Pitani ku nkhani yake

Pitani ku mitu ya nkhani

Mavuto a Kuphunzitsa Ana Masiku Ano

Mavuto a Kuphunzitsa Ana Masiku Ano

 Mavuto a Kuphunzitsa Ana Masiku Ano

NDI nthaŵi yamadzulo ndithu ndipo mwini lesitilanti ina akukonzekera kutseka lesitilantiyo kuti azipita kunyumba. Kenako mukuloŵa amayi aŵiri ndi mwana wamng’ono ndipo akuitanitsa chakudya. Popeza kuti watopa kwambiri, mwini lesitilantiyo akufuna kuwauza kuti lesitilantiyo watseka, koma kenako akuganiza zowakonzera chakudyacho. Amayiwo ali m’kati mocheza ndiponso kudya chakudyacho, mwana uja akuthamangathamanga m’lesitilantimo, n’kumagwetseramo mabisiketi ndi kuwapondaponda. M’malo momuletsa mwanayo, amayi ake akungomwetulira. Makasitomalawo atachoka, mwini lesitilantiyo yemwe watheratu n’kutopa akuyenera kusesamo.

Muyenera kuti mukudziŵa kuti zinthu ngati zimenezi zomwe zimachitikadi zikusonyeza kuti m’mabanja ambiri, ntchito yophunzitsa ana sikuyenda bwino kwenikweni. Pali zifukwa zosiyanasiyana zimene zikuchititsa zimenezi. Makolo ena amalekerera ana awo kuti azingochita zofuna zawo, poganiza kuti ana ayenera kupatsidwa ufulu wochita zimene mtima wawo ukulakalaka. Kapena chifukwa chotanganidwa kwambiri, makolo sangapeze nthaŵi yowayang’anira bwino anawo ndiponso kuwaphunzitsa zinthu zofunikira. Makolo ena amaganiza kuti maphunziro a ana awo ndiwo chinthu chofunika kwambiri, motero amapatsa anawo ufulu wonse malinga ngati akukhoza bwino kusukulu ndiponso ngati aloledwa kukaphunzira ku koleji yapamwamba.

Komabe ena amanena kuti makolo ndiponso anthu ena onse akufunika kusintha mfundo zimene amatsatira pamoyo wawo. Amatero, chifukwa chakuti amati ana masiku ano akukhudzidwa ndi mitundu yosiyanasiyana ya zauchigaŵenga komanso ziwawa zochitika kusukulu zikuwonjezeka tsiku ndi tsiku. Motero, mkulu wa pa sukulu ina ya pulayimale mu mzinda wa Seoul, m’dziko la Korea, anatsindika kufunika koyamba kuphunzitsa kaye ana khalidwe. Iye anati: “Munthu amafunika kumuphunzitsa kaye khalidwe, kenaka n’kumuthandiza kudziŵa zinthu.”

Makolo ambiri amene amafuna kuti ana awo adzapite ku koleji ndi kuti zinthu zidzawayendere bwino m’moyo, salabadira chenjezo lililonse. Ngati ndinu kholo, kodi mukufuna kuti mwana wanu adzakhale munthu wotani? Kodi mukufuna kuti akadzakula adzakhale munthu wakhalidwe ndi wochita zinthu mwachikulu? Adzakhale munthu woganizira ena, wopanda liuma, ndiponso wolimbikitsa ena? Ngati ndi choncho, ŵerengani nkhani yotsatirayi.