Pitani ku nkhani yake

Pitani ku mitu ya nkhani

Mafunso Ochokera kwa Owerenga

Mafunso Ochokera kwa Owerenga

 Mafunso Ochokera kwa Owerenga

Kodi ndibwino kuti Mkristu azipereka ndalama kapenanso mphatso kwa munthu wogwira ntchito m’boma pofuna kuti amuchitire ntchito inayake, kapena kodi kuchita zimenezi tingati n’kupereka ziphuphu?

Kulikonse kumene amakhala, Akristu amafuna kuchita zinthu mwanzeru, malingana ndi kuderalo, ndipo saiwala kuti zinthu zololeka ndiponso zovomerezeka mwalamulo m’dziko linalake zimatha kukhala zosaloleka ndiponso zosavomerezeka mwalamulo m’dziko lina. (Miyambo 2:6-9) Inde, Mkristu ayenera kukumbukira nthawi zonse kuti munthu aliyense amene akufuna ‘kugonera m’chihema [cha Yehova]’ ayenera kupewa kupereka ziphuphu.​—Salmo 15:1, 5; Miyambo 17:23.

Kodi kupereka ziphuphu n’kutani makamaka? Buku lakuti The World Book Encyclopedia limati “kupereka ziphuphu n’kupereka chinthu chamtengo wapatali kwa . . . munthu waudindo, kuti akalandira chinthucho anyalanyaze malamulo a ntchito yake n’kutsatira zofuna za munthu amene wam’patsa chinthuyo.” Motero, m’dziko lina lililonse n’kulakwa kupereka ndalama kapena mphatso inayake kwa woweruza kapena wapolisi n’cholinga choti akhotetse lamulo. Ndiponso n’kulakwa kupereka zinthu zotere kwa woyendera kuti anyalanyaze vuto kapena zolakwika zinazake. Kupereka mphatso n’cholinga choti mupatsidwe mwayi winawake wapadera monga kusuntha dzina lanu pa ndandanda ya anthu odikirira zinazake n’kuliika poyamba, kapenanso kupitirira anzanu pamzere, kulinso m’gulu la kupereka ziphuphu. Kuchita zoterezi kungasonyezenso kusowa chikondi.​—Mateyu 7:12; 22:39.

Koma kodi tingati n’kupereka ziphuphu ngati titapereka mphatso, mwachitsanzo, kwa munthu wa m’boma, n’cholinga choti atichitire ntchito inayake yololeka kapena n’cholinga choti tipewe kuponderezedwa? Mwachitsanzo, m’mayiko ena, akuluakulu amaudindo akapanda kupatsidwa kangachepe amavuta kuti alembe ana sukulu, kaya kulola kuti odwala agonekedwe m’chipatala. Akuluakulu ena amavuta kuvomereza ziphaso zolowera kapena kukhalira m’dziko. Enanso amachedwa kuthandizapo anthu akalemba kalata yofuna kukonzanso malaisensi awo osiyanasiyana amene atha ntchito.

Nkhani ya kupereka kangachepe kwa munthu ndiponso mmene anthu ambiri amaionera imasiyana m’mayiko osiyanasiyana. M’mayiko amene anthu amapereka kangachepe malingana ndi chikhalidwe chawo kapenanso malingana ndi zimene aliyense amayembekezera, Akristu ena angaone kuti malinga ngati potero sakuswa mfundo za m’Baibulo, ndiye kuti angathe kupereka kangachepe kwa munthu winawake waudindo kuti awachitire ntchito inayake. M’mayiko ena anthu amaona kuti imeneyi ndi mphatso yothandiza munthu wogwira ntchito m’bomayo kuti akokere, popeza kuti amalandira ndalama zochepa. Komano musaiwale kuti kupereka mphatso kuti munthu akuchitireni zinthu zololeka mwalamulo n’kosiyana ndi kupereka ziphuphu kuti munthuyo akuchitireni zinthu zosemphana ndi lamulo.

Komabe, pantchito zololeka mwalamulo, a Mboni za Yehova ena akanapo kupereka kangachepe kwa anthu oyendera, a kasitomu, kapenanso anthu ena, ngakhale m’madera amene anthu ambiri anazolowera kutero. Popeza kuti m’maderawo a Mboni amadziwika kuti chikumbumtima chawo sichiwalola kuchita khalidwe limeneli ndiponso kuti n’ngoona mtima, nthawi zina amathandizidwa kwaulere pa zinthu zimene anthu ambiri amachita kulipira kuti athandizidwe.​—Miyambo 10:9; Mateyu 5:16.

Mwachidule, tinganene kuti mtumiki aliyense wa Yehova ayenera kuona yekha ngati zili zoyenera kwa iyeyo kupereka kangachepe kenakake kuti munthu wina amuchitire ntchito inayake yololeka kapena kuti apewe kuponderezedwa. Koma chachikulu n’chakuti azichita zinthu zosamuwonongera chikumbumtima, zosanyozetsa dzina la Yehova, ndiponso zosakhumudwitsa anthu ena.​—Mateyu 6:9; 1 Akorinto 10:31-33; 2 Akorinto 6:3; 1 Timoteo 1:5.