Pitani ku nkhani yake

Pitani ku mitu ya nkhani

Omaliza Maphunziro a Gileadi Apita Kukagwira Mwakhama Ntchito Yotuta!

Omaliza Maphunziro a Gileadi Apita Kukagwira Mwakhama Ntchito Yotuta!

 Omaliza Maphunziro a Gileadi Apita Kukagwira Mwakhama Ntchito Yotuta!

“ZOTUTA zichulukadi koma antchito ali oŵerengeka. Chifukwa chake pempherani Mwini zotuta kuti akokose antchito kukututa kwake.” (Mateyu 9:37, 38) Mawu amaneŵa anali ndi tanthauzo lapadera kwa anthu omwe anamaliza maphunziro awo a kalasi ya nambala 116 ya Sukulu ya Gileadi ya Watchtower Yophunzitsa Baibulo, pamene anali kukonzekera kupita ku magawo awo a ntchito yaumishonale.

Loŵeruka, pa March 13, 2004, anthu 6,684 anasonkhana kaamba ka mwambo wokondwerera kumaliza maphunzirowo pa Likulu la Maphunziro a Watchtower ku Patterson, mu mzinda wa New York, ndiponso m’malo ena omwe anaonetsa mwambowu pa TV. Pamwambowu, anthu omwe anamaliza maphunzirowo analandira mawu otsanzikirana nawo omwe anali owalimbikitsa kwambiri. Tonsefe tingapindule ndi malangizo amene anaperekedwawo pamene tikugwira mwakhama ntchito yotuta mwauzimu.

Mawu oyamba omwe anaperekedwa ndi Theodore Jaracz, wa m’Bungwe Lolamulira amenenso anaphunzira m’kalasi ya nambala seveni ya Gileadi, anaunika mawu a Yesu akuti: “Mukani, phunzitsani anthu a mitundu yonse.” (Mateyu 28:19, 20) Mawuŵa analidi oyenerana ndi mwambowu, chifukwa chakuti omaliza maphunzirowo anatumizidwa kukatumikira m’mayiko 20! Iye anakumbutsa ophunzirawo kuti malangizo a m’Mawu a Mulungu awakonzekeretsa bwino kwambiri kukagwira mwakhama ntchito yofunika kwambiri ya kututa kwauzimu.​—Mateyu 5:16.

Mmene Angagwirire Mopindulitsa Ntchito Yotuta

Wokamba nkhani yoyamba pa mwambowo anali Robert Wallen, amene wakhala akugwira ntchito zina zokhudzana ndi Sukulu ya Gileadi kwa zaka zambiri. Pokamba nkhani yakuti “Khalidwe Labwino la Chifundo,” iye anauza ophunzirawo kuti: “Chifundo ndi chinenero chimene ngakhale anthu osamva angathe kumva ndiponso ngakhale anthu osaona angathe kuchiona.” Yesu ankadziŵa bwino kwambiri mavuto a ena ndipo ankayesetsa kuthetsa mavutowo. (Mateyu 9:36) Ophunzirawo adzapeza mipata yambiri yochitira chimodzimodzi, pamene ali m’ntchito yolalikira, mu mpingo, pa nyumba za amishonale, ndi m’mabanja mwawo. Wokamba nkhaniyo analimbikitsa kuti: “Lolani khalidwe labwino la chifundo kuonekera mosavuta m’moyo wanu pamene mukutumikira ena. Khalidwe lanu labwino n’lokhalo lomwe likakuthandizeni pamoyo wanu watsiku ndi tsiku pa nyumba ya amishonale. Motero, khalani ofunitsitsa kuvala chifundo.”​—Akolose 3:12.

Kenako Gerrit Lösch, wa m’Bungwe Lolamulira yemwenso anaphunzira m’kalasi ya nambala 41 ya Gileadi, anakamba nkhani yakuti “Obukitsa Chipulumutso.” (Yesaya 52:7) Kuti anthu adzapulumuke pa kuwonongedwa kwa dzikoli, iwo ayenera kudziŵa mfundo zolondola za m’Mawu a Mulungu, avomereze kapena kuti alengeze poyera chikhulupiriro chawocho, kenaka n’kubatizidwa. (Aroma 10:10; 2 Timoteo  3:15; 1 Petro 3:21) Komabe, chifukwa chachikulu chobukitsira chipulumutso si kupulumutsa anthu koma kuti Mulungu atamandidwe. Chotero, Mbale Lösch analimbikitsa anthu oyembekezera kukhala amishonalewo kuti: “Pitani ndi uthenga wa Ufumu ku malekezero a dziko lapansi, ndipo chitani khama pobukitsa chipulumutso, kuti Yehova atamandidwe.”​—Aroma 10:18.

“Kodi Ndinu Woŵala Motani?” ndilo linali funso limene mlangizi wa Gileadi, Lawrence Bowen, anadzutsa. Iye ananena za mawu a Yesu a pa Mateyu 6:22 ndi kulimbikitsa omaliza maphunzirowo kukhala ndi diso “lakumodzi” kuti athe “kusonyeza kuunika kwauzimu kumene kumalemekeza Yehova ndiponso kumapindulitsa anthu anzathu.” Kungochokera poyambirira pa utumiki wake, Yesu anasonyeza chitsanzo chabwino kwambiri pankhaniyi mwa kuika maganizo ake pa kuchita chifuniro cha Mulungu. Kusinkhasinkha zinthu zosangalatsa zimene Atate wake anam’phunzitsa kumwamba kunathandiza Yesu kupirira ziyeso za Satana m’chipululu. (Mateyu 3:16; 4:1-11) Yesu anadalira Yehova ndi mtima wonse pamene ankachita zimene Mulungu anamuuza kuti achite. N’chimodzimodzinso ndi amishonalewo. Kuti adzathe kupirira ziyeso zimene adzakumane nazo, iwo ayenera kupitiriza kukhala ndi chizoloŵezi chabwino cha kuphunzira Baibulo ndiponso kudalira Yehova ndi mtima wonse.

Mark Noumair, mlangizi wa Gileadi yemwenso  anaphunzira m’kalasi ya nambala 77 ya Gileadi, anakamba nkhani yomaliza pamndandanda wa nkhanizi, yomwe inali ndi mutu wakuti “Taonani, Tili M’dzanja Lanu.” (Yoswa 9:25) Iye analimbikitsa ophunzirawo kutsanzira mtima wa Agibeoni akale. Ngakhale kuti mudzi wa Gibeoni unali “mudzi waukulu, . . . ndi amuna ake onse ndiwo amphamvu,” Agibeoni sanafune kutchuka kapena kuyembekezera kukhala ndi zinthu malinga ndi zofuna zawo. (Yoswa 10:2) Iwo anatumikira mosanyinyirika monga ‘otema nkhuni, ndi otunga madzi’ moyang’aniridwa ndi Alevi pothandizira pa kulambira Yehova. (Yoswa 9:27) Tinganene kuti, omaliza maphunzirowo anauza Yoswa Wamkulu, Yesu Kristu, kuti “Taonani, ife tili m’dzanja lanu.” Tsopano, pamene akupita kumagawo awo kumayiko ena, akufunika kuvomera ntchito iliyonse imene Yoswa Wamkulu angawapatse.

Zokumana Nazo ndi Mafunso

“Tsegulani Malemba Bwinobwino” ndiwo unali mutu wa zimene Wallace Liverance, amene anaphunzira m’kalasi ya nambala 61 ya Gileadi ndiponso ndi mmodzi wa alangizi a sukuluyi, anakambirana ndi kagulu ka ophunzirawo. Ophunzirawo anafotokoza ndi kuchita zitsanzo za zinthu zimene zinawachitikira mu utumiki wakumunda panthaŵi ya sukuluyo. Zinali zoonekeratu kuti ophunzirawo anakhudzidwa mtima ndi zinthu zozama zimene anaphunzira m’Malemba m’kati mwa miyezi isanu ya sukuluyo ndiponso analimbikitsidwa kufotokozera ena zinthu zimene anali kuphunzirazo. (Luka 24:32) M’kati mwa maphunziro a miyezi isanuwo, wophunzira wina anatha kufotokozera mng’ono wake zinthu zimene anali kuphunzira. Izi zinalimbikitsa mng’ono wakeyo kuti afufuze mpingo wa m’dera lakwawo ndi kuyamba kuphunzira Baibulo nayenso. Tsopano, iye anayenerera kukhala wofalitsa wosabatizidwa.

Pambuyo poti ophunzirawo alongosola zimene anakhala akukumana nazo, Richard Ashe ndi John Gibbard anafunsa anthu angapo amene akhala akutumikira Yehova mokhulupirika kwa nthaŵi yaitali, kuphatikizaponso oyang’anira oyendayenda amene anali kuchita maphunziro apadera pa Likulu la Maphunziro a Watchtower. Anthu ameneŵa anali amene anaphunzira m’makalasi oyambirira a Sukulu ya Gileadi. Mmodzi mwa ofunsidwawo anafotokoza kuti Mbale Knorr ananena izi panthaŵi ya maphunziro a kalasi yawo: “Kuno ku Gileadi mukhala mukuphunzira kwambiri. Koma ngati muchoka kuno ndi mtima wodzitukumula, ndiye kuti talephera ntchito yathu. Tikufuna kuti muchoke kuno ndi mtima wowoloŵa manja.” Abale oyendayendawo analangiza ophunzirawo kuti azidera nkhaŵa anthu ndi zofuna zawo, azikhala ndi anthu monga momwe Kristu ankakhalira nawo, ndiponso azivomera modzichepetsa ntchito iliyonse imene apatsidwa. Mosakayikira, kugwiritsa ntchito malangizo ameneŵa kukathandiza amishonale atsopanowo kukhala aphindu pantchito yawo.

Pitani Kukagwira Mwakhama Ntchito Yotuta!

Omvera anali ndi mwayi womvetsera nkhani ya Mbale Stephen Lett, yemwenso ndi wa m’Bungwe Lolamulira. Iye anakamba nkhani yaikulu pa mwambowo, yamutu wakuti “Pitani Kukagwira Mwakhama Ntchito Yotuta!” (Mateyu 9:38) Pa kututa kwenikweni, nyengo yokolola imakhala yaifupi. Pamafunika kuti anthu okolola agwire ntchito yawo mwakhama. Ndiye kuli bwanji ndi mapeto a dziko ili! Pantchito yaikulu yotuta mwauzimu, miyoyo ndiyo ifunika kupulumutsidwa. (Mateyu 13:39) Mbale Lett analimbikitsa omaliza maphunzirowo kuti asakakhale ‘aulesi m’machitidwe awo,’ koma akakhale “achangu mumzimu” ndi ‘kutumikira Ambuye’ pantchito imeneyi yomwe sidzabwerezedwanso. (Aroma 12:11) Wokamba nkhaniyo anagwira mawu a Yesu, akuti: “Kwezani maso anu, nimuyang’ane m’minda, kuti mwayera kale kufikira kumweta.” (Yohane 4:35) Kenako analimbikitsa omaliza maphunzirowo kuti akasonyeze khama lawo pantchito yotuta mwa kuyesetsa kufikira anthu panthaŵi ndi pamalo amene angapezeke ndiponso mwa kugwiritsa ntchito mwayi uliwonse womwe angapeze wochita ulaliki wamwamwayi. Pokhala tcheru kuti tikonze mpata wolalikira tingathe kupereka umboni wogwira mtima. Yehova ndi Mulungu wachangu kapena kuti wakhama, ndipo amayembekezera tonsefe kutengera chitsanzo chake ndi kugwira mwakhama ntchito yotuta mwauzimu.​—2 Mafumu 19:31; Yohane 5:17.

Pamapeto pake, tcheyamani wa mwambowo, Mbale Jaracz, anapereka moni wochoka ku maofesi ambirimbiri a nthambi za Mboni za Yehova ndi kupatsa ophunzirawo madipoloma awo. Mmodzi mwa omaliza maphunzirowo anaŵerenga kalata imene kalasiyo inalemba, yoyamikira kwambiri zinthu zimene anaphunzira. N’zoonekeratu kuti mwambo wokondwerera kumaliza maphunziro a kalasi ya nambala 116 unathandiza onse omwe anamvetsera kutsimikiza mtima kwambiri kuti akagwire mwakhama ntchito yotuta.

[Bokosi patsamba 25]

ZIŴERENGERO ZA KALASI

Chiŵerengero cha mayiko kumene ophunzira anachokera: 6

Chiŵerengero cha mayiko kumene anawatumiza: 20

Chiŵerengero cha ophunzira: 46

Avareji ya zaka zakubadwa: 34.2

Avareji ya zaka zimene akhala m’choonadi: 17.2

Avareji ya zaka zimene akhala mu utumiki wa nthaŵi zonse: 13.9

[Chithunzi patsamba 26]

Kalasi ya 116 ya Omaliza Maphunziro a Sukulu ya Gileadi ya Watchtower Yophunzitsa Baibulo

Pa m’ndandanda umene uli pansipa, mizera yayambira kutsogolo kupita kumbuyo, ndipo mayina tawandandalika kuyambira kumanzere kupita kumanja mumzera uliwonse.

(1) Ceansu, R.; Sparks, T.; Piña, C.; Turner, P.; Cheney, L. (2) Suardy, M.; Sjöqvist, Å.; Amadori, L.; Smith, N.; Jordan, A.; Boissonneault, L. (3) Matlock, J.; Ruiz, C.; Dular, L.; Vigneron, M.; Henry, K. (4) Sjöqvist, H.; Laux, J.; Ruzzo, J.; Gustafsson, K.; Boissonneault, R.; Jordan, M. (5) Henry, D.; Turner, D.; Kirwin, S.; Florit, K.; Ceansu, S. (6) Amadori, S.; Cheney, J.; Ross, R.; Nelson, J.; Ruiz, J.; Vigneron, M. (7) Florit, J.; Matlock, D.; Ross, B.; Laux, C.; Ruzzo, T.; Dular, D.; Kirwin, N. (8) Gustafsson, A.; Nelson, D.; Suardy, W.; Piña, M.; Smith, C.; Sparks, T.