Pitani ku nkhani yake

Pitani ku mitu ya nkhani

Mafunso Ochokera kwa Oŵerenga

Mafunso Ochokera kwa Oŵerenga

 Mafunso Ochokera kwa Oŵerenga

Kodi “osakhulupira” amene Paulo anawatchula pa 2 Akorinto 6:14 ndi ndani?

Pa 2 Akorinto 6:14 timaŵerenga kuti: “Musakhale omangidwa m’goli ndi osakhulupira osiyana.” Tikaona nkhani yonse imene mukupezeka lembali, zikuonekeratu kuti Paulo anali kunena za anthu amene ndi odziŵika bwino kuti sali mumpingo wachikristu. Izi zikugwirizana ndi mavesi ena a m’Baibulo mmene Paulo anagwiritsa ntchito mawu akuti “wosakhulupira” kapena “osakhulupira.”

Mwachitsanzo, Paulo anadzudzula Akristu chifukwa chosumirana milandu “kwa osakhulupira.” (1 Akorinto 6:6) Apa, osakhulupiriraŵa anali oweruza milandu m’makhoti a ku Korinto. M’kalata yake yachiŵiri, Paulo ananena kuti Satana ‘anachititsa khungu maganizo awo a osakhulupirira.’ Maso a anthu osakhulupirirawo ‘anaphimbidwa’ kuti asaone uthenga wabwino. Osakhulupirira ameneŵa ndi anthu amene sanasonyeze chidwi chilichonse chofuna kutumikira Yehova, popeza Paulo asananene zimenezi anafotokoza kuti: “Koma pamene akatembenukira kwa Mulungu, chophimbacho chichotsedwa.”​—2 Akorinto 3:16; 4:4.

Osakhulupirira ena amachita zinthu zosokoneza kapena amalambira mafano. (2 Akorinto 6:15, 16) Koma sikuti ndi onse amene amadana ndi atumiki a Yehova. Ena ali ndi chidwi ndi choonadi. Ambiri ali ndi akazi kapena amuna amene ndi Akristu ndipo akusangalala kukhala nawo pabanja. (1 Akorinto 7:12-14; 10:27; 14:22-25; 1 Petro 3:1, 2) Komabe, nthaŵi zonse Paulo anali kugwiritsa ntchito mawu akuti “wosakhulupira” ponena za anthu amene, monga tatchulira kale, sali mumpingo wachikristu, umene umakhala ndi anthu ‘okhulupirira Ambuye.’​—Machitidwe 2:41; 5:14; 8:12, 13.

Mfundo ya pa 2 Akorinto 6:14 ndi yothandiza kwambiri kwa Akristu pa mbali zosiyanasiyana m’moyo wawo ndipo yakhala ikugwiritsidwa ntchito kaŵirikaŵiri monga malangizo anzeru kwa Akristu amene akufunafuna munthu womanga naye banja. (Mateyu 19:4-6) Mkristu wodzipatulira ndi wobatizidwa, mwanzeru safunafuna munthu amene angamange naye banja pakati pa osakhulupirira, chifukwa chakuti mfundo zimene osakhulupirira amatsatira m’moyo wawo, zolinga zawo, ndi zikhulupiriro zawo n’zosiyana kwambiri ndi za Mkristu woona.

Koma bwanji za anthu amene akuphunzira Baibulo ndipo amasonkhana ndi mpingo wachikristu? Bwanji za ofalitsa osabatizidwa? Kodi ameneŵa n’ngosakhulupirira? Ayi. Anthu amene alabadira choonadi cha uthenga wabwino ndipo akupita patsogolo moti angabatizidwe sayenera kutchedwa osakhulupirira. (Aroma 10:10; 2 Akorinto 4:13) Korneliyo asanabatizidwe anali kutchedwa “munthu wopembedza, ndi wakuopa Mulungu.”​—Machitidwe 10:2.

Motero, kodi chingakhale chinthu chanzeru kuti Mkristu wodzipatulira afune kukhala pa chibwenzi ndi kumanga banja ndi munthu amene wavomerezedwa kukhala wofalitsa wosabatizidwa, popeza kuti, kwenikweni malangizo a Paulo a pa 2 Akorinto 6:14 satanthauza anthu ngati iyeyo? Ayi, sichinthu chanzeru kutero. Chifukwa chiyani? Chifukwa cha malangizo osapita m’mbali amene Paulo anapereka okhudza akazi amasiye achikristu. Paulo analemba kuti: ‘Ali womasuka, kuti akwatiwe naye amene afuna, koma mwa Ambuye.’ (1 Akorinto 7:39) Mogwirizana ndi malangizo amenewo, Akristu odzipatulira akulimbikitsidwa kufunafuna omanga nawo banja pakati pa anthu okhawo amene ali “mwa Ambuye.”

Kodi mawu akuti “mwa Ambuye” ndiponso mawu ena ofanana nawo akuti “mwa Kristu,” amatanthauza chiyani? Paulo analankhula za anthu amene anali “mwa Kristu” kapena “mwa Ambuye” pa Aroma 16:8-10 ndi Akolose 4:7. Mukaŵerenga mavesi ameneŵa  muona kuti anthuŵa ndi ‘antchito anzathu,’ ‘ovomerezedwa,’ ‘abale okondedwa,’ ‘atumiki okhulupirika,’ ndiponso ‘akapolo anzathu.’

Kodi ndi liti pamene munthu amakhala ‘kapolo mwa Ambuye’? Izi zimachitika pamene iye modzipereka achita zimene kapolo amafunika kuchita ndi kudzikana yekha. Yesu anafotokoza kuti: “Ngati munthu afuna kudza pambuyo panga, adzikane yekha, natenge mtanda wake, nanditsate Ine.” (Mateyu 16:24) Munthu amayamba kutsata Kristu ndi kudzipereka yense kuchita chifuniro cha Mulungu akadzipatulira kwa Mulungu. Kenako, amadzipereka kuti abatizidwe ndi kukhala mtumiki woikidwa amene Yehova Mulungu amamuyanja. * Motero, ‘kukwatiwa mwa Ambuye’ kukutanthauza kukwatira kapena kukwatiwa ndi munthu amene wasonyeza kuti alidi wokhulupirira, “kapolo [wodzipatulira] wa Mulungu ndi wa Ambuye Yesu Kristu.”​—Yakobo 1:1.

Timayamikira kwambiri munthu amene akuphunzira Baibulo ndi Mboni za Yehova ndipo akupita patsogolo kwambiri mwauzimu. Komabe, iye sanadzipatulire kwa Yehova ndi kudzipereka kuti amutumikire ndi mtima wonse komanso modzimana. Panthaŵiyi amakhala akusinthabe zinthu zomwe akufunika kusintha. Amayenera kutsiriza kaye kusintha kwambiri moyo wake kuti akhale Mkristu wodzipatulira ndi wobatizidwa asanayambe kuganizira zosinthanso chinthu china chachikulu m’moyo wake, monga kuloŵa m’banja.

Kodi kungakhale koyenera kuti Mkristu akhale pa chibwenzi ndi munthu amene akuoneka kuti akupita patsogolo kwambiri pophunzira Baibulo, mwinamwake ali ndi cholinga chomudikirira kuti adzakwatirane atabatizidwa? Ayi. Zolinga za munthu wophunzira Baibuloyo zingasokonezeke kwambiri ngati wazindikira kuti Mkristu wina wodzipatulira akufuna kudzamanga naye banja, koma adzatero pokhapokha iye akabatizidwa.

Nthaŵi zambiri, munthu amakhala wofalitsa wosabatizidwa kwa nthaŵi yochepa, kufikira atayenerera kubatizidwa. Motero, malangizo ali pamwambaŵa, okwatira mwa Ambuye, si okhwimitsa zinthu kwambiri. Nanga bwanji za kukhala pa chibwenzi ndi munthu amene ali wausinkhu wokhala pabanja, anakulira m’banja lachikristu, wakhala wachangu mu mpingo kwa zaka zingapo, ndipo ndi wofalitsa wosabatizidwa? Ngati ndi choncho, kodi n’chiyani chikumulepheretsa kupereka moyo wake kwa Yehova mwa kudzipatulira? N’chifukwa chiyani akuchedwachedwa? Kodi pali zimene amakayikira? Ngakhale kuti si munthu wosakhulupirira, koma sitinganene kuti ali “mwa Ambuye.”

Malangizo a Paulo okhudza ukwati ndi opindulitsa ife tomwe. (Yesaya 48:17) Anthu amene akuyembekezera kukwatirana akakhala kuti anadzipatulira kwa Yehova, kudzipereka kwawo kwa wina ndi mnzake mu ukwati kumakhala ndi maziko olimba ndiponso auzimu. Mfundo zimene amatsatira m’moyo wawo zimakhala zofanana ndiponso amakhala ndi zolinga zofanana. Izi zimathandiza kwambiri kuti ukwati ukhale wosangalatsa. Kuwonjezera pamenepo, munthu ‘akakwatiwa mwa Ambuye’ amasonyeza kuti ndi wokhulupirika kwa Yehova, ndipo zimenezo zimam’bweretsera madalitso amuyaya, chifukwa chakuti “kwa wokhulupirika [Yehova] amakhala wokhulupirika.”​—Salmo 18:25, NW.

[Mawu a M’munsi]

^ ndime 10 Kwa Akristu odzozedwa omwe Paulo anawalembera kalatayi poyambirirapo, kukhala ‘kapolo mwa Ambuye’ kunkaphatikizaponso kudzozedwa monga ana a Mulungu ndiponso abale a Kristu.

[Chithunzi patsamba 31]

“Kwa wokhulupirika [Yehova] amakhala wokhulupirika”