Pitani ku nkhani yake

Pitani ku mitu ya nkhani

kodi zozizwitsa za yesu zinali zenizeni kapena ndi Nthano Chabe?

kodi zozizwitsa za yesu zinali zenizeni kapena ndi Nthano Chabe?

 kodi zozizwitsa za yesu zinali zenizeni kapena ndi Nthano Chabe?

“ANABWERA nawo kwa iye [Yesu Kristu] anthu ambiri ogwidwa ndi mizimu yoipa; ndipo iye anatulutsa mizimuyo ndi mawu, nachiritsa akudwala onse.” (Mateyu 8:16) “[Yesu] anauka, nadzudzula mphepo, nati kwa nyanja, kuti, Tonthola, khala bata. Ndipo mphepo inaleka, ndipo kunagwa bata lalikulu.” (Marko 4:39) Kodi mumawaona bwanji mawu ameneŵa? Kodi mumakhulupirira kuti amanena zimene zinachitikadi, kapena mumaganiza kuti ndi nkhani zongoyerekezera, nthano chabe?

Anthu ambiri masiku ano amakayikira kwambiri kuti zozizwitsa za Yesu zinachitikadi. Kutsogola kwa sayansi popanga zipangizo monga zoonera zinthu zakutali, zoonera zinthu zazing’ono zimene sitingathe kuziona ndi maso paokha, komanso kumvetsa sayansi yachibadwa cha zinthu, kwapangitsa anthu kusakhulupirira zozizwitsa.

Ena amaona kuti nkhani za zozizwitsa n’zoti sizingachitike kapena kuti n’zongoyerekezera. Malinga ndi zimene ananena wolemba buku lina limene limati limafotokoza za Yesu “weniweni,” nkhani zonena za zozizwitsa za Kristu ndi zongokopa anthu kuti atengeke ndi Chikristu.

Anthu ena amaona zozizwitsa za Yesu kuti ndi chinyengo chokhachokha. Nthaŵi zina amati Yesu weniweniyo anali wachinyengo. Malinga ndi zimene ananena Justin Martyr wa m’zaka za m’ma 100 Kristu Atabwera, otsutsa za Yesu “anafika pomutchula kuti wamatsenga ndi wonyengeza anthu.” Anthu ena amati Yesu  “sanachite zozizwitsa monga mneneri wachiyuda, koma monga wamatsenga amene anakaphunzira ku akachisi achikunja.”

Kodi Akati Chosatheka Amatanthauzanji?

Mungaone kuti kukayikira koteroko, n’kumene makamaka kwapangitsa anthu kusakhulupirira zozizwitsa. Amaona kuti n’zovuta, kapena n’zosatheka kumene kukhulupirira kuti zolengedwa zauzimu zingachite zozizwitsa zimenezi. Mnyamata wina amene ankati amakayikira kuti kuli Mulungu anati: “Tisamanamizane, kulibe zozizwitsa.” Ndiyeno anagwira mawu a David Hume, yemwe anali wafilosofi wa ku Scotland zaka za m’ma 1700, amene analemba kuti: “Zozizwitsa zimatsutsana ndi mmene chilengedwe chilili.”

Komabe, anthu ambiri sangafulumire kukaniratu kuti chinthu chinachake chodabwitsa sichingachitike. Buku lakuti The World Book Encyclopedia limati chozizwitsa ndi “chinthu chimene sitingachimvetse kudzera m’zinthu zimene tikudziŵa zokhudza chilengedwe.” Malinga ndi tanthauzo limeneli, kwa anthu ambiri zaka 100 zokha zapitazo, kuyenda ndi zombo mlengalenga, kugwiritsa ntchito zinthu monga mawailesi ndiponso njira zapamwamba zimene oyendetsa ndege kapena sitima za pamadzi amadziŵira kumene akuloŵera zikanakhala ngati “zozizwitsa.” Ndithudi si nzeru kunena kuti zozizwitsa sizingachitike chifukwa chakuti sitingazimvetse malinga ndi zimene tikudziŵa panopa.

Tikapenda umboni wina wa m’Malemba wokhudza zozizwitsa za Yesu Kristu, kodi timapeza zotani? Kodi zozizwitsa za Yesu zinali zenizeni kapena ndi nthano chabe?