Pitani ku nkhani yake

Pitani ku mitu ya nkhani

Mafunso Ochokera kwa Oŵerenga

Mafunso Ochokera kwa Oŵerenga

Mafunso Ochokera kwa Oŵerenga

Kodi n’chifukwa chiyani amuna achiisrayeli ankaloledwa kukwatira akazi achikunja amene awagwira ukapolo ngakhale kuti Chilamulo cha Mose chinali chitanena kuti asakwatirane ndi anthu akunja?​—Deuteronomo 7:1-3; 21:10, 11.

Anali kulola zimenezi pa zifukwa zapadera. Yehova anali atawalamula Aisrayeli kuti awononge midzi ya mitundu isanu ndi iŵiri ya m’dziko la Kanani, n’kupha anthu onse a m’dzikolo. (Deuteronomo 20:15-18) Ponena za mitundu ina, anthu akuluakulu amene akanapulumuka anali anamwali amene awagwira ukapolo. (Numeri 31:17, 18; Deuteronomo 20:14) Mwamuna wachiisrayeli anali kuloledwa kukwatira mkazi ameneyo, pokhapokha ngati mkaziyo wachita kaye zinthu zinazake.

Pa zimene mkaziyo ankafunika kuchita, Baibulo limati: “Ndipo amete tsitsi la pamutu pake, ndi kuwenga makadabo ake; navule zovala za ukapolo wake, nakhale m’nyumba mwanu, nalire atate wake, ndi mayi wake mwezi wamphumphu; ndipo atatero mulowe naye ndi kukhala mwamuna wake, ndi iye akhale mkazi wanu.”​—Deuteronomo 21:12, 13.

Namwali amene wagwidwa ukapolo yemwe Mwisrayeli akufuna kum’kwatira, ankafunika kumeta tsitsi la m’mutu mwake. Kumetako kunkasonyeza kulira kapena kuvutika maganizo. (Yesaya 3:24) Mwachitsanzo, pamene ana onse a kholo lakale Yobu anamwalira komanso chuma chake chonse chitatha, iye anameta tsitsi la m’mutu posonyeza kulira. (Yobu 1:20) Mkazi wachikunjayo ankafunikanso kuwenga makadabo ake, n’cholinga chakuti manja ake asamaoneke okongola ngakhale makadabowo atakhala opentapenta. (Deuteronomo 21:12) Kodi “zovala za ukapolo wake” zimene mkazi amene wagwidwa ukapolo ankafunika kuvula zinali chiyani? Kuvala zovala zabwino kwambiri unali mwambo wa akazi a m’midzi yachikunja imene yatsala pang’ono kugonjetsedwa. Iwo ankachita zimenezi pofuna kutenga mtima anthu owagwirawo. Mkazi amene wagwidwa ukapolo ndiponso amene akulira ankafunika kuvula zovala zimenezo.

Mkazi amene wagwidwa ukapolo yemwe Mwisrayeli amafuna kumukwatira ankafunika kuti kwa mwezi umodzi alire maliro a anthu amene anali kuwakonda. Midzi yogonjetsedwayo ankafunika kuifafaniziratu moti mkaziyo sankakhalanso ndi achibale kapena munthu aliyense amene ankadziŵana naye kale. Popeza asilikali achiisrayeli anali kuwononga mafano a milungu yake, zimene anali kuzigwiritsa ntchito polambira zinkakhala zitawonongedwa. Mwezi umene mkaziyo anali kulira unalinso monga nthaŵi yomuyeretsa imene mkazi wogwidwa ukapolo anali kusiyana ndi zinthu zonse zokhudzana ndi kulambira kwake kwa m’mbuyomo.

Komabe, sizinkakhala choncho ndi akazi onse achikunja. Pankhani ya akazi ameneŵa, ankagwiritsa ntchito mfundo iyi: “Musakwatitsane nawo; musam’patse mwana wake wamwamuna mwana wanu wamkazi, kapena kutenga mwana wake wamkazi akhale wa mwana wanu wamwamuna.” (Deuteronomo 7:3) Kodi n’chifukwa chiyani anawaletsa chonchi? Pa Deuteronomo 7:4 pamati: “Popeza adzapatutsa mwana wanu aleke kunditsata ine, kuti atumikire milungu ina.” Choncho, anawaletsa pofuna kuteteza Aisrayeli kuti asatengere ziphunzitso za zipembedzo zonyenga. Komabe, mkazi wachikunja amene wachita zimene zafotokozedwa pa Deuteronomo 21:10-13 sakanachititsa vuto limeneli. Achibale ake onse anali atafa, ndipo mafano a milungu yake anali atawonongedwa. Analibe anzake achipembedzo chonyenga. Zikatere, Mwisrayeli ankaloledwa kukwatira m’kunja.