Pitani ku nkhani yake

Pitani ku mitu ya nkhani

“Mucherezane Wina ndi Mnzake”

“Mucherezane Wina ndi Mnzake”

 “Mucherezane Wina ndi Mnzake”

FEBE, Mkristu wa m’zaka 100 zoyambirira, anathedwa nzeru. Chinam’thetsa nzeru chinali chakuti anali paulendo wochokera ku Kenkreya, m’dziko la Girisi kupita ku Roma, koma sankadziwana ndi Akristu anzake ku Romako. (Aroma 16:1, 2) Edgar Goodspeed, yemwe anamasulira Baibulo linalake anati, “[nthawi imeneyo] ku Roma, anthu anali oipa ndiponso ankhanza kwambiri, ndipo malo ogona alendo sanali malo opezekako mkazi wolongosoka, makamaka wachikristu.” Motero kodi Febe akanakagona kuti?

M’nthawi za Baibulo anthu ankayenda kwambiri. Yesu Kristu ndi ophunzira ake ankayenda kwambiri polalikira uthenga wabwino ku Yudeya konse ndiponso ku Galileya konse. Pambuyo pa iwowa, panabwera amishonale achikristu monga Paulo amene uthengawu anakafika nawo mpakana kumadera ozungulira nyanja ya Mediterranean, kuphatikizapo Roma, lomwe linali likulu la Ufumu wa Roma. Kodi Akristu a m’nthawi imeneyo ankagona kuti akamayenda ulendo, kaya wongozungulira m’gawo la Ayuda lomwelo kapena wotuluka m’gawolo? Kodi ankakumana ndi mavuto otani pofuna kupeza malo ogona? Kodi tingaphunzire chiyani kwa Akristu amenewa pankhani yochereza alendo?

“Lero Ndiyenera Kukhala M’nyumba Mwako”

Buku la Mtanthauziramawu wa Chinyanja limati kuchereza ndi ‘kusamala mlendo pocheza naye mom’sangalatsa kuti aiwale kwawo.’ Ndipotu kuyambira kale anthu olambira Yehova moona akhala akudziwika ndi khalidwe limeneli. Mwachitsanzo, Abrahamu, Loti ndi Rebeka anali anthu akhalidwe lotere. (Genesis 18:1-8; 19:1-3; 24:17-20) Yobu ananena mawu otsatirawa pankhani ya mmene iye ankaonera alendo: “Mlendo sakagona pakhwalala, koma ndinatsegulira wam’njira pakhomo panga.”​—Yobu 31:32.

Nthawi imeneyo anthu akakhala alendo, ankangodikirira panja, pabwalo la mzinda ndipo Aisrayeli anzawo ankawaitanira kunyumba kwawo. (Oweruza 19:15-21) Nthawi zambiri anthu akaitana alendo kunyumba kwawo ankawasambitsanso mapazi alendowo n’kuwapatsa chakudya ndi zakumwa. Ziweto zimene alendowo ayenda nazo ankazipatsanso chakudya. (Genesis 18:4, 5; 19:2; 24:32, 33) Alendo amene sankafuna kuvutitsa amene akuwachereza ankatengeratu zonse zofunikira paulendowo, monga mkate ndi vinyo komanso udzu woti abulu awo azidya. Motero ankangofuna malo oti agone usiku basi.

Ngakhale kuti Baibulo silinena kawirikawiri za mmene Yesu ankapezera malo ogona pa maulendo ake olalikira, iye ndi ophunzira ake ankayenera kupeza kogona. (Luka 9:58) Atapita ku Yeriko, Yesu anangomuuza Zakeyu kuti: “Lero ndiyenera kukakhala m’nyumba mwako.” Zakeyu analandira mlendo wakeyu ‘mokondwera.’ (Luka 19:5, 6) Nthawi zambiri Yesu ankapita kukacheza kwa Mariya, Marita ndi Lazaro ku Betaniya. Iwowa anali anzake. (Luka 10:38; Yohane 11:1, 5, 18) Ndipo zikuoneka kuti ku Kapernao, Yesu ankagona kwa Simoni Petro.​—Marko 1:21, 29-35.

 Zimene Yesu anaphunzitsa atumwi ake 12 zokhudza utumiki zimasonyeza kuti iwowo ankadziwa mmene akawalandirire mu Israyeli. Yesu anawauza kuti: “Musatenge golide kapena siliva kapena mkuwa m’zikwama zanu za ndalama, kapena thumba la chakudya cha paulendo, kapena malaya awiri amkati, kapena nsapato kapena ndodo; chifukwa wantchito ayenera kulandira chakudya chake. Mukalowa mu mzinda kapena mudzi uliwonse, fufuzani mmenemo yemwe ali woyenerera, ndipo mukhalebe momwemo kufikira nthawi yochoka.” (Mateyu 10:9-11) Yesu ankadziwa kuti anthu a mtima wabwino akalandira ophunzira akewo, ndipo akawapatsa chakudya, malo ogona, ndiponso zinthu zina zofunikira.

Komabe, patsogolo pake inadzafika nthawi imene olengeza uthenga wabwino anayenera kudzipezera okha chakudya ndiponso kudzisamalira okha akakhala paulendo. Podziwa kuti patsogolo anthu om’tsatira adzayamba kudedwa, ndiponso podziwa kuti ntchito yolalikira idzafika m’madera ena a kunja kwa Israyeli, Yesu anati: “Iye amene ali ndi thumba la ndalama, alitenge, ndi thumba la kamba lomwe.” (Luka 22:36) Panthawiyi, kuti alalikire uthenga wabwino, anayenera kuyenda maulendo aatali ndiponso kupeza malo ogona.

“Cherezani Alendo”

M’zaka 100 zoyambirira, anthu ankayendayenda kwambiri chifukwa chakuti nkhondo zinachepa ndiponso misewu yowaka inali ponseponse mu Ufumu wa Aroma. * Chifukwa cha kuchuluka kwa anthu oyenda maulendo, pankafunika malo ogona ambiri. Motero m’mphepete mwa misewu ikuluikulu munkakhala malo ogona omwe anali otalikirana mtunda woyenda tsiku limodzi. Komabe buku lakuti, The Book of Acts in Its Graeco-Roman Setting limati: “Zimene mabuku amanena zokhudza malo amenewa n’zomvetsa chisoni. Mabuku ndiponso zokumbidwa m’mabwinja nthawi zambiri zimasonyeza kuti malo ogonawa ankakhala osambuka ndiponso osasamalika. Pogona pake sipanali pabwino, anali ndi nsikidzi, zakudya ndiponso zakumwa zake zinali zosalongosoka, eni ake ndiponso antchito awo anali osakhulupirika, anthu ogonako ankakhala anthu osalongosoka, ndipo nthawi zambiri kunkachitika khalidwe loipa.” Motero n’zosachita kufunsa kuti munthu aliyense wakhalidwe labwino ankayesetsa kupewa kugona m’malo amenewa.

Motero n’zosadabwitsa kuti Malemba amalimbikitsa Akristu mobwerezabwereza kuti azicherezana. Paulo analimbikitsa Akristu ku Roma kuti: “Patsani zosowa oyera mtima; cherezani aulendo.” (Aroma 12:13) Iye anakumbutsa Akristu achiyuda kuti: “Musaiwale kuchereza alendo; pakuti mwa ichi ena anachereza angelo osachidziwa.” (Ahebri 13:2) Petro analimbikitsa olambira anzake kuti, “mucherezane wina ndi mnzake, osadandaula.”​—1 Petro 4:9.

Komabe panali anthu ena amene sanali oyenera kuwachereza. Mtumwi Yohane anati: “Yense wakupitirira, wosakhala m’chiphunzitso cha Kristu . . . musam’landire iye kunyumba, ndipo musam’lankhule. Pakuti iye wakum’lankhula ayanjana nazo ntchito zake zoipa.” (2 Yohane 9-11) Ponena za anthu osalapa, Paulo analemba kuti: “Musayanjane naye, ngati wina wotchedwa mbale ali wachigololo, kapena wosirira, kapena wopembedza mafano, kapena wolalatira, kapena woledzera, kapena wolanda, kungakhale kukadya naye wotere, iyayi.”​—1 Akorinto 5:11.

Anthu achinyengo ndiponso anthu ena otere ayenera kuti ankafuna kudyera masuku pamutu Akristu oona chifukwa cha kukoma mtima kwawo. Chikalata china cholembedwa m’ma 100 C.E. chotchedwa The Didache, kapena kuti Teaching of the Twelve Apostles (Chiphunzitso cha Atumwi 12), chomwe chimalongosola za chikhulupiriro cha Akristu, chimanena kuti wolalikira amene ali paulendo anayenera kuloledwa kugona panyumba ya munthu kwa “tsiku limodzi, apo ayi zikavuta, masiku awiri.” Pambuyo pake, akamanyamuka, “m’patseni kamba wa paulendo basi . . . Akapempha ndalama, dziwani kuti ndi mneneri wonyenga.” Chikalatachi chinapitirira kunena kuti: “Ngati akufuna kukhazikika kwanuko ndipo ngati ali ndi luso la ntchito inayake, m’patseni ntchito yoti azigwira kuti apeze chakudya. Koma ngati alibe luso la ntchito iliyonse m’thandizeni malingana ndi mmene inuyo mukuonera, kuti pakati panu pasapezeke munthu wongokhala manja lende chifukwa choti ndi Mkristu. Koma ngati  munthuyu atakana kutero, ndiye kuti akungofuna kudyerapo pa Chikristu; motero samalani naye.”

Mtumwi Paulo ankayesetsa kuti akapita m’mizinda inayake n’kukakhalako nthawi yaitali, anthu omusamalira kumeneko asamawononge chuma chawo. Iye ankagwira ntchito yosoka mahema kuti azidzithandiza yekha. (Machitidwe 18:1-3; 2 Atesalonika 3:7-12) Pofuna kuthandiza Akristu anzawo a paulendo, zikuoneka kuti Akristu oyambirira ankalemba makalata oikira umboni munthuyo, monga kalata imene Paulo analemba yonena za Febe. M’kalatamo Paulo analemba kuti: “Ndipereka kwa inu Febe, mlongo wathu . . . kuti mum’landire iye mwa Ambuye . . . ndi kuti mum’thandize m’zinthu zilizonse adzazifuna kwa inu.”​—Aroma 16:1, 2.

Madalitso Obwera Chifukwa Chochereza

Amishonale a m’zaka 100 zoyambirira ankakhulupirira kuti Yehova aziwapatsa zonse zimene akufunikira. Koma kodi amishonalewa ankawerengera Akristu anzawo kuti angawachereze? Inde, mwachitsanzo Lidiya analola kuti Paulo komanso anthu ena azifikira kunyumba kwake. Ku Korinto, mtumwiyu ankakhala kwa Akula ndi Priskila. Munthu wina woyang’anira akaidi ku Filipi anakonzera chakudya Paulo ndi Sila. Paulo analandiridwa ndi manja awiri ndi Yasoni ku Tesalonika, ndi Filipo ku Kaisareya, komanso analandiridwa ndi Mnaso m’dera limene munadutsa msewu wa pakati pa Kaisareya ndi Yerusalemu. Akupita ku Roma, abale anamusamalira Paulo ku Potiyolo. Anthu amene anamulandira Paulowa ayenera kuti anapindula kwambiri mwauzimu panthawi zimenezi.​—Machitidwe 16:33, 34; 17:7; 18:1-3; 21:8, 16; 28:13, 14.

Munthu wina wa maphunziro apamwamba dzina lake Frederick F. Bruce anati: “Anzake a Paulowa, amenenso ankagwira nawo ntchito ndiponso amene ankamusunga kunyumba kwawo analibe cholinga china chilichonse chapadera pomuthandiza kwambiri chonchi; chachikulu chinali kumukonda basi, komanso kukonda Mbuye amene Pauloyu ankatumikira. Iwo ankadziwa kuti potumikira Paulo ndiye kuti akutumikiranso Mbuyeyo.” Ichitu n’chifukwa chabwino kwambiri chokhalira ochereza.

Masiku ano timafunikirabe kukhala ochereza. Pali nthumwi zambiri za Mboni za Yehova zimene m’maulendo awo zimalandiridwa ndi manja awiri ndi Mboni zinzawo. Pali ofalitsa Ufumu ena amene amayendera ndalama zawo kukalalikira m’madera amene sikufikafika uthenga wabwino. Timapindula kwambiri polola anthu oterewa kukhala nawo m’nyumba zathu, ngakhale zitakhala kuti sizapamwamba. Kuchereza alendo m’njira zina monga kungowaitanira chakudya chimene inuyo mumadya nthawi zonse kumathandiza kwambiri kupeza mpata ‘wotonthozana’ ndiponso wosonyeza kuti timakonda abale athu ndi Mulungu wathu. (Aroma 1:11, 12) Amene amapindula kwambiri pa macheza oterewa ndi ocherezawo, chifukwa choti “kupatsa kutidalitsa koposa kulandira.”​—Machitidwe 20:35.

[Mawu a M’munsi]

^ ndime 11 Akuti mmene chinkafika chaka cha 100 C.E., panali misewu yowaka ya Aroma yaitali mtunda wokwana makilomita 80,000.

[Chithunzi patsamba 23]

Akristu ‘amachereza alendo’