Pitani ku nkhani yake

Pitani ku mitu ya nkhani

Achinyamata Lolani Kuti Makolo Anu Akuthandizeni Kuteteza Mtima Wanu

Achinyamata Lolani Kuti Makolo Anu Akuthandizeni Kuteteza Mtima Wanu

 Achinyamata Lolani Kuti Makolo Anu Akuthandizeni Kuteteza Mtima Wanu

KODI mumaganiza kuti ndi vuto lalikulu liti limene woyendetsa sitima za pamadzi amakhala nalo? Kodi n’kuwoloka bwinobwino nyanja yaikulu? Osati kwenikweni. Nthaŵi zambiri sitima za pamadzi zimachita ngozi pafupi ndi gombe, osati pakatikati pa nyanja. Ndipotu, kukocheza sitima ku gombe kungakhale koopsa kwambiri kuposa kuteretsa ndege. N’chifukwa chiyani zili choncho?

Woyendetsa sitima ya pamadzi asanakocheze bwinobwino sitima ku gombe, amafunika kupeŵa zinthu zimene zingamuchititse ngozi pa doko limene akufuna kukocheza sitimayo. Iye amafunika kudziŵa mmene madzi akuyendera pansi panyanja komanso amafunika kuwongolera bwino sitimayo kuti isagundane ndi sitima zina. Iye amafunika kudutsa kutali ndi malo amene mchenga unaunjikana wambiri, miyala, ndiponso malo amene pali sitima zimene zinamira. Komanso zinthu zimakhala zovuta kwambiri, ngati uli ulendo wake woyamba kupita ku gombelo.

Kuti athane ndi mavuto ameneŵa, woyendetsa sitima wanzeru angapemphe thandizo kwa katswiri yemwe akulidziŵa bwino gombelo. Katswiriyo amathandiza kuyendetsa sitimayo komanso amam’patsa woyendetsa sitimayo malangizo abwino kwambiri. Aŵiriŵa amathandizana kupeŵa malo angozi ndipo amawongolera sitimayo kuti idutse bwinobwino pa malo aliwonse ovuta kudutsa popita kugombeko.

Malangizo ofunika kwambiri amene katswiri amapatsa woyendetsa sitima akusonyeza thandizo limene Akristu achinyamata omwe ayenera kudziŵa bwino mmene angapeŵere mavuto osiyanasiyana m’moyo wawo amafunikira. Kodi thandizo limeneli ndi lotani? N’chifukwa chiyani achinyamata akufunika thandizoli?

Tiyeni tipitirize chitsanzo chathu cha sitima ya pamadzi. Ngati ndinu wachinyamata, muli ngati woyendetsa sitima ya pamadzi chifukwa chakuti idzafika nthaŵi imene muyenera kudzaima panokha. Ndipo makolo anu ali ndi ntchito yofanana ndi ya katswiri woyendetsa sitima za pamadzi, yokutsogolerani kuthana ndi zinthu zovuta kwambiri zimene mungakumane nazo pamoyo wanu. Komabe, panthaŵi yaunyamata, zingakuvuteni kumvera zimene makolo anu akukulangizani. Chifukwa chiyani zimakhala choncho?

Nthaŵi zambiri, vuto limakhala ndi mtima. Mtima wanu wophiphiritsira ungakulimbikitseni kufuna kuchita zinthu zoletsedwa kapena kusamvera chilichonse chimene mukuona kuti chikukuikani pampanipani. Baibulo limati: “Ndingaliro ya mtima wa munthu ili yoipa kuyambira pa unyamata wake.” (Genesis 8:21) Yehova  amaneneratu kuti m’tsogolo mwanu muli mavuto aakulu. Iye amachenjeza kuti: “Mtima ndiwo wonyenga koposa, ndi wosachiritsika.” (Yeremiya 17:9) Mtima umalakalaka zinthu zoipa ndiponso ungapangitse wachinyamata kuganiza kuti n’ngozindikira kuposa makolo ake, ngakhale kuti makolowo aona zambiri pamoyo. Komabe, pali zifukwa zomveka zimene muyenera kufunira thandizo la makolo anu panthaŵi yovuta yaunyamata.

N’chifukwa Chiyani Muyenera Kumvera Makolo Anu?

Chifukwa chachikulu pa zonse n’chakuti Woyambitsa banja, Yehova, amati muzimvera zimene makolo anu amakulangizani. (Aefeso 3:15) Popeza Mulungu anasankha makolo anu kuti azikusamalirani, iye amakulangizani kuti: “Ananu, mverani akukubalani mwa Ambuye, pakuti ichi n’chabwino.” (Aefeso 6:1-3; Salmo 78:5) Ngakhale kuti mwina panopo mwasinkhukirapo ndithu, makolo anu akadali ndi udindo wokutsogolerani, ndipo mufunika kuwamvera. Mawu achigiriki amene mtumwi Paulo anagwiritsira ntchito ponena kuti ana angatanthauze ana a misinkhu yonse. Mwachitsanzo, Yesu pa Mateyu 23:37, ananena anthu a ku Yerusalemu kuti “ana” a Yerusalemuyo, ngakhale kuti ambiri anali akuluakulu.

Anthu ambiri okhulupirika akale anapitirizabe kumvera makolo awo ngakhale anthuwo anali atakula. Yakobo, ngakhale kuti anali wamkulu, anadziŵa kuti anayenera kumvera zimene Atate ake analamula, zoti asakwatire mkazi wosalambira Yehova. (Genesis 28:1, 2) Mosakayikira, Yakobo analinso ataona kuti zimene mchimwene wake anachita zokwatira akazi achikunja achikanani zinali kuwasoŵetsa mtendere makolo ake.​—Genesis 27:46.

Kuwonjezera pamfundo yakuti Mulungu wawapatsa udindo wokutsogolerani, makolo anu achikristu ndi amene ali oyenera kwambiri kukulangizani. Izi zili choncho chifukwa chakuti amakudziŵani bwino kwambiri ndiponso mosakayikira asonyeza kwa zaka zambiri kuti amakukondanidi. Monga katswiri woyendetsa sitima za pamadzi, iwo amanena zimene anakumana nazo. Iwowo anakumanapo ndi “zilakolako za unyamata.” Ndipo popeza ndi Akristu oona, adzionera okha kufunika kotsatira mfundo za m’Baibulo.​—2 Timoteo 2:22.

Popeza kuti thandizo labwino lotereli muli nalo pafupi, mungathe kulimbana bwinobwino ngakhale ndi zinthu zovuta kwambiri pamoyo wanu. Titenge chitsanzo cha ubwenzi wa mwamuna ndi mkazi. Kodi makolo achikristu angakuthandizeni bwanji pankhani yovuta imeneyi?

Kukopeka ndi Mwamuna Kapena Mkazi

Akatswiri oyendetsa sitima za pamadzi amalangiza oyendetsa sitima kuti asamadutse pafupi ndi malo amene mchenga unaunjikana wambiri chifukwa chakuti mchenga umapusitsa, ndipo umasunthasuntha. Mofanana ndi zimenezi, makolo anu amafuna kuti musamayandikire zinthu zimene zingakusokonezeni maganizo. Mwachitsanzo, makolo amadziŵa kuti m’posavuta kukondana kwambiri ndi mwamuna kapena mkazi ndiponso kuti chikondi chotere chimakhala chovuta kuchimvetsa. Koma mukangoyamba zimenezi, mungagwe nazo m’mavuto.

Chitsanzo cha Dina chimasonyeza kuipa koyandikira malo angozi. Mwina chidwi chofuna kudziŵa zinthu ndiponso kufuna kusangalala n’zimene zinapangitsa Dina kukacheza ndi atsikana achikanani, amene mosakayikira anali otayirira. Zimene poyamba zinali kuoneka ngati zosangalatsa zosapweteketsa posapita nthaŵi zinam’gwetsera m’mavuto aakulu. Iye anagwiriridwa ndi mnyamata ‘wolemekezedwa koposa’ kumeneko.​—Genesis 34:1, 2, 19.

Ngozi zimenezi zachuluka chifukwa chakuti masiku ano anthu akulimbikitsa kwambiri chigololo. (Hoseya 5:4) Achinyamata ambiri  angakupangitseni kuganiza kuti kusangalala ndi amuna kapena akazi ndiko chinthu chosangalatsa koposa. Mtima wanu ungakopeke ndi maganizo ofuna kucheza panokha ndi munthu amene mumamuona kuti ndi wooneka bwino. Koma makolo amene amakukondani angakuletseni kucheza ndi achinyamata amene satsatira mfundo za Mulungu.

Laura anavomereza kuti chidwi chofuna kudziŵa zinthu chikhoza kupusitsa achinyamata kuti asaone mavuto amene angakhalepo. “Atsikana a m’kalasi mwathu amandiuza kuti anachezera kuvina ndi anyamata ena ooneka bwino, ndipo amanena mokhala ngati kuti zinali zosangalatsa mwakuti sadzaiwala mpaka kalekale. Ndikudziŵa kuti nthaŵi zambiri amangokokomeza, komabe mtimawu umalakalaka nditachita nawo zimenezi ndipo ndimaganiza kuti mwina ndikumanidwa zabwino. Ngakhale kuti ndikudziŵa kuti makolo anga amachita bwino kundiletsa kupita malo amenewo, ndimasirirabe n’tapitako.”

Sitima ya pamadzi ilibe mabuleki, choncho imatenga nthaŵi kuti iime. Makolo amadziŵa kuti ndi mmenenso chimakhalira chikondi. Buku la Miyambo limayerekezera munthu wochita zinthu chifukwa cha chikondi chonyanyira ndi n’gombe yopita kukaphedwa. (Miyambo 7:21-23) Simungafune kuti zimenezi zikuchitikireni, zimene zingasokoneze maganizo ndi moyo wanu wauzimu. Makolo anu angathe kudziŵa bwinobwino kuti mtima wanu wayamba kukunyengani pankhani imeneyi, ndipo angakulangizeni. Ndi nzeru kuwamvera kuti mupeŵe mavuto.​—Miyambo 1:8; 27:12.

Mumafunikanso kuti makolo anu akuthandizeni polimbana n’kuti musatengere zochita za anzanu. Kodi angakuthandizeni bwanji?

Anzanu Angakusokonezeni Mosavuta

Mphepo kapena mafunde amphamvu angapatutse sitima ya pamadzi n’kuichititsa kuti iloŵere kwina. Kuti zimenezi zisachitike, ayenera kuiwongolera bwinobwino sitimayo. Moteronso, achinyamata anzanu angathe kukusocheretsani mwauzimu mukapanda kudziteteza.

Monga taonera zimene zinachitikira Dina, ‘anzanu akakhala opusa mudzapwetekedwa.’ (Miyambo 13:20) Kumbukirani kuti m’Baibulo, mawu akuti “opusa” amatanthauza munthu wosadziŵa Yehova kapena amene wafuna dala kusayenda m’njira Zake.

 Komabe, n’zovuta kukana kutsatira maganizo kapena zochita za anthu a m’kalasi mwanu. María José anati: “Ndinkafuna kuti achinyamata anzanga azindikonda. Popeza sindinkafuna kuti anzangawo azindiona kuti ndine munthu wochita zinthu zachilendo, ndinatengera kwambiri zochita zawo.” Mosadziŵa, mungatengere anzanu pankhani ya nyimbo zimene mumakonda, zovala zanu, kapenanso malankhulidwe anu. Mwina mumamasuka kukhala ndi achinyamata a msinkhu wanu. Zimenezi sizodabwitsa, koma zingakuchititseni kutengera zochita zawo, zimene mungagwe nazo m’mavuto.​—Miyambo 1:10-16.

Caroline amakumbukira vuto limene anali nalo zaka zingapo zapitazo: “Kuyambira ndili ndi zaka 13, atsikana ambiri amene ndinkacheza nawo anali ndi zibwenzi, ndipo kwa zaka zingapo ankakhalira kundikakamiza kuti inenso ndikhale ndi chibwenzi. Komabe, mayi anga ananditsogolera panthaŵi yovuta imeneyi. Anali kukhala nane maola ambiri kumva zonena zanga, kukambirana nane, ndiponso kundithandiza kuona kufunika kosathamangira kuchita zimenezi mpaka nditakhwima.”

Mofanana ndi amayi a Caroline, makolo anu angaone kuti akufunika kukuchenjezani pankhani yotengera zochita za anzanu, angafunike kukuletsani kuchita zinthu zinazake kapenanso kucheza ndi anthu enaake. Nathan akukumbukira maulendo angapo amene anayambana ndi makolo ake pankhani zimenezi. Iye anati: “Anzanga nthaŵi zambiri ankandiitana kuti ndipite nawo kocheza, koma makolo anga ankandiletsa kuyenda ndi gulu lalikulu la anthu kapena kupita ku phwando la anthu ambiri lopanda munthu woyang’anira. Panthaŵiyo, sindinkamvetsa chifukwa chake makolo anga anali ovuta kusiyana ndi makolo ena.”

Komabe, patapita nthaŵi Nathan anamvetsa chifukwa chake. Iye anati: “Ndikudziŵa kuti lemba lakuti ‘utsiru umamangidwa mumtima mwa mwana’ linkagwirizanadi ndi zochita zanga. Utsiru umenewu umaonekera kwambiri anyamata akapita koyenda ali kagulu. Mmodzi akayambitsa kuchita chinthu choipa, wina amachita choipa kuposa pamenepo, ndipo winanso amachita zoposa zimene mnzakeyo wachita. Posapita nthaŵi onse amafuna kuchita zomwezo. Ngakhale achinyamata amene amanena kuti amatumikira Yehova amatha kuchita nawo zimenezi.”​—Miyambo 22:15.

Nathan ndi María José zinkawapweteka mtima kwambiri makolo awo akawakaniza kuchita zinthu zimene anzawo ananena. Komabe, iwo anali kumvera makolowo, ndipo patapita nthaŵi anasangalala kuti anali kumvera. Mwambi wina umati: “Tchera makutu ako, numvere mawu a anzeru, nulozetse mtima wako kukadziŵa zanga.”​—Miyambo 22:17.

Ndi Ofunika Kupatsidwa Ulemu

Sitima ya pamadzi imene yapendekeka imavuta kuiwongolera, ndipo ngati yapendekeka kwambiri, ikhoza kutembenuzika. Chifukwa chakuti ndife opanda ungwiro, tonsefe sizitivuta kuchita  zinthu zongotikomera ifeyo ndiponso zinthu zoipa. Ngakhale ndi choncho, achinyamata zingawayendere bwino pamoyo wawo, ngati atatsatira bwinobwino malangizo a makolo awo.

Mwachitsanzo, makolo anu angakuthandizeni kukana maganizo akuti pakati pa njira yopapatiza yopita nayo kumoyo ndi pa njira yotakata yopita nayo kuchiwonongeko, pali njira ina. (Mateyu 7:13, 14) Si nzeru kuganiza kuti mungachite pang’ono zoipa koma osapitirira muyeso, komanso kuti ‘mungalaŵe’ koma osameza. Anthu amene amachita zimenezi ndiye kuti ‘akukayikakayika,’ chifukwa akutumikira Yehova komanso kwinaku akukonda dziko ndi zinthu za m’dziko, ndipo m’posavuta kuti amire mwauzimu. (1 Mafumu 18:21; 1 Yohane 2:15) N’chifukwa chiyani zimenezi zimachitika? Chifukwa chokonda kuchita zoipa.

Zimene timalakalaka monga anthu opanda ungwiro timazilakalaka kwambiri tikapanda kudziletsa. ‘Mtima wathu wonyengawu’ sukhutira ndi kungolaŵa kokha. Umafuna zambiri. (Yeremiya 17:9) Tikangoyamba kupatuka mwauzimu, tingayambe kutengera kwambiri zochita za dziko. (Ahebri 2:1) Mwina simungadziŵe kuti mwapendekeka mwauzimu, koma mwachionekere makolo anu achikristu angadziŵe. N’zoona kuti iwo angavutikirepo kuphunzira zinthu zina zamakono kusiyana ndi inuyo, komabe amadziŵa bwino za mmene mtima umanyengera kuposa inuyo. Ndipo akufuna kukuthandizani ‘kulunjikitsa mtima wanu m’njira’ imene ingakutsogolereni kumoyo.​—Miyambo 23:19.

Komabe musayembekezere makolo anu kusalakwitsa zinthu pokulangizani pankhani zovuta, monga zokhudza nyimbo, zosangalatsa, ndiponso kudzikongoletsa. Makolo anu sangakhale anzeru ngati Solomo kapena oleza mtima ngati Yobu. Monga katswiri woyendetsa sitima za pamadzi, iwo angakhwimitse zinthu poopa ngozi. Komabe, malangizo awo angakuthandizeni kwambiri mukamamvera ‘mwambo wa atate wanu, ndi kusasiya chilangizo cha amayi anu.’​—Miyambo 1:8, 9.

Achinyamata ena anganyoze makolo awo. Komabe, ngati makolo anu akuyesetsa kutsatira Malemba, amakhala nanu m’zochitika zonse, nthaŵi zonse, pamene mukukumana ndi mavuto alionse. Monga woyendetsa sitima ya pamadzi amene akulangizidwa ndi katswiri, mumafunika makolo anu kukutsogolerani, kukuuzani njira yabwino. Ndipo zimenezi zingakupindulitseni koposa.

“Pakuti nzeru idzaloŵa m’mtima mwako, moyo wako udzakondwera ndi kudziŵa, kulingalira kudzakudikira, kuzindikira kudzakutchinjiriza; kukupulumutsa ku njira yoipa, kwa anthu onena zokhota; akusiya mayendedwe olungama, akayende m’njira za mdima . . . Pakuti oongoka mtima adzakhala m’dziko, angwiro nadzatsalamo.”​—Miyambo 2:10-13, 21.

[Chithunzi patsamba 22]

Kutengera zochita za achinyamata anzanu kungakugwetseni mwauzimu

[Chithunzi patsamba 23]

Kumbukirani zimene zinachitikira Dina

[Chithunzi patsamba 24]

Mofanana ndi woyendetsa sitima ya pamadzi amene amafunsira malangizo kwa katswiri, achinyamata ayenera kufunsira malangizo kwa makolo awo

[Mawu a Chithunzi patsamba 24]

Photo: www.comstock.com