Pitani ku nkhani yake

Pitani ku mitu ya nkhani

Ndani Amene Akupatsa Mulungu Ulemerero Masiku Ano?

Ndani Amene Akupatsa Mulungu Ulemerero Masiku Ano?

 Ndani Amene Akupatsa Mulungu Ulemerero Masiku Ano?

Muyenera inu, Ambuye wathu, ndi Mulungu wathu, kulandira ulemerero ndi ulemu ndi mphamvu.”​—CHIVUMBULUTSO 4:11.

1, 2. (a) Kodi ndi zitsanzo ziti zimene zikusonyeza kuti anthu amapanga zinthu motengera zachilengedwe? (b) Kodi pali funso lotani, ndipo yankho lake ndi lotani?

TSIKU lina m’ma 1940, katswiri wina wokonza makina wa ku Switzerland, dzina lake George de Mestral, anatenga galu wake n’kupita naye kokayenda, powongola miyendo. Atabwerera kunyumba, anaona kuti zovala zake komanso bweya wa galu uja zinali ndi tizitsotso tangati chisoso. Pofuna kutionetsetsa tizitsotsoti, iye anatitenga n’kutiika pa makina oonera zinthu zing’onozing’ono ndipo anachita chidwi kwambiri ndi timinga ting’onoting’ono tomwe tinkagwira ku chinthu chilichonse chopotanapotana. M’kupita kwa nthaŵi de Mestral anatulukira njira yopangira mtundu winawake wa zipi amene potseka amachita kumata ndipo potsegula amangomatula. Sikuti ndi de Mestral yekha amene anapanga zinthu potengera zachilengedwe. Ku United States, anthu aŵiri apachibale, omwe dzina la bambo wawo linali Wright, anapanga ndege pambuyo pophunzira bwino mmene mbalame zikuluzikulu zimaulukira. Mu mzinda wa Paris ku France, katswiri wina wokonza makina wa ku France komweko, dzina lake Alexandre-Gustave Eiffel, anapanga nsanja yomwe imadziŵika ndi dzina lake. Anapanga nsanjayi potengera mmene mafupa a pantchafu amanyamulira thupi lonse la munthu.

2 Zitsanzo zimenezi zikungosonyeza zimene anthu amachita kaŵirikaŵiri, zopanga zinthu motengera zachilengedwe. Komano, m’pomveka kufunsa kuti: Kodi anthu opanga zinthu zatsopano amatamanda amene anapanga tizitsotso ting’onoting’ono tangati chisoso, mbalame zikuluzikulu, fupa la pantchafu ya munthu, ndiponso zinthu zina zonse zochititsa kaso zachilengedwe zomwe anthu anatengera popanga zinthu zambiri? Zomvetsa chisoni n’zakuti Mulungu masiku ano kaŵirikaŵiri satamandidwa, kapena kupatsidwa ulemerero pa zimene anthu anatengera kwa iye popanga zinthu zawo.

3, 4. Kodi mawu a Chihebri omwe anawamasulira kuti “ulemerero” amatanthauza chiyani, ndipo mawu ameneŵa amatanthauza chiyani akawatchula pofotokoza za Yehova?

3 Ena angafunse kuti, ‘N’chifukwa chiyani Mulungu amafunika kupatsidwa ulemerero? Kodi Mulungu sali nawo kale ulemerero?’ Ndi zoona kuti Yehova ndi Waulemerero kwambiri m’chilengedwe chonse, komatu izi sizikutanthauza kuti umu ndi mmene anthu onse amamuonera. M’Baibulo, mawu a Chihebri omwe anawamasulira kuti “ulemerero,” kwenikweni amatanthauza “kulemera.” Amawatchula pa chinthu chilichonse chimene chimachititsa munthu kuoneka wolemerera kapena kuoneka kuti ndi wofunika kwa anthu ena. Mawu amenewo akawatchula pofotokoza za Mulungu, amakhala akunena za zinthu zimene zimapangitsa Mulunguyo kukhala wogometsa kwa anthu.

 4 Masiku ano pali anthu ochepa chabe amene amati akaona zinthu zinazake amaganiza kuti Mulungu ndi wogometsa. (Salmo 10:4; 14:1) Ndipotu, anthu otchuka, ngati amakhulupirira n’komwe kuti kuli Mulungu, nthaŵi zambiri amalimbikitsa anthu kusapereka ulemu kwa Mlengi waulemerero wa chilengedwe chonse. Kodi iwo achita zimenezi motani?

‘Alibe Mawu Akuŵiringula’

5. Posafuna kuvomereza kuti kuli Mlengi, kodi akatswiri ambiri a sayansi amati zinthu zodabwitsa za m’chilengedwechi zinakhalako bwanji?

5 Akatswiri ambiri a sayansi amaumirira kunena kuti kulibe Mulungu. Ndiyeno, kodi amafotokoza kuti zinthu zodabwitsa za m’chilengedwechi, kuphatikizapo anthu, zinakhalako bwanji? Iwo amati zinthu zimenezi zinachita kusanduka kuchokera ku zinthu zina, moti zinangokhalako zokha popanda wina wozipanga. Mwachitsanzo, mwamuna wina amene amakhulupirira chiphunzitso chimenechi, dzina lake Stephen Jay Gould, analemba kuti: “Anthufe kuti tikhalepo n’chifukwa chakuti nsomba zina zosiyana ndi nsomba zonse zinali ndi zipsepse zodabwitsa kwambiri zomwe zinasanduka miyendo ya zamoyo zapamtunda . . . Tingafunefune yankho ‘lomveka’ pankhaniyi, koma sitingalipeze.” Mofanana ndi mfundo imeneyi, Richard E. Leakey ndi Roger Lewin analemba kuti: “Mwinamwake anthufe tinakhalapo mwangozi yaikulu imene inachitika m’zamoyo zina.” Ngakhale akatswiri ena a sayansi amene amachita chidwi ndi kukongola ndiponso mmene zinthu za m’chilengedwemu zinapangidwira, iwo satamanda nazo Mulungu.

6. Kodi n’chiyani chimakopa anthu ambiri kuti asiye kupatsa Mulungu ulemerero umene amayenera kulandira popeza kuti ndiye Mlengi?

6 Anthu ophunzira kwambiri akamafotokoza kuti zinthu zamoyo zinachita kusanduka kuchokera ku zinthu zopanda moyo, iwo amalankhula mosonyeza kuti ndi anthu osaphunzira okha amene sakhulupirira zimenezi. Ndiyeno kodi anthu ambiri amati bwanji akamva zimenezi? Zaka zingapo zapitazo, katswiri wina wa chiphunzitso chakuti zamoyo zinachita kusanduka anacheza ndi anthu okhulupirira chiphunzitso chimenechi. Iye anati: “Ndinapeza kuti anthu ambiri okhulupirira kuti zamoyo zinachita kusanduka amatero chifukwa chouzidwa kuti anthu onse anzeru amakhulupirira zimenezi.” Zoonadi, anthu ophunzira kwambiri akamafotokoza kuti iwo amaona kuti kulibe Mulungu, anthu ena amakopeka nazo n’kusiya kupatsa Mulungu ulemerero umene amayenera kulandira popeza kuti ndiye Mlengi.​—Miyambo 14:15, 18.

7. Malingana ndi Aroma 1:20, kodi ndi zinthu zotani zokhudza Mulungu zimene zimaonekera bwino m’chilengedwechi, ndipo n’chifukwa chiyani?

7 Kodi asayansi akamanena zimenezo amatero chifukwa chakuti akudziŵa zoona zake ndiponso kuti ali ndi umboni wokwanira? Ayi. Paliponse pali umboni wosonyeza kuti kuli Mlengi. Pofotokoza za Mlengi ameneyu, mtumwi Paulo analemba kuti: “Chilengedwere dziko lapansi [lomwe likutanthauza anthu] zaoneka bwino zosaoneka zake ndizo mphamvu yake yosatha ndi umulungu wake; popeza zazindikirika ndi zinthu zolengedwa, kuti iwo [osakhulupirira] adzakhale opanda mawu akuŵiringula.” (Aroma 1:20) Tingathe kuona bwinobwino umboni wakuti kuli Mlengi kudzera m’zimene anapanga. Motero Paulo anali kunena kuti kuchokera pamene anthu analengedwa, poona chilengedwe iwo ‘azindikira’ umboni wosonyeza kuti kuli Mulungu. Kodi umboni umenewu umapezeka kuti?

8. (a) Kodi zinthu zakumwamba zimene timaziona zimapereka motani umboni wakuti Mulungu ndi wamphamvu ndiponso wanzeru? (b) Kodi n’chiyani chikusonyeza kuti pali amene anapangitsa kuti chilengedwechi chikhalepo?

8 Thambo lodzala ndi nyenyezi limationetsa umboni wakuti kuli Mulungu. “Zakumwamba zimalalikira ulemerero wa Mulungu,” limatero Salmo 19:1. “Zakumwamba,” zomwe ndi dzuŵa, mwezi, ndi nyenyezi, zimapereka umboni wakuti Mulungu ndi wamphamvu ndiponso wanzeru. Timasoŵa chonena tikaganizira kuchuluka kwa nyenyezi. Ndipotu zinthu zakumwamba zonsezi zimayenda mumlengalengamu, osati mwachisawawa, koma motsatira malamulo  ake. * (Yesaya 40:26) Ndiye kodi m’pomveka kunena kuti dongosolo limeneli linangochitika lokha? N’zochititsa chidwi kuona kuti akatswiri ambiri a sayansi amati zinangochitika mwadzidzidzi kuti chilengedwechi chiyambe kukhalapo. Pofuna kusonyeza kuti mfundo imeneyi n’njosamveka, pulofesa wina analemba kuti: “Anthu amene amanena kuti kulibe Mulungu kapena amene amakayikira kuti kuli Mulungu amakhulupirira kwambiri kuti chilengedwechi chinayamba kukhalapo kalekale. Motero, povomereza kuti chilengedwechi chinali ndi poyambira ndiye kuti pali china chomwe chinapangitsa kuti chilengedwechi chikhalepo. Tikutero chifukwa chakuti munthu wanzeru sangaganize kuti chinthu choterechi chingachitike popanda chochititsa.”

9. Kodi nzeru za Yehova zimaonekera motani pa zinyama zimene analenga?

9 Timaonanso umboni wakuti kuli Mulungu padziko lapansi pompano. Wamasalmo anafuula kuti: “Ntchito zanu zichulukadi, Yehova! Munazichita zonse mwanzeru; dziko lapansi lidzala nacho chuma chanu.” (Salmo 104:24) “Chuma” cha Yehova, chomwe chikuphatikizapo zinyama, chimasonyeza kuti iye ndi wanzeru. Monga momwe taonera poyamba paja, zinthu zamoyo zinapangidwa bwino kwambiri moti asayansi nthaŵi zambiri amayesetsa kutengera mmene zinapangidwira. Taonani zitsanzo zinanso zochepa chabe. Akatswiri ochita kafukufuku akuphunzira mmene nyanga za nyama monga mphalapala zinapangidwira, ndipo cholinga chawo n’choti azipanga zisoti zolimba kwambiri. Iwo akuphunziranso za mtundu wina wa ntchentche zimene zimamva kwambiri, ndipo cholinga chawo n’choti akonzenso bwino zida zothandizira anthu ovutika kumva. Komanso akuphunzira mmene nthenga za mapiko a kadzidzi zinapangidwira pofuna kuti achepetseretu phokoso la ndege zoyenda mwakabisira. Komabe, ngakhale anthu atayesetsa motani, sangathe kutengera ndendende mmene zinthu zachilengedwe zinapangidwira. Buku lina lofotokoza za kutengera kapangidwe ka zinthu zachilengedwe (lakuti Biomimicry​—Innovation Inspired by Nature) linati: “Zinthu zamoyo zakhala zikuchita chilichonse chimene anthufe timafuna kuchita, ndipo zakhala zikuchita izi popanda kufuna mafuta ambirimbiri, kuwononga dziko, kapenanso kudziwonongera tsogolo.” Izitu ndi nzerudi zenizeni.

10. N’chifukwa chiyani n’zosamveka kunena kuti kulibe Mlengi? Perekani chitsanzo.

10 Mukayang’ana kumwamba kapena zolengedwa zapadziko lapansi pompano, mumaona bwinobwino umboni wakuti kuli Mlengi. (Yeremiya 10:12) Tiyenera kugwirizana mochokera pansi pamtima ndi zolengedwa zakumwamba zimene zimafuula kuti: “Muyenera inu, Ambuye wathu, ndi Mulungu wathu, kulandira ulemerero ndi ulemu ndi mphamvu; chifukwa mudalenga zonse.” (Chivumbulutso 4:11) Komabe, akatswiri ambiri a sayansi amalephera kuona ndi ‘maso a mitima yawo’ umboni wakuti kuli Mlengi, ngakhale kuti nthaŵi zina amachita chidwi ndi kapangidwe ka zinthu zimene maso awo enieni amaona. (Aefeso 1:18) Pamenepa tingapereke chitsanzo ichi: N’zosamveka kuti munthu azichita chidwi ndi kukongola kwa zinthu zachilengedwe ndiponso mmene zinthuzo zinapangidwira koma n’kumakana kuti kuli Mlengi. Izi zingafanane ndi munthu amene akuchita chidwi ndi chithunzi chojambulidwa mwaluso kwambiri koma akukana kuvomereza kuti chinachita kujambulidwa ndi katswiri pa nsalu, imene poyamba inalibe kanthu kalikonse. Motero n’zosadabwitsa kuti anthu amene amakana kukhulupirira kuti kuli Mulungu alibe “mawu akuŵiringula.”

“Atsogoleri Akhungu” Akusocheretsa Anthu Ochuluka

11, 12. Kodi n’chifukwa chiyani zipembedzo zimaphunzitsa kuti zinthu zomwe zimatichitikira zinakonzedweratu ndi Mulungu, ndipo n’chiyani chimasonyeza kuti chiphunzitso chimenechi sichipatsa Mulungu ulemerero?

11 Anthu ambiri opembedza amakhulupirira ndi mtima wonse kuti kulambira kwawo kumapatsa Mulungu ulemerero. (Aroma 10:2, 3) Komabe zipembedzo nazonso zikulepheretsa miyandamiyanda ya anthu kupatsa Mulungu ulemerero. Kodi zikuchita zimenezi motani? Tiyeni tione njira ziŵiri.

12 Njira yoyamba n’njakuti zipembedzo zimachotsera Mulungu ulemerero pophunzitsa zinthu zonyenga. Mwachitsanzo, taganizirani za chiphunzitso chakuti zinthu zomwe zimatichitikira zinakonzedweratu ndi Mulungu. Zipembedzo zimaphunzitsa zimenezi poganiza kuti popeza kuti Mulungu amatha kudziŵa za m’tsogolo, ayeneranso kuti amadziŵiratu mmene zinthu zonse zidzachitikire. Motero chiphunzitso chakuti zinthu zomwe zimatichitikira ndi zokonzedweratu chimasonyeza kuti Mulungu anakonzeratu  kalekale zinthu zimene zidzachitikire munthu aliyense, kaya ndi zinthu zabwino kapena zoipa. Malinga ndi mfundo imeneyi, anthu amati Mulungu ndiye amachititsa mavuto ndiponso kuipa konse komwe kukuchitika masiku ano. Mulungu salemekezedwa ngakhale pang’ono anthu akamamunena kuti ndiye amachititsa mavuto koma pamene woyenerera kuimbidwa mlanduwu ndi Satana, Mdani wake wamkulu, amene Baibulo limam’tchula kuti “mkulu wa dziko lapansi.”​—Yohane 14:30; 1 Yohane 5:19.

13. N’chifukwa chiyani kuli kupanda nzeru kuganiza kuti Mulungu sangasiyire dala kudziŵa zam’tsogolo? Perekani chitsanzo.

13 M’malemba mulibe chiphunzitso chakuti zinthu zomwe zimatichitikira zinakonzedweratu ndipo chiphunzitsochi chimaipitsa dzina la Mulungu. Sichisiyanitsa pakati pa zinthu zimene iye angathe kuchita ndi zinthu zimene iye amachitadi. Baibulo limanena momveka bwino kuti Mulungu angathe kudziŵiratu zinthu zodzachitika m’tsogolo. (Yesaya 46:9, 10) Koma sizomveka kuganiza kuti iye atafuna sangathe kusadziŵira dala zimene zidzachitike m’tsogolo ndiponso sizomveka kuganiza kuti ndi iye amene amachititsa zinthu zonse. Mwachitsanzo: Tiyerekezere kuti inu ndinu munthu wamphamvu kwambiri. Kodi bwenzi mukunyamula chinthu chilichonse cholemera chimene mwachiona? N’zodziŵikiratu kuti simungatero. N’chimodzimodzinso ndi Mulungu, kukhala ndi mphamvu zotha kudziŵa zinthu zodzachitika m’tsogolo sikum’pangitsa kudziŵa kapena kukonzeratu mmene chinthu chilichonse chidzachitikire. Iye amachita kusankha zinthu zam’tsogolo zimene akufuna kudziŵiratu. * Motero, n’zoonekeratu kuti ziphunzitso zonyenga, kuphatikizapo chiphunzitso chonena kuti zinthu zomwe zimatichitikira ndi zokonzedweratu ndi Mulungu, sizilemekeza Mulungu.

14. Kodi zipembedzo zanyoza Mulungu motani?

14 Njira yachiŵiri imene zipembedzo zimanyozera Mulungu ndi ya makhalidwe a anthu awo. Akristu ayenera kutsatira zinthu zimene Yesu anaphunzitsa. Mwa zina, Yesu anaphunzitsa anthu omutsatira kuti ‘azikondana’ ndiponso kuti ‘asakhale a dziko lapansi.’ (Yohane 15:12; 17:14-16) Kodi atsogoleri a Matchalitchi Achikristu achita zotani? Kodi iwo atsatiradi zimene Yesu anaphunzitsazi?

15. (a) Kodi atsogoleri achipembedzo akhala akuchita zotani mayiko akakhala pankhondo? (b) Kodi anthu ambiri achita zotani chifukwa cha khalidwe la atsogoleri achipembedzo?

15 Taonani zimene atsogoleri achipembedzo akhala akuchita panthaŵi za nkhondo. Iwo akhala akuthandizira, kulekerera, ndipo mwinanso kutsogolera kumene pankhondo zambiri zimene mayiko akhala akumenya. Iwo akhala akudalitsa asilikali ndiponso kumanena kuti kupha anthu sikulakwa. Motero sitingachitire mwina, koma kufunsa kuti, ‘Kodi atsogoleri ameneŵa anayamba aganizirapo zoti amene akumenyana nawowo akuchitanso chimodzimodzi?’ (Onani bokosi lakuti “Kodi Mulungu Ali Mbali ya Ndani?”) Atsogoleri achipembedzo sapatsa Mulungu ulemerero akamanena kuti Mulunguyo anawathandiza pankhondo zimene zaphetsa anthu ambirimbiri; ndiponso sam’patsa ulemu akamanena kuti mfundo za m’Baibulo n’zachikale ndiyeno n’kumalekerera mitundu yosiyanasiyana yachiwerewere. Atsogoleri ameneŵa akungotikumbutsa za atsogoleri achipembedzo amene Yesu anawatcha kuti “akuchita kusayeruzika” ndiponso “atsogoleri akhungu.” (Mateyu 7:15-23; 15:14) Zochita za atsogoleri achipembedzo  zachititsa kuti chikondi chimene anthu ambiri anali nacho kwa Mulungu chizilale.​—Mateyu 24:12.

Kodi Ndani Akupatsadi Mulungu Ulemerero?

16. Kuti tiyankhe funso lakuti ndani akupatsadi Mulungu ulemerero, n’chifukwa chiyani tiyenera kuona m’Baibulo?

16 Ngati anthu otchuka m’dzikoli alephera kupatsa Mulungu ulemerero, ndiyeno ndani amene akupatsadi Mulungu ulemerero? Kuti tiyankhe funso limeneli, tiyenera kuona m’Baibulo. Ndipotu Mulungu ndiye woyenerera kufotokoza mmene tingam’lemekezere, komanso m’Mawu ake, omwe ndi Baibulo, iye anafotokozamo mmene tingachitire zimenezi. (Yesaya 42:8) Tiyeni tione njira zitatu zomwe tingalemekezere Mulungu, ndipo pa mfundo iliyonse tiona kuti ndani amene akupatsadi Mulungu ulemerero masiku ano.

17. Kodi Yehova mwiniwakeyo anasonyeza motani kuti kulemekeza dzina lake ndi mbali yofunika kwambiri pa zofuna zake, ndipo ndi ndani masiku ano amene akutamanda dzina la Mulungu padziko lonse?

17 Njira yoyamba ndi yakuti tingalemekeze Mulungu mwa kutamanda dzina lake. Zimene Yehova anauza Yesu zimasonyeza kuti kuchita zimenezi ndi mbali yofunika kwambiri pa kukwaniritsidwa kwa cholinga cha Mulungu. Patatsala masiku ochepa kuti Yesu afe, iye anapemphera kuti: “Atate, lemekezani dzina lanu.” Ndiye panamveka yankho lakuti: “Ndalilemekeza, ndipo ndidzalilemekezanso.” (Yohane 12:28) Sitingakayikire n’komwe kuti amene anali kulankhulayo anali Yehova mwiniwakeyo. Malinga ndi zimene ananenazi, ndi zoonekeratu kuti kwa iye kulemekeza dzina lake n’kofunika kwambiri. Motero, ndani masiku ano amene akulemekeza Yehova mwa kulengeza dzina lake ndi kulitamanda padziko lonse? Ndi Mboni za Yehova, ndipo zikuchita zimenezi m’mayiko 235.​—Salmo 86:11, 12.

18. Kodi tingawazindikire motani anthu amene akulambira Mulungu “m’choonadi,” ndipo ndi gulu liti limene lakhala likuphunzitsa choonadi cha m’Baibulo kwa zaka zoposa 100?

18 Njira yachiŵiri ndi yakuti tingalemekeze Mulungu mwa kuphunzitsa zinthu zoona zenizeni zokhudza iye. Yesu ananena kuti olambira oona ‘adzalambira [Mulungu] . . . m’choonadi.’ (Yohane 4:24) Kodi tingawazindikire motani anthu amene akulambira Mulungu “m’choonadi”? Ayenera kukana ziphunzitso zimene sizichokera m’Baibulo ndiponso zimene zimaipitsa Mulungu ndi chifuno chake. M’malo mwake ayenera kuphunzitsa choonadi chenicheni cha m’Mawu a Mulungu, kuphatikizapo zinthu izi: Yehova ndi Mulungu Wam’mwambamwamba, ndipo ndi yekhayo amene ayenera kulandira ulemerero chifukwa cha udindo wakewo (Salmo 83:18); Yesu ndi Mwana wa Mulungu ndiponso ndi Wolamulira amene anasankhidwa wa Ufumu wa Mulungu Waumesiya (1 Akorinto 15:27, 28); Ufumu wa Mulungu udzayeretsa dzina la Yehova ndi kukwaniritsa cholinga chake chokhudza dziko lapansi lino ndiponso anthu amene akukhala padzikoli (Mateyu 6:9, 10); uthenga wabwino wonena za Ufumu umenewu uyenera kulalikidwa padziko lonse. (Mateyu 24:14) Kwa zaka zoposa 100, ndi gulu limodzi lokha limene lakhala likuphunzitsa mokhulupirika choonadi chamtengo wapatali chimenechi, ndipo gulu limeneli ndi la Mboni za Yehova.

19, 20. (a) N’chifukwa chiyani khalidwe labwino la Mkristu lingapereke ulemerero kwa Mulungu? (b) Kodi ndi mafunso ati amene angatithandize kuzindikira kuti ndi ndani masiku ano amene akupatsa Mulungu ulemerero chifukwa cha makhalidwe abwino?

19 Njira yachitatu ndi yakuti tingalemekeze Mulungu mwa kutsatira mfundo zake pamoyo wathu. Mtumwi Petro analemba kuti: “Mayendedwe anu mwa amitundu akhale okoma, kuti, mmene akamba za inu ngati ochita zoipa, akalemekeze Mulungu pakuona ntchito zanu zabwino, m’tsiku la kuyang’anira.” (1 Petro 2:12) Khalidwe limene Mkristu ali nalo limasonyeza zinthu zimene iye amakhulupirira. Anthu akamaona khalidwe labwino la Mkristuyo n’kuzindikira kuti ali ndi khalidwe lotero chifukwa cha chikhulupiriro chake, Mulungu amapatsidwa ulemerero.

20 Kodi ndani masiku ano amene akulemekeza Mulungu mwa makhalidwe awo abwino? Kodi ndi gulu la chipembedzo liti limene maboma ambiri  amaliyamikira chifukwa chakuti n’lokonda mtendere, anthu ake amamvera malamulo ndiponso amakhoma misonkho? (Aroma 13:1, 3, 6, 7) Kodi ndi anthu ati amene akudziŵika padziko lonse kuti n’ngogwirizana ndi olambira anzawo, mosaganizira za kusiyana mafuko, mayiko, ndiponso mitundu? (Salmo 133:1; Machitidwe 10:34, 35) Kodi ndi gulu liti limene likudziŵika padziko lonse kuti limagwira ntchito yophunzitsa Baibulo imene imalimbikitsa anthu kumvera malamulo, kulemekeza banja, ndiponso kutsatira mfundo za makhalidwe abwino zimene Baibulo limanena? Pali gulu limodzi lokha limene makhalidwe ake abwino pankhani zimenezi ndiponso nkhani zina amapereka umboni wakuti likulemekeza Mulungu, ndipo gululi ndi la Mboni za Yehova.

Kodi Inuyo Panokha Mukupatsa Mulungu Ulemerero?

21. Kodi n’chifukwa chiyani tiyenera kudzifunsa ngati ifeyo patokha tikupatsa Yehova ulemerero?

21 Ndi bwino kuti aliyense wa ife adzifunse kuti, ‘Kodi ineyo pandekha ndikupatsa Yehova ulemerero?’ Malinga ndi Salmo 148, mbali yaikulu ya chilengedwe ikupatsa Mulungu ulemerero. Angelo, miyamba yomwe timaona, dziko lapansi ndiponso zinyama zimene zili padziko pano, zonse zimatamanda Yehova. (Mavesi 1-10) Koma n’zomvetsa chisoni kwambiri kuti anthu ambiri masiku ano sakutero. Mwa kukhala ndi moyo umene umapatsa Mulungu ulemerero, mumagwirizana ndi chilengedwe chonse chomwe chikutamanda Yehova. (Mavesi 11-13) Palibenso njira ina yabwino yogwiritsira ntchito moyo wanu.

22. Mukamapatsa Yehova ulemerero, kodi mumadalitsidwa m’njira zotani, ndipo kodi muyenera kutsimikiza mtima kuchita chiyani?

22 Mukamapatsa Yehova ulemerero, mumadalitsidwa m’njira zambiri. Mukamakhulupirira nsembe ya dipo ya Kristu, mumayanjanitsidwa ndi Mulungu ndipo mumakhala pamtendere ndiponso paubwenzi wopindulitsa kwambiri ndi Atate wanu wakumwamba ameneyu. (Aroma 5:10) Mukamayesetsa kuona zifukwa zopatsira Mulungu ulemerero, mumakhala wachimwemwe, ndiponso woyamikira kwambiri. (Yeremiya 31:12) Mukatero, nanunso mungathe kuthandiza anthu ena kukhala moyo wachimwemwe, zomwenso zimakupatsani inuyo chimwemwe chodzadza tsaya. (Machitidwe 20:35) Ndiyetu khalani m’gulu la anthu amene atsimikiza mtima kupatsa Mulungu ulemerero, tsopano lino ndiponso kwa muyaya.

[Mawu a M’munsi]

^ ndime 8 Kuti mumve tsatanetsatane wa mmene zinthu zakumwamba zimene timaziona zimasonyezera kuti Mulungu ndi wanzeru ndiponso ndi wamphamvu, ŵerengani machaputala 5 ndi 17 m’buku lakuti Yandikirani kwa Yehova, lofalitsidwa ndi Mboni za Yehova.

^ ndime 13 Onani buku la Insight on the Scriptures, Voliyumu 1, tsamba 853, ndi buku la Kukambitsirana za m’Malemba, masamba 117 mpaka 118, ofalitsidwa ndi Mboni za Yehova.

Kodi Mukukumbukira?

• N’chifukwa chiyani tinganene kuti akatswiri a sayansi sanathandize anthu kupatsa Mulungu ulemerero?

• Kodi chipembedzo chalepheretsa anthu kupatsa Mulungu ulemerero m’njira ziŵiri ziti?

• Kodi tingapatse Mulungu ulemerero m’njira ziti?

• Kodi n’chifukwa chiyani muyenera kudzifunsa ngati inuyo panokha mukupatsa Yehova ulemerero?

[Mafunso]

[Bokosi patsamba 12]

“Kodi Mulungu Ali Mbali ya Ndani?”

Mwamuna wina amene asanakhale wa Mboni za Yehova anali m’gulu la asilikali apandege a dziko la Germany pankhondo yachiŵiri ya padziko lonse, anati:

“Chimene chinkandivuta kwambiri kumvetsa m’zaka zimene nkhondoyi inali kumenyedwa . . . chinali chakuti atsogoleri a zipembedzo pafupifupi zonse, za Katolika, Lutheran, Episikopi, ndi zinanso, ankadalitsa ndege zankhondo ndiponso asilikali oyendetsa ndengezo asanapite kukaponya mabomba owopsa kwambiri. Nthaŵi zambiri ndinkadzifunsa kuti, ‘Kodi Mulungu ali mbali ya ndani?’

“Asilikali a dziko la Germany ankavala malamba okhala ndi zomangira zachitsulo zolembedwa kuti Gott mit uns (Mulungu ali nafe). Koma ndinkadzifunsa kuti, ‘Ngati Mulungu ali nafe, kodi sangakhalenso ndi asilikali a gulu limene tikumenyana nalo, omwenso ndi achipembedzo chathu ndiponso akupemphera kwa Mulungu yemweyu?’”

[Chithunzi patsamba 10]

Padziko lonse lapansi, Mboni za Yehova zikupatsadi Mulungu ulemerero