Pitani ku nkhani yake

Pitani ku mitu ya nkhani

Samsoni Anapambana Chifukwa cha Mphamvu za Yehova

Samsoni Anapambana Chifukwa cha Mphamvu za Yehova

 Samsoni Anapambana Chifukwa cha Mphamvu za Yehova

SAMSONI wagwidwa ndi adani ake ouma mtima. Amuchotsa maso ndipo akum’gwiritsa ntchito yakalavula gaga. Kenako akumutulutsa m’ndende ndi kupita naye m’kachisi wachikunja kuti akasangalatse anthu. Akum’kakamiza kuguba pamaso pa anthu zikwizikwi oonerera ndipo akumunyoza. Mkaidi ameneyu si wachifwamba kapena mtsogoleri wa gulu lankhondo la adani awo ayi. Iye ndi wolambira wa Yehova ndipo watumikira monga woweruza mu Israyeli kwa zaka 20.

Zinatheka bwanji kuti zinthu zochititsa manyazi choterezi zim’chitikire Samsoni, amene anali wamphamvu kuposa munthu wina aliyense padziko lapansi? Kodi mphamvu zake zosanenekazo zikanatha kum’pulumutsa? Kodi chinsinsi cha mphamvu za Samsoni chinagona pati? Kodi tikuphunzirapo chiyani m’nkhani yakeyi?

‘Adzayamba Ndi Iye Kupulumutsa Israyeli’

Ana a Israyeli anali atapandukira kulambira koona kangapo konse. Choncho pamene iwo “anawonjeza kuchita choipa pamaso pa Yehova; [a]nawapereka Yehova m’dzanja la Afilisti zaka makumi anayi.”​—Oweruza 13:1.

Nkhani ya Samsoni inayambira pamene mngelo wa Yehova anaonekera mkazi wosabala wa Mwisrayeli wina dzina lake Manowa, ndi kum’dziwitsa kuti adzabereka mwana wamwamuna. Mngeloyo analangiza mkaziyo kuti: “Pamutu pake sipadzafika lumo; pakuti mwanayo adzakhalira kwa Mulungu Mnaziri chibadwire; nadzayamba iye kupulumutsa Israyeli m’dzanja la Afilisti.” (Oweruza 13:2-5) Mayiyu asanatenge pathupi pa Samsoni, Yehova anali atatsimikiza kudzapatsa Samsoni ntchito yapadera. Kuchokera tsiku la kubadwa kwake, anayenera kudzakhala Mnaziri, kapena kuti munthu wosankhidwa kuchita utumiki wopatulika wapadera.

Mkazi Ameneyu Ndiye ‘Woyenera Kwa Ine’

Pamene Samsoni anali kukula, ‘Yehova anam’dalitsa.’ (Oweruza 13:24) Tsiku lina Samsoni anapita kwa bambo ndi mayi ake ndi kuwauza kuti: “Ndapenya mkazi m’Timna wa ana aakazi a Afilisti; ndipo tsono munditengere uyu akhale mkazi wanga.” (Oweruza 14:2) Tangoganiza mmene iwo anadabwira. M’malo mopulumutsa Israyeli m’manja mwa adani oponderezawo, mwana wawo akufuna kukwatira mkazi wamtundu umenewo. Kukwatira mkazi wolambira milungu yachikunja kunali kotsutsana ndi Chilamulo cha Mulungu. (Eksodo 34:11-16) Pachifukwa chimenechi, makolo akewo anatsutsa  nati: “Kodi palibe mkazi mwa ana aakazi a abale ako, kapena mwa anthu a mtundu wanga onse, kuti wamuka kutenga mkazi wa Afilisti osadulidwawo?” Koma Samsoni anaumirirabe nati: “Nditengereni iye, pakuti andikonda pamaso panga [“ndiye woyenera kwa ine,” NW].”​—Oweruza 14:3.

Kodi mkazi wachifilisti ameneyu anali “woyenera” motani kwa Samsoni? Buku lotchedwa Cyclopedia lolembedwa ndi McClintock ndi Strong limati, sikuti anali woyenera m’lingaliro lakuti anali “wokongola, wosangalatsa, kapena wokopa ayi, koma anali woyenera mogwirizana ndi kukwaniritsa cholinga chake.” Kukwaniritsa cholinga chotani? Lemba la Oweruza 14:4 limafotokoza kuti Samsoni “anali kufuna kutola chifukwa ndi Afilisti.” Samsoni ankafuna mkaziyo kuti apezerepo mpata wolimbana ndi Afilistiwo. Samsoni atakula, “mzimu wa Yehova unayamba kum’fulumiza mtima,” kapena kuti kumulimbikitsa kuchitapo kanthu. (Oweruza 13:25) Chotero mzimu woyera ndi umene unalimbikitsa Samsoni kupereka pempho lake lodabwitsali lokhudza mkazi ameneyu, komanso ndi umene unali kum’tsogolera pa ntchito yake yonse monga woweruza wa Israyeli. Kodi mpata umene Samsoni anali kuufuna unapezeka? Choyamba tiyeni tione mmene Yehova anam’tsimikizira kuti adzam’thandiza.

Samsoni anali paulendo wopita ku Timna, kwawo kwa mkwatibwi wake wam’tsogolo. Malemba amafotokoza nkhaniyi kuti: “Nadza ku minda yamphesa ya Timna; ndipo taona, mwana wa mkango wakomana naye nam’dzumira. Ndipo unam’gwera iye kolimba mzimu wa Yehova, naung’amba.” Samsoni anali yekhayekha pamene mphamvu zake zinaonekera modabwitsa chomwechi. Panalibe aliyense woonerera. Kodi imeneyi inali njira ya Yehova yotsimikizira Samsoni kuti monga Mnaziri, anali wokhoza kukwaniritsa ntchito imene Mulungu anam’patsa? Baibulo silinena chilichonse, koma mosakayikira Samsoni anazindikira kuti mphamvu zodabwitsazo sizinali zake zachibadwa. Anadziwa kuti zachokera kwa Mulungu. Izi zinam’thandiza kudalira Yehova kuti adzam’thandiza pa ntchito imene anali nayo m’tsogolo. Zimene anachitira mkangowo zitamulimbikitsa, Samsoni “anatsika nakamba ndi mkazi, nam’konda [“ndipo anali woyenera,” NW] pamaso pake.”​—Oweruza 14:5-7.

Pambuyo pake, pamene Samsoni anali kupita kukatenga mkaziyo, “[a]napambuka iye kukaona mtembo wa mkango; ndipo taona, m’chitanda cha mkango munali njuchi zoundana, ndi uchi.” Pa ukwati wake, Samsoni anakumbukira zimenezi, ndipo anaphera mwambi anzake achifilisti okwana 30, iye anati: “Chakudya chinatuluka m’mwini kudya, ndi chozuna chinatuluka m’mwini mphamvu.” Samsoni anawauza kuti ngati adzamasulira mwambiwu molondola, adzawapatsa malaya a m’kati ndi zovala zina zokwana makumi atatu. Koma ngati atalephera, iwowo adzam’patsa zovala zofananazo. Mwambi  umenewu unawathetsa nzeru Afilistiwo kwa masiku atatu. Tsiku lachinayi, anangoganiza zokawopseza mkazi wa Samsoni uja. Iwo anamuuza kuti: “Kopa mwamuna wako, atitanthauzire mwambiwo; tingatenthe iwe ndi nyumba ya atate wako ndi moto.” Anali ankhanza bwanji! Ngati Afilistiwo anali kuwopseza Afilisti anzawo moteremu, ganizirani mmene zinalili kwa Aisrayeli oponderezedwawo.​—Oweruza 14:8-15.

Chifukwa cha mantha, mkaziyo anaumiriza Samsoni kuti amuululire tanthauzo la mwambiwo. Mwamsanga mkaziyo anapita kukauza anzake amkwatiwo, ndipo izi zinasonyezeratu kuti analibe chikondi komanso sanali wokhulupirika kwa Samsoni. Iwo anatanthauzira mwambiwo, ndipo Samsoni anadziwa chifukwa chake anatha kuumasulira. Iye anati kwa iwo: “Mukadapanda kulima ndi mthandi wanga, Simukadakumika mwambi wanga.” Umenewu tsopano unali mpata umene Samsoni anali kuuyembekezera. “Mzimu wa Yehova unam’gwera Samsoni, natsikira iye kwa Asikeloni, nawakantha amuna makumi atatu, natenga zovala zawo, nawapatsa okumika mwambiwo zovala zosinthanitsa.”​—Oweruza 14:18, 19.

Kodi zimene Samsoni anachita ku Asikeloni anazichita pongofuna kubwezera? Ayi. Inali ntchito ya Mulungu kudzera mwa mpulumutsi amene iye anamusankha. Kudzera mwa Samsoni, Yehova anayambitsa nkhondo yolimbana ndi anthu ankhanza amene anali kupondereza anthu ake. Mtopola umenewu sunathere pomwepa. Samsoni anapezanso mpata wina pamene anapita kukacheza kwa mkazi wake.

Samsoni Anamenya Yekha Nkhondo

Atafika ku Timna, Samsoni anapeza kuti bambo ake a mkazi wake anakwatitsa mwana wawoyo kwa mwamuna wina, poganiza kuti Samsoni anali kudana naye. Zinali zoonekeratu kuti Samsoni wakwiya koopsa. Chotero anagwira ankhandwe 300, ndi kuwamangirira michira awiriawiri ndipo anamangiriranso miuni yamoto pa michirayo. Mmene anawasiya kuti azipita, ananka natentha minda ya tirigu, ya mpesa ndi minda ya azitona. Chaka chimenecho, mitundu itatu ya mbewu zofunika kwambiri mu Filistiya zinawonongedwa. Afilisti okwiyawo anasonyeza nkhanza zawo. Iwo anaganiza kuti mkazi wa Samsoni ndi bambo akewo ndiwo anachititsa zonsezi chotero anawatentha. Kubwezera kwawo kwankhanzako kunakwaniritsa cholinga cha Samsoni. Mwakuti pobwezera, nayenso anawakantha koopsa.​—Oweruza 15:1-8.

Kodi Aisrayeli anazindikira kuti Yehova Mulungu anali kudalitsa Samsoni, ndipo kodi anagwirizana naye kuti athetse ulamuliro wopondereza wa Afilistiwo? Kutalitali. Pofuna kupewa mavuto, amuna a Yuda anatumiza anthu 3,000 kuti akagwire mtsogoleri wawo wosankhidwa ndi Mulunguyo ndi kum’pereka kwa adani ake. Komatu kusakhulupirika kwa Aisrayeliku, kunam’patsa Samsoni mpata wokhaulitsabe adani akewo. Atatsala pang’ono kum’pereka kwa Afilistiwo, “mzimu wa Yehova unam’gwera kolimba, ndi zingwe zokhala pa manja ake zinanga bwazi lopserera ndi moto, ndi zomangira zake zinanyotsoka pa manja ake.” Kenako anatenga chibwano cha bulu nakantha nacho adani okwana 1,000.​—Oweruza 15:10-15.

Popemphera kwa Yehova, Samsoni anati: “Mwapatsa Inu chipulumutso ichi chachikulu ndi dzanja la kapolo wanu; ndipo kodi ndife nalo ludzu tsopano ndi kugwa m’dzanja la osadulidwa awa?” Yehova anamva pemphero la Samsoni ndipo anamuyankha. “Mulungu anang’amba pokumbika paja . . . , natulukamo madzi; namwa iye, nubwera moyo wake, natsitsimuka.”​—Oweruza 15:18, 19.

Samsoni anali wotsimikiza kukwaniritsa cholinga chake, chomenyana ndi Afilisti. Samsoni anakakhala kunyumba ya mkazi wadama ku Gaza ndi cholinga chomenyana ndi adani a Mulungu. Samsoni anafunikira malo ogona usiku m’mzinda wa adaniwo, ndipo malowo anapezeka m’nyumba ya mkazi wadama. Samsoni analibe cholinga chochita dama. Iye anachoka kunyumba kwa mkaziyo pakati pa usiku, nazula mageti apachipata cha m’zindawo limodzi ndi zimitengo zake zam’mbali ziwiri. Ndipo anazinyamula kupita nazo pamwamba pa phiri pafupi ndi Hebroni, mtunda wa pafupifupi makilomita 60. Mulungu anavomereza zomwe anachitazi ndipo anam’patsa mphamvu yochitira zimenezi.​—Oweruza 16:1-3.

 Mzimu woyera unagwira ntchito mwapadera kwambiri mwa Samsoni chifukwa cha mmene zinthu zinalili panthawiyo. Atumiki okhulupirika a Mulungu masiku ano angadalire mzimu womwewo kuwapatsa mphamvu. Yesu anatsimikizira otsatira ake kuti Yehova “adzapatsa Mzimu Woyera kwa iwo akum’pempha Iye.”​—Luka 11:13.

N’chifukwa Chiyani ‘Yehova Anam’chokera’ Samsoni?

Nthawi ina Samsoni anapalana ubwenzi ndi mkazi wina dzina lake Delila. Akalonga asanu achifilisti anali otsimikiza mtima kugonjetsa Samsoni mwakuti ananyengerera Delila kuti awathandize. Iwo anafikira Delila ndi kumuuza kuti: “Um’kope nuone umo muchokera mphamvu yake yaikulu, ndi umo tingakhoze kum’tha khama.” Pofuna kum’kopa, aliyense wa akalonga asanuwo analonjeza kuti adzam’patsa chiphuphu cha “ndalama mazana khumi ndi limodzi.”​—Oweruza 16:4, 5.

Ngati ndalama zimenezi zinali masekeli, ndiye kuti anamulonjeza ndalama zambiri zedi zokwana masekeli 5,500. Abrahamu anagula manda oikamo mkazi wake ndi masekeli 400, ndipo kapolo anali kum’gulitsa masekeli 30 okha. (Genesis 23:14-20; Eksodo 21:32) Popeza kuti akalongawo, omwe anali olamulira a mizinda isanu ya Afilisti, anagwiritsa ntchito dyera la Delila, osati kumukakamiza kutumikira anthu a mtundu wake, zikungosonyeza kuti mwina anali mkazi wachiisrayeli. Mulimonse mmene zinalili, Delila anavomera chiphuphucho.

Katatu konse, Samsoni anauza Delila mayankho abodza pamene anali kumufunsa za mphamvu zakezo, ndipo katatu konseko Delila anayesa kumupereka Samsoni kwa adani ake. Koma “popeza anamuumiriza masiku onse ndi mawu ake, nam’kakamiza, moyo wake unavutika n’kufuna kufa.” Pamapeto pake Samsoni anaulula zoona zake, anati tsitsi lake linali lisanametedwepo chibadwire. Akadzangometa tsitsi lakelo, adzafooka ndipo adzafanana ndi munthu wina aliyense.​—Oweruza 16:6-17.

Samsoni atangoulula komwe mphamvu zakezo zinali kuchokera, kugonja kwake kunali kumeneko. Delila anamupusitsa kuti apeze mpata womumeta tsitsi lakelo. Komatu sikuti mphamvu za Samsoni zinalidi m’tsitsi lake ayi. Tsitsilo linkangoimira ubwenzi wapadera umene anali nawo ndi Mulungu, monga Mnaziri. “Yehova adam’chokera” Samsoni chifukwa cholola kumetedwa tsitsi lakelo, zomwe zinakhudza Unaziri wake. Tsopano Afilistiwo anagonjetsa Samsoni, anamukolowola maso, ndi kumutsekera m’ndende.​—Oweruza 16:18-21.

Palitu phunziro lofunika kwambiri kwa ife pamenepa. Kodi sitiyenera kuona kuti ubwenzi wathu ndi Yehova ndi wamtengo wapatali? Ngati titachita zinthu zosephana ndi kudzipereka kwathu kwa Mulungu monga Akristu, kodi tingayembekezere bwanji Mulungu kupitirizabe kutidalitsa?

“Ndife Nawo Afilisti”

Mosangalala Afilistiwo anayamika mulungu wawo Dagoni chifukwa chogonjetsa Samsoni. Pokondwerera kupambana kwawoko, anam’tenga Samsoni ndi kupita naye ku kachisi wa Dagoni. Koma Samsoni anadziwa chifukwa chake anagonjetsedwa. Anadziwa chifukwa chake Yehova anam’chokera, ndipo Samsoni analapa kulakwa kwakeko. Pamene Samsoni anali m’ndende, tsitsi lake lija linayamba kukula kwambiri. Tsopano popeza kuti anali pamaso pa Afilisti zikwizikwi, kodi iye anachitanji?

Samsoni anapemphera nati: “Yehova, Mulungu, mundikumbukire, ndikupemphani, ndi kundilimbitsa, ndikupemphani, nthawi ino yokha, Mulungu, kuti ndidzilipsiriretu tsopano apa Afilisti, chifukwa cha maso anga awiri.” Pamenepo iye anagwira mwamphamvu mizati iwiri yapakati m’nyumbamo, “nadziweramira mwamphamvu.” Kodi zotsatira zake zinali zotani? “Nyumba idagwa pa akalonga, ndi pa anthu onse anali m’mwemo. Motero akufa amene anawapha pa kufa kwake anaposa amene anawapha akali moyo.”​—Oweruza 16:22-30.

Samsoni anali ndi mphamvu zochuluka ndipo panalibe munthu wofanana naye. Zochita zake zinasonyezeratu mphamvu zimene anali nazo. Koma koposa zonse, Mawu a Yehova amatchula Samsoni monga mmodzi wa anthu amene anali ndi chikhulupiriro cholimba.​—Ahebri 11:32-34.

[Chithunzi patsamba 26]

Kodi chinsinsi cha mphamvu za Samsoni chinagona pati?