Pitani ku nkhani yake

Pitani ku mitu ya nkhani

Kodi ‘Ofatsa Choloŵa Chawo ndi Dziko Lapansi’ Motani?

Kodi ‘Ofatsa Choloŵa Chawo ndi Dziko Lapansi’ Motani?

 Kodi ‘Ofatsa Choloŵa Chawo ndi Dziko Lapansi’ Motani?

“MWINA mumawadziŵa mawu olimbikitsa a Yesu akuti ‘ofatsa choloŵa chawo ndi dziko lapansi.’ Koma mukaona zimene anthu akuchitirana ndiponso zimene akulichita dziko lapansili, kodi mukuganiza kuti n’chiyani chidzatsale kuti chikhale choloŵa cha ofatsa?”​—Mateyu 5:5, Chipangano Chatsopano mu Chichewa cha Lero; Salmo 37:11.

Myriam, yemwe ndi wa Mboni za Yehova, anafunsa munthu wina funso limeneli poyamba kukambirana naye za m’Baibulo. Mwamuna amene anam’funsayo anayankha kuti ngati Yesu analonjeza zimenezi, ndiye kuti dziko lapansili lidzakhaladi choloŵa cholongosoka osati bwinja losati munthu n’kukhalapo.

Yankho la munthuyu linasonyeza kuti sanali kukayikira kuti zinthu zidzakhala bwino. Koma kodi tili ndi chifukwa chomveka chokhalira ndi maganizo ngati amenewo? Inde tili nacho, popeza Baibulo limatipatsa zifukwa zomveka bwino zokhulupirira kuti lonjezoli lidzakwaniritsidwa. Ndipotu, kukwaniritsidwa kwa lonjezo limeneli n’kogwirizana kwambiri ndi cholinga chimene Mulungu anali nacho polenga anthu ndi dziko lapansili. Ndipo sitikukayikira kuti Mulungu adzachita zimene amafuna. (Yesaya 55:11) Motero, kodi Mulungu pachiyambi anali nawo cholinga chotani anthu, ndipo kodi chidzakwaniritsidwa bwanji?

Mmene Mulungu Anafunira Kuti Dziko Lapansi Likhalire Mpaka Kalekale

Yehova Mulungu anali ndi cholinga chapadera polenga dziko lapansi. “Atero Yehova amene analenga kumwamba, Iye ndiye Mulungu amene anaumba dziko lapansi, nalipanga; Iye analikhazikitsa, sanalilenga mwachabe; Iye analiumba akhalemo anthu; Ine ndine Yehova; ndipo palibenso wina.” (Yesaya 45:18) Motero, cholinga chenicheni polenga dziko lapansi chinali chakuti anthu azikhalamo. Komanso, ndi cholinga cha Mulungu kuti dziko lapansi likhale kwawo kwa anthu mpaka kalekale. “Anakhazika dziko lapansi pa maziko ake, silidzagwedezeka ku nthaŵi yonse.”​—Salmo 104:5; 119:90.

Timazindikiranso cholinga cha Mulungu polenga dziko lapansi tikaganizira ntchito imene anapatsa anthu aŵiri oyambirira. Yehova anati kwa Adamu ndi Hava: “Mubalane, muchuluke, mudzaze dziko lapansi, muligonjetse: mulamulire pa nsomba za m’nyanja, ndi pa mbalame za m’mlengalenga, ndi pa zamoyo zonse zakukwawa pa dziko lapansi.” (Genesis 1:28) Dziko lapansi, limene Mulungu anapatsa Adamu ndi Hava, linali loti azikhalamo mpaka kalekale pamodzi ndi ana awo. Patapita zaka mazana ambiri wamasalmo anati: “Kunena za kumwamba, kumwamba ndiko kwa Yehova; koma dziko lapansi analipereka kwa ana a anthu.”​—Salmo 115:16.

 Kuti zimenezo zitheke, Adamu ndi Hava komanso ana awo, aliyense payekha anafunika kuona Yehova Mulungu, yemwe ndi Mlengi ndi Wopatsa Moyo, monga Mfumu yawo ndipo anayenera kumumvera. Pankhani imeneyi Yehova sananene mopita m’mbali pamene anauza mwamunayo lamulo ili: “Mitengo yonse ya m’munda udyeko; koma mtengo wakudziŵitsa zabwino ndi zoipa usadye umenewo; chifukwa tsiku lomwe udzadya umenewo udzafa ndithu.” (Genesis 2:16, 17) Adamu ndi Hava kuti apitirize kukhala m’munda wa Edene, anafunika kumvera lamulo losavuta komanso lomveka bwino limeneli. Kuchita zimenezo kukanasonyeza kuti anali kuyamikira zonse zimene Atate wakumwamba anawachitira.

Pamene Adamu ndi Hava anasankha mwadala kusamvera Mulungu mwa kuswa lamulo limene anawapatsa, anasonyezeratu kuti anakana amene anawapatsa zinthu zonse zimene anali nazo. (Genesis 3:6) Chifukwa chochita zimenezi, anataya mudzi wokongola wa Paradaiso, womwe ukanakhala wawo komanso wa ana awo. (Aroma 5:12) Kodi kusamvera kwa banja loyambirira kumeneku kunalepheretsa cholinga chimene Mulungu anali nacho polenga dziko lapansi?

Mulungu Sanasinthe

Mulungu ananena kudzera mwa mneneri wake Malaki kuti: “Ine Yehova sindisinthika.” (Malaki 3:6) Ponena za vesi limeneli, katswiri wachifalansa wa maphunziro a Baibulo L. Fillion anati, mawu ameneŵa ndi ogwirizana kwambiri ndi kukwaniritsidwa kwa malonjezo a Mulungu. Fillion analemba kuti: “Yehova akanatha kuwononga anthu ake opandukawo, koma popeza kuti akalonjeza walonjeza, mulimonse mmene zingakhalire, amachita zimene walonjezazo.” Zimene Mulungu walonjeza, kaya kwa munthu aliyense payekha, mtundu, kapena anthu onse, samaziiŵala koma amazichita nthaŵi yake ikakwana. “Akumbukira chipangano chake kosatha, mawuwo anawalamulira mibadwo zikwi.”​—Salmo 105:8.

Komabe, kodi tingakhulupirire bwanji kuti Yehova sanasinthe cholinga chake choyambirira chokhudza dziko lapansi? Tingatsimikizire zimenezi chifukwa chakuti m’Baibulo lonse, lomwe ndi Mawu ouziridwa a Mulungu, timapezamo lonjezo lakuti Mulungu adzapatsa anthu omvera dziko lapansi. (Salmo 25:13; 37:9, 22, 29, 34) Komanso, Malemba amati anthu amene Yehova adzawadalitse adzakhala mosatekeseka, aliyense adzakhala “patsinde pa  mpesa wake, ndi patsinde pa mkuyu wake,” ndipo “sipadzakhala wakuwawopsa.” (Mika 4:4; Ezekieli 34:28) Anthu amene Yehova adzawasankhe “adzamanga nyumba ndi kukhalamo; ndipo iwo adzawoka minda yamphesa, ndi kudya zipatso zake.” Iwo adzakhala pamtendere ngakhale ndi nyama zam’thengo.​—Yesaya 11:6-9; 65:21, 25.

Baibulo limasonyeza mwa njira ina mmene lonjezo la Mulungu lidzakhalire. Panthaŵi ya ulamuliro wa Mfumu Solomo, mtundu wa Israyeli unali pamtendere ndiponso zinthu zinali kuuyendera bwino. Mu ulamuliro wake, “Ayuda ndi Aisrayeli anakhala mosatekeseka, munthu yense patsinde pa mpesa wake ndi mkuyu wake, kuyambira ku Dani mpaka ku Beeriseba, masiku onse a Solomo.” (1 Mafumu 4:25) Baibulo limanena kuti Yesu ndi “woposa Solomo,” ndipo ponena za ulamuliro wa Yesu, wamasalmo analosera kuti: “Masiku ake wolungama adzakhazikika; ndi mtendere wochuluka, kufikira sipadzakhala mwezi.” Panthaŵi imeneyo, “m’dzikomo mudzakhala dzinthu dzochuluka pamwamba pa mapiri.”​—Luka 11:31; Salmo 72:7, 16.

Yehova Mulungu pamene azidzakwaniritsa mawu ake, adzaonetsetsa kuti choloŵa chimene analonjeza chilipo komanso wachikongoletsa monga mwakale. Mawu a Mulungu pa Chivumbulutso 21:4, amatiuza kuti m’dziko latsopano lolonjezedwa, Mulungu ‘adzapukuta misozi yonse kuichotsa pamaso [pa anthu]; ndipo sipadzakhalanso imfa; ndipo sipadzakhalanso maliro, kapena kulira, kapena chowawitsa.’ Zimene analonjeza ndi Paradaiso weniweni.​—Luka 23:43.

Mmene Tingadzapezere Choloŵa Chimene Walonjeza

Dziko lidzasandutsidwa paradaiso mu ulamuliro wa boma limene lidzalamulira kuchokera kumwamba, lomwe ndi Ufumu umene Mfumu yake ali Yesu Kristu. (Mateyu 6:9, 10) Choyamba, Ufumu umenewo ‘udzawononga amene amawononga dziko.’ (Chivumbulutso 11:18; Danieli 2:44) Ndiyeno, Yesu Kristu yemwe ndi “Kalonga wa mtendere” adzakwaniritsa mawu aulosi aŵa: “Za kuyenjezera ulamuliro wake, ndi za mtendere sizidzatha.” (Yesaya 9:6, 7) Mu Ufumu umenewo, anthu ambirimbiri, kuphatikizapo amene adzaukitsidwe kwa akufa, adzakhala ndi mwayi wolandira dziko lapansi monga choloŵa.​—Yohane 5:28, 29; Machitidwe 24:15.

Kodi ndani adzalandire choloŵa chosangalatsa chimenechi? Taganizirani mawu a Yesu akuti: “Odala ali ofatsa chifukwa choloŵa chawo  ndi dziko lapansi.” (Mateyu 5:5, Chipangano Chatsopano mu Chichewa cha Lero.) Kodi kukhala wofatsa n’kutani? Nthaŵi zambiri mabuku omasulira mawu amati “kufatsa” kumatanthauza kudekha, kumvera, kukhala phee. Komabe, mawu achigiriki oyambirira amene anawamasulira kuti kufatsa amatanthauza zambiri. Buku la New Testament Wordbook la William Barclay limati mawu ameneŵa amatanthauzanso “kudekha, koma munthu wodekha amakhala wa mtima wolimba ngati chitsulo.” Mawuŵa amasonyeza mtima umene umam’pangitsa munthu kupirira zowawa popanda kusunga chakukhosi kapena kuganiza zobwezera, ndipo amachita zimenezi chifukwa chakuti ali paubwenzi wabwino ndi Mulungu. Ubwenzi umenewu ndi umene umamupatsa mphamvu zochitira zimenezo.​—Yesaya 12:2; Afilipi 4:13.

Munthu wofatsa amavomereza modzichepetsa mfundo za Mulungu m’zochita zake zonse pamoyo wake; sakakamira kuchita zimene akuganiza kapena kuyendera maganizo a anthu ena. Amakhalanso munthu wophunzitsika, wofuna kuphunzitsidwa ndi Yehova. Wamasalmo Davide analemba kuti: “[Yehova] adzawatsogolera ofatsa m’chiweruzo: ndipo adzaphunzitsa ofatsa njira yake.”​—Salmo 25:9; Miyambo 3:5, 6.

Kodi mudzakhala pagulu la “ofatsa” amene choloŵa chawo chidzakhale dziko lapansi? Mukam’dziŵa Yehova ndi zimene amafuna mwa kuphunzira mwakhama Mawu ake ndi kuchita zimene mumaphunzira, inunso mungayembekezere kuti choloŵa chanu chidzakhala dziko lapansi la paradaiso ndipo mudzakhalamo kosatha.​—Yohane 17:3.

[Chithunzi patsamba 5]

Timazindikira cholinga cha Mulungu polenga dziko lapansi tikaganizira ntchito imene anapatsa Adamu ndi Hava

[Chithunzi pamasamba 6, 7]

Mtendere ndiponso kukhala mosatekeseka kumene kunalipo panthaŵi ya ulamuliro wa Solomo kunali chitsanzo cha choloŵa chimene Mulungu analonjeza

[Mawu a Chithunzi]

Sheep and background hill: Pictorial Archive (Near Eastern History) Est.; Arabian oryx: Hai-Bar, Yotvata, Israel; farmer plowing: Garo Nalbandian

[Chithunzi patsamba 7]

Kodi inuyo mudzakhalamo m’dziko latsopano lolungama limene lili m’tsogolomu?