Pitani ku nkhani yake

Pitani ku mitu ya nkhani

Mafunso Ochokera kwa Owerenga

Mafunso Ochokera kwa Owerenga

 Mafunso Ochokera kwa Owerenga

Kodi kudya mkate wopatulika kwa Davide ndi anyamata ake kumasonyeza kuti ngati zinthu zavuta munthu angaswe lamulo la Mulungu koma osalangidwa?​—1 Samueli 21:1-6.

Malinga ndi lemba la Levitiko 24:5-9, mkate wopatulika womwe anali kuuchotsa tsiku la Sabata lililonse ndi kuikapo watsopano, unayenera kudyedwa ndi ansembe okha basi. Ansembe okha ndi amene anali oyenera kudya mkatewo chifukwa chakuti unali wopatulika ndipo umayenera kukhala chakudya cha anthu omwe akutumikira Mulungu. Kuupereka kwa munthu wamba kapena kudya mwachisawawa kunali kulakwa. Komabe, wansembe Ahimeleki sanalakwe pamene anagawira Davide ndi anyamata ake mkate wopatulikawo.

Ahimeleki anaona kuti Davide anali kugwira ntchito yapadera motumidwa ndi Mfumu Sauli. Davide ndi anyamata akewo anamva njala. Ahimeleki anatsimikizira kuti iwo anali oyera. Ngakhale kuti anachita zosemphana ndi chilamulo mwa kudya mkate wopatulikawo, zinali zogwirizana ndi cholinga cha mkate wopatulikawo. Ahimeleki anaganizira zimenezi posankha kusatsatira lamulo limeneli. Ngakhalenso Yesu Kristu anatchula nkhani imeneyi monga chitsanzo chosonyeza kuti sikunali koyenera kukhwimitsa chilamulo cha Sabata monyanyira monga mmene Afarisi ankachitira.​—Mateyu 12:1-8.

Komatu zimenezi sizikutanthauza kuti ngati zinthu zavuta, n’zololeka kuswa lamulo la Mulungu ayi. Mwachitsanzo, pamene asilikali a Israyeli anali kumenyana ndi Afilisti, zikuoneka kuti zinthu zinafika povuta. Mfumu Sauli inali itanena kuti: “Atembereredwe iye wakudya kanthu kufikira madzulo, ndikabwezere chilango adani anga.” Baibulo limanena kuti: “Anakantha Afilisti tsiku lija.” Asilikaliwo anatopa chifukwa cha kumenyanako ndipo anamva njala, mwakuti ‘anthuwo anatenga nyama, naziphera pansi; nazidya zili ndi mwazi wawo.’ (1 Samueli 14:24, 31-33) Anthuwo anachimwira Yehova mwa kuswa lamulo lake pankhani ya magazi. Zomwe anachitazo zinali zosemphana ndi njira yokha yogwiritsira ntchito magazi imene Mulungu analamula yomwe ndi ‘kutetezera’ machimo. (Levitiko 17:10-12; Genesis 9:3, 4) Mwa chifundo chake, Yehova, analandira nsembe zapadera zomwe zinaperekedwa chifukwa cha ochimwawo.​—1 Samueli 14:34, 35.

Inde, Yehova amafuna kuti tizimvera malamulo ake kaya zinthu zili bwino kapena ayi. Mtumwi Yohane anati: “Ichi ndi chikondi cha Mulungu, kuti tisunge malamulo ake.”​—1 Yohane 5:3.

[Chithunzi patsamba 30]

Sabata lililonse, ankaika mikate yopatulika yatsopano mu chihema