Pitani ku nkhani yake

Pitani ku mitu ya nkhani

Chiyembekezo Chimalimbikitsa

Chiyembekezo Chimalimbikitsa

 Chiyembekezo Chimalimbikitsa

CHIYEMBEKEZO chenicheni, chotchulidwa m’Baibulo, si kungolakalaka zinthu zosatsimikizirika kuti zichitikadi. Ndipo si kungodikirira zinazake, chifukwa sizonse zimene timadikirira zimene zimakhala zabwino.

Baibulo limaonetsa kuti anthu ambiri m’dzikoli alibe chiyembekezo chenicheni, cholimba. Imfa yatizinga anthufe ndipo popanda kudziwa zimene Mulungu watichitira, sitingakhale ndi chiyembekezo chilichonse. Solomo analongosola kuti kulimbana ndi mavuto athuwa popanda Mulungu ‘n’kwachabe!’​—⁠Mlaliki 12:⁠8.

Zonena za anthu ambiri osayembekezera Mulungu ndi lonjezo lake la chiukiriro zimafanana ndi zonena za anthu osamvera a ku Yerusalemu. Iwowa anatengeka maganizo ndi zosangalatsa m’malo molapa ndi kudzimvera chisoni pamene chilango cha Mulungu chowononga mzindawo chinayandikira. Iwo anati: “Tiyeni tidye ndi kumwa, chifukwa mawa tidzafa.” (Yesaya 22:13) Mtumwi Paulo anachenjeza kuti tisatengere maganizo a anthu okanikawa.​—⁠1 Akorinto 15:​32, 33.

Paulo sikuti anali kutsutsa kuti zinthu zina zimene anthu a m’dzikoli amayembekezera n’zofunika, ndipotu tikudziwa kuti zina mwa izo n’zabwino ndithu. M’malo mwake, iye anali kusonyeza kuti popanda Mulungu, zonse zimene munthu angayembekezere sizingaphule kanthu kalikonse pamapeto pake.

Amene Amatipatsa Chiyembekezo

Yehova Mulungu ndiye amatipatsa chiyembekezo chenicheni ndiponso ndiye angathe kukwaniritsa malonjezo ake onse ndiponso chiyembekezo cha anthu amene amamukhulupirira. Mwa chisomo chake, Mulungu anapatsa anthu “chisangalatso chosatha ndi chiyembekezo chokoma.” (2 Atesalonika 2:16) M’Malemba a Chihebri muli mawu ambiri ofotokoza za kuyembekeza, kukhulupirira ndiponso kudalira Yehova. Chifukwa choti ndi wachisomo kwa anthu ake, ngakhale pamene anthuwo ankapita kunja kwa dziko lawo kuukapolo chifukwa chosamumvera, iye anawauza kuti: “Ndidziwa malingiriro amene ndilingiririra inu, . . . malingiriro a mtendere, si a choipa, akukupatsani inu adzukulu ndi chiyembekezero.”​—⁠Yeremiya 29:⁠11.

Malonjezo a Yehova analimbikitsa chikhulupiriro ndiponso chiyembekezo cha Aisrayeli okhulupirika pamene anali muukapolo ku Babulo. Analimbikitsa kwambiri anthu monga Ezekieli ndi Danieli, pakuti Yehova anali atanena kuti: “Chilipo chiyembekezero cha chitsirizo chako, . . . ndipo ana ako adzafikanso ku malire awo.” (Yeremiya 31:17) Chiyembekezo chimenecho chinakwaniritsidwa pamene otsalira okhulupirika Achiyuda anabwerera kwawo mu 537 B.C.E. kuti akamangenso Yerusalemu ndi kachisi wake.​—⁠Ezara 1:​1-6.

Mtumiki wa Mulungu akakhala ndi chiyembekezo chodzalandira mphoto, sizitanthauza kuti akungofuna kupezapo mphotoyo ayi. Kuti munthu azimuona Mulungu m’njira yoyenereradi amayenera kudziwa kuti Mulungu n’ngokoma mtima mwachikondi ndiponso n’ngowolowa m’manja kwambiri. Munthuyo amayenera kukhulupirira kuti Mulungu alikodi komanso kuti “ali wobwezera mphoto iwo akum’funa Iye.”​—⁠Ahebri 11:⁠6.

Chiyembekezo N’chofunika pa Chikhulupiriro

Chiyembekezo n’chofunikanso kwambiri pa chikhulupiriro chifukwa ndicho chimayala maziko a chikhulupirirocho. (Ahebri 11:⁠1) Komano chikhulupiriro ndicho chimachititsa kuti chiyembekezo chikhale chenicheni ndiponso champhamvu. Mtumwi Paulo anatchula chitsanzo chabwino cha Abrahamu pofuna kulimbikitsa Akristu.

Panthawi imene kwa anthu zingaoneke kuti Abrahamu ndi mkazi wake Sara sakanathanso kukhala ndi ana, Malemba amati: “Amene anakhulupira nayembekeza zosayembekezeka, kuti iye akakhale kholo la mitundu yambiri ya anthu, monga mwa chonenedwachi, Mbewu yako idzakhala yotere.” Abrahamu ankadziwa kuti pankhani yobereka, iye pamodzi ndi mkazi wake Sara anali ndi matupi ‘akufa.’ Koma Abrahamu sanafooke pa chikhulupiriro. N’chifukwa chiyani sanafooke? “Poyang’anira lonjezo la Mulungu sanagwedezeka chifukwa cha kusakhulupirira, koma analimbika m’chikhulupiriro.”​—⁠Aroma 4:​18-20.

Kenaka mtumwi Pauloyo analimbikitsa Akristu kutengera chitsanzo chabwino cha Abrahamu pankhani ya chikhulupiriro ndi chiyembekezo. Iye anati: “Tikondwera m’chiyembekezo cha ulemerero wa Mulungu . . . ndipo chiyembekezo sichichititsa manyazi; chifukwa chikondi cha Mulungu chinatsanulidwa m’mitima  mwathu mwa mzimu woyera, amene wapatsidwa kwa ife.”​—⁠Aroma 5:​2, 5.

Chiyembekezo Chachikristu

Chiyembekezo cha Akristu ndiponso cha anthu onse chagona mwa Yesu Kristu. Mwayi wakuti munthu aliyense angakhale ndi moyo wosatha kumwamba kapena padziko lapansi pano kunalibe mpaka pamene Kristu Yesu ‘anaonetsera poyera moyo ndi chosavunda mwa Uthenga Wabwino.’​—⁠2 Timoteo 1:⁠10.

Chiyembekezo cha moyo wosatha ndiponso chisavundi kwa “olandirana nawo maitanidwe akumwamba” chili ndi maziko olimba zedi ndipo n’chosakayikitsa ngakhale pang’ono. (Ahebri 3:⁠1) Maziko ake ndiwo zinthu ziwiri zimene Mulungu sanganame ndipo zinthu zake ndizo lonjezo lake ndiponso lumbiro lake. Ndipo chiyembekezochi chagona mwa Kristu, amene tsopano ali ndi moyo wosafa kumwamba. Motero Malemba amati chiyembekezochi chili “ngati nangula wa moyo, chokhazikika ndi cholimbanso, ndi chakulowa m’katikati mwa chophimba [monga mmene mkulu wa ansembe ankalowera m’Malo Opatulikitsa pa Tsiku la Chitetezo]; mmene Yesu mtsogoleri analowamo chifukwa cha ife, atakhala mkulu wa ansembe nthawi yosatha monga mwa dongosolo la Melikizedeke.”​—⁠Ahebri 6:​17-20.

Ubwino Wokhalabe N’chiyembekezo

M’malemba ambiri Baibulo limalimbikitsa Akristu kuti ayenera kupitiriza kukhala ndi “chiyembekezo chimodzi.” (Aefeso 4:⁠4) Kuti atero Akristuwo amafunika kupitiriza kuchita khama ndiponso kulankhula mwaufulu komanso “kudzitamandira” pa chiyembekezo chawocho.​—⁠Ahebri 3:6; 6:⁠11.

Chiyembekezo cha munthu chimakula akamapirira masautso. Zimenezi zimachititsa kuti ayanjidwe ndi Mulungu, mwini chiyembekezo. (Aroma 5:​2-5) Chiyembekezo chinatchulidwa pamodzi ndi chikhulupiriro ndiponso chikondi monga khalidwe limodzi mwa makhalidwe atatu odziwikitsa mpingo wachikristu kuchokera panthawi imene zinatha mphatso za zozizwitsa zamzimu, zomwe zinalipo mumpingo wa m’zaka 100 zoyambirira.​—⁠1 Akorinto 13:⁠13.

Chiyembekezo n’chofunika kwambiri kwa Akristu. Chimayenderana ndi chimwemwe, mtendere ndiponso mphamvu ya mzimu woyera. (Aroma 15:13) Chimalimbikitsa anthu kulankhula mwaufulu ndi Mulungu pomupempha chisomo ndiponso chifundo chake. (2 Akorinto 3:12) Chimathandiza Mkristu kupirira mwachimwemwe, ngakhale zinthu zitathina bwanji. (Aroma 12:12) Monga mmene chisoti chinali kutetezera mutu wa msilikali, nacho chiyembekezo chimateteza maganizo, motero chimathandiza Mkristu kuti akhalebe wowongoka mtima.​—⁠1 Atesalonika 5:⁠8.

Chiyembekezo chimathandiza kuti Mkristu azikhala moyo wopanda zonyansa, pakuti amadziwa kuti Mulungu ndiponso Kristu, amene amapereka chiyembekezo, n’ngoyera komanso kuti sizingatheke kuti iyeyo atsanzire Mulungu n’kudzalandira mphotho koma kwinaku akuchita zonyansa kapena zosalungama. (1 Yohane 3:​2, 3) Chiyembekezo chimagwirizana kwambiri ndi khalidwe lofunika koposa la chikondi pakuti munthu amene amakondadi Mulungu amakhalanso ndi chiyembekezo mu malonjezo onse a Mulungu. Ndipo amawafunira zabwino abale ake a m’chikhulupiriro, amawakonda ndipo sakayikira kuti iwowo amamvera Kristu moona mtima.​—⁠1 Akorinto 13:​4, 7; 1 Atesalonika 2:19.