Pitani ku nkhani yake

Pitani ku mitu ya nkhani

Mafunso Ochokera kwa Oŵerenga

Mafunso Ochokera kwa Oŵerenga

 Mafunso Ochokera kwa Oŵerenga

Pamene mtumwi Yohane analemba kuti “chikondi changwiro chitaya kunja mantha,” kodi anali kutanthauzanji ponena kuti “chikondi changwiro,” komanso kodi ndi “mantha” otani amene amatayidwa kunjawo?

“Mulibe mantha m’chikondi,” analemba motero mtumwi Yohane, “koma chikondi changwiro chitaya kunja mantha, popeza mantha ali nacho chilango, ndipo wamanthayo sakhala wangwiro m’chikondi.”​—1 Yohane 4:18.

Nkhani imene mukupezeka lembali imasonyeza kuti Yohane anali kufotokoza za kulimbika mtima kapena kuti kulankhula mwaufulu. Pamenepa makamaka anali kunena za kugwirizana kumene kulipo pakati pa kukonda Mulungu ndi kulankhula naye mwaufulu. Tingathe kuona zimenezi tikaŵerenga mu vesi 17, limene limati: “Mmenemo chikondi chathu chikhala changwiro kuti tikhale nako kulimbika mtima m’tsiku la mlandu.” Mkristu angamalankhule mwaufulu akamapemphera, ngati iyeyo amakonda kwambiri Mulungu ndiponso ngati amamva kuti amakondedwa ndi Mulungu.

Mawu akuti “chikondi changwiro” ali ndi tanthauzo lalikulu kwambiri. Baibulo likatchula kuti ‘ungwiro’ sikuti nthaŵi zonse limatanthauza ungwiro wopanda polakwika paliponse. Mwachitsanzo, Yesu, pa Ulaliki wake wa pa Phiri, anati: “Chifukwa chake inu mukhale angwiro, monga Atate wanu wa Kumwamba ali wangwiro.” Yesu anali kuuza anthu omutsatira kuti ngati amakonda anthu okhawo amene amakondana nawo, chikondi chawo chingakhale chosakwanira, chopereŵera, ndiponso chachilema. Ayenera kukonza chikondi chawocho kuti chikhale changwiro, kapena chokwanira, mwa kukondanso anthu ena ngakhale amene ali adani awo. Motero, mogwirizana ndi mfundoyi, pamene Yohane analemba za “chikondi changwiro,” anali kunena za kukonda Mulungu ndi mtima wonse, motsimikiza, kum’konda pa mbali zonse za moyo wa munthu.​—Mateyu 5:46-48; 19:20, 21.

Popemphera, Mkristu amakhala akudziŵiratu kuti iye ndi wochimwa ndiponso wopanda ungwiro. Komabe, ngati amakonda kwambiri Mulungu komanso ngati amatsimikizira kuti Mulungu amam’konda, Mkristuyo salephera kupemphera poopa kuti adzudzulidwa kapena kuti pemphero lake silimvedwa. M’malo mwake amalankhula zakukhosi kwake mwaufulu ndi kupempha kuti akhululukidwe machimo kudzera mu nsembe ya dipo, imene Mulungu anakonza mwa Yesu Kristu chifukwa chakuti amatikonda. Amakhala wotsimikiza kuti Mulungu ayankha mapemphero ake.

Kodi munthu angakhale bwanji “wangwiro m’chikondi” ndi ‘kutaya kunja’ mantha, poopa kudzudzulidwa kapena kusamvedwa? Mtumwi Yohane ananena kuti, “iye amene akasunga mawu ake [a Mulungu], mwa iyeyu zedi chikondi cha Mulungu chathedwa,” kapena kuti ndi changwiro. (1 Yohane 2:5) Taganizirani izi: Ngati Mulungu anayamba kutikonda ifeyo tidakali ochimwa, kodi sangatikonde kwambiri tonsefe ngati talapadi ndiponso timayesetsa ‘kusunga mawu ake’? (Aroma 5:8; 1 Yohane 4:10) Zoonadi, malinga ngati tipitiriza kukhala okhulupirika, nafenso tingakhale ndi chitsimikizo chimene mtumwi Paulo anali nacho pamene ananena za Mulungu kuti: “Iye amene sanatimana Mwana wake wa iye yekha, koma anam’pereka chifukwa cha ife tonse, adzalekeranji kutipatsanso ife zinthu zonse kwaulere pamodzi ndi iye?”​—Aroma 8:32.