Pitani ku nkhani yake

Pitani ku mitu ya nkhani

Kupeza Malangizo Abwino Kwambiri

Kupeza Malangizo Abwino Kwambiri

 Kupeza Malangizo Abwino Kwambiri

MOYO wabwino ndi wofunikadi. Kuti tipeze moyo umenewu m’dziko lovutali, chinsinsi chake chagona pa kupeza ndi kutsatira malangizo abwino. Komabe, nthaŵi zambiri anthu safuna kutsatira malangizo abwino. Anthu ambiri amanena kuti munthu azichita zimene akufuna. Ndipo nkhani ya m’Baibulo imasonyeza kuti Satana, mdani wamkulu wa ulamuliro wa Mulungu, anauza anthu oyambirira kuti angathe kupeza ufulu wochita zofuna zawo. Pa Genesis 3:5 pali zimene Satana ananena kwa Hava kuti: “Adziŵa Mulungu kuti tsiku limene mukadya [mtengo wodziŵitsa zabwino ndi zoipa], adzatseguka maso anu, ndipo mudzakhala ngati Mulungu, wakudziŵa zabwino ndi zoipa.”

Ndiyeno potsatira maganizo awo, kodi Adamu ndi Hava anakhala moyo wabwino, popanda kukumana ndi mavuto aakulu? Ayi ndithu. Nthaŵi yomweyo ananong’oneza bondo chifukwa cha zimene zinawachitikira poganiza molakwa kuti akudziŵa kusiyanitsa chabwino ndi choipa. N’chifukwa chake Mulungu anadana nawo ndipo iwo anayamba moyo wovuta wopanda ungwiro, umene mapeto ake anali imfa. (Genesis 3:16-19, 23) Imfa imakhudza tonsefe. Baibulo limati: “Uchimo unaloŵa m’dziko lapansi mwa munthu mmodzi [Adamu], ndi imfa mwa uchimo; chotero imfa inafikira anthu onse, chifukwa kuti onse anachimwa.”​—Aroma 5:12.

Ngakhale kuti pali mavuto aakulu chifukwa cha zimene Adamu ndi Hava anachita, anthu ambiri sakhulupirirabe kuti kutsatira malangizo a Mulungu, amene analenga anthu, n’chinthu chanzeru. Komabe, Baibulo limati ilo ndi ‘louziridwa ndi Mulungu, ndipo lipindulitsa,’ ndipo lingatithandize kukhala “woyenera, wokonzeka kuchita ntchito iliyonse yabwino.” (2 Timoteo 3:16, 17) Ndithudi tingasangalale kwambiri tikamatsatira malangizo a m’Baibulo. Mfundo imeneyi imathandiza kwambiri makamaka pamoyo wa banja.

Kukhulupirika mu Ukwati

Malinga ndi zimene Baibulo limanena, cholinga cha Mulungu chinali chakuti ukwati usamathe. (Genesis 2:22-24; Mateyu 19:6) Komanso,  Malemba amanena kuti “pogona pakhale posadetsedwa,” kutanthauza kuti ukwati suyenera kuipitsidwa mwa kugonana ndi anthu ena. (Ahebri 13:4) Komabe, mwina mukudziŵa kuti masiku ano maukwati ambiri satsatira mfundo imeneyi. Anthu ena akakhala kuntchito, amakonda kukopana ndi anthu amene si mkazi kapena mwamuna wawo. Ena amanamiza mabanja awo n’cholinga chokasangalala ndi chibwenzi chawo. Ena amafika mpaka posiya mkazi kapena mwamuna wawo kuti akakwatirane ndi wina wachinyamata ndipo amati akachita zimenezi amadzimva kuti akadali achinyamata ndiponso amasangalala, monga zimene zinachitikira Verónica, amene tamutchula m’nkhani yoyamba ija.

Komabe, mtima wongofuna kudzisangalatsa mosaganizira kuti zotsatira zake zikhala zotani, subweretsa chimwemwe chokhalitsa. Ronald akuikira umboni pa mfundo imeneyi. Poganiza kuti moyo wake ukhala wabwinopo, iye anasiya mkazi wake n’kukakwatira mkazi amene anali naye pachibwenzi chobisa kwa zaka sikisi komanso amene anali atam’berekera ana aŵiri. Komabe, patapita nthaŵi chithetsereni ukwati wake uja, chibwenzi chake chija chinam’thaŵira. Mapeto ake Ronald anakakhala ndi makolo ake. Iye anati zimenezi zinali zochititsa manyazi kwambiri. Ichi n’chitsanzo chimodzi chabe. Khalidwe limeneli, lomwe anthu amachita chifukwa chodzikonda, lachititsa kuti anthu osudzulana komanso mabanja opasuka achuluke kwambiri, zimene zikuika pavuto anthu ambirimbiri, ana ndi akulu omwe.

Komabe, kutsatira malangizo a m’Baibulo kumabweretsa chimwemwe chenicheni. Ndi zimene anaona Roberto, amene anati: “Malangizo a m’Baibulo andithandiza kuti ndisasiye mkazi wanga. Kutengeka ndi munthu amene si mkazi kapena mwamuna wathu n’kuchita naye zinthu zosayenera sikungatipatse chimwemwe chenicheni, ngakhale munthuyo atakhala wokongola bwanji. Kuphunzira Baibulo kwandithandiza kukonda mkazi wanga amene ndakhala naye zaka zambiri.” Malangizo a m’Baibulo akuti ‘osachitira monyenga mkazi wa ubwana wako’ anamuthandiza kwambiri Roberto. (Malaki 2:15) Kodi malangizo a Mulungu angatipindulitsenso m’njira zina ziti?

Kulera Ana Athu

M’zaka makumi angapo zapitazo mfundo yakuti makolo azilera ana awo mosawaikira malamulo ambiri inayamba kufala. Zinkaoneka kuti kulola ana kuganiza ndi kuchita zimene akufuna n’kothandiza. Cholinga chinali chakuti asalepheretse ana kukula. M’madera ena, sukulu zina zinakhazikitsa malamulo, amene ena mwa iwo anali kulola ana kusankha kuloŵa kapena kusaloŵa m’kalasi, kuchuluka kwa zosangalatsa zimene akufuna  kuchita ndiponso malangizo amene angamvere. Lamulo la pa sukulu ina yotere linali “lolola ana kuchita zimene akuganiza popanda kudzudzulidwa ndiponso kuuzidwa zochita ndi munthu wamkulu.” Masiku ano, akatswiri ena oona za khalidwe la anthu amakayikira kuti kulanga ana m’njira zinazake n’kopindulitsadi, ngakhale pamene makolo akuona kuti n’kofunika kulanga mwanayo mwachikondi.

Kodi zotsatira zake n’zotani? Pali anthu ambiri amene amaona kuti kulera ana mowalekerera kwawapatsa anawo ufulu wochuluka kwambiri. Iwo akuganiza kuti zimenezi zachititsa kuti upandu ndi kugwiritsa ntchito mankhwala osokoneza bongo kukhale kofala. Pa kafukufuku wina amene anachitika ku United States anapeza kuti pafupifupi anthu 70 pa anthu 100 alionse amene anafunsidwa ankaganiza kuti makolo salangiza ana awo aang’ono ndiponso achinyamata monga mmene anawo amafunikirira. Pankhani ya chifukwa chimene chimapangitsa achinyamata kuwomberana ndi mfuti kusukulu ndiponso kupalamula milandu ina ikuluikulu, ambiri anati n’chifukwa chakuti “makolo amalera ana awo mowalekerera.” Ndipo ngakhale patakhala kuti palibe mavuto aakulu, kulera ana mowalekerera kumapweteketsa anawo komanso makolo.

Kodi Baibulo limati chiyani pankhaniyi? Malangizo a m’Malemba ndi akuti makolo azichita udindo wawo mwachikondi komanso mosalekerera. Baibulo limati: “Utsiru umangidwa mumtima mwa mwana; koma nthyole yom’langira idzauingitsira kutali.” (Miyambo 22:15) N’zoona kuti chilango chilichonse chimene makolo amapereka chiyenera kukhala choyenererana ndi mmene zinthu zilili. Nthaŵi zonse chiziperekedwa mofatsa, modziletsa ndiponso moganizira. Kuchita zimenezi kumasonyeza kuti timamukonda mwanayo. Kaŵirikaŵiri chilango chimakhala ndi zotsatira zabwino makolo akachipereka mwachikondi, osati mokhaulitsa ndi mwankhanza.

Pali umboni wooneka wakuti kutsatira zimenezi kumathandiza. Arturo, bambo wa zaka 30 wa ku Mexico amene anakwatira posachedwapa, anati: “Bambo anga ankatiuziratu, ineyo pamodzi ndi azichimwene anga, kuti iwo ndi amayi ndiwo amene anali ndi mphamvu m’banjamo. Akafuna kutilanga sanali kutinyengerera. Komabe, nthaŵi zonse ankapatula nthaŵi yocheza nafe. Popeza tsopano ndakula, ndimasangalala ndi moyo wabwino umene ndili nawo, ndipo ndimadziŵa kuti zimenezi zatheka makamaka chifukwa cha malangizo abwino amene ndinalandira.”

 Tsatirani Malangizo Abwino Kwambiri

Mawu a Mulungu, Baibulo, ali ndi malangizo abwino kwambiri othandiza anthu. Malangizo ake si abanja okha. Amatithandiza m’njira zambiri chifukwa amatiphunzitsa mmene tingachitire zinthu m’dziko lino, limene anthu ambiri savomereza kuti m’pofunika nzeru zoposa za munthu kuti ziwatsogolere kuti zinthu ziwayendere bwino.

Yehova Mulungu, Mlengi wa anthu, anatitsimikizira kudzera mwa wamasalmo Davide kuti: “Ine ndidzakulangiza ndi kuphunzitsa iwe za njira ukayendayo; ndidzakupangira ndi diso langa lakuyang’ana iwe.” (Salmo 32:8) Tangoganizirani, Mlengi kutiyang’anira n’cholinga chotiteteza ku mavuto. Komabe, funso limene aliyense angadzifunse n’lakuti: ‘Kodi ndizitsatira modzichepetsa malangizo a Yehova amene amateteza?’ Mawu Ake amatiuza mwachikondi kuti: “Khulupirira Yehova ndi mtima wako wonse, osachirikizika pa luntha lako; um’lemekeze m’njira zako zonse, ndipo Iye adzawongola mayendedwe ako.”​—Miyambo 3:5, 6.

Kudziŵa Yehova kumafuna khama ndiponso kudzipereka, komabe anthu akhoza kuchita zimenezi pogwiritsira ntchito Baibulo. Njira ya moyo imene Yehova amatilangiza kuti tiyendemo ‘ili nalo lonjezano la ku moyo uno, ndi la moyo ulinkudza.’ Ndithudi ndi njira yopindulitsa kwambiri tikaona zotsatira zake.​—1 Timoteo 4:8; 6:6.

Ngati mwasangalala ndi luntha la Baibulo ndiponso madalitso amene amabwera chifukwa chotsatira zimenezo, kuŵerenga ndi kusinkhasinkha Mawu a Mulungu kukhale kofunika kwambiri pamoyo wanu. Kuchita zimenezo kuzikuthandizani kuthana bwinobwino ndi mavuto a masiku ano komanso alionse amene ali m’tsogolo. Komanso, kukuthandizani kupeza chiyembekezo chokhala ndi moyo m’dziko latsopano la Mulungu, dziko limene anthu onse adzaphunzitsidwa ndi Yehova ndipo mtendere wawo udzakhala wochuluka.​—Yesaya 54:13.

[Chithunzi patsamba 5]

Malangizo a m’Baibulo angalimbitse ukwati

[Zithunzi patsamba 6]

Malangizo a m’Baibulo ndiwo malangizo abwino kwambiri, komanso amalola munthu kusangalala

[Zithunzi patsamba 7]

Anthu amene amatsatira malangizo a m’Baibulo amakhala ndi moyo wabwino