsa zimene zimadza chifukwa chochita zinthu mosaganiza bwino. Amene amalephera kusankha bwino zochita amangochititsa moyo wawo kukhala wovuta. Baibulo limanena kuti: “Ntchito ya zitsiru izitopetsa zonsezo.” (Mlaliki 10:15) Anthu oterowo angamagwire ntchito yolimba nthawi zonse n’kumadzitopetsa, koma osapeza phindu lililonse.

Baibulo lili ndi uphungu wambirimbiri wokhudza ukhondo, kulankhulana, khama, kuthana ndi umphawi, komanso wokhudza zinthu zosiyanasiyana m’moyo. Anthu mamiliyoni angachitire umboni kuti kukhala opambana kapena olephera m’moyo wawo, mokulira kwadalira mmene agwiritsira ntchito mfundo za m’Baibulo. Mfundo zimenezi zawathandiza kuchita zinthu mwanzeru.

Kulingalira bwino sikumangotithandiza kutsatira mndandanda wa malangizo kapena malamulo atsatanetsatane. Kumatithandiza kukwaniritsa udindo wathu. Komabe, si kuti ukakhala wolingalira bwino ndiye kuti sufunikira kuphunzira zinthu zowonjezeka. ‘Wanzeru amamva, nawonjezera kuphunzira,’ limatero lemba la Miyambo 1:5. Tiyeneranso kuphunzira kuganizira mwakuya za mfundo zosiyanasiyana zimene tapeza, n’kutengapo mfundo zazikulu zoyenera. Kutero kungatithandize ‘kuyenda mwanzeru.’​—Miyambo 28:26.

Kudzichepetsa kumagwirizana ndi kulingalira bwino. Ngakhale kuti tingafune kusamalira udindo wambiri, tiyenera kulingalira bwino n’kulola zokhazo zimene tingathedi kuchita malinga ndi mphamvu zathu. N’zoona kuti mtumwi Paulo anatiuza kukhala “akuchuluka mu ntchito ya Ambuye.” (1 Akorinto 15:58) Koma langizo limeneli tiziligwirizanitsa ndi mfundo yolembedwa pa Mlaliki 9:4 yakuti: “Galu wamoyo aposa mkango wakufa.” Kusamalira bwino thanzi lathu pamene tikutumikira Yehova kungathandize kuti tikhale ndi moyo wautali, n’kupitirizabe kum’tumikira. Kulingalira bwino kungatithandize kudziwa malire a mphamvu zathu, zimene zingatichititse kukwaniritsa zinthu zofunikira mosataya chimwemwe chathu. Ndithudi, kulingalira bwino n’kopindulitsa kwambiri.

[Chithunzi patsamba 14]

Baibulo lili ndi uphungu wochuluka wothandiza

[Chithunzi patsamba 15]

Munthu angaphunzire kulingalira bwino mwa kuonetsetsa zochitika zosiyanasiyana, kuphunzitsidwa ndiponso mwa zimene zam’chitikirapo m’moyo