Pitani ku nkhani yake

Pitani ku mitu ya nkhani

Kodi Anthu Angathetse Umphawi?

Kodi Anthu Angathetse Umphawi?

 Kodi Anthu Angathetse Umphawi?

ANTHU ambiri sanakhalepo paumphawi chibadwire. Sanagonepo ndi njala kapena kugona osafunda. Komabe, ambiri mwa anthu oterewa amamvera chisoni anthu osauka ndipo amayesetsa kuwathandiza.

Koma umphawi ukusautsabe anthu m’madera amene kuli nkhondo yapachiweniweni, kusefukira kwa madzi, chilala ndi mavuto ena. Mavuto ngati amenewa n’ngosautsa kwambiri kwa alimi ang’onoang’ono mu Africa. Ena akakamizika kuchoka kumudzi kwawo ndi kusamukira m’mizinda ikuluikulu kapena kuthawira m’dziko lina. Anthu ena akumudzi amasamukira m’mizinda chifukwa chokopeka ndi malonjezo akuti kumeneko zinthu zikawayendera bwino.

Kawirikawiri m’mizinda momwe muli anthu ambiri, mumakhala umphawi wadzaoneni. Malo oti n’kulima mbewu amakhala ochepa, ndipo nthawi zina sapezeka n’komwe. Nthawi zambiri ntchito imasowa. Posowa chochita, anthu ambiri amangoyamba umbava. Anthu okhala m’mizinda amapempha boma kuti liwathandize, koma maboma a anthu akulephera kuthetsa vuto la umphawi limene likukulirakulira. Ponena za lipoti limene bungwe la United Nations linatulutsa mu November 2003, nyuzipepala ya ku London yotchedwa The Independent inati: “Anthu osowa chakudya pa dziko lonse akuchulukirachulukira.” Kenako inawonjezera kuti: “Lerolino anthu pafupifupi 842 miliyoni pa dziko lonse sakudya mokwanira, ndipo chaka chilichonse chiwerengero chimenechi chikuwonjezeka ndi anthu 5 miliyoni.”

Nthawi zina ofesi ya nthambi ya Mboni za Yehova ku South Africa imalandira makalata kuchokera kwa anthu omwe akuvutika ndi umphawi. Mwachitsanzo, munthu wina wa ku Bloemfontein analemba kuti: “Ine sindigwira ntchito yolembedwa, ndiye ndimabera anthu m’tauni mpata ukapezeka. Ndikapanda kutero, timakhala ndi njala masiku ambiri. Izi zikuwonjezera pa vuto lakale lomangozizidwa chifukwa chosowa zovala ndi zofunda. Ntchito kulibiretu. Anthu ambiri akungoyendayenda m’misewu kufufuza ntchito ndi chakudya. Ndikudziwa anthu ena amene amatola chakudya m’zitini zotayamo zinyalala. Ena amadzipha. Ndipo mofanana ndi ineyo, ambiri ndi ovutika maganizo komanso otaya mtima. Ndikungoona ngati tilibe tsogolo lililonse. Kodi Mulungu, amene anatilenga ndi chilakolako chofuna kudya ndi kuvala, sakuona zimenezi?”

Pali mayankho olimbikitsa a mafunso amene munthu ameneyu ali nawo. Monga mmene nkhani yotsatira ikusonyezera, mayankho amenewa akupezeka m’Mawu a Mulungu, Baibulo.